Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WANGA

Ndadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chomvera Yehova

Ndadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chomvera Yehova

Ndimakumbukirabe pamene bambo anga anatiuza kuti: “Nkhani ya Nowa imatiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri. Nowa ankamvera Yehova ndiponso kukonda kwambiri banja lake. Iye limodzi ndi banja lake analowa m’chingalawa ndipo anapulumuka Chigumula.”

BAMBO anga anali munthu wodzichepetsa komanso wakhama. Ankakonda kwambiri chilungamo choncho atamva choonadi cha m’Baibulo mu 1953, anasangalala nacho. Kuyambira nthawi imeneyo, ankayesetsa kutiuza zimene ankaphunzira. Poyamba, mayi anga sankafuna kusiya Chikatolika. Koma patapita nthawi, iwonso anayamba kukonda mfundo za m’Baibulo.

Sizinali zophweka kuti makolo athu azitiphunzitsa. Mayi sankawerenga bwino ndipo bambo ankatanganidwa kwambiri kumunda. Nthawi zina bambo ankatoperatu moti ankasinza pophunzira nafe Baibulo. Koma ankachita khama kwambiri ndipo izi zinatithandiza. Ine ndinali woyamba kubadwa choncho ndinkathandiza kuphunzitsa mng’ono wanga ndi achimwene anga awiri. Ndinkawauzanso zimene bambo ankakonda kutiuza. Ndinkawafotokozera kuti Nowa ankakonda kwambiri banja lake ndiponso ankamvera Mulungu. Nkhani ya Nowayi inkandisangalatsa kwambiri. Pasanapite nthawi, tonse tinayamba kusonkhana ku Nyumba ya Ufumu mumzinda wa Roseto degli Abruzzi, womwe uli m’mphepete mwa nyanja ya Adriatic ku Italy.

Mu 1955, ine ndi mayi anga tinayenda ulendo kudutsa m’mapiri chakumadzulo popita ku msonkhano wachigawo umene unachitika ku Rome. Pa nthawiyo, ndinali ndi zaka 11 zokha ndipo unali msonkhano wathu woyamba. Kuyambira nthawi imeneyo, ndimaona kuti misonkhano yotereyi ndi mbali yosangalatsa kwambiri polambira Mulungu.

Chaka chotsatira, ndinabatizidwa ndipo kenako ndinayamba kuchita upainiya. Pamene ndinali ndi zaka 17, ndinayamba kuchita upainiya wapadera. Ndinatumizidwa kumzinda wa Latina, womwe uli kum’mwera kwa Rome ndipo uli pa mtunda wa makilomita 300 kuchokera kwathu. Popeza kuti mzindawu sunali wakalekale, anthu a kumeneko sankadandaula ndi zimene anthu ena angaganize. Ine ndi mnzanga amene ndinkachita naye upainiya tinkasangalala kugawira mabuku ambiri. Koma popeza ndinali wamng’ono, zinkandivuta kukhala kutali ndi kwathu. Ngakhale zinali choncho, ndinkafunitsitsa kumvera zimene Yehova ankafuna kuti ndizichita.

Pa tsiku la ukwati wathu

Patapita nthawi, anandipempha kupita ku Milan kuti ndikathandize nawo pa ntchito yokonzekera msonkhano wamayiko  wakuti “Uthenga Wabwino Wosatha,” umene unachitika mu 1963. Pa msonkhanowu, ndinadzipereka kugwira ntchito limodzi ndi anthu ena ambiri. Wina amene ndinagwira naye ntchito anali m’bale wachinyamata wa ku Florence, dzina lake Paolo Piccioli. Pa tsiku lachiwiri la msonkhanowu, iye anakamba nkhani yogwira mtima yokhudza ubwino wosalowa m’banja. Ndimakumbukira kuti ndinkaganiza kuti, ‘M’bale ameneyu sadzakwatira basi.’ Koma tinayamba kulemberana makalata ndipo patapita nthawi tinaona kuti timagwirizana pa zinthu zambiri. Tinali ndi zolinga zofanana, tinkakonda kwambiri Yehova ndiponso tinkafunitsitsa kumumvera. Kenako ine ndi Paolo tinakwatirana mu 1965.

TINKAKUMANA NDI AKULUAKULU AKUTCHALITCHI

Ndinachita upainiya wokhazikika mumzinda wa Florence kwa zaka 10. Zinali zosangalatsa kuona mpingo ukukula komanso achinyamata ambiri akuchita bwino. Ine ndi Paolo tinkakonda kukambirana ndi achinyamatawo nkhani zokhudza kulambira Yehova komanso tinkachita nawo zinthu zosangalatsa. Mwachitsanzo, Paolo ankakonda kusewera nawo mpira. Ndinkafunitsitsa kukhala ndi nthawi yambiri yocheza ndi mwamuna wanga. Koma ndinazindikira kuti achinyamatawo komanso mabanja ena mu mpingo ankafunanso kuti azilimbikitsidwa naye.

