Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikhululukirana ndi Mtima Wonse

Muzikhululukirana ndi Mtima Wonse

“Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.”—AKOL. 3:13.

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira ngati ndife okhululuka kapena ayi?

MAWU a Yehova amatiphunzitsa mmene iye amaonera machimo ndiponso zimene amachita tikachimwa. Amatiphunzitsanso zambiri pa nkhani ya kukhululuka. M’nkhani yapita ija, tinaphunzira zimene zinachititsa Yehova kukhululukira Davide ndi Manase. Iwo anamva chisoni ndi zimene anachita. Choncho anaulula machimo awo kwa Yehova, kuwasiya ndiponso kulapa mochokera pansi pa mtima. Izi zinachititsa kuti akhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.

2 Tsopano tiyeni tikambirane za ifeyo. Kodi tili ndi mtima wokhululuka? Kodi mukanamva bwanji ngati wachibale wanu akanaphedwa ndi Manase? Kodi mukanamukhululukira? Funsoli ndi lofunika chifukwa masiku anonso anthu ndi oipa, achiwawa ndiponso odzikonda. Koma n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala okhululuka? Kodi mungatani ngati mwachitiridwa zoipa? Nanga n’chiyani chingakuthandizeni kuugwira mtima, kuchita zimene zingasangalatse Yehova ndiponso kukhululuka?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHALA OKHULULUKA?

3-5. (a) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito fanizo liti pothandiza anthu kudziwa kufunika kokhululukira ena? (b) Kodi fanizo la Yesu la pa Mateyu 18:21-35 limatanthauza chiyani?

3 Tiyenera kukhala ndi mtima wokhululukira anthu amene atilakwira, kaya akhale Akhristu anzathu kapena ayi. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi achibale athu, anzathu, anthu ena ndiponso Yehova. Malemba amasonyeza kuti Mkhristu aliyense ayenera kukhululukira ena ngakhale anthuwo atamulakwira kambirimbiri. Pofuna kusonyeza kuti kukhululukira  ena n’kofunika, Yesu anagwiritsa ntchito fanizo lonena za kapolo amene anali ndi ngongole.

4 Kapoloyu anakongola kwa mbuye wake ndalama zokwana malipiro a masiku 60 miliyoni n’kukhululukidwa kuti asabwezenso. Koma atachoka pamenepo, anakakumana ndi kapolo mnzake amene anamukongoza ndalama zongokwana malipiro a masiku 100. Mnzakeyo anamuchonderera kuti amukhululukire koma sanamumvere chisoni mpaka anapita kukam’pereka kundende. Izi zinapsetsa mtima mbuye wawo uja moti anati: “Kodi nawenso sukanam’chitira chifundo kapolo mnzako, monga momwe ine ndinakuchitira chifundo?” Kenako “mbuye wakeyo anakwiya, ndipo anamupereka kwa oyang’anira ndende, mpaka pamene adzabweze ngongole yonse.”—Mat. 18:21-34.

5 Kodi Yesu ankatanthauza chiyani ponena fanizoli? Iye anamaliza ndi mawu akuti: “Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba adzathana ndi inu ngati aliyense wa inu sakhululukira m’bale wake ndi mtima wonse.” (Mat. 18:35) Apa mfundo ndi yoonekeratu. Machimo amene timachita chifukwa chopanda ungwiro ndi ambirimbiri. Choncho n’zosatheka kumvera Yehova popanda kulakwitsa kenakake. Komabe Yehova amafunitsitsa kutikhululukira ndiponso kuiwaliratu machimo athu. Chotero aliyense amene amafuna kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ayenera kukhululuka zolakwa za anzake. Pajatu, Yesu pa ulaliki wake wa paphiri anati: “Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani. Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.”—Mat. 6:14, 15.

