Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndi Wofunitsitsa Kukukhululukirani

Yehova Ndi Wofunitsitsa Kukukhululukirani

“Yehova [ndi] Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga . . . , wokhululukira zolakwa ndi machimo.”—EKS. 34:6, 7.

1, 2. (a) Kodi Yehova anali Mulungu wotani kwa Aisiraeli? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

M’MASIKU a Nehemiya, Alevi ena anavomereza pa gulu m’pemphero kuti makolo awo akale “anakana kumvera” malamulo a Yehova mobwerezabwereza. Koma Yehova anali “Mulungu wokhululuka, wachisomo ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha.” Yehova anapitirizabe kusonyeza Aisiraeli kukoma mtima kwakukulu.—Neh. 9:16, 17.

2 Aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingapindule bwanji ndi mtima wokhululuka wa Yehova?’ Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane mmene Mulungu anakhululukirira Mfumu Davide ndiponso Mfumu Manase komanso mmene iwowo anapindulira.

MACHIMO AKULUAKULU A DAVIDE

3-5. Kodi Davide anachita machimo akuluakulu ati?

3 Ngakhale kuti Davide anali munthu woopa Mulungu, iye anachita machimo akuluakulu. Machimo awiri anakhudza Uriya ndi mkazi wake Bati-seba. Machimowo anabweretsa mavuto aakulu kwambiri kwa Davide, Uriya ndiponso Bati-seba. Koma zimene Mulungu anachita ndi Davide zimatiphunzitsa zambiri zokhudza mmene Yehova amakhululukira. Tiyeni tikambirane nkhani imeneyi.

4 Davide anatumiza asilikali a Aisiraeli kuti akazungulire mzinda wa Raba, womwe linali likulu la Amoni. Mzindawu unali pa mtunda wa makilomita 80 kum’mawa kwa Yerusalemu kupitirira mtsinje wa Yorodano. Asilikali ali ku nkhondo, Davide anali kuyenda padenga la nyumba yachifumu ku Yerusalemu ndipo anaona Bati-seba akusamba. Mwamuna wake anali atapitanso ku nkhondo. Davide ataona Bati-seba, analakalaka kugona naye moti anamuitanitsa ndipo anachita naye chigololo.—2 Sam. 11:1-4.

 5 Davide atadziwa kuti Bati-seba ali ndi pakati, anaitanitsa mwamuna wake Uriya kuti abwere ku Yerusalemu. Anachita izi poganiza kuti Uriya akabwera, adzagona ndi mkazi wake. Davide anakakamiza Uriya kuti akagone kunyumba. Koma Uriya anakana ngakhale kulowa m’nyumba mwake. Choncho Davide analemba kalata mwamseri yopita kwa mkulu wa asilikali. M’kalatayo, anapempha kuti Uriya amuike “kutsogolo kumene nkhondo yakula” komanso kuti asilikali ena abwerere m’mbuyo. Izi zinachititsa kuti Uriya aphedwe mosavuta pa nkhondoyo mogwirizana ndi zimene Davide anakonza. (2 Sam. 11:12-17) Choncho kuwonjezera pa kuchita chigololo, Davide anachititsanso kuti munthu wosalakwa aphedwe.

DAVIDE ANALAPA

6. Kodi Mulungu anachita chiyani Davide atachimwa? Kodi nkhaniyi imatiphunzitsa chiyani za Yehova?

6 Yehova amaona chilichonse, choncho n’zosachita kufunsa kuti anaona zonse zimene Davide anachita. (Miy. 15:3) Ngakhale kuti patapita nthawi, iye anakwatira Bati-seba, “zimene Davide anachitazi zinamuipira kwambiri Yehova.” (2 Sam. 11:27) Ndiyeno kodi Mulungu anachita chiyani ndi Davide? Iye anatumiza mneneri wake Natani kuti akalankhule naye. Popeza kuti Mulungu ndi wokhululuka, iye anafuna kusonyeza chifundo kwa Davide. Koma anayenera kuona ngati panali chifukwa chochitira zimenezi. N’zolimbikitsa kwambiri kuti Yehova anali wofunitsitsa kumusonyeza chifundo. Yehova sanakakamize Davide kuti aulule machimo ake. Koma anangouza Natani kuti amuuze fanizo losonyeza kuipa kwa zimene anachita. (Werengani 2 Samueli 12:1-4.) Imeneyitu inali njira yabwino kwambiri yodziwira mtima wa Davide.