Ndimasangalalabe ndikaganizira maphunziro a Baibulo ambirimbiri amene tinkachititsa pa nthawiyo. Munthu wina amene ndinkaphunzira naye anali Adriana. Iye ankauza mabanja ena awiri zinthu zimene ankaphunzira. Ndiyeno pa nthawi ina, mabanjawo anakonza zoti tidzakumane ndi wansembe kuti tikambirane zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani yoti pali Mulungu Atate, Mwana ndi Mzimu komanso zoti munthu ali ndi mzimu umene sufa. Tsikulo litafika, kunabwera akuluakulu atatu akutchalitchi. Zimene iwo anafotokoza zinali zosokoneza kwambiri. Anthu amene tinkaphunzira nawo Baibulo anaona mosavuta kuti zimene ankanenazo zinali zosemphana ndi Baibulo. Chifukwa cha zimenezi, patapita nthawi anthu 15 ochokera m’mabanja awiriwo anakhala Mboni.

Kale anthu ankalalikira m’njira yosiyana ndi masiku ano. Paolo ankakumanakumana ndi akuluakulu akutchalitchi moti anafika pokhala katswiri pa nkhani yokambirana nawo. Tsiku lina, anakambirana nawo pamaso pa gulu la anthu omwe sanali Mboni. Atayamba kukambirana, zinadziwika kuti anthu ena anapangana zoti azikafunsa mafunso ongofuna kusokoneza zinthu. Koma zinthu zinasintha. Munthu wina anafunsa ngati zinali zoyenera kuti akuluakulu a matchalitchi azichita nawo zandale ngati mmene akhala akuchitira kwa zaka zambirimbiri. Apa tsopano zinaonekeratu kuti akuluakulu akutchalitchiwo ali pa mpanipani. Ndiyeno tinangodabwa kuti magetsi azima ndipo zokambiranazo zinathera pomwepo. Patapita zaka zambiri, tinamva kuti akuluakulu aja anauziratu  munthu wina kuti adzazimitse magetsi akaona kuti zinthu sizikuwayendera bwino.

KUTUMIKIRA M’NJIRA ZATSOPANO

Titakhala m’banja zaka 10, ine ndi Paolo tinapemphedwa kuti tigwire ntchito yoyang’anira dera. Zinali zovuta kuti tivomere chifukwa Paolo anali pa ntchito yabwino. Koma titapemphera n’kuiganizira bwino nkhaniyi, tinavomera. Titayamba ntchitoyo, tinkasangalala kwambiri kucheza ndi mabanja amene ankatisunga. Nthawi zambiri, tinkaphunzira Baibulo limodzi ndi mabanjawo madzulo. Kenako Paolo ankathandiza ana awo homuweki, makamaka masamu. Paolo ankakondanso kuwerenga ndipo akawerenga zinthu zochititsa chidwi kapena zolimbikitsa, ankatifotokozera. Nthawi zambiri, Lolemba tinkapita kukalalikira kumatauni kumene kunalibe Mboni n’kumaitana anthu kuti adzamvere nkhani ya madzulo.

Tinkakonda kucheza ndi achinyamata ndipo Paolo ankakonda kusewera nawo mpira

Titangotumikira kudera zaka ziwiri, tinaitanidwa kukatumikira ku Beteli ku Rome. Paolo ankatumikira m’dipatimenti yoona zamalamulo ndipo ine ndinali m’Dipatimenti ya Magazini. Patapita nthawi, tinasangalala kwambiri kuona nthambi ikukula komanso ofalitsa akuchuluka m’dziko la Italy. Pa nthawiyi, chipembedzo cha Mboni za Yehova chinavomerezedwa ndi boma la Italy. Sizinali zophweka kuti tichoke kudera n’kuyamba moyo wa pa Beteli, koma tinkayesetsa kukhala omvera ndipo tinayamba kusangalala kwambiri kutumikira ku Beteli.

Paolo ankakonda kwambiri utumiki wake wa pa Beteli

Cha m’ma 1980, pa nthawi imene tinkatumikira pa Beteli, mlandu wina wokhudza Mboni za Yehova unadziwika m’dziko lonse la Italy. Makolo ena amene anali Mboni anaimbidwa mlandu wakuti anaphetsa mwana wawo wamkazi chifukwa sanalole kuti aikidwe magazi. Koma mlanduwu unali wabodza chifukwa mwanayu anafa ndi matenda enaake a magazi omwe ndi ofala kwambiri ku Italy ndi kumayiko ena apafupi. Abale ndi alongo a ku Beteli anathandiza maloya amene ankaimira makolowo. Gulu linasindikiza kapepala ndiponso Galamukani! yapadera n’cholinga choti zithandize anthu kudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya magazi. Pa miyezi imeneyo, Paolo ankagwira ntchito mpaka maola 16 pa tsiku popanda kupuma. Inenso ndinkayesetsa kumuthandiza pa ntchito yofunikayo.