6. N’chifukwa chiyani zimavuta kukhululukira ena nthawi zina?

6 Mwina mungavomereze kuti kukhululukira ena n’kofunika koma nthawi zina si kophweka. Izi zili choncho chifukwa ena akatilakwira, timakhumudwa kwambiri. Munthu akalakwiridwa angakwiye kapena kupwetekedwa mtima. Iye angafune kubwezera kapena kufuna kuti munthuyo alangidwe. Anthu ena amaona kuti sangakhululukirenso munthu amene wawalakwirayo. Koma Yehova amafuna  kuti tizikhululukira ena. Choncho ngati inunso zimakuvutani, kodi mungatani kuti mukhale ndi mtima wokhululuka?

DZIWANI CHIFUKWA CHAKE MWAKHUMUDWA

7, 8. N’chiyani chingakuthandizeni kukhululuka ngati munthu wina wakukhumudwitsani?

7 Tikalakwiridwa kapena kuganiza kuti ena atilakwira, zimatipweteka kwambiri. Mwachitsanzo, mnyamata wina anafotokoza zimene zinamuchitikira. Iye anati: “Nthawi ina . . . nditakwiya kwambiri, ndinachoka pakhomo n’kuneneratu kuti sindidzabweranso. Pa tsikulo, nyengo inali yabwino kwambiri ndipo ndinkayenda m’kanjira kooneka bwino. Kumene ndinkadutsa kunali kwa zii ndiponso malo ake anali okongola. Zimenezi zinandikhazika mtima pansi moti patapita maola angapo, ndinabwerera kunyumba ndikumva chisoni kuti ndinakwiya mosakhala bwino.” Chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti mukakwiya, ndi bwino kudikira kaye kuti mtima ukhale pansi. Zimenezi zingakuthandizeni kupewa kuchita zimene mungamve nazo chisoni pambuyo pake.—Sal. 4:4; Miy. 14:29; Yak. 1:19, 20.

8 Koma kodi mungatani ngati kuchita zimenezi sikukuthandiza? Yesetsani kudziwa kuti n’chifukwa chiyani mwakhumudwa kwambiri. Kodi mwakhumudwa chifukwa ena sanakuchitireni zabwino kapena anakuchitirani zopanda ulemu? Kapena kodi mukuganiza kuti munthuyo wakukhumudwitsani mwadala? Kodi zimene munthuyo anakuchitirani zinalidi zoipa? Kuganizira ndiponso kudziwa chifukwa chake mwakhumudwa kungakuthandizeni kuchita zinthu zogwirizana ndi Malemba. (Werengani Miyambo 15:28; 17:27.) Kuganizira zimenezi kungakuthandizeninso kuona zinthu moyenera ndiponso kukhululuka. Ngakhale kuti kuchita zimenezi kungakhale kovuta, Baibulo lingakuthandizeni kuzindikira zimene ‘mukuganiza komanso zolinga za mtima wanu.’ Lingakuthandizeninso kukhala ndi mtima wokhululuka ngati Yehova.—Aheb. 4:12.

MUSAMAFULUMIRE KUKHUMUDWA

9, 10. (a) Kodi timatani munthu wina akatikhumudwitsa? (b) Kodi kukhala ndi mtima wokhululuka ndiponso kuona zinthu moyenera kungatithandize bwanji?

9 Pali zinthu zambiri pa moyo zimene zingachititse munthu kukwiya. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukuyendetsa galimoto kapena njinga ndipo galimoto kapena njinga ina yatsala pang’ono kukuwombani. Kodi mungachite chiyani? Mwina mwawerengapo nkhani za anthu amene anakwiya kwambiri mpaka kufika pomenyana ndi munthu winayo. Koma inuyo monga Mkhristu simungafune kuchita zimenezi.

