Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Tinapangidwa Modabwitsa’

‘Tinapangidwa Modabwitsa’

 ‘Tinapangidwa Modabwitsa’

‘Chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa.’​—SALMO 139:14.

1. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri anzeru amati Mulungu ndiye analenga zinthu zodabwitsa za padziko lapansi?

CHILENGEDWE chili ndi zinthu zambiri zodabwitsa. Kodi zonsezo zinakhalako bwanji? Anthu ena amakhulupirira kuti yankho lake lingapezeke popanda kuganizira za Mlengi wanzeru. Pamene ena amakhulupirira kuti popanda kuganizira za Mlengi, chilengedwe sitingachimvetse bwinobwino. Iwo amakhulupirira kuti zolengedwa za padziko lapansi ndi zovuta kuzimvetsa, zili m’mitundu yambirimbiri yosatheka kuidziwa yonse, ndipo tingati ndi zodabwitsa kwambiri moti sizikanatheka kukhalako zokha. Anthu ambiri, kuphatikizapo asayansi, amaona umboni wosonyeza kuti chilengedwe chinapangidwa ndi Mlengi wanzeru, wamphamvu ndi wokoma mtima. *

2. Kodi n’chifukwa chiyani Davide anatamanda Yehova?

2 Davide, mfumu ya Isiraeli, ankakhulupiriranso kuti Mlengi ayenera kutamandidwa chifukwa chakuti analenga zinthu zodabwitsa. Ngakhale kuti masiku amenewo sayansi inali isanapite patsogolo, Davide anatha kuona zinthu zambirimbiri zodabwitsa zimene Mulungu analenga. Ataganizira za thupi lake, anachita nthumanzi ndi mphamvu za Mulungu za kulenga. Analemba kuti: ‘Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.’​—Salmo 139:14.

3, 4. Kodi n’chifukwa chiyani aliyense wa ife ayenera kuganizira mozama ntchito za Yehova?

3 Kuti Davide akhale ndi chikhulupiriro champhamvu ngati chimenechi, ankaganiza mozama. Masiku ano anthu, kusukulu ndi m’nkhani zofalitsidwa m’mabuku ndi m’mawailesi, amaphunzitsidwa mfundo zambirimbiri zowononga chikhulupiriro, za mmene munthu anakhalirako. Ngati tikufuna kukhala ndi chikhulupiriro ngati cha Davide, ifenso tiyenera kuganiza mozama. Si bwino kutengera maganizo a ena pankhani zazikulu, makamaka pankhani yokhudza kukhalapo kwa Mlengi ndi udindo wake.

4 Tikamaganizira za ntchito za Yehova, timayamba kumukonda kwambiri n’kukhala ndi mtima woyamikira ndipo timakhala ndi chikhulupiriro chakuti malonjezo ake onse adzakwaniritsidwa. Kenako, zimenezi zingatilimbikitse kumudziwa bwino Yehova ndi kumutumikira. Choncho, tiyeni tione mmene sayansi yamakono ikutsimikizira mfundo ya Davide yakuti ‘tinapangidwa modabwitsa.’

Anthu Amakula Modabwitsa

5, 6. (a) Kodi tonsefe moyo wathu unayamba bwanji? (b) Kodi impso zathu zimagwira ntchito yotani?

5 “Inu munalenga impso zanga; munandiumba  ndisanabadwe ine.” (Salmo 139:13) Tonsefe moyo wathu unayambira m’mimba mwa mayi athu. Tinayamba ngati kaselo kakang’ono kochepa kuposa kadontho kamene mungalembe ndi pensulo. Kaselo kosatheka kukaona ndi maso kameneka kanali kocholowana ngati kafakitale kakang’ono. Kanakula mofulumira. Potha miyezi iwiri m’mimba, ziwalo zanu zofunikira kwambiri monga impso zinali zitapangika kale. Mutabadwa, impso zanuzo zinayamba kusefa magazi anu, kuchotsamo zinthu zoipa ndi madzi osafunikira ndi kusiyamo zinthu zofunikira. Ngati ndinu munthu wamkulu ndipo impso zanu zikugwira ntchito bwinobwino, madzi okwana pafupifupi malita asanu amasefedwa m’magazi anu pamphindi 45 zilizonse.

6 Impso zanu zimathandizanso kuti mchere ndi asidi zisamachuluke kwambiri m’magazi anu ndi kuti magaziwo asamathamange kwambiri. Zimagwiranso ntchito zina zofunikira, monga kusintha vitamini D kuti thupi lithe kugwiritsa ntchito popanga mafupa olimba ndi mahomoni amene amathandiza kuti maselo ofiira a magazi apangike m’mafupa. M’pake kuti anthu ena amati impso ndi “akatswiri odziwa za mankhwala m’thupi.” *

7, 8. (a) Fotokozani mmene mwana amayambira kukula m’mimba. (b) Kodi mwana wosabadwa ‘amaombedwa monga m’munsi mwa dziko lapansi’ m’njira yotani?

