Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesu Anatipatsa Chitsanzo cha Kudzichepetsa

Yesu Anatipatsa Chitsanzo cha Kudzichepetsa

“Ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.”—YOH. 13:15.

1, 2. Kodi Yesu anapereka phunziro lotani kwa atumwi ake usiku woti aphedwa mawa lake?

USIKU woti aphedwa mawa lake, Yesu anali ndi ophunzira ake m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu. Pa nthawi ya chakudya chamadzulo, iye anaimirira n’kuvula malaya ake akunja. Kenako anatenga thaulo ndi kuimanga m’chiuno. Ndiyeno anathira madzi m’beseni n’kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake n’kumawapukuta ndi thauloyo. Atamaliza, anavalanso malaya ake akunja aja. N’chifukwa chiyani Yesu anagwira ntchito yonyozekayi?—Yoh. 13:3-5.

2 Yesu anati: “Kodi mukudziwa zimene ndachita kwa inu? . . . Ngati ine, wokhala Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi. Pakuti ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.” (Yoh. 13:12-15) Yesu anagwira ntchito yonyozekayi pofuna kupereka phunziro losaiwalika kwa ophunzira ake. Zimene Yesu anachitazi zinawalimbikitsa kuti akhale odzichepetsa pa moyo wawo wonse.

3. (a) Fotokozani zimene Yesu anachita pofuna kusonyeza kuti kudzichepetsa n’kofunika. (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

3 Koma aka sikanali koyamba kuwaphunzitsa za kudzichepetsa. Nthawi inayake, atumwi ena anakangana pa nkhani yofuna kudziwa kuti wamkulu ndani. Yesu anangoitana kamwana n’kukaimika pafupi kenako n’kuwauza kuti: “Aliyense wolandira mwana wamng’ono uyu m’dzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense wolandira ine walandiranso amene anandituma ine. Pakuti aliyense wokhala ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.” (Luka 9:46-48) Yesu ankadziwa kuti Afarisi ankafuna kuoneka apamwamba, choncho tsiku lina ananena kuti: “Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.” (Luka 14:11) Apa zikuonekeratu  kuti Yesu amafuna kuti otsatira ake azikhala odzichepetsa osati odzikuza kapena onyada. Tiyeni tikambirane chitsanzo chimene anapereka n’cholinga choti nafenso tikhale odzichepetsa. Tionanso mmene kudzichepetsa kungatithandizire ifeyo komanso anthu ena.

“SINDINATEMBENUKIRE KWINA”

4. Kodi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa asanabwere padziko?

4 Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anali wodzichepetsa ngakhale asanabwere padziko lapansi. Yesu anakhala zaka zambirimbiri kumwamba limodzi ndi Atate ake. Pofotokoza mmene ankakhalira ndi Atate ake, buku la Yesaya limati: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wandipatsa lilime la anthu ophunzitsidwa bwino kuti ndidziwe mmene ndingamuyankhire munthu wotopa. Iye amandidzutsa m’mawa uliwonse. Amandidzutsa kuti makutu anga amve ngati anthu ophunzitsidwa bwino. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanditsegula khutu ndipo ineyo sindinapanduke. Sindinatembenukire kwina.” (Yes. 50:4, 5) Mwana wa Mulungu anali wodzichepetsa ndipo ankamvetsera mwatcheru zimene Yehova ankamuphunzitsa. Iye anali wofunitsitsa kuphunzitsidwa ndi Mulungu woona. Yesu ayenera kuti ankaona bwinobwino mmene Yehova ankadzichepetsera pochitira chifundo anthu ochimwa.

