NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) June 2013

Magaziniyi itithandiza kuti tiziyamikira kwambiri makhalidwe a Yehova omwe amaoneka ngati osafunika kwenikweni tikawayerekezera ndi makhalidwe ake akuluakulu.

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chomvera Yehova

Werengani nkhani ya Elisa Piccioli. Sanataye chikhulupiriro ndipo ankakhala wosangalala ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto, ankadzimana zinthu zina komanso anaferedwa.

Makhalidwe a Yehova Ndi Amtengo Wapatali

Kodi munthu womasuka ndi anthu komanso wopanda tsankho amatani? Kuganizira chitsanzo cha Yehova Mulungu kungatithandize kuti tizisonyeza makhalidwe amenewa.

Yehova Ndi Wowolowa Manja Ndiponso Wololera

Yehova amatipatsa chitsanzo chabwino pa nkhani yowolowa manja komanso kulolera. Kuwerenga za Yehova kungatithandize kuti nafenso tizisonyeza makhalidwe amenewa.

Yehova Ndi Wokhulupirika Ndiponso Amakhululuka

Munthu yemwe ndi mnzathu weniweni amakhala wokhulupirika komanso amakhululuka. Mnzathu weniweni ayenera kukhala ndi makhalidwe abwino monga kukhulupirika komanso kukhululuka. Kutsatira chitsanzo cha Yehova kungatithandize kuti tikhale ndi makhalidwe abwino amenewa.

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, kodi “ana a Mulungu woona” anali ndani? Nanga ”mizimu imene inali m’ndende” ikuimira ndani?

Lolani Kuti Yehova Azikuumbani Ndi Malangizo Ake

Yehova monga ”Wotiumba” amaumba anthu kapena mitundu ya anthu. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimenezi, nanga tingapindule chiyani tikamalola kuti atiumbe masiku ano?

Akulu, Kodi Mumalimbikitsa Anthu ‘Olefuka’?

Kodi akulu Achikhristu amakonzekera bwanji kupanga maulendo a ubusa? Akulu akhoza kulimbikitsa munthu amene wafooka pomupatsa mphatso yauzimu.

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga magazini a Nsanja ya Olonda aposachedwapa? Tayesani kuti muone ngati mukukumbukira zimene munaphunzira.