Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mphatso Yosatha Yochokera kwa Mlengi

Mphatso Yosatha Yochokera kwa Mlengi

 Mphatso Yosatha Yochokera kwa Mlengi

KODI si zodabwitsa kuti zinthu zimene asayansi amati n’zofunikira kuti papulaneti pakhale zamoyo, zatchulidwa m’chaputala choyamba cha m’Baibulo? Kodi zinthu zimenezi n’ziti?

Kuti zamoyo zikhale bwino, payenera kukhala madzi ambiri, omwe atchulidwa pa Genesis 1:2. Papulanetipo pafunika kukhala potentha bwino kuti madzi asaundane kapena kusanduka nthunzi. Kuti zimenezi zitheke, pulaneti limafunika kuti likhale lotalikirana bwino ndi dzuwa lake. Nkhani ya m’Genesis imatchula kangapo za dzuwa ndi mmene dzuwalo limakhudzira dziko lapansi.

Kuti anthu athe kukhala pa pulaneti, pulanetilo liyenera kukhala ndi thambo la mpweya wosiyanasiyana wofunika. Thambo lotereli latchulidwa pa Genesis 1:6-8. Zomera zotchulidwa pa Genesis 1:11, 12, zimathandiza kuti pakhale mpweya wabwino wambiri. Pamafunika mtunda kapena nthaka yachonde, ngati yomwe yafotokozedwa pa Genesis 1:9-12, kuti zinyama zosiyanasiyana zithe kukhala bwinobwino papulaneti. Ndipo, kuti nyengo ikhale yabwino, pulaneti liyenera kupendekeka bwino ndi kusasunthasuntha. Mphamvu yokoka ya mwezi ndi chimodzi cha zinthu zimene zimathandiza dziko lapansi kuchita zimenezi. Lemba la Genesis 1:14, 16 limafotokoza za mwezi ndi ubwino wake wina.

Popanda kuthandizidwa ndi sayansi yamakono, kodi Mose anatha bwanji kufotokoza zinthu zimene tatchula pamwambazi? Kodi anangokhala ndi luso lozindikira kufunika kwa zinthu zimene ena sanazindikire pa nthawiyo? Ayi, koma anazindikira zimenezi chifukwa anauziridwa ndi Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi. Zimenezi n’zomveka popeza nkhani ya m’Genesis n’njogwirizana kwambiri ndi sayansi.

Baibulo limatiuza kuti zinthu zodabwitsa zomwe timaona m’chilengedwe zili ndi cholinga. Lemba la Salmo 115:16 limati: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” Salmo lina limati: “Anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthawi yonse.” (Salmo 104:5) Ngati chilengedwe chonse ndi dziko lapansi lokongolali zinalengedwa ndi Mlengi, n’kwanzeru kukhulupirira kuti akhozanso kuzisamalira. Choncho mungayembekezere kukwaniritsidwa kwa lonjezo losangalatsa lakuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Ndithudi, Mulungu “sanalilenga [dziko lapansi] mwachabe,” koma “analiumba akhalemo [kosatha] anthu” omwe amazindikira kuti iyeyo ndiye analenga zinthu.​—Yesaya 45:18.

Malemba amasonyeza kuti Yesu anabwera pa dziko lapansi kuti atiphunzitse za Mulungu ndi cholinga Chake chopatsa anthu omvera moyo wosatha. (Yohane 3:16) Tikudziwa kuti posachedwapa Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko,’ koma adzapulumutsa anthu okonda mtendere a m’mitundu yonse omwe amatsatira njira yake yopulumutsira anthu. (Chivumbulutso 7:9, 14; 11:18) Moyo udzakhaladi wosangalatsa kwabasi anthu akamadzaphunzirabe ndi kusangalala kwa muyaya ndi zinthu zabwino kwambiri zomwe Mulungu analenga.​—Mlaliki 3:11; Aroma 8:21.

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

NASA photo