Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Makhalidwe a Yehova Ndi Amtengo Wapatali

Makhalidwe a Yehova Ndi Amtengo Wapatali

“Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.”—AEF. 5:1.

1. (a) Kodi ndi makhalidwe ati a Yehova amene angabwere msanga m’maganizo mwa Akhristu? (b) Kodi kuphunzira za makhalidwe a Yehova kungatithandize bwanji?

KODI ndi makhalidwe a Yehova ati amene amabwera msanga m’maganizo mwanu? Ambirife timaganizira kwambiri za chikondi, chilungamo, nzeru ndi mphamvu. Koma timadziwa kuti Yehova ali ndi makhalidwe abwino ambiri. Mabuku athu afotokozapo makhalidwe a Yehova oposa 40. Choncho tikhoza kuphunzira patokha kapena ndi banja lathu zinthu zosangalatsa zambiri zokhudza makhalidwe a Yehova. Kodi kuchita zimenezi kungatithandize bwanji? Kungatithandize kudziwa bwino ndiponso kuyamikira kwambiri Atate wathu wakumwamba. Ndiyeno tidzafunitsitsa kwambiri kukhala naye pa ubwenzi ndiponso kumutsanzira.—Yos. 23:8; Sal. 73:28.

2. (a) Fotokozani zimene zingatithandize kuti tizikonda kwambiri makhalidwe a Yehova. (b) Kodi tikambirana chiyani?

2 Kuti tione kuti chinthu chinachake ndi chamtengo wapatali kwambiri, timafunika kuchimvetsa n’kuzindikira ubwino wake. Zimenezi zimachitika pang’onopang’ono. Mwachitsanzo, timayamba kukonda chakudya chatsopano tikamva kununkhira kwake kenako n’kuchilawa. Ndiyeno timayamba kuchikonda kwambiri tikamatha kuchiphika tokha. N’chimodzimodzi ndi makhalidwe a Yehova. Tikamaphunzira za makhalidwe ake, kuwaganizira ndiponso kuwatsanzira, timayamba kuwakonda ndiponso kuwaona kuti ndi amtengo wapatali. (Aef. 5:1) Nkhani ino komanso ziwiri zotsatira zitithandiza kukonda kwambiri makhalidwe a Mulungu amene mwina sabwera msanga m’maganizo mwathu. Pokambirana khalidwe lililonse, tiziona mmene Yehova amalisonyezera ndiponso zimene tingachite kuti timutsanzire.

 YEHOVA AMATHANDIZA ANTHU KUTI AZIMASUKA NAYE

3, 4. (a) Kodi inuyo mumamasuka ndi munthu wotani? (b) Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu kuti azimasuka naye?

3 Choyamba, tiyeni tikambirane zimene zimathandiza anthu kumasuka ndi munthu wina. Kodi inuyo mumamasuka kulankhula ndi munthu wotani? Mwina mungayankhe kuti mumamasuka ndi munthu wokoma mtima ndiponso amene amapatula nthawi yocheza ndi ena. Mukhoza kumasuka ndi munthu mutangoona mmene akuonekera, kumva zolankhula zake ndiponso kuona mmene amachitira zinthu.

4 Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu kuti azimasuka naye? Ngakhale kuti iye ndi amene analenga zinthu zonse, amatitsimikizira kuti amafunitsitsa kumva mapemphero athu ndiponso kuwayankha. (Werengani Salimo 145:18; Yesaya 30:18, 19.) Tikhoza kulankhula ndi Yehova pa nthawi iliyonse ndiponso kulikonse. Komanso tingalankhule naye ngakhale kwa nthawi yaitali. Tikhoza kulankhula naye momasuka chifukwa chodziwa kuti sangadandaule. (Sal. 65:2; Yak. 1:5) Mawu a Mulungu amafotokoza Yehova ngati kuti ndi munthu mnzathu. Zimenezi zimathandiza kuti tizimasuka naye. Mwachitsanzo, Davide analemba m’buku la Masalimo kuti “maso a Yehova” ali pa ife ndipo ‘dzanja lake lamanja latigwira mwamphamvu.’ (Sal. 34:15; 63:8) Mneneri Yesaya anayerekezera Yehova ndi m’busa. Analemba kuti: “Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.” (Yes. 40:11) Ndiye tangoganizani. Yehova amafuna kuti timuyandikire ngati mmene kamwana ka nkhosa kamakhalira kakanyamulidwa pachifuwa cha m’busa wachikondi. Izitu zikungosonyeza kuti Yehova amafuna kuti tizimasuka naye. Kodi tingamutsanzire bwanji?

