Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesetsani Kukhala Ngati Wamng’ono

Yesetsani Kukhala Ngati Wamng’ono

“Aliyense wokhala ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.”—LUKA 9:48.

1, 2. Kodi Yesu anapereka malangizo otani kwa atumwi ake ndipo n’chifukwa chiyani?

YESU ali ku Galileya mu 32 C.E., atumwi ake ena anayamba kukangana. Nkhani yake inali yofuna kudziwa amene anali wamkulu. Mu uthenga wake wabwino, Luka analemba kuti: “Iwo anayamba kukhala ndi maganizo ofuna kudziwa amene ali wamkulu koposa pakati pawo. Yesu podziwa zimene anali kuganiza mumtima mwawo, anatenga mwana wamng’ono, n’kumuimika pafupi ndi iye. Ndiyeno anawauza kuti: ‘Aliyense wolandira mwana wamng’ono uyu m’dzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense wolandira ine walandiranso amene anandituma ine. Pakuti aliyense wokhala ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.’” (Luka 9:46-48) Yesu anathandiza atumwi ake moleza mtima koma mosapita m’mbali kuti adziwe kufunika kwa kudzichepetsa.

2 Kodi malangizo a Yesu amenewa ankagwirizana ndi maganizo a Ayuda a pa nthawiyo kapena ayi? Buku lina lofotokoza nkhani za m’Malemba Achigiriki limanena mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Limati: “Pochita chilichonse, anthu ankafuna kudziwa kuti wamkulu ndani. Nthawi zonse ankafuna kupereka ulemu woyenera kwa aliyense.” Choncho Yesu anali kulimbikitsa atumwi ake kuti akhale ndi maganizo osiyana ndi anthu ena onse.

3. (a) Kodi kukhala ngati wamng’ono kumatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani nthawi zina zimativuta kuchita zimenezi? (b) Kodi tingafunse mafunso ati pa nkhani ya kukhala ngati wamng’ono?

3 Mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti “wamng’ono” amanena za munthu wozindikira zimene sangakwanitse, wodzichepetsa, wooneka ngati wachabechabe ndiponso wosalemekezedwa kwenikweni. Yesu anagwiritsa ntchito mwana pophunzitsa atumwi ake kuti ayenera kukhala odzichepetsa. Malangizo amenewa ndi othandizanso kwa Akhristu masiku ano. Nthawi zina zingativute kukhala wodzichepetsa. Anthufe timavutika ndi mtima wofuna kukhala apamwamba. Mzimu wa dziko ndiponso anthu okonda zampikisano amene timakhala nawo angatichititse kukhala odzikuza, amakani, kapena ofuna kuti anthu azingochita zimene ife tikufuna. Koma n’chiyani chingatithandize kukhala ngati wamng’ono? Kodi zingatheke bwanji kuti ‘wamng’ono pakati pathu akhale wamkulu’? Kodi tiyenera kuyesetsa kudzichepetsa pa nthawi ziti?

‘NZERU ZAKE N’ZOZAMA NDIPO NDI WODZIWA ZINTHU KWAMBIRI’

4, 5. N’chiyani chingatithandize kukhala odzichepetsa? Perekani chitsanzo.

4 Chinthu chimodzi chimene chingatithandize kukhala odzichepetsa ndi kuganizira mmene Yehova amatiposera. Ndipotu “palibe amene angadziwe zimene iyeyo amazimvetsa.” (Yes. 40:28) Mtumwi Paulo anachemerera Yehova ponena kuti: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?” (Aroma 11:33) Paulo analemba zimenezi zaka 2,000 zapitazo ndipo chilembereni mawuwa, anthu akhala akuphunzira zinthu zina zambirimbiri. Komabe mfundo ya m’lembali sinasinthe. Ngakhale titadziwa zinthu zochuluka bwanji, pali zinthu zambirimbiri zokhudza Yehova, ntchito zake ndiponso njira zake zimene sitikuzidziwa.