10 Mungachite bwino kuganiza kaye musanachite chilichonse. N’kutheka kuti inunso penapake munalakwitsa chifukwa chosokonezedwa ndi zinazake. Apo ayi mwina galimoto kapena njinga ya munthu winayo ili ndi vuto linalake. Chitsanzochi chikutithandiza kuona zimene tingachite kuti tisakwiye kapena kukhumudwa kwambiri. Tiyenera kuyesetsa kumvetsa zimene zachititsa vutolo, kuzindikira kuti sitingadziwe zonse komanso kukhala wofunitsitsa kukhululuka. Lemba la Mlaliki 7:9 limati: “Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.” Tingaganize kuti munthu wina watikhumudwitsa mwadala. Koma nthawi zambiri zinthu zimachitika chifukwa cha kupanda ungwiro kapena kusamvetsetsana. Yesetsani kukumbukira kuti simungadziwe zonse zimene zachititsa munthu winayo kunena kapena kuchita zimene mwakhumudwa nazo. Muyeneranso kumusonyeza chikondi n’kumukhululukira. Mukamachita zimenezi, mudzakhala wosangalala kwambiri.—Werengani 1 Petulo 4:8.

 ‘MTENDERE WANU UBWERERE KWA INU’

11. Kaya anthu atilandire mu utumiki kapena ayi, kodi tiyenera kuchita chiyani?

11 Kodi muyenera kuchita chiyani ngati munthu wina wakuchitirani zamwano mu utumiki? Pamene Yesu ankatumiza anthu 70 kukalalikira, anawauza kuti azinena panyumba iliyonse imene afika kuti: “Mtendere ukhale panyumba pano.” Yesu ananenanso kuti: “Ngati pakhomopo pali munthu wokonda mtendere, mtendere wanu udzakhala pa iye. Koma ngati palibe, udzabwerera kwa inu.” (Luka 10:1, 5, 6) Timasangalala anthu akatilandira bwino mu utumiki chifukwa akhoza kupindula ndi uthenga wathu. Koma nthawi zina satilandira bwino. Kodi zikatero tizitani? Yesu ananena kuti mtendere umene tinkafuna kuti ukhale panyumbayo ukhalebe ndi ife. Kaya anthu atilandire kapena ayi, tiyenera kuchoka panyumba iliyonse tili ndi mtendere mumtima. Tikapsa mtima ndi anthu amene sanatilandire bwino ndiye kuti sitingakhalebe ndi mtendere mumtima.

12. Mogwirizana ndi mawu a Paulo pa Aefeso 4:31, 32, kodi tiyenera kuchita chiyani?

12 Muziyesetsa kukhala ndi mtendere mumtima nthawi zonse osati mu utumiki mokha. Kukhala wofunitsitsa kukhululukira ena sikutanthauza kuti muyenera kuvomereza zinthu zoipa zimene achita kapena kuona kuti zimene achitazo n’zosapweteka kwambiri. Koma kumatanthauza kusasunga chakukhosi n’kumakhalabe ndi mtendere mumtima. Anthu ena amangokhalira kuganizira zinthu zoipa zimene ena awachitira moti amasowa mtendere. Musalole maganizo amenewa kukulamulirani. Muyenera kukumbukira kuti simungakhale osangalala mukamasunga chakukhosi. Choncho muzikhululuka.—Werengani Aefeso 4:31, 32.

MUZICHITA ZIMENE ZINGASANGALATSE YEHOVA

13. (a) Kodi Mkhristu angaunjike bwanji “makala a moto pamutu” pa mdani wake? (b) Kodi kukhalabe aulemu pamene wina watiyamba n’kothandiza bwanji?

13 Nthawi zina munthu amene si Mkhristu akhoza kukulakwirani. Zikatero, mwina mukhoza kumuthandiza kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “‘Ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse chakumwa. Pakuti mwa kutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.’ Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:20, 21) Mukamakhalabe aulemu pamene wina wakuyambani, mukhoza kumuthandiza kuti nayenso ayambe kukhala munthu wabwino. Mukamasonyeza kuti mukumumvetsa ndiponso mukamamuchitira chifundo, iye angayambe kufuna kuphunzira Baibulo. Kaya aphunziradi kapena ayi, ulemu wanu ungamuthandize kuti achite chidwi ndi khalidwe lanu.—1 Pet. 2:12; 3:16.