KUMASUKA NDI ANTHU N’KOFUNIKA KWAMBIRI

5. N’chifukwa chiyani mkulu ayenera kukhala wochezeka?

5 Posachedwapa, abale ndi alongo m’mayiko  osiyanasiyana anafunsidwa kuti: “Kodi mumafuna kuti mkulu akhale ndi khalidwe liti?” Pafupifupi onse anayankha kuti: “Azikhala wochezeka.” N’zoona kuti Mkhristu aliyense ayenera kukhala ndi khalidwe limeneli koma ndi lofunika kwambiri kwa akulu. (Yes. 32:1, 2) Mlongo wina anafotokoza kufunika kwa khalidweli ponena kuti: “Ngakhale atakhala ndi makhalidwe ena abwino, mkulu sangatithandize ngati si wochezeka.” Mwina inunso mukuvomereza zimenezi. Koma kodi munthu angatani kuti anthu azimasuka naye?

6. Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti anthu azimasuka naye?

6 Anthu amamasuka ndi munthu amene amawakonda ndiponso kuwaganizira. Mkulu akamakonda anthu ena ndiponso kudzipereka powathandiza, Akhristu onse, ngakhale ana, amaona zimenezi. (Maliko 10:13-16) Mnyamata wina wazaka 12 dzina lake Carlos anati: “Ndimaona akulu mu mpingo wathu akumwetulira ndiponso kuchita zinthu mokoma mtima. Zimenezi zimandisangalatsa kwambiri.” Mkulu sangathe kungonena kuti ndi wochezeka koma ayenera kusonyeza kuti ndi wochezekadi. (1 Yoh. 3:18) Kodi angachite bwanji zimenezi?

7. N’chifukwa chiyani anthu amamasuka kulankhula nafe tikavala baji? Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yovala baji?

7 Posachedwapa, m’bale wina anayenda pa ndege pochokera kudziko lina kumene anakachita msonkhano wachigawo. Iye anavala baji yake yonena kuti “Ufumu wa Mulungu Ubwere.” Munthu wogwira ntchito m’ndegeyo ataona bajiyo, anauza m’baleyo kuti: “Koma ufumuwu ubweredi! Bwanji tikambirane nthawi ina za Ufumuwo?” Nthawi ina anakambiranadi ndipo munthuyo analandira magazini athu. Ambirife takumanapo ndi zinthu ngati zimenezi. N’chifukwa chiyani anthu amamasuka kulankhula nafe tikavala baji? Chifukwa chakuti zimakhala ngati tikuuza anthu kuti amasuke kutifunsa kumene tikupita. Baji ndi chizindikiro chosonyeza kuti timafuna kukambirana ndi anthu zimene timakhulupirira. Nawonso akulu ayenera kupereka zizindikiro zosonyeza kuti anthu akhoza kumasuka nawo. Kodi zizindikiro zake ndi ziti?

8. Kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amakonda anthu? Nanga zimenezi zimathandiza bwanji mpingo?

8 Ngakhale kuti m’mayiko ena zikhalidwe zingasiyane, nthawi zambiri tikamwetulira ndiponso kupereka moni momasuka, timasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu. Kodi ndani ayenera kuyamba kuchita zimenezi? Yesu anapereka chitsanzo pa nkhaniyi. Mateyu anafotokoza kuti Yesu atakumana ndi ophunzira ake, “anayandikira ndi kulankhula nawo.” (Mat. 28:18) Masiku anonso, akulu ayenera kuyamba iwowo kupita pamene pali Akhristu anzawo n’kulankhula nawo. Kodi zimenezi zingathandize bwanji mpingo? Mlongo wina wazaka 88, yemwe ndi mpainiya, anati: “Ndimakonda kwambiri akulu chifukwa chakuti ndikamalowa m’Nyumba ya Ufumu, amandilandira bwino uku akumwetulira ndiponso kundilimbikitsa.” Mlongo wina wokhulupirika anati: “Ngakhale kuti zingaoneke ngati zazing’ono, ndimasangalala kwambiri mkulu akandilandira bwino ndiponso kumwetulira pamene ndafika ku misonkhano.”

