Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo za M’dzikoli Zikusinthasintha

Mfundo za M’dzikoli Zikusinthasintha

Mfundo za M’dzikoli Zikusinthasintha

AKUTI m’zaka za m’ma 300 ku Athens kunali katswiri wina wa maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba dzina lake Dioginisi, yemwe ankayatsa nyale n’kumayenda nayo dzuwa likuswa mtengo, n’cholinga chofunafuna anthu amakhalidwe abwino, koma sanapeze ngakhale munthu mmodzi wotere.

N’zosatsimikizirika ngati nkhani imeneyi ili yoona kapena ayi. Koma n’zosakayikitsa kuti Dioginisi akanakhalabe ndi moyo masiku ano, akanayenera kufufuza mwakhama koposa kuti apeze anthu amakhalidwe abwino m’dzikoli. Ndipotu zikuoneka kuti anthu ambiri savomereza mfundo yoti anthufe tiyenera kumatsatira mfundo zinazake zodziwika za makhalidwe abwino. Kawirikawiri timamva kapena kuwerenga nkhani zochititsa manyazi zochitika m’mabanja, m’boma, kuntchito, m’zamasewera, m’zamalonda ndiponso m’malo ena ambiri. Masiku ano anthu ambiri atayiratu chikhalidwe chawo ndipo amaona kuti mfundo za chikhalidwecho n’zachikale. Mfundo zakalezi amaziunikanso ndipo kawirikawiri amazinyalanyaza. Ena amangotama mfundozo, koma sazitsatira n’komwe.

Katswiri wina wodziwa za chikhalidwe cha anthu a m’chipembedzo, dzina lake Alan Wolfe anati: “Masiku ano aliyense amayendera mfundo zakezake. Anthu sakutsatiranso chikhalidwe chawo ndiponso mabungwe olimbikitsa chikhalidwecho.” Ponena za zomwe zakhala zikuchitika m’zaka 100 zapitazi, nyuzi ya Los Angeles Times inatchulapo zomwe ananena Jonathan Glover, katswiri wa maphunziro apamwamba, kuti kulowa pansi kwa zipembedzo ndiponso kuwonongeka kwa chikhalidwe kunachititsa kuti ziwawa zichuluke kwambiri padziko lonse.

Komabe ngakhale pali chipwirikiti choterechi, anthu ena sanasiye kufunafuna mfundo za makhalidwe abwino. Zaka zingapo zapitazo, Federico Mayor, yemwe anali mkulu wa bungwe la UNESCO, ananena kuti “masiku ano, kuposa kale lonse, nkhani yomwe ili m’kamwam’kamwa padziko lonse ndi ya makhalidwe abwino.” Komatu kulephera kwa anthu kutsatira mfundo zamakhalidwe abwino sikukutanthauza kuti mfundo zamakhalidwe abwinozo palibe.

Koma kodi anthu onse angamvane chimodzi pankhani ya mfundo zoyenera kutsatira? N’zachidziwikire kuti sangatero. Ndiyeno kodi zingatheke bwanji kuti munthu adziwe kuti ichi n’chabwino icho n’choipa? Anthu masiku ano akuyendera makonda pamfundo zamakhalidwe abwino. Ndipotu mungathe kuona kuti maganizo amenewa sanachititse chikhalidwe kuti chikhale chabwinopo.

Wolemba mbiri wina wa ku Britain, dzina lake Paul Johnson, amakhulupirira kwambiri kuti maganizo a sankhawekha pankhani ya mfundo zamakhalidwe abwino, achititsa kuti “anthu azichita zinthu motayirira kwambiri.” Umutu si mmene zinthu zinalili chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900.

Kodi n’zothekadi kuti anthu apeze mfundo zenizeni za makhalidwe abwino zomwe zingakhale zothandizadi kulikonse padziko lapansili? Kodi tingapeze kuti mfundo zamakhalidwe abwino, zomwe n’zosasinthasintha ndiponso zogwira ntchito m’moyo wathu zimene zingatipatsedi chiyembekezo cha m’tsogolo? M’nkhani yotsatirayi tikambirana mafunso amenewa.