Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukutsanzira Yehova mwa Kukhala ndi Mtima Wosamalira Ena?

Kodi Mukutsanzira Yehova mwa Kukhala ndi Mtima Wosamalira Ena?

 Kodi Mukutsanzira Yehova mwa Kukhala ndi Mtima Wosamalira Ena?

‘TULIRANI [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amasamala za inu.’ (1 Petulo 5:7) Mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri. Yehova Mulungu amaganizira anthu ake aliyense payekha. Motero, timamva kuti ndife otetezeka.

Ifenso tiyenera kukhala ndi mtima wosamalira ena. Koma popeza ndife opanda ungwiro tiyenera kusamala ndi zinthu zina tikamaganizira ena. Tisanakambirane zinthu zimenezi, tiyeni tione kaye njira zina zimene Yehova amasamalira anthu ake.

Wamasalmo Davide anagwiritsa ntchito fanizo la m’busa pofotokoza mmene Mulungu amasamalira anthu ake. Iye anati: “Yehova ndiye m’busa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa ku busa lamsipu: Anditsogolera ku madzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; . . . ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzawopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine.”​—Salmo 23:1-4.

Popeza kuti Davide anali m’busa, anadziwa zimene zimafunika posamalira nkhosa. M’busa amateteza nkhosa zake ku zilombo monga mikango, mimbulu, ndi zimbalangondo. Amaonetsetsa kuti nkhosa zisamwazikane, amafunafuna zomwe zasowa, amanyamula tiana totopa pachifuwa chake, ndipo amasamalira zodwala kapena zovulala. Tsiku lililonse amazipatsa madzi akumwa. Koma sikuti m’busa amalamulira chilichonse chimene nkhosazo zimachita. Choncho ngakhale kuti m’busa amateteza nkhosa zake, nkhosazo zimakhala ndi ufulu wochita zinthu zambiri.

Yehova amachita chimodzimodzi posamalira anthu ake. Mtumwi Petulo ananena kuti: “Mukutetezedwa ndi mphamvu ya Mulungu.” M’lembali mawu oti ‘kutetezedwa’ amatanthauza kuyang’aniridwa. (1 Petulo 1:5) Yehova nthawi zonse amatiyang’anira chifukwa amatikonda kwambiri ndipo amakhala wokonzeka nthawi zonse kutithandiza tikam’pempha. Komabe, Yehova anatilenga ndi ufulu wosankha zochita, choncho salamulira chilichonse chimene timachita. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa zimenezi?

Tsanzirani Mulungu Mukamasamalira Ana Anu

Makolo ayenera kuteteza ndi kusamalira ana awo chifukwa “ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova.” (Salmo 127:3) Zimenezi zingafune kuti makolo azilimbikitsa ana kunena zakukhosi kwawo ndipo pochita nawo zinthu aziganizira zimene ana anenazo. Ngati makolo amayesa kulamulira ana awo pachilichonse ndi kumanyalanyaza zofuna zawo, angakhale ngati m’busa amene akuyesa kulamula nkhosa zake mwa kuzimangirira  chingwe m’khosi. Palibe m’busa amene angawete nkhosa zake mwanjira imeneyi, ndipo Yehova nayenso satisamalira motere.

Mariko * anati: “Kwa zaka zambiri, ndakhala ndikungouza ana anga kuti, ‘Mupange zakuti’ kapena ‘Musapange zakuti.’ Ndinkaona kuti umenewu ndi udindo wanga monga kholo. Sindinkawayamikira akachita bwino, ndipo sindinkacheza nawo kwenikweni.” Ngakhale kuti mwana wa Mariko ankacheza nthawi yaitali pafoni ndi anzake, ankangocheza nthawi yochepa chabe ndi mayi ake. Mariko ananenanso kuti: “Ndipo ndinazindikira chifukwa chake zinthu zinkakhala choncho. Akamalankhula ndi anzake, mwana wangayo ankanena mawu osonyeza kuti akumvetsa mmene anzakewo akumvera, monga ‘Inenso’ kapena ‘Ndikugwirizana nazo.’ Nanenso ndinayamba kunena mawu omwewo kuti ndilimbikitse mwanayo kunena maganizo ake, ndipo posapita nthawi tinayamba kucheza nthawi yaitali ndiponso mosangalala.” Zimenezi zikusonyeza kuti n’zofunika kumvetsera maganizo a munthu wina osati kungomuuza zochita.

Makolo amafunika kulimbikitsa ana kuti azinena maganizo awo, ndipo ana amafunika kuzindikira kuti makolo amawasamalira n’cholinga choti awateteze. Baibulo limalangiza ana kuti azimvera makolo awo, ndipo kenako limanena chifukwa chochitira zimenezi. Limati: “Kuti zinthu zikuyendere bwino, ndi kutinso ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.” (Aefeso 6:1, 3) Ana amene amadziwadi ubwino wogonjera savutika kumvera makolo awo.

Mukamasamalira Nkhosa za Yehova

Yehova amatisamalira mwachikondi ndipo zimenezi zimaonekera mu mpingo wachikhristu. Pokhala Mutu wa mpingo, Yesu Khristu anauza akulu kuti azisamalira nkhosa. (Yohane 21:15-17) Mawu akuti oyang’anira mu Chigiriki amafananako ndi mawu amene amatanthauza “kuyang’ana mosamala.” Potsindika mmene akulu ayenera kuchitira zimenezi, Petulo anawalangiza kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe anakuikizani, osati mokakamizika, koma mwaufulu; osatinso chifukwa chofuna kupindulapo, koma ndi mtima wonse; osati mochita ufumu pa aja ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma kukhala zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”​—1 Petulo 5:2, 3.