5 Kuzindikira mfundo yoti palibe munthu amene angatulukire njira za Mulungu kunathandiza m’bale wina, dzina lake Leo, * kuti azidziona ngati wamng’ono. Ali mnyamata, Leo ankachita chidwi kwambiri ndi sayansi. Iye ankafunitsitsa kwambiri kudziwa za chilengedwe choncho anaphunzira sayansi ya zakuthambo. Zimenezi zinamuthandiza kuzindikira mfundo yofunika. Iye anati: “Zimene ndinaphunzira kusukulu zinandichititsa kuzindikira kuti anthu sangamvetse chilengedwe pongophunzira zimene asayansi akudziwa panopa. Choncho ndinayamba kuphunzira zamalamulo.” Patapita nthawi, Leo anadzakhala loya woimira boma ndipo kenako woweruza milandu. Ndiyeno iye ndi mkazi wake anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova n’kudzipereka kwa Mulungu. Koma n’chiyani chathandiza Leo kukhala ngati wamng’ono ngakhale kuti waphunzira zambiri komanso wagwira ntchito yapamwamba? Iye anayankha kuti, “Nthawi zonse ndimakumbukira kuti kaya ndiphunzire zotani za Yehova ndi chilengedwe, pali zinthu zambirimbiri zimene sindikuzidziwa.”

6, 7. (a) Kodi Yehova amapereka chitsanzo chotani cha kudzichepetsa? (b) Kodi kudzichepetsa kwa Mulungu kumakweza bwanji munthu?

6 Chinthu china chimene chingatithandize kukhala odzichepetsa n’chakuti nayenso Yehova amadzichepetsa. Mwachitsanzo, Baibulo limati: “Ndife antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Ndiye tangoganizani. Yehova Mulungu, yemwe ndi wapamwamba kuposa aliyense, watilemekeza kwambiri potipatsa mwayi wolalikira uthenga wabwino pogwiritsa ntchito Baibulo, lomwe ndi Mawu ake. Ngakhale kuti Yehova ndi amene amakulitsa mbewu zimene timabzala ndiponso kuthirira, iye amatilemekeza potipatsa mwayi wogwira naye ntchito. (1 Akor. 3:6, 7) Apatu Yehova amasonyeza kudzichepetsa kwambiri. Chitsanzo chakechi chiyenera kutilimbikitsa kuti tizidziona monga aang’ono.

7 Davide anakhudzidwa kwambiri ataona kudzichepetsa kwa Mulungu. Iye anaimbira Yehova kuti: “Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso, ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.” (2 Sam. 22:36) Davide ankaona kuti udindo uliwonse umene anali nawo mu Isiraeli anaupeza chifukwa cha kudzichepetsa kwa Yehova. Zili ngati Mulungu anadzichepetsa n’kutsika m’munsi kuti amuone Davideyo. (Sal. 113:5-7) Izitu n’zimene Yehova amachitanso ndi ifeyo. Kaya tili ndi khalidwe linalake labwino, kaya luso kapena udindo winawake, tizikumbukira kuti ‘tinangochita kulandira’ kuchokera kwa Yehova. (1 Akor. 4:7) Munthu amene amakhala ngati wamng’ono amakhala “wamkulu” chifukwa Yehova akhoza kumugwiritsa ntchito kwambiri. (Luka 9:48) N’chifukwa chiyani tikutero?

‘WAMNG’ONO PAKATI PANU NDI AMENE ALI WAMKULU’

8. Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova?

8 Kudzichepetsa n’kumene kungatithandize kuchita zinthu mogwirizana ndi gulu la Mulungu ndiponso mpingo. Mwachitsanzo, taganizirani za mlongo wina dzina lake Petra amene anakulira m’banja la Mboni. Ali mtsikana, sankafuna kuuzidwa zochita choncho anasiya kusonkhana. Patapita zaka, anayambiranso kusonkhana ndi mpingo. Panopa, iye akusangalala kwambiri m’gulu la Yehova ndipo amafunitsitsa kuchita zinthu mogwirizana ndi mpingo. N’chiyani chamuthandiza kusintha? Iye analemba kuti: “Panopa ndimasangalala m’gulu la Mulungu chifukwa ndaona kufunika kwa kudzichepetsa.”