MUZIPEZA NTHAWI YOCHEZA NDI ANTHU

9, 10. (a) Kodi Yehova amapereka chitsanzo chotani? (b) Kodi akulu angatani kuti azipeza nthawi yocheza ndi abale ndi alongo?

 9 Koma anthu sangamasuke kulankhula nafe ngati timatanganidwa nthawi zonse. Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Pajatu “iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:27) Misonkhano isanayambe ndiponso ikatha, akulu ayenera  kupatula nthawi kuti azilankhula ndi abale ndi alongo, kaya achikulire kapena achinyamata. M’bale wina amene ndi mpainiya anati: “Ndimasangalala pamene mkulu wafunsa za moyo wanga kenako kuima kuti amvetsere.” Mlongo wina amene wakhala akutumikira Yehova zaka pafupifupi 50 anati: “Ndimamva bwino kwambiri akulu akamapeza nthawi yondilankhula misonkhano ikatha.”

10 N’zoona kuti akulu amakhala ndi zinthu zina zoti achite. Koma ndi bwino kuti akafika pa misonkhano aziyamba kaye alankhulana ndi abale ndi alongo asanayambe zinazo.

YEHOVA ALIBE TSANKHO

11, 12. (a) Kodi munthu wopanda tsankho amatani? (b) Kodi Yehova amapereka chitsanzo chotani pa nkhani ya kupanda tsankho?

11 Khalidwe lina la Yehova labwino kwambiri ndi kupanda tsankho. Munthu wopanda tsankho amachita zinthu mwachilungamo ndiponso mosakondera. Ngakhale mumtima mwake mumakhala mopanda tsankho. Koma ngati munthu ali ndi tsankho mumtima mwake sangathe kuchita zinthu mosakondera. M’Malemba Achigiriki, mawu amene anamasuliridwa kuti “alibe tsankho” kwenikweni amatanthauza kuti “sayang’ana nkhope.” (Mac. 10:34) Choncho munthu amene alibe tsankho saganizira maonekedwe a munthu kapena zinthu zimene ali nazo koma mmene munthuyo alili mumtima mwake.

12 Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Mawu ake amanena kuti iye “alibe tsankho.” (Werengani Machitidwe 10:34, 35; Deuteronomo 10:17.) Tingaone zimenezi tikaganizira zimene zinachitika m’nthawi ya Mose.

Ana aakazi a Tselofekadi anayamikira kuti Mulungu anawathandiza mopanda tsankho (Onani  ndime 13 ndi 14)

13, 14. (a) Kodi ana aakazi a Tselofekadi anakumana ndi vuto liti? (b) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti alibe tsankho?

 13 Aisiraeli atangotsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, atsikana asanu apachibale anali ndi vuto. Iwo ankadziwa kuti banja lawo linafunika kulandira malo a bambo awo ngati mmene zinkakhalira ndi mabanja onse. (Num. 26:52-55) Bambo awo anali a Tselofekadi a fuko la Manase ndipo anali atamwalira. Malinga ndi mwambo wa pa nthawiyo, bambo akamwalira, ana aamuna ndi amene ankayenera kulandira malo. Koma vuto linali lakuti a Tselofekadiwo anali ndi ana aakazi okhaokha. (Num. 26:33) Choncho funso linali lakuti: Popeza m’banjali munalibe mwana wamwamuna, kodi malo awo akanaperekedwa kwa achibale ena n’kusiya ana aakaziwo chimanjamanja?

14 Ana aakazi asanuwo anapita kwa Mose n’kumufunsa kuti: “Kodi dzina la bambo athu lichotsedwe ku banja lawo chifukwa chakuti analibe mwana wamwamuna?” Ndiyeno anachonderera kuti: “Chonde, tipatseni cholowa pakati pa abale awo a bambo athu.” Koma Mose sananene kuti, ‘Kodi mwaiwala zimene  malamulo amanena?’ M’malomwake, “anapereka dandaulo lawolo pamaso pa Yehova.” (Num. 27:2-5) Kodi Yehova anayankha bwanji? Iye anauza Mose kuti: “Ana aakazi a Tselofekadi akunena zoona. Uwapatsedi malo monga cholowa chawo, pakati pa abale a bambo awo. Cholowa cha bambo awocho chikhale chawo.” Koma Yehova sanasiyire pomwepo. Anasintha lamulolo n’kunena kuti: “Mwamuna akamwalira wopanda mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi.” (Num. 27:6-8; Yos. 17:1-6) Kuyambira nthawi imeneyo, akazi onse a ku Isiraeli amene anakumana ndi vuto limeneli ankathandizidwa.