N’zoona kuti ntchito ya akulu n’njofanana ndi ya abusa. Akulu achikhristu ayenera kusamalira anthu amene akudwala mwauzimu ndi  kuwathandiza kuti azitsatira mfundo zolungama za Yehova. Akulu ali ndi udindo woyendetsa zinthu mumpingo. Iwo amakonza misonkhano ndi kuona kuti zinthu zikuchitika mwadongosolo mumpingowo.​—1 Akorinto 14:33.

Koma mawu a Petulo amene tatchula kalewo, akuchenjeza akulu za ‘kuchita ufumu’ mumpingo. Njira imodzi yosonyeza kuti mkulu wayamba kuchita ufumu ndiyo kuika malamulo osafunikira mumpingo. Pofuna kuteteza kwambiri anthu mumpingo, mkulu angayambe kuchita zinthu mopyola malire. Mumpingo wina kumayiko a kum’mawa, akulu anaika malamulo a mmene anthu ayenera kulonjerana ku Nyumba ya Ufumu. Mwachitsanzo, iwo anaika lamulo lonena za amene aziyamba kupereka moni. Ankaona kuti malamulo amenewa angathandize kuti mumpingo mukhale mtendere. Ngakhale kuti akulu amenewo mosakayikira anali ndi zolinga zabwino pochita zimenezi, kodi anali kutsanzira mmene Yehova amasamalira anthu ake? Yehova amakhulupirira anthu ake ndipo tingaone zimenezi m’mawu a mtumwi Paulo, yemwe ankatsanzira Yehova. Iye anati: “Sikuti ndife olamulira chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe, pakuti ndinu okhazikika chifukwa cha chikhulupiriro chanu.”​—2 Akorinto 1:24.

Kuwonjezera pa kupewa kuika malamulo amene sachokera mu Malemba, akulu achikondi amasonyeza kuganizira kwambiri ena mwa kupewa kuulula zinsinsi za anthu. Amatsatira chenjezo la Mulungu lakuti: “Osaulula zinsinsi za mwini.”​—Miyambo 25:9.

Mtumwi Paulo anayerekezera mpingo wa Akhristu odzozedwa ndi thupi la munthu. Iye anati: “Mulungu analunzanitsa bwino thupi lonse . . . kuti thupi lisakhale logawikana, koma ziwalo zake zipatsane chisamaliro chofanana.” (1 Akorinto 12:12, 24-26) Mawu a Chigiriki akuti “zipatsane chisamaliro chofanana” amatanthauza kuti ‘aziderana nkhawa.’ Anthu a mumpingo wachikhristu ayenera kusamala kwambiri za ena.​—Afilipi 2:4.

Kodi Akhristu oona angasonyeze bwanji kuti ‘amaderana nkhawa’? Angasonyeze kuti amaganizira ena m’mpingo mwa kuwatchula mu mapemphero awo ndiponso mwa kuthandiza osowa. Zimenezi zimalimbikitsa enanso kuchita zinthu zabwino. Taganizani za Tadataka amene anabatizidwa ali ndi zaka 17 ndipo nthawi imeneyo m’banja mwawo, anali yekha amene ankatumikira Yehova. Iye anathandizidwa ndi anthu ena omwe anam’samalira mwachikondi ndipo anati: “Banja lina mumpingo wathu nthawi zambiri linkandiitanira ku nyumba kwawo kuti ndikadye kapena kucheza nawo. Pafupifupi tsiku lililonse popita ku sukulu, ndinkadzera ku nyumba kwawo kuti ndikapezeke nawo pa makambirano a lemba la tsiku. Ankandilangiza za mmene ndingapirire mavuto anga kusukulu, ndipo tinkatchula mavutowo m’mapemphero tili pamodzi. Banja limeneli linandiphunzitsa kukhala ndi mtima wopatsa.” Tadataka akugwiritsa ntchito zimene anaphunzira mwa kutumikira ku ofesi ya nthambi ina ya Mboni za Yehova.

Mtumwi Paulo anachenjeza za zimene tiyenera kusamala nazo poganizira ena. Anatchula akazi ena amene anali “kudyera miseche ndi kulowerera nkhani za eni, kumalankhula zimene sayenera kulankhula.” (1 Timoteyo 5:13) Ngakhale kuti ndi koyenera kukhala ndi chidwi mwa ena, tiyenera kusamala kuti tisayambe kulowerera m’nkhani zawo zosatikhudza. Ndipo kukhala ndi chidwi chosayenerera mwa ena kungaoneke munthu ‘akamalankhula zimene sayenera kulankhula,’ monga kuweruza ena.

Tingachite bwino kukumbukira kuti Akhristu angasiyane mmene amachitira zinthu zawo, monga zimene amadya kapena zosangalatsa zimene amasankha. Aliyense ali ndi ufulu wosankha zochita malinga ngati sizikusemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Paulo analangiza Akhristu a ku Roma kuti: “Tisamaweruzane wina ndi mnzake. . . . Tiyeni titsatire zinthu zodzetsa mtendere ndi zinthu zolimbikitsana wina ndi mnzake.” (Aroma 14:13, 19) Tiyenera kusonyeza kuti timaganizira kwambiri ena mwa kukhala okonzeka kuwathandiza osati kulowerera m’nkhani zawo zosatikhudza. Tikamasamalirana m’njira imeneyi, anthu m’banja ndiponso mumpingo amakondana ndi kugwirizana.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Mayina ena tawasintha.

[Chithunzi patsamba 19]

Thandizani ana anu kuti amasuke ndi kunena zakukhosi kwawo mwa kuwayamikira ndi kusonyeza kuti mumawamvetsa