7. Kodi Davide anatani atamva fanizo la Natani?

7 Davide anaona kuti munthu wolemera wa m’fanizo limene Natani ananena sanachite chilungamo. Iye anakwiyira kwambiri munthu wolemerayo ndipo anauza Natani kuti: “Ndithu, pali Yehova Mulungu wamoyo, munthu wochita zimenezi ayenera kufa!” Ananenanso kuti munthu wolakwiridwayo ayenera kulandira chipukuta misozi. Koma nkhaniyi inatembenuka. Natani anauza Davide kuti: “Munthu ameneyo ndiwe!” Kenako anamuuza kuti: “Lupanga silidzachoka panyumba yako.” Anafotokozanso kuti tsoka lidzagwera a m’banja lake ndipo adzachititsidwa manyazi chifukwa cha machimo akewo. Davide anazindikira kuti anachita zinthu zoipa kwambiri. Iye anadzimvera chisoni n’kuvomereza kuti: “Ndachimwira Yehova.”—2 Sam. 12:5-14.

DAVIDE ANAPEMPHERA NDIPO YEHOVA ANAMUKHULULUKIRA

8, 9. Kodi Salimo 51 limasonyeza bwanji mmene Davide anamvera mumtima mwake? Nanga salimoli limatiphunzitsa chiyani za Yehova?

8 Mawu a m’nyimbo imene Davide anadzalemba pambuyo pake amasonyeza kuti anamva chisoni kwambiri chifukwa cha zimene anachita. M’Salimo 51, Davide anachonderera Yehova kuti amuthandize. Salimoli limasonyeza kuti Davide sanangovomereza machimo ake koma analapanso. Iye anaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi wofunika kwambiri kuposa chilichonse. Davide anauza Yehova kuti: “Ine ndakuchimwirani kwambiri.” Kenako anachonderera Yehova kuti: “Inu Mulungu, lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine. . . . Bwezeretsani mwa ine chisangalalo chifukwa cha chipulumutso chanu, ndichirikizeni ndi mzimu wofunitsitsa.” (Sal. 51:1-4, 7-12) Kodi inunso mukalakwitsa zinthu, mumalankhula ndi Yehova mochokera pansi pa mtima ndiponso momasuka chonchi?

9 Yehova sanachotse zotsatirapo zowawa za machimo a Davide. Anayenera kulimbana nazo moyo wake wonse. Koma analapa ndipo anali ndi “mtima wosweka ndi wophwanyika.” Choncho Yehova anamukhululukira. (Werengani Salimo 32:5; Sal. 51:17) Yehova amadziwa bwino zimene zili mumtima mwa munthu zomwe  zimamuchititsa kuchimwa. Choncho iye sanalole kuti oweruza a mu Isiraeli aphe Davide ndi Bati-seba potsatira zimene zinalembedwa m’Chilamulo cha Mose. (Lev. 20:10) M’malomwake, anawaweruza yekha n’kuwachitira chifundo. Ndipotu Mulungu anasankha mwana wawo Solomo kukhala mfumu yotsatira ya Isiraeli.—1 Mbiri 22:9, 10.

10. (a) Kodi n’kutheka kuti Yehova anakhululukira Davide pa chifukwa chinanso chiti? (b) Kodi tiyenera kutani kuti Yehova atikhululukire?

10 N’kutheka kuti chinthu china chimene chinachititsa Yehova kukhululukira Davide n’chakuti Davideyo anasonyeza chifundo kwa Sauli. (1 Sam. 24:4-7) Pajatu Yesu ananena kuti Yehova amachita nafe zinthu malinga ndi mmene ifenso timachitira ndi ena. Iye anati: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe, pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho. Ndipo muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.” (Mat. 7:1, 2) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amatikhululukira ngakhale machimo akuluakulu ngati chigololo kapena kupha munthu. Iye amachita zimenezi ngati tili ndi mtima wokhululuka, ngati tiulula machimo athu kwa iye ndiponso ngati tisintha maganizo athu n’kuyamba kuona machimowo monga mmene iyeyo amawaonera. Anthu ochimwa akalapa mochokera pansi pa mtima, “nyengo zotsitsimutsa” zimabwera kuchokera kwa Yehova.—Werengani Machitidwe 3:19.