15. (a) Kodi Yehova amachita bwanji zinthu ndi anthu ake, makamaka ovutika? (b) Tchulani nkhani zina za m’Baibulo zosonyeza kuti Mulungu sakondera.

15 Apatu Mulungu anachita zinthu mokoma mtima ndiponso mopanda tsankho. Yehova anachita zinthu ndi akazi ovutikawo mwaulemu ngati mmene ankachitira ndi Aisiraeli ena amene zinthu zinkawayendera bwino. (Sal. 68:5) Pali nkhani zambiri m’Baibulo zosonyeza kuti Yehova sakondera pochita zinthu ndi atumiki ake onse.—1 Sam. 16:1-13; Mac. 10:30-35, 44-48.

N’ZOTHEKA KUTSANZIRA YEHOVA

16. Kodi tingatani kuti tizitsanzira kwambiri Yehova pa nkhani ya kupanda tsankho?

16 Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yochita zinthu mopanda tsankho? Kumbukirani kuti kuchita zinthu mopanda tsankho kumayambira mumtima. Koma anthufe timakonda kuganiza kuti, ‘Aa ine ndilibe tsankho ndipo sindiyang’ana nkhope pochita zinthu.’ Ngakhale zili choncho, mukhoza kuvomereza kuti nthawi zina sitingaone bwinobwino vuto lathu. Ndiyeno kodi tingadziwe bwanji mmene anthu ena amationera pa nkhani imeneyi? Kumbukirani zimene Yesu anachita pofuna kudziwa maganizo a anthu ena. Iye anafunsa anzake amene ankawadalira kuti: “Kodi anthu akumanena kuti Mwana wa munthu ndani?” (Mat. 16:13, 14) Mwina nanunso mungafunse mnzanu amene mukuona kuti sangakubisireni zinthu kuti akuuzeni ngati mumadziwika kuti ndinu wopanda tsankho kapena ayi. Kodi mungatani ngati atakuuzani kuti muli ndi kamtima kokondera anthu amtundu winawake, otchuka kapena achuma? Muyenera kupempha Yehova kuchokera pansi pa mtima kuti akuthandizeni kusintha n’cholinga choti muzimutsanzira kwambiri pa nkhani yochita zinthu mopanda tsankho.—Mat. 7:7; Akol. 3:10, 11.

17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife opanda tsankho?

 17 Akhristufe tiyenera kuyesetsa kutsanzira Yehova pochita zinthu ndi abale ndi alongo athu. Tizichita zinthu mosakondera, mwaulemu komanso mokoma mtima. Mwachitsanzo, tikamaitana anthu kunyumba kwathu, tiziganiziranso anthu osauka, amasiye kapenanso amene tikuona kuti ndi osiyana nafe chikhalidwe. (Werengani Agalatiya 2:10; Yakobo 1:27.) Tikakhala mu utumiki, tiyenera kulalikira anthu onse mopanda tsankho, ngakhale ochokera kumayiko ena. N’zosangalatsa kudziwa kuti panopa mabuku athu amamasuliridwa m’zinenero zoposa 600. Uwutu ndi umboni wamphamvu wakuti gulu lathu lilibe tsankho.

18. Posonyeza kuti mumaona kuti makhalidwe a Yehova amene takambiranawa ndi amtengo wapatali kwambiri, kodi muzichita chiyani?

18 M’nkhaniyi taona kuti Yehova amathandiza anthu kuti azimasuka naye komanso kuti ndi wopanda tsankho. Tikamaganizira mofatsa makhalidwe ake amenewa m’pamene timamuyamikira kwambiri. Zikatero, timafunitsitsa kumutsanzira kwambiri pochita zinthu ndi Akhristu anzathu komanso polalikira.

“Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.”—Sal. 145:18 (Onani  ndime 9)

“Yehova Mulungu wanu . . . alibe tsankho.”—Deut. 10:17 (Onani  ndime 17)