Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amuna, Muzitsanzira Umutu wa Khristu

Amuna, Muzitsanzira Umutu wa Khristu

 Amuna, Muzitsanzira Umutu wa Khristu

“Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.”​—1 AKORINTO 11:3.

1, 2. (a) Kodi mwamuna wabwino tingam’zindikire bwanji? (b) N’chifukwa chiyani m’pofunika kwambiri kuzindikira kuti ukwati anauyambitsa ndi Mulungu?

KODI mwamuna wabwino mungam’zindikire bwanji? Poona nzeru, luso, kapena mphamvu zake? Poona ndalama zimene amapeza? Kapena kodi makamaka ndi poona mmene amasamalirira mkazi wake ndi ana ake mwachikondi? Tikatengera njira yomalizirayi, amuna ambiri amalephera, chifukwa amatsanzira mzimu wa dzikoli ndi mfundo za anthu. Chifukwa chiyani? Makamaka n’chifukwa choti amalephera kuzindikira ndi kutsatira malangizo a Woyambitsa ukwati, amene anatenga nthiti ‘mwa Adamu naipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.’​—Genesis 2:21-24.

2 Yesu Khristu anatsimikizira nkhani ya m’Baibulo imeneyi yosonyeza kuti ukwati anauyambitsa ndi Mulungu, ndipo ananena kwa anthu otsutsa a m’nthawi yake kuti: “Kodi simunawerenge kuti iye amene analenga iwo pachiyambi pomwe anapanga iwo mwamuna ndi mkazi ndi kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho, chimene Mulungu wachimanga pamodzi [mu ukwati], munthu asachilekanitse.” (Mateyo 19:4-6) Zoona zake n’zakuti munthu amakhala ndi ukwati wabwino akazindikira kuti ukwati anauyambitsa ndi Mulungu ndipo umayenda bwino munthu akamatsatira malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo.

Zimene Zingathandize Mwamuna

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Yesu amadziwa bwino kwambiri nkhani ya ukwati? (b) Kodi mkazi wa Yesu wophiphiritsira ndani, ndipo kodi amuna ayenera kutengera chitsanzo cha ndani pochita zinthu ndi akazi awo?

3 Chinthu chimodzi chimene chingathandize mwamuna ndicho kuphunzira zimene Yesu ananena ndi kutsanzira zimene anachita. Iye amadziwa bwino kwambiri nkhani ya ukwati, chifukwa analipo pamene mwamuna ndi mkazi oyambirira analengedwa komanso paukwati wawo. Yehova Mulungu anauza Yesu kuti: ‘Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu.’ (Genesis 1:26) Mulungu anali kulankhula ndi Yesu, amene anamulenga asanalenge aliyense kapena chilichonse, ndiponso amene ‘anali pambali pake ngati mmisiri.’ (Miyambo 8:22-30) Ameneyu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” kapena kuti, ndi “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu,” ndipo analipo zinthu zina zonse zisanalengedwe.​—Akolose 1:15; Chivumbulutso 3:14.

4 Yesu amatchedwa “Mwanawankhosa wa Mulungu” ndipo amafotokozedwa mophiphiritsira ngati mwamuna. Nthawi ina mngelo anati: “Bwera kuno ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.” (Yohane 1:29; Chivumbulutso 21:9) Nanga kodi mkwatibwi, kapena kuti mkazi wake, ndani? “Mkazi wa Mwanawankhosa” wapangidwa ndi otsatira a Khristu okhulupirika odzozedwa ndi mzimu, amene adzalamulire naye limodzi kumwamba. (Chivumbulutso 14:1, 3) Choncho mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ophunzira ake pamene anali nawo padziko lapansi, n’chitsanzo kwa amuna cha momwe ayenera kuchitira zinthu ndi akazi awo.

5. Kodi Yesu ndi chitsanzo kwa ndani?

5 N’zoona kuti Yesu amatchulidwa m’Baibulo monga chitsanzo kwa otsatira ake onse, chifukwa timawerenga kuti: “Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa.” (1 Petulo 2:21) Komabe, iye ndi chitsanzo makamaka kwa amuna. Baibulo limati: “Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna; ndi  mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Popeza Khristu ndi mutu wa mwamuna, amuna ayenera kutsatira chitsanzo chake. Choncho mfundo ya umutu iyenera kutsatiridwa kuti banja liziyenda bwino ndiponso kuti likhale losangalala. Kuti zimenezi zitheke, amuna ayenera kuchita zinthu mwachikondi ndi akazi awo monga momwe Yesu amachitira zinthu ndi mkazi wake wophiphiritsira. Mkazi ameneyu ndi ophunzira ake odzozedwa.