7 “Thupi langa [“mafupa anga,” NW] silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m’munsi mwake mwa dziko lapansi.” (Salmo 139:15) Selo loyamba litagawikana, maselo atsopanowo anapitiriza kugawikana. Posachedwa maselowo anayamba kudziwika ntchito yake, ena anakhala a minyewa, ena a minofu, ena a khungu, ndi zina zotero. Maselo amtundu umodzi analumikizana ndi kupanga ziwalo. Mwachitsanzo, patadutsa milungu itatu kuchokera pamene mayi anu anatenga pathupi, mafupa anu anayamba kupangika. Pofika milungu 7, munali wamtali pafupifupi masentimita awiri ndi theka, ndipo mafupa anu onse 206 anali atapangika kale ngakhale kuti anali osalimba.

8 Kukula kodabwitsa kumeneku kunachitika muli m’mimba mwa mayi anu, ndipo kunali kobisika kwa anthu ngati kuti munali m’munsi mwa dziko lapansi. Zoonadi, anthu sadziwa zambiri za mmene mwana amakulira. Mwachitsanzo, kodi n’chiyani chinachititsa kuti majini ayambe kugawa maselo kuti akhale ziwalo zosiyanasiyana? Mwina m’tsogolomu asayansi adzadziwa chifukwa chake, koma malinga ndi zimene Davide ananena m’vesi lotsatira, Mlengi wathu Yehova, wakhala akudziwa zimenezi kuyambira kalekale.

9, 10. Kodi kapangidwe ka mluza ‘kanalembedwa m’buku’ la Mulungu m’njira yotani?

9 “Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.” (Salmo 139:16) Selo lanu loyamba linali ndi ndondomeko yonse ya mmene thupi lanu lidzakhalira. Miyezi 9 musanabadwe komanso zaka zoposa 20 mutabadwa, munakula motsatira ndondomeko imeneyi. Nthawi imeneyo, thupi lanu linasintha kwambiri, ndipo zonsezo zinachitika motsatira malamulo a m’selo loyamba lija.

10 Davide sankadziwa za maselo ndi majini, ndipo analibe ngakhale makina oonera tinthu ting’onoting’ono. Koma anazindikira bwinobwino kuti mmene thupi lake linkakulira, zinali umboni wakuti mapulani ake anali atalembedwa kale. Davide ayenera kuti ankadziwa mmene mluza umakulira, n’chifukwa chake anatha kufotokoza  kuti mluza umasintha motsatira ndondomeko ndi nthawi yake. M’ndakatulo yake, anafotokoza kuti ndondomeko imeneyi ‘inalembedwa m’buku’ la Mulungu.

11. Kodi zinatheka bwanji kuti tizioneka mmene timaonekeramu?

11 Masiku ano, ndi zodziwika bwino kuti maonekedwe amene munatengera kwa makolo ndi agogo anu, monga msinkhu, nkhope, maso ndi tsitsi, ndi zinthu zina zambirimbiri, munazitenga kudzera m’majini. Selo lililonse limakhala ndi majini zikwi zambiri, ndipo jini iliyonse imakhala mu kachingwe kakatali kopangidwa ndi DNA. Malangizo a kakulidwe ka thupi lanu ‘analembedwa’ mu DNA. Maselo anu akamagawikana, popanga maselo atsopano kapena oti alowe m’malo mwa maselo akale, DNA imatumiza malangizowo m’maselowo. Chifukwa cha zimenezi, mumapitiriza kukhala ndi moyo ndipo maonekedwe anu sasintha kwenikweni. Zimenezi zimasonyezadi mphamvu ndi nzeru za Mlengi wathu wakumwamba.

Anthu Ali ndi Nzeru Zapadera

12. Kodi ndi chiyani makamaka chimasiyanitsa anthu ndi zinyama?

12 “Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu zamtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga.” (Salmo 139:17, 18a) Zinyamanso zinalengedwa modabwitsa, ndipo zimatha kuchita zinthu zina zimene anthufe sitingakwanitse. Koma Mulungu anapatsa anthu nzeru zoposa nyama iliyonse. Buku lina la sayansi limati: “Ngakhale kuti anthufe timafanana m’njira zambiri ndi zinyama zina, ndife apadera kwambiri chifukwa chakuti tili ndi nzeru zotha kulankhula ndi kuganiza. Ndife apaderanso chifukwa chakuti tili ndi chidwi chofuna kudzidziwa bwino. N’chifukwa chake timadzifunsa kuti: Kodi thupi langa ndi lolumikizana bwanji? Nanga ndinapangidwa bwanji?” Davide nayenso anali ndi mafunso amenewa.