9. Kodi munthu wodzichepetsa amaona bwanji chakudya chauzimu chimene timalandira? Kodi zimene amachita zimamuthandiza bwanji?

9 Munthu wodzichepetsa amayamikira kwambiri zimene Yehova amatipatsa monga chakudya chauzimu. Munthu wotereyu amaphunzira Baibulo mwakhama. Amawerenganso mwakhama magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mofanana ndi atumiki ena okhulupirika, iye akalandira buku latsopano samangolisiya pashelefu koma amaonetsetsa kuti waliwerenga lonse. Tikakhala odzichepetsa n’kumawerenga ndiponso kuphunzira mabuku athu ofotokoza Baibulo, timapita patsogolo ndipo Yehova amatha kutigwiritsa ntchito kwambiri m’gulu lake.—Aheb. 5:13, 14.

10. Kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa mu mpingo?

10 Munthu amene amachita zinthu ngati wamng’ono amakhalanso “wamkulu” m’njira ina. Mu mpingo uliwonse mumakhala akulu amene amaikidwa motsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Yehova. Iwo amakonza dongosolo lokhudza misonkhano ya mpingo, utumiki wakumunda komanso maulendo aubusa. Tikamakhala odzichepetsa n’kumachita zinthu mogwirizana ndi dongosolo limene akonza, timathandiza kuti mpingo ukhale wosangalala, wamtendere ndiponso wogwirizana. (Werengani Aheberi 13:7, 17.) Ngati ndinu mkulu kapena mtumiki wothandiza, muyenera kukhala wodzichepetsa n’kumayamikira Yehova chifukwa chokupatsani mwayi umenewu.

11, 12. Kodi ndi mtima wotani umene ungatithandize kukhala wofunika m’gulu la Yehova ndipo n’chifukwa chiyani?

11 Munthu amene amachita zinthu ngati wamng’ono amakhala “wamkulu,” kapena kuti wofunika kwambiri m’gulu la Yehova. Tikutero chifukwa chakuti amakhala mtumiki wa Mulungu wabwino komanso wothandiza. Yesu anafunika kulangiza ophunzira ake kuti azikhala ngati aang’ono chifukwa chakuti ena anatengera mtima wa anthu a m’nthawiyo. Pa Luka 9:46, timawerenga kuti: “Iwo anayamba kukhala ndi maganizo ofuna kudziwa amene ali wamkulu koposa pakati pawo.” Mwina nafenso tingayambe kuganiza kuti timaposa Akhristu anzathu kapena anthu ena onse. Anthu ambiri m’dzikoli ndi onyada ndiponso odzikonda. Tiyeni tisatengere mtima wawo koma tiziyesetsa kukhala odzichepetsa. Tikamatero ndiponso tikamaika patsogolo zofuna za Yehova, timatsitsimula abale ndi alongo athu.

12 Malangizo a Yesu pa nkhani ya kudzichepetsa ndi olimbikitsa kwambiri. Tiyeni tiziyesetsa nthawi zonse kukhala ngati aang’ono. Koma tsopano tiyeni tikambirane mmene tingachitire zimenezi.

YESETSANI KUKHALA NGATI WAMNG’ONO

13, 14. Kodi mwamuna ndi mkazi angasonyeze bwanji kudzichepetsa m’banja? Kodi ubwino wake ndi wotani?

13 M’banja. Anthu ambiri masiku ano amangochita zinthu moganizira ufulu wawo ngakhale pamene zochita zawozo zikuphwanya ufulu wa ena. Koma munthu wodzichepetsa amachita zimene Paulo ananena m’kalata yake yopita kwa Aroma. Iye analemba kuti: “Tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.” (Aroma 14:19) Munthu wodzichepetsa amayesetsa kukhala pa mtendere ndi aliyense. Amatero makamaka ndi mkazi kapena mwamuna wake chifukwa amamuona kuti ndi wamtengo wapatali.