5. Monga Mikayeli mkulu wa angelo, kodi Yesu anasonyeza bwanji kudzichepetsa atasemphana maganizo ndi Mdyerekezi?

5 Koma si onse kumwambako amene anali odzichepetsa ngati Mwana wa Mulungu. Mngelo amene anadzakhala Satana Mdyerekezi sanafune kuphunzitsidwa ndi Yehova. M’malo modzichepetsa, iye anayamba kudzikuza ndiponso kunyada. Kenako anapandukira Yehova. Mosiyana ndi Satanayo, Yesu ankakhutira ndi udindo wake kumwambako ndipo sankaugwiritsa ntchito molakwika. Mikayeli mkulu wa angelo, yemwe ndi Yesu, sanagwiritse ntchito udindo wake molakwika pamene ‘anasemphana maganizo ndi Mdyerekezi zokhudza mtembo wa Mose.’ Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa. Anafuna kuti Yehova, yemwe ndi Woweruza Wamkulu wa chilengedwe chonse, asamalire nkhaniyi mmene ankafunira komanso pa nthawi yake.—Werengani Yuda 9.

6. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa povomera kukhala Mesiya?

6 Yesu ali kumwamba, mosakayikira anaphunziranso maulosi onena za zimene zidzamuchitikire akadzakhala Mesiya padziko lapansi. Choncho ayenera kuti ankadziwa mavuto amene adzakumane nawo. Koma iye anavomerabe kubwera padziko lapansi n’kudzaphedwa monga Mesiya amene Mulungu analonjeza. N’chifukwa chiyani anavomera? Chifukwa chakuti Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anali wodzichepetsa. Mtumwi Paulo anasonyeza zimenezi polemba kuti: “Ngakhale kuti iye anali ndi maonekedwe a Mulungu, kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande. Sanatero ayi, koma anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo, ndi kukhala wofanana ndi anthu.”—Afil. 2:6, 7.

“ATAKHALA MUNTHU, ANADZICHEPETSA”

7, 8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kudzichepetsa ali wamng’ono komanso pa utumiki wake?

7 Paulo analemba kuti: “[Yesu] atakhala munthu, anadzichepetsa ndi kukhala womvera mpaka imfa. Anakhala womvera mpaka imfa ya pamtengo wozunzikirapo.” (Afil. 2:8) Yesu anapereka chitsanzo cha kudzichepetsa kuyambira ali wamng’ono. Yosefe ndi Mariya, omwe anali makolo ake, anali opanda ungwiro koma iye ankadzichepetsa ndipo “anapitiriza kuwamvera.” (Luka 2:51) Ichitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa achinyamata. Mulungu adzawadalitsa akamamvera makolo awo ndi mtima wonse.

 8 Atakula, Yesu anasonyeza kudzichepetsa poika patsogolo zofuna za Yehova osati zake. (Yoh. 4:34) Pa nthawi ya utumiki wake, Yesu Khristu ankagwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Iye ankathandizanso anthu ofuna choonadi kudziwa bwino makhalidwe a Yehova ndiponso cholinga chake chokhudza anthu. Yesu ankatsatiranso zinthu zokhudza Yehova zimene ankaphunzitsa anthu. Mwachitsanzo, m’pemphero lake lachitsanzo, iye anayamba ndi kunena kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) Yesu analangiza otsatira ake kuti aziganizira kwambiri za kuyeretsa dzina la Mulungu. Ndipotu izi n’zimene iye ankachita. Atatsala pang’ono kuphedwa, Yesu anauza Yehova m’pemphero kuti: “Ine ndachititsa kuti iwo [atumwi] adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo.” (Yoh. 17:26) Pa zonse zimene Yesu ankachita padziko lapansi, iye ankaonetsetsa kuti ulemerero uzipita kwa Yehova.—Yoh. 5:19.

9. Kodi Zekariya analosera chiyani zokhudza Mesiya? Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji ulosiwo?

9 Ponena za Mesiya, Zekariya analosera kuti: “Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni sangalala kwambiri. Fuula mokondwera iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu. Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe. Mfumuyo ndi yolungama ndipo yapambana. Iyo ndi yodzichepetsa ndipo ikubwera itakwera bulu. Ikubwera itakwera nyama yokhwima, imene ndi mwana wamphongo wa bulu.” (Zek. 9:9) Zimenezi zinakwaniritsidwa pamene Yesu ankalowa mu Yerusalemu m’chaka cha 33 C.E., Pasika asanachitike. Anthu anali kuyala malaya awo akunja ndiponso nthambi za mitengo mumsewu. Pamene ankalowa, mzinda wonse unagwedezeka. Pa nthawiyi, anthu ankamuchemerera kuti ndi Mfumu koma iye anakhalabe wodzichepetsa.—Mat. 21:4-11.