13. (a) Kodi ndi chiyani chinathandiza Davide kusinkhasinkha maganizo a Mulungu? (b) Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo cha Davide?

13 Ndiponso mbali yaikulu imene timasiyanirana ndi nyama ndi yakuti, tili ndi luso lapadera lotha kusinkhasinkha maganizo a Mulungu. * Mphatso yapadera imeneyi ndi imodzi mwa njira zosonyeza kuti tinalengedwa “m’chifanizo cha Mulungu.” (Genesis 1:27) Davide anagwiritsa ntchito bwino mphatso imeneyi. Anasinkhasinkha umboni wosonyeza kuti Mulungu aliko ndi makhalidwe ake abwino amene anaona m’chilengedwe. Davide analinso ndi mabuku akale a Malemba Oyera, m’mene Mulungu anafotokozamo za iyeyo ndi ntchito zake. Mabuku ouziridwa amenewa anathandiza Davide kumvetsa maganizo a Mulungu, umunthu wake, ndi cholinga chake. Chifukwa chosinkhasinkha Malemba, chilengedwe, ndi mmene Mulungu ankachitira ndi iye, Davide ankatamanda Mlengi wake.

 Kodi Chikhulupiriro Chimafuna Chiyani?

14. Kodi n’chifukwa chiyani kukhala ndi chikhulupiriro sikufuna kuti tichite kudziwa zonse zokhudza Mulungu?

14 Pamene Davide ankasinkhasinkha kwambiri chilengedwe ndi Malemba, m’pamenenso ankazindikira kuti ndi zosatheka kumvetsa zonse zokhudza nzeru ndi mphamvu ya Mulungu. (Salmo 139:6) N’chimodzimodzinso ifeyo. Sitingamvetse ndipo sitidzamvetsa zonse zokhudza zimene Mulungu analenga. (Mlaliki 3:11; 8:17) Koma Mulungu ‘wasonyeza’ nzeru zokwanira m’Malemba ndi m’chilengedwe, zimene panthawi iliyonse, zingathandize anthu ofuna choonadi kukhala ndi chikhulupiriro chozikidwa pa umboni wodalirika.​—Aroma 1:19, 20; Aheberi 11:1, 3.

15. Perekani chitsanzo chosonyeza kugwirizana kwa chikhulupiriro ndi ubale wathu ndi Mulungu.

15 Chikhulupiriro chimafuna zambiri osati kungovomereza chabe kuti moyo ndi chilengedwe zinakhalako chifukwa cholengedwa ndi winawake wanzeru. Chimafunanso kukhulupirira kuti Yehova Mulungu alikodi ndipo amafuna kuti timudziwe ndi kukhala pa ubale wolimba ndi iye. (Yakobe 4:8) Zimenezi tingaziyerekezere ndi chikhulupiriro chimene mwana amakhala nacho pa bambo ake amene amamukonda. Ngati munthu wina angatsutse kuti bambo anu sangakuthandizeni nthawi ya mavuto, popanda umboni zingakuvuteni kumutsimikizira kuti bambo anu ndi munthu wodalirika. Koma ngati muli ndi umboni wakuti bambo anu ndi munthu wabwino chifukwa cha zimene akhala akukuchitirani, mutha kukhala ndi chikhulupiriro chakuti akuthandizani. Mofananamo, tikamudziwa Yehova chifukwa chophunzira Malemba, kusinkhasinkha chilengedwe, ndi kuona mmene amayankhira mapemphero athu ndi kutithandiza, timamukhulupirira. Ndiponso timafuna kuphunzira zambiri za iye ndi kumutamanda kosatha. Timatero chifukwa chomukonda ndi mtima wathu wonse komanso chifukwa cha kudzipereka kwathu. Kuchita zimenezi ndi kofunika kwambiri kuposa chilichonse.​—Aefeso 5:1, 2.

Tizipempha Mlengi Wathu Kutitsogolera

16. Kodi tikuphunzirapo chiyani paubale wolimba wa Davide ndi Yehova?

16 “Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.” (Salmo 139:23, 24) Davide ankadziwa kuti Yehova ankamudziwa bwino iyeyo. Chilichonse chimene ankaganiza, kulankhula kapena kuchita, Mlengi wake ankachidziwa. (Salmo 139:1-12; Aheberi 4:13) Popeza kuti Mulungu ankamudziwa bwino Davide, Davideyo ankaona kuti ndi wotetezeka monga mmene mwana wamng’ono amamvera akakhala ndi makolo ake amene amamukonda. Davide ankaona ubale wake ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali ndipo ankayesetsa kuulimbitsa mwa kuganizira mozama za ntchito Zake ndi mwa kupemphera. Pajatu masalmo ambiri a Davide, kuphatikizapo Salmo 139, ndi mapemphero amene kwenikweni anali kuchita kuwaimba. Kusinkhasinkha ndi kupemphera kungatithandize ifenso kuyandikira Yehova.