ZINTHU ZINASINTHA PA MOYO WATHU

Titakhala m’banja zaka 20, zinthu zinasinthanso mosayembekezereka. Ndinazindikira kuti ndine woyembekezera ndipo ndinauza mwamuna wanga. Pa nthawiyo, ine ndinali ndi zaka 41 ndipo Paolo anali ndi zaka 49. Pa tsikulo, iye analemba pemphero lake kwa Yehova m’buku limene ankalembamo tsiku ndi tsiku kuti: “Ngati mkazi wanga alidi woyembekezera, tithandizeni kuti tikhalebe akhama n’kupitiriza utumiki wa nthawi zonse. Tithandizeninso kuti tidzakhale zitsanzo zabwino kwa mwana wathu. Koma kwenikweni mundithandize kuti ndiziyesetsa kutsatira zimene ndakhala ndikuphunzitsa papulatifomu  zaka 30 zapitazi.” Panopa ndikuona kuti Yehova anayankha pemphero limeneli.

Zinthu zinasintha kwambiri pamene mwana wathu wamkazi dzina lake Ilaria anabadwa. Kunena zoona, nthawi zina tinkakhumudwa ndipo tinkaona kuti mawu a pa Miyambo 24:10 ndi oona. Lembali limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” Koma tinkalimbikitsana nthawi zonse.

Ilaria amanena kuti amayamikira kuti anabadwira m’banja la makolo amene anali mu utumiki wa nthawi zonse. Amaona kuti makolo akefe tinkamukonda kwambiri ndi kumusamalira bwino. Ine ndinkakhala naye masana onse. Paolo ankafika madzulo kuchokera kuntchito ndipo ankakhalabe ndi ntchito ina yoti agwire. Komabe ankapeza nthawi yocheza naye. Ankasewera naye ndiponso kumuthandiza homuweki. Izi zinkachititsa kuti nthawi zina azigwirabe ntchito yakeyo mpaka cha m’ma 2 kapena 3 koloko m’bandakucha. Ilaria ankakonda kunena kuti, “Mnzanga weniweni ndi bambo anga.”

Kuti tithandize Ilaria kuchita zabwino ndiponso kukonda Yehova, tinkamuphunzitsa mwakhama ndipo nthawi zina tinkafunika kumulanga. Ndikukumbukira kuti tsiku lina iye anafuntha akusewera ndi mnzake. Tinagwiritsa ntchito Baibulo pomufotokozera kuti sanachite bwino. Tinamuuzanso kuti apepese mnzakeyo ife tili pomwepo.

Ilaria amanenanso kuti amakonda utumiki chifukwa chakuti makolo akefe tinkakondanso utumiki. Panopa iye ali pa banja ndipo akumvetsa bwino kwambiri kufunika komvera Yehova ndiponso kutsatira malangizo ake.

KUMVERA MULUNGU NGAKHALE PA MAVUTO

Mu 2008, Paolo anauzidwa kuti ali ndi matenda a khansa. Poyamba, tinkaona kuti Paolo achira matendawa ndipo iye ankandilimbikitsa kwambiri. Tinkayesetsa kupeza thandizo loyenerera la mankhwala komanso ine ndi Ilaria tinkapemphera kwa Yehova kwa nthawi yaitali kuti atithandize kupirira. Koma mwamuna wanga, yemwe poyamba anali munthu wamphamvu, anayamba kufooka pang’ono ndi pang’ono. Kenako iye anamwalira mu 2010 ndipo zinandipweteka kwambiri. Komabe ndimalimbikitsidwa ndikaganizira zimene tachitira limodzi kwa zaka 45 zimene tinali m’banja. Tinachita zonse zomwe tikanatha potumikira Yehova ndipo ndikudziwa kuti Yehova sadzaiwala zimenezi. Tikuyembekezera nthawi imene Paolo adzaukitsidwe, mogwirizana ndi mawu a Yesu a pa Yohane 5:28, 29.

“Nkhani ya Nowa, yomwe ndinkaikonda kwambiri ndili mwana, imandisangalatsabe mpaka pano. Ndimafunabe kumvera Yehova zivute zitani”

Nkhani ya Nowa, yomwe ndinkaikonda kwambiri ndili mwana, imandisangalatsabe mpaka pano. Ndimafunabe kumvera Yehova zivute zitani. Panopa ndaona kuti vuto lililonse limene tingakumane nalo ndi laling’ono kwambiri tikaliyerekezera ndi madalitso osangalatsa amene Mulungu wathu wachikondi amapereka. Pa moyo wanga, ndaona kuti ukamamvera Yehova, zinthu zimakuyendera bwino nthawi zonse.