14. N’chifukwa chiyani simuyenera kusunga chakukhosi ngakhale pamene munthu wina wakulakwirani kwambiri?

14 Koma pali anthu ena amene sitiyenera kucheza nawo. Mwachitsanzo, sitiyenera kucheza ndi anthu amene anachimwa koma sanalape ndipo anachotsedwa mu mpingo. Ngati anthu oterewa anakulakwirani ndipo zikukuwawani mumtima, zingakhale zovuta kuwakhululukira ngakhale atalapa. Izi zikachitika, muyenera kupempha Yehova mosalekeza kuti akuthandizeni kukhululukira munthu wolapayo. Muyenera kuchita zimenezi chifukwa simungadziwe zimene zili mumtima mwa munthuyo koma Yehova ndi amene amadziwa. Iye amadziwa chilichonse chimene munthu akuganiza ndipo amaleza mtima ndi anthu ochimwa. (Sal. 7:9; Miy. 17:3) N’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti: “Musabwezere choipa pa choipa. Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino. Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Okondedwa, musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu. Pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera  ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.’” (Aroma 12:17-19) Sindife oyenera kuweruza anzathu. (Mat. 7:1, 2) Koma tisamakayikire kuti Mulungu amaweruza mwachilungamo.

15. Kuti tisasungire chakukhosi munthu amene watilakwira, kodi tiyenera kukumbukira chiyani?

15 Ngati mukuona kuti mwalakwiridwa ndi munthu wina ndipo zikukuvutani kukhululuka ngakhale kuti walapa, mungachite bwino kukumbukira kuti munthuyo akuvutikanso. Iyenso amakhala akulimbana ndi kupanda ungwiro. (Aroma 3:23) Yehova amamvera chisoni anthu onse chifukwa ndi opanda ungwiro. Choncho tingachite bwino kupempherera munthu amene watilakwirayo. Kumupempherera kungatithandize kuti tisamusungire chakukhosi. Yesu anatsindika mfundo yakuti sitiyenera kusungira chakukhosi ngakhale munthu amene tikuona kuti watilakwiradi. Iye anati: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.”—Mat. 5:44.

16, 17. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati akulu aona kuti munthu wochimwa walapa? N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezo?

16 Yehova wapereka kwa akulu mu mpingo udindo woweruza anthu amene achimwa. Abale amenewa sadziwa zonse zimene Mulungu akudziwa pa nkhani imene akuweruza. Komabe amayesetsa kuti asankhe zinthu mogwirizana ndi malangizo a m’Mawu a Mulungu komanso motsogoleredwa ndi mzimu woyera. Popeza amayamba ndi pemphero kuti Yehova awathandize, zosankha zawo zimasonyeza mmene Yehova akuionera nkhaniyo.—Mat. 18:18.

17 Ndiyeno nkhani ya kukhulupirika imafunika pamenepa. Kodi mudzakhululukira ndiponso kukondabe anthu amene akulu aona kuti alapa? (2 Akor. 2:5-8) Zimenezi zimakhala zovuta ngati munthuyo analakwira inuyo kapena wachibale wanu. Koma mukamakhulupirira Yehova ndiponso mmene amachitira zinthu mu mpingo, mudzachita zinthu mwanzeru. Mudzasonyezanso kuti muli ndi mtima wofunitsitsa kukhululukira ena.—Miy. 3:5, 6.

18. Kodi kukhala ndi mtima wokhululuka kumatithandiza bwanji?

18 Madokotala a matenda amaganizo amanena kuti mtima wokhululuka umathandiza. Kusunga chakukhosi kungatichititse kuvutika maganizo, kudwala ndiponso kusagwirizana ndi anzathu. Koma kukhululuka kumatithandiza kuti tikhale athanzi, osangalala ndiponso ogwirizana ndi anzathu. Chofunika kwambiri n’chakuti mtima wokhululuka umachititsa kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba.—Werengani Akolose 3:12-14.