MANASE ANACHITA MACHIMO AKULUAKULU KOMA ANALAPA

11. Kodi Mfumu Manase inachita zinthu zoipa ziti?

11 Tiyeni tikambirane chitsanzo china cha m’Malemba chimene chimasonyeza kuti Yehova ndi wofunitsitsa kukhululuka. Patapita zaka 360 kuchokera nthawi imene Davide anayamba kulamulira, Manase anakhala mfumu ya Yuda. Iye analamulira kwa zaka 55. Pa ulamuliro wake, anachita zinthu zoipa kwambiri ndipo Yehova anakwiya naye. Manase anachita zinthu monga kumanga maguwa ansembe operekera nsembe kwa Baala, kulambira “khamu lonse la zinthu zakuthambo,” kutentha ana ake pamoto ndiponso kulimbikitsa zamatsenga. Kunena zoona, “iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova.”—2 Mbiri 33:1-6.

12. Kodi Manase anabwerera bwanji kwa Yehova?

12 Patapita nthawi, Manase anatengedwa kuchoka kudziko lake n’kukaikidwa m’ndende ku Babulo. N’kutheka kuti ali m’ndendemo, anakumbukira zimene Mose anauza Aisiraeli. Iye anawauza kuti: “Pamapeto pake, mawu amenewa akadzakwaniritsidwa pa inu, n’kukhala pamavuto aakulu, mudzabwereradi kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumvetsera mawu ake.” (Deut. 4:30) Izi n’zimene zinachitika ndi  Manase. Iye anabwereradi kwa Yehova. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iye “anadzichepetsa kwambiri” ndipo “anayamba kupemphera kwa Mulungu.” (2 Mbiri 33:12, 13; onani chithunzi patsamba 21.) Sitikudziwa mawu enieni amene Manase anatchula m’mapemphero ake koma n’kutheka kuti ananena zinthu zina zofanana ndi zimene Mfumu Davide inatchula mu Salimo 51. Kaya ananena zotani, mfundo ndi yakuti Manase anasinthiratu mtima wake.

13. N’chifukwa chiyani Yehova anakhululukira Manase?

13 Kodi Yehova anatani Manase atapemphera? “Iye anamva kupembedzera [kwa Manase] ndi pempho lake lopempha chifundo.” Mofanana ndi Davide, Manase anazindikira kuti anachimwa kwambiri ndipo analapa mochokera pansi pa mtima. Chifukwa cha zimenezi, Mulungu anamukhululukira n’kumubwezera ku Yerusalemu kuti akakhalenso mfumu. Izi zinachititsa ‘Manase kudziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.’ (2 Mbiri 33:13) Chitsanzochi ndi umboni winanso wolimbikitsa umene umasonyeza kuti Mulungu wathu wachifundo amakhululukira anthu amene amalapa moona mtima.

KUKHULULUKA KWA YEHOVA KULI NDI MALIRE

14. Kodi Yehova amakhululukira ochimwa akachita chiyani?

14 Davide ndi Manase anachita machimo aakulu kwambiri moti ndi atumiki a Mulungu ochepa okha amene anachitapo machimo akuluakulu ngati amenewa. Koma Yehova anakhululukira Davide ndi Manase. Zimenezi zimatithandiza kudziwa kuti Mulungu wathu ndi wofunitsitsa kutikhululukira ngakhale machimo aakulu kwambiri. Komabe iye amakhululuka ngati wochimwayo walapa kuchokera pansi pa mtima.

15. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova samangokhululukira wochimwa aliyense?