17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Davide anapempha Yehova kusanthula mtima wake? (b) Kodi njira imene timagwiritsira ntchito ufulu wathu imakhudza bwanji moyo wathu?

 17 Popeza kuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, tili ndi ufulu wosankha zochita. Tingasankhe kuchita zabwino kapena zoipa. Chifukwa cha ufuluwu, tidzayankha mlandu wa zimene timachita. Davide sanafune kuikidwa m’gulu la anthu oipa. (Salmo 139:19-22) Sanafune kuchita zinthu zimene zikanamubweretsera mavuto. Choncho, atasinkhasinkha mfundo yakuti Yehova amadziwa zonse, Davide modzichepetsa anapempha Mulungu kusanthula mtima wake ndi kumutsogolera pa njira ya kumoyo. Mfundo zolungama za Mulungu za makhalidwe abwino zimagwira ntchito kwa aliyense, choncho ifenso tiyenera kuchita zinthu mwanzeru. Yehova amalimbikitsa tonsefe kumumvera. Tikatero, amatiyanja ndipo timapindula kwambiri. (Yohane 12:50; 1 Timoteyo 4:8) Kuyenda ndi Yehova tsiku ndi tsiku kumatithandiza kukhala pa mtendere, ngakhale tili m’mavuto aakulu.​—Afilipi 4:6, 7.

Tizitsatira Mlengi Wathu Wodabwitsayo

18. Kodi Davide atasinkhasinkha chilengedwe, anamanga mfundo yotani?

18 Ali mnyamata, Davide nthawi zambiri ankakhala kobusa nkhosa. Ali kumeneko, nkhosa zikawerama kudya msipu, iye ankakweza maso ake kumwamba. Madzulo kukada, Davide ankaganizira za ukulu wa chilengedwe ndi zimene ankaphunzirapo. Analemba kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Usana ndi usana uchulukitsa mawu, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.” (Salmo 19:1, 2) Davide anaona kuti afunika kufunafuna ndi kutsatira amene analenga zinthu zonse zodabwitsazo. Ifenso tifunika kutero.

19. Kodi achichepere ndi achikulirefe tikuphunzira chiyani pamfundo yakuti ‘tinapangidwa modabwitsa’?

19 Zimene Davide anachita zinapereka chitsanzo cha uphungu umene Solomo mwana wake anadzapereka kwa achinyamata. Iye anati: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako . . . Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” (Mlaliki 12:1, 13) Ali mnyamata, Davide anali atadziwa kale kuti ‘anapangidwa modabwitsa.’ Zimene anachita chifukwa chodziwa zinthu zimenezi zinamupindulitsa moyo wake wonse. Ngati ifeyo, achichepere ndi achikulire omwe, tikutamanda ndi kutumikira Mlengi Wamkuluyo, tidzakhala ndi moyo wosangalala panopa ndi m’tsogolo. Za anthu oyandikana ndi Yehova ndi amene amatsatira njira zake zolungama, Baibulo limati: “Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri: Kulalikira kuti Yehova n’ngolunjika.” (Salmo 92:14, 15) Choncho, tingayembekezere kudzasangalala kosatha ndi ntchito zodabwitsa za Mlengi wathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Onani Galamukani! ya July 8, 2004, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 6 Onaninso nkhani yakuti “Your Kidneys​—A Filter for Life,” mu Galamukani! ya Chingelezi ya August 8, 1997.

^ ndime 13 Mawu a Davide pa Salmo 139:18b akuoneka kuti akutanthauza kuti, akanati awerengetse maganizo a Yehova tsiku lonse mpaka usiku n’kugona kenako n’kudzuka m’mawa ndi kuyambiranso, sakanamaliza kuwerengetsako.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi kakulidwe ka mluza kamasonyeza bwanji kuti ‘tinapangidwa modabwitsa’?

• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusinkhasinkha maganizo a Yehova?

• Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chikhulupiriro ndi ubale wathu ndi Yehova?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 23]

Mwana wosabadwa amakula motsatira ndondomeko yapadera

DNA

[Mawu a Chithunzi]

Unborn fetus: Lennart Nilsson

[Chithunzi patsamba 24]

Mofanana ndi mwana amene amakhulupirira bambo ake, ifenso timakhulupirira Yehova

[Chithunzi patsamba 25]

Kusinkhasinkha ntchito za Yehova kunalimbikitsa Davide kutamanda Mulungu