10. Kodi kumvera kwa Yesu mpaka imfa kunasonyeza chiyani?

10 Yesu Khristu anakhalabe wodzichepetsa komanso womvera mpaka pamene anaphedwa pamtengo wozunzikirapo. Apa anasonyezeratu kuti munthu akhoza kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale atakumana ndi mayesero aakulu kwambiri. Satana anati  anthu amatumikira Yehova chifukwa cha dyera. Koma Yesu anasonyeza kuti zonena zakezi ndi zabodza. (Yobu 1:9-11; 2:4) Kukhulupirika kwa Khristu kunasonyezanso kuti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndiponso kuti ulamuliro wake ndi wachilungamo. N’zosachita kufunsa kuti Yehova anasangalala kwambiri kuona Mwana wake wodzichepetsayu akukhalabe wokhulupirika.—Werengani Miyambo 27:11.

11. Kodi dipo la Yesu linapereka mwayi wotani kwa anthu okhulupirira?

11 Yesu anafa pamtengo wozunzikirapo n’kupereka dipo lowombola anthu. (Mat. 20:28) Chifukwa cha dipoli, anthu ochimwa anapatsidwa mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha koma popanda kunyalanyaza mfundo za chilungamo. Paulo analemba kuti: “Mwa kuchita chinthu chimodzi cholungamitsa, anthu kaya akhale amtundu wotani akuyesedwa olungama kuti akhale ndi moyo.” (Aroma 5:18) Imfa ya Yesu inatsegula mwayi woti Akhristu odzozedwa apeze moyo wosafa kumwamba ndiponso woti “nkhosa zina” zipeze moyo wosatha padziko lapansi.—Yoh. 10:16; Aroma 8:16, 17.

‘NDINE WODZICHEPETSA’

12. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kudzichepetsa ndiponso kufatsa pochita zinthu ndi anthu opanda ungwiro?

12 Yesu anaitana anthu onse “ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa.” Iye anawauza kuti: “Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mat. 11:28, 29) Yesu analibe tsankho ndiponso anali wokoma mtima pochita zinthu ndi anthu opanda ungwiro. Anatha kuchita zimenezi chifukwa anali wodzichepetsa ndiponso wofatsa. Yesu sankayembekezera ophunzira ake kuchita zimene iwo sangakwanitse. Koma ankawayamikira ndiponso kuwalimbikitsa. Iye sankawapangitsa kudzimva ngati ndi opanda pake kapena osanunkha kanthu. Yesu sanali wankhanza kapena wopondereza. M’malomwake, anauza otsatira ake kuti akabwera kwa iye n’kumachita zimene ankaphunzitsa, adzatsitsimulidwa. Zinali choncho chifukwa chakuti goli lake linali lofewa ndipo katundu wake anali wopepuka. Amuna, akazi, ana ndiponso anthu akuluakulu ankamasuka naye.—Mat. 11:30.

13. Kodi Yesu anasonyeza bwanji chifundo kwa anthu ovutika?

13 Yesu akakhala ndi anthu wamba, ankawamvera chifundo chifukwa cha mavuto awo ndipo ankawathandiza mwachikondi. Pafupi ndi mzinda wa Yeriko, Yesu anakumana ndi opemphapempha awiri akhungu. Wina dzina lake linali Batimeyu koma winayo dzina lake silinatchulidwe. Iwo anapempha Yesu mobwerezabwereza kuti awathandize koma khamu la anthu linawakalipira kuti akhale chete. Zikanakhala zosavuta kuti Yesu angowasiya. Koma anawaitanitsa ndipo anawamvera chisoni n’kuwachiritsa. Yesu ankatsanzira Atate  ake Yehova posonyeza kudzichepetsa ndiponso kuchitira chifundo anthu ochimwa.—Mat. 20:29-34; Maliko 10:46-52.