14 Mwachitsanzo, kodi chingachitike n’chiyani ngati zosangalatsa zimene mwamuna amakonda n’zosiyana ndi zimene mkazi wake amakonda? Tiyerekeze kuti pa nthawi yopuma mwamuna amafuna kungokhala pakhomo pomwe mkazi wake amafuna kupita kukacheza kwinakwake. Ngati mwamuna amadzichepetsa n’kumaganizira zofuna za mkazi wake osati zake zokha, zimathandiza kuti mkaziyo azimulemekeza kwambiri. Nayenso mwamuna angamakonde kwambiri mkazi wake ndiponso kumunyadira ngati mkaziyo amaganiziranso zofuna za mwamuna wakeyo. Banja limalimba kwambiri ngati aliyense amadzichepetsa.—Werengani Afilipi 2:1-4.

15, 16. Kodi Davide analimbikitsa Aisiraeli kuchita chiyani pa Salimo 131? Kodi tingatsatire bwanji malangizo amenewa mu mpingo?

15 Mu mpingo. Anthu ambiri m’dzikoli amangofuna kuti apeze mwamsangamsanga zimene akulakalaka. Iwowo zoleza mtimazi si kwenikweni ndipo amaona kuti kudikira ndi chintchito. Koma kudzichepetsa kumatithandiza kuti tiziyembekezera Yehova. (Werengani Salimo 131:1-3.) Tikamakhala odzichepetsa n’kumayembekezera Yehova, timadalitsidwa ndipo timakhala mwamtendere komanso mosangalala. M’pake kuti Davide analimbikitsa Aisiraeli anzake kuyembekezera Mulungu wawo moleza mtima.

16 Nanunso zinthu zingakuyendereni bwino mukamayembekezera Yehova modzichepetsa. (Sal. 42:5) Mwina ‘mukuyesetsa kuti mukhale woyang’anira’ mu mpingo n’cholinga choti mugwire ‘ntchito yabwino.’ (1 Tim. 3:1-7) Ngati ndi choncho, muyenera kuyesetsa kuti mzimu woyera ukuthandizeni kukhala ndi makhalidwe ofunika kuti mukhale woyang’anira. Koma bwanji ngati zimenezi zikutenga nthawi koma anzanu ena sakuchedwa kukhala oyang’anira? Munthu wodzichepetsa, amene amayembekeza moleza mtima, amatumikirabe Yehova mosangalala. Iye amasangalala kuchita chilichonse chimene wapemphedwa kuti achite.

17, 18. (a) Kodi kupepesa ndiponso kukhululukira anzathu kumathandiza bwanji? (b) Kodi pa Miyambo 6:1-5 pali malangizo otani?

17 Pochita zinthu ndi ena. Anthu ambiri amavutika kupepesa. Koma atumiki a Yehova amayesetsa kukhala odzichepetsa ndipo amavomereza zolakwa zawo n’kupempha kuti akhululukidwe. Iwo amakhalanso ndi mtima wokhululuka akalakwiridwa. Kudzikuza kumachititsa anthu kukangana ndiponso kudana koma mtima wokhululuka umalimbikitsa mtendere mu mpingo.

18 Mwachitsanzo, ngati talonjeza zinazake n’kulephera kuchita pa zifukwa zomveka, tiyenera kudzichepetsa n’kupepesa mnzathuyo kuchokera pansi pa mtima. Mkhristu wodzichepetsa amaganizira zimene iyeyo walakwitsa n’kupepesa ngakhale pamene akuona kuti munthu winayo walakwanso.—Werengani Miyambo 6:1-5.

19. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira malangizo a m’Baibulo okhudza kudzichepetsa?

19 Tikuyamikira kwambiri malangizo ochokera m’Malemba amene talandira okhudza kudzichepetsa. N’zoona kuti nthawi zina tingamavutike kuchita zimenezi. Koma kuganizira mmene Mulungu amatiposera ndiponso mmene amadzichepetsera kungatilimbikitse kukhala odzichepetsa. Tikamatero, timakhala anthu ofunika kwambiri m’gulu la Yehova. Choncho tiyeni tonse tiziyesetsa kukhala ngati wamng’ono.

^ ndime 5 Mayina asinthidwa.