15 N’zoona kuti Yehova samangokhululukira wochimwa aliyense. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tione zimene Davide ndi Manase anachita poyerekezera ndi zimene Aisiraeli ndi Ayuda opanduka anachita. Mulungu anatumiza Natani kuti akalankhule ndi Davide n’kumupatsa  mpata woti asinthe mtima wake. Davide anayamikira zimenezi ndipo analapa. Nayenso Manase analapa atakumana ndi zowawa. Koma nthawi zambiri Aisiraeli ndi Ayuda sankalapa ngakhale kuti Yehova ankawatumizira aneneri ake mobwerezabwereza kuti akawadziwitse mmene iye ankaonera khalidwe lawo losamvera. Choncho Mulungu sankawakhululukira. (Werengani Nehemiya 9:30.) Ngakhale pamene Aisiraeli anabwerera kwawo kuchokera ku Babulo, Yehova anapitirizabe kuwatumizira anthu okhulupirika monga wansembe Ezara ndi mneneri Malaki kuti awathandize. Aisiraeli ankasangalala kwambiri akamachita zinthu mogwirizana ndi zofuna za Yehova.—Neh. 12:43-47.

16. (a) N’chiyani chinachitikira mtundu wa Isiraeli chifukwa chokana kulapa machimo? (b) Kodi Mwisiraeli aliyense payekha ali ndi mwayi wotani?

16 Yehova anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake monga nsembe yangwiro. Atatero, sankalandiranso nsembe za nyama zimene Aisiraeli ankapereka. (1 Yoh. 4:9, 10) Yesu ali padziko, anasonyeza maganizo a Atate ake pamene analankhula mawu ogwira mtima awa akuti: “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneri iwe ndi woponya miyala anthu otumizidwa kwa iwe. Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, muja nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko. Koma anthu inu simunafune zimenezo.” Kenako iye ananenanso kuti: “Tsopano tamverani! Mulungu wachoka n’kukusiyirani nyumba yanuyi.” (Mat. 23:37, 38) Choncho mtundu wopanduka ndiponso wosalapa wa Isiraeli unalowedwa m’malo ndi Isiraeli wauzimu. (Mat. 21:43; Agal. 6:16) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mwisiraeli aliyense payekha sangakhululukidwe? Ayi. Yehova akhoza kuwakhululukira ndi kuwachitira chifundo ngati iwo akhulupirira Mulungu ndiponso nsembe ya Yesu Khristu. Palinso anthu ochimwa amene anamwalira asanalape koma adzaukitsidwa m’dziko latsopano. Iwonso adzakhala ndi mwayi wokhululukidwa machimo awo.—Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15.

ZIMENE TINGACHITE KUTI YEHOVA ATIKHULULUKIRE

17, 18. Kodi tingatani kuti Yehova atikhululukire?

17 Popeza kuti Yehova ndi wofunitsitsa kutikhululukira, kodi tiyenera kuchita chiyani? Tingachite bwino kutsatira chitsanzo cha Davide ndi Manase. Tiyenera kuzindikira kuti ndife ochimwa, kulapa zolakwa zathu, kupempha Yehova mochokera pansi pa mtima kuti atikhululukire ndiponso kuti atipatse mtima wolungama. (Sal. 51:10) Koma ngati tachita machimo aakulu, tiyeneranso kupempha thandizo kwa akulu mu mpingo. (Yak. 5:14, 15) Kaya tachita machimo aakulu bwanji, n’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova sanasinthe. Monga anadzifotokozera kwa Mose, iye adakali “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo.”—Eks. 34:6, 7.

18 Yehova analonjeza Aisiraeli olapa kuti adzawakhululukira machimo awo onse. Iye ananena kuti ngakhale machimo awo ndi “ofiira ngati magazi,” adzawachititsa kukhala oyera ngati “thonje.” (Werengani Yesaya 1:18.) Nanga kodi ifeyo timapindula bwanji Yehova akatikhululukira? Machimo athu onse amafafanizidwa. Zimenezi zimatheka ngati tasonyeza mtima woyamikira ndiponso wolapa.

19. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 Popeza kuti Yehova amatikhululukira machimo athu, kodi tingamutsanzire bwanji pochita zinthu ndi anzathu? N’chiyani chingatithandize kukhululukira anthu amene achita machimo aakulu koma alapa moona mtima? Nkhani yotsatira idzatithandiza kufufuza mtima wathu n’cholinga choti tikhale ngati Atate athu Yehova. Iye ndi Mulungu ‘wabwino ndiponso wokonzeka kukhululuka.’—Sal. 86:5.