“ALIYENSE WODZICHEPETSA ADZAKWEZEDWA”

14. Kodi kudzichepetsa kwa Yesu kwathandiza bwanji anthu?

14 Chitsanzo cha Yesu Khristu cha kudzichepetsa n’chosangalatsa komanso chothandiza kwambiri. Yehova anasangalala kwambiri kuona Mwana wake akudzichepetsa n’kumachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake. Atumwi ndiponso ophunzira a Yesu ankatsitsimulidwa kwambiri chifukwa chakuti iye anali wofatsa ndiponso wodzichepetsa. Chitsanzo chake, zimene ankaphunzitsa komanso zimene ankanena powayamikira zinkawalimbikitsa kuti azitumikira Yehova mwakhama. Anthu wamba ankapindulanso ndi kudzichepetsa kwa Yesu. Tikutero chifukwa chakuti iye ankawathandiza, kuwaphunzitsa ndiponso kuwalimbikitsa. Ndipotu anthu onse okhulupirira adzapindula kwambiri ndi nsembe ya dipo imene Yesu anapereka.

15. Kodi Yesu anapindula bwanji chifukwa chodzichepetsa?

15 Nanga bwanji Yesuyo? Kodi anapindulanso ndi kudzichepetsa kwake? Inde. Tikutero chifukwa Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.” (Mat. 23:12) Zimenezi n’zimene zinamuchitikira. Paulo anafotokoza kuti: “Mulungu anamukweza [Yesu] n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse. Anachita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse akumwamba, apadziko lapansi, ndi apansi pa nthaka apinde mawondo awo. Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.” Chifukwa chakuti Yesu anali wodzichepetsa ndiponso wokhulupirika ali padziko lapansi, Yehova Mulungu anamukweza. Anamupatsa ulamuliro pa zolengedwa zonse zakumwamba ndiponso zapadziko lapansi.—Afil. 2:9-11.

YESU ADZAMENYA NKHONDO ‘CHIFUKWA CHA CHOONADI NDI KUDZICHEPETSA’

16. N’chiyani chimasonyeza kuti Mwana wa Mulungu adzapitiriza kukhala wodzichepetsa?

16 Mwana wa Mulungu adzapitiriza kukhala wodzichepetsa. Wamasalimo analosera m’nyimbo yake za Yesu ali pamalo ake okwezedwa kumwamba. Iye anafotokoza mmene Yesu adzamenyera adani ake. Anaimba kuti: “Upambane mu ulemerero wako. Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo.” (Sal. 45:4) Pa nthawi ya Aramagedo, Yesu Khristu adzakwera pahatchi chifukwa cha choonadi, chilungamo ndiponso kudzichepetsa. Nanga n’chiyani chidzachitike kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000, iye akadzathetsa “maboma onse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse”? Kodi adzasonyezabe kudzichepetsa? Inde. Yesu “adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake.”—Werengani 1 Akorinto 15:24-28.

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani zili zofunika kuti atumiki a Yehova azitsatira Yesu pa nkhani ya kudzichepetsa? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

17 Kodi ifeyo tidzatsatira chitsanzo cha Yesu chokhala wodzichepetsa? Kodi zidzatiyendera bwanji Yesu Khristu akamadzapereka chiweruzo pa Aramagedo? Pa nthawiyo, iye adzakwera pahatchi chifukwa cha kudzichepetsa ndi chilungamo. Izi zikusonyeza kuti Yesu adzangopulumutsa anthu okhawo amene amasonyeza makhalidwe amenewa. Choncho, kukhala odzichepetsa n’kofunika kwambiri kuti tidzapulumuke. Chifukwa cha kudzichepetsa kwake, Yesu Khristu limodzi ndi anthu ena anapindula. Ifenso tingapindule m’njira zosiyanasiyana tikamakhala odzichepetsa.

18 N’chiyani chingatithandize kutsatira chitsanzo cha Yesu chokhala wodzichepetsa? Kodi tingatani kuti tikhalebe odzichepetsa ngakhale pamene zili zovuta kutero? Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.