Mmene Mungalimbanirane ndi Mavuto a M’banja

6. Kodi amuna ayenera kukhala bwanji ndi akazi awo?

6 M’dziko lovuta la masiku anoli, amuna makamaka ayenera kutsanzira chitsanzo cha Yesu cha chikondi, kuleza mtima, ndi kulimba mtima potsatira mfundo zolungama. (2 Timoteyo 3:1-5) Ponena za chitsanzo chimene Yesu anapereka, Baibulo limati: “Amuna, pitirizani kukhala nawo [akazi anu] mowadziwa bwino.” (1 Petulo 3:7) Inde, amuna ayenera kulimbana ndi mavuto a m’banja mwanzeru, monga momwe Yesu analimbanirana ndi mavuto. Iye anakumana ndi mayesero ambiri kuposa munthu wina aliyense, koma ankadziwa kuti mayeserowo ankawachititsa ndi Satana, ziwanda zake, ndi dziko loipali. (Yohane 14:30; Aefeso 6:12) Yesu sanadabwe pokumana ndi mayesero, choncho mwamuna ndi mkazi wake sayeneranso kudabwa akamakumana ndi “nsautso m’thupi mwawo.” Baibulo limachenjeza kuti amene alowa m’banja angayembekezere kukhala ndi nsautso yoteroyo.​—1 Akorinto 7:28.

7, 8. (a) Kodi kukhala ndi akazi mowadziwa bwino kumatanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani akazi ayenera kulemekezedwa?

7 Baibulo limati amuna ayenera kukhala ndi akazi awo “mowadziwa bwino, kupatsa ulemu mkazi monga chiwiya chosalimba.” (1 Petulo 3:7) Baibulo linaneneratu kuti amuna ambiri azidzalamulira akazi awo mwankhanza. M’malo mochita zimenezi, mwamuna amene amayanjidwa ndi Mulungu amalemekeza mkazi wake. (Genesis 3:16) Amamuchitira zinthu ngati kuti mkaziyo ndi chinthu cha mtengo wapatali, ndipo sagwiritsa ntchito mphamvu zake mwankhanza. M’malo mwake, amaganizira momwe mkaziyo akumvera, ndipo nthawi zonse amamulemekeza.

8 N’chifukwa chiyani amuna ayenera kulemekeza akazi awo? Baibulo limayankha kuti: ‘Pakutinso mudzalandira nawo limodzi mphatso yachisomo ya moyo, kuti mapemphero anu asatsekerezedwe.’ (1 Petulo 3:7) Amuna ayenera kuzindikira kuti Yehova saona kuti olambira ake aamuna ndi apamwamba m’njira iliyonse kuposa olambira ake aakazi. Akazi ovomerezedwa ndi Mulungu adzalandira mphoto ya moyo wosatha limodzi ndi amuna, ndipo ambiri adzapatsidwa moyo kumwamba, kumene ‘kulibe mwamuna kapena mkazi.’ (Agalatiya 3:28) Choncho amuna ayenera kukumbukira kuti kukhulupirika n’kumene kumam’chititsa munthu kukhala wamtengo wapatali kwa Mulungu. Si chifukwa chakuti munthuyo ndi mwamuna, mkazi, kapena mwana.​—1 Akorinto 4:2.

9. (a) Malinga ndi zimene ananena Petulo, kodi amuna ayenera kulemekeza akazi awo pachifukwa chiti? (b) Kodi Yesu analemekeza bwanji akazi?

9 Kufunika koti mwamuna azilemekeza mkazi wake kukugogomezeredwa ndi mawu a Petulo, oti “kuti mapemphero anu asatsekerezedwe.” Kutsekerezedwa koteroko kukhozadi  kukhala koopsa kwambiri! Mpaka kungachititse kuti mapemphero a mwamuna atchingidwe, monga momwe zinachitikira ndi atumiki ena a Mulungu akale amene sanachite bwino zinthu. (Maliro 3:43, 44) Amuna achikhristu, okwatira komanso amene akuganizira zokwatira, angachite bwino kuphunzira mmene Yesu ankalemekezera akazi. Iye anasangalala kukhala ndi akazi m’gulu la anthu amene ankatsagana naye mu utumiki wake, ndipo ankawachitira zinthu mokoma mtima ndi mwaulemu. Panthawi ina, Yesu mpaka anauza akazi mfundo yodabwitsa kwambiri ya choonadi asanauze amuna, n’kuwauza kuti akauze amunawo mfundoyo.​—Mateyo 28:1, 8-10; Luka 8:1-3.

Chitsanzo Makamaka kwa Amuna

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani amuna makamaka ayenera kuganizira mozama za chitsanzo cha Yesu? (b) Kodi amuna ayenera kusonyeza bwanji chikondi kwa akazi awo?

10 Monga taonera kale, Baibulo limayerekezera ubwenzi wa mwamuna ndi mkazi wake ndi ubwenzi wa Khristu ndi “mkwatibwi” wake, yemwe ndi mpingo wa otsatira ake odzozedwa. Limati: “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso Khristu alili mutu wa mpingo.” (Aefeso 5:23) Mawu amenewa ayenera kulimbikitsa amuna kuganizira mozama mmene Yesu ankatsogolera otsatira ake. Amuna akaganizira zimenezi mozama m’pamene angathe kutsatira bwino chitsanzo cha Yesu n’kutsogolera, kukonda, ndi kusamalira akazi awo ngati mmene Yesu anachitira ndi mpingo wake.

11 Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aefeso 5:25) M’chaputala chachinayi cha Aefeso, “mpingowo” ukutchedwa “thupi la Khristu.” Thupi lophiphiritsira limeneli n’lopangidwa ndi anthu ambiri, amuna ndi akazi, ndipo onse amathandizira kuti thupilo lizigwira ntchito bwino. Koma Yesu ndiye “mutu wa thupilo, mpingo.”​—Aefeso 4:12; Akolose 1:18; 1 Akorinto 12:12, 13, 27.

12. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anakonda thupi lake lophiphiritsira?

12 Yesu anasonyeza kuti anakonda thupi lake lophiphiritsira, “mpingowo” makamaka m’njira yachikondi imene anasamalira anthu amene anadzakhala mbali ya mpingowo. Mwachitsanzo, ophunzira ake atatopa, iye anati: “Bwerani . . . kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.” (Maliko 6:31) Pofotokoza zimene Yesu anachita patangotsala maola ochepa kuti aphedwe, mmodzi mwa atumwi ake analemba kuti: “Yesu . . . popeza kuti anali kuwakonda akewo [kutanthauza anthu omwe anali ziwalo za thupi lake lophiphiritsira] . . . anawakonda mpaka mapeto.” (Yohane 13:1) Yesu anaperekadi chitsanzo chabwino kwambiri cha momwe amuna ayenera kuchitira zinthu ndi akazi awo!

13. Kodi amuna akulangizidwa kuti azikonda motani akazi awo?

13 Popitiriza kugwiritsira ntchito chitsanzo chimene Yesu anasiyira amuna, mtumwi Paulo anawalangiza kuti: “Mwa njira imeneyi amuna akonde akazi awo monga matupi awoawo. Amene akonda mkazi wake adzikonda iye mwini, pakuti  palibe munthu anadapo thupi la iye mwini; koma amalidyetsa ndi kulisamala, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo.” Paulo anawonjezera kuti: “Aliyense wa inu akonde mkazi wake monga adzikonda iye mwini.”​—Aefeso 5:28, 29, 33.

14. Kodi mwamuna amasamalira bwanji thupi lake lopanda ungwiro, ndipo zimenezi zikusonyeza chiyani za mmene ayenera kuchitira zinthu ndi mkazi wake?

14 Taganizirani mawu a Paulo ali pamwambawa. Kodi munthu amene mutu wake ukuyenda bwinobwino angavulaze dala thupi lake? Munthu akapunthwa ndi chala chake, kodi amachimenya chifukwa cham’punthwitsa? Ayi, satero! Kodi mwamuna amadzichititsa yekha manyazi pamaso pa anzake kapena kudzinena yekha miseche? Ayi! Nangano n’chifukwa chiyani angalalatire mkazi wake kapena kum’menya kumene akalakwitsa kanthu? Amuna ayenera kuganiziranso zofuna za akazi awo, osati zawo zokha.​—1 Akorinto 10:24; 13:5.

15. (a) Kodi Yesu anachita chiyani poganizira kufooka kwa ophunzira ake? (b) Kodi amuna angaphunzire chiyani ku chitsanzo chake?

15 Taganizirani zimene zinachitika patatsala tsiku limodzi kuti Yesu afe. Iye anasonyeza kuti anali kudera nkhawa ophunzira ake, ophunzirawo atasonyeza kufooka. Ngakhale kuti ali m’munda wa Getsemane iye anawapempha mobwerezabwereza kuti apemphere, m’malo mopemphera iwo anagona katatu. Mwadzidzidzi, amuna onyamula zida anawazungulira. Yesu anafunsa amunawo kuti: “Mukufuna ndani?” Atayankha kuti: “Yesu Mnazareti,” iye anati: “Ndine amene.” Podziwa kuti “nthawi yakwana” yoti afe, iye anati: “Ngati mukufuna ine, alekeni awa apite.” Yesu nthawi zonse ankaganizira ophunzira ake, omwe anali mbali ya mkwatibwi wake wophiphiritsira, ndipo anawapezera njira yothawira. Poona momwe Yesu anachitira zinthu ndi ophunzira ake, amuna angapeze mfundo zambiri zomwe angatsatire pochita zinthu ndi akazi awo.​—Yohane 18:1-9; Maliko 14:34-37, 41.

Chikondi cha Yesu Si Chongotengeka Maganizo

16. Kodi Yesu anali ndi ubwenzi wotani ndi Marita, komabe kodi anam’langiza bwanji?

16 Baibulo limati: ‘Yesu anali kukonda Marita ndi m’bale wake, ndi Lazaro,’ amene nthawi zambiri ankamulandira monga mlendo m’nyumba mwawo. (Yohane 11:5) Komabe, Yesu sanalephere kumulangiza Marita pamene ankadera nkhawa kwambiri za chakudya chimene anali kukonza, n’kusowa nthawi yoti alandire malangizo auzimu kwa iye. Iye anati: “Marita, Marita, ukuda nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri. Komatu zinthu zofunika kwenikweni n’zochepa chabe, mwinanso n’chimodzi chokha basi.” (Luka 10:41, 42) Mosakayikira Marita sanavutike kutsatira malangizo a Yesu chifukwa choti Yesuyo ankamukonda. Chimodzimodzinso, amuna ayenera kuchita zinthu ndi akazi awo mokoma mtima ndi mwachikondi, ndipo aziwalankhula ndi mawu abwino. Komabe, pakafunika kuwongolera zinthu, m’pofunika kulankhula molimba mtima ngati mmene Yesu anachitira.

17, 18. (a) Kodi Petulo anadzudzula bwanji Yesu, ndipo n’chifukwa chiyani Petulo anafunika kudzudzulidwa? (b) Kodi mwamuna ali ndi udindo wotani?

17 Panthawi ina, Yesu anafotokozera atumwi ake kuti iye ayenera kupita ku Yerusalemu,  kumene akazunzidwe ndi “akulu, ndi ansembe aakulu, komanso alembi. Ndiyeno akaphedwa, ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” Petulo atamva zimenezi anamutengera Yesu pambali n’kuyamba kumudzudzula kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye; musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” N’zoonekeratu kuti Petulo anangotengeka maganizo ndipo anafunika kudzudzulidwa. Chotero Yesu anamuuza kuti: “Ndichokere, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”​—Mateyo 16:21-23.

18 Yesu anali atangonena kumene zimene Mulungu ankafuna, zoti adzavutika kwambiri n’kuphedwa. (Salmo 16:10; Yesaya 53:12) Choncho Petulo analakwa poyamba kum’dzudzula Yesu. Motero Petulo anafunika kudzudzulidwa mwamphamvu, monga momwe tonsefe timafunikira nthawi ndi nthawi. Monga mutu wa banja, mwamuna ali ndi mphamvu komanso udindo wodzudzula banja lake, kuphatikizapo mkazi wake. Ngakhale kuti nthawi zina pamafunika kudzudzula mwamphamvu, ayenera kuchita zimenezi mokoma mtima ndi mwachikondi. Choncho monga momwe Yesu anathandizira Petulo kuti aone bwino zinthu, nthawi zina amuna angafunike kuchita zomwezo ndi akazi awo. Mwachitsanzo, mwamuna angafunike kufotokoza mokoma mtima chifukwa chimene mkazi wake akufunikira kusintha. Angafunike kuchita zimenezi ngati zovala, zibangili, ndolo, kapena zodzoladzola za mkazi wake zayamba kusiyana ndi zimene Malemba amalimbikitsa.​—1 Petulo 3:3-5.

Ndi Bwino Kuti Amuna Azikhala Oleza Mtima

19, 20. (a) Kodi pakati pa atumwi a Yesu panali vuto lotani, ndipo Yesu anachitapo chiyani? (b) Kodi khama la Yesu linam’pindulira?

19 Ngati pali vuto, amuna sayenera kuyembekezera kuti khama lawo lofuna kuthetsa vutolo lingabale zipatso nthawi yomweyo. Zinatenga nthawi kuti Yesu asinthe maganizo a atumwi ake. Mwachitsanzo, ankapikisana pakati pawo ndipo zimenezi zinadzaonekeranso chakumapeto kwa utumiki wa Yesu pamene atumwiwo anakangananso kuti ndani pakati pawo anali wamkulu. (Maliko 9:33-37; 10:35-45) Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anakangana kachiwiri, Yesu anakonza zokondwerera nawo limodzi Pasika yake yomaliza. Panthawi imeneyo, palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anadzipereka kugwira ntchito yooneka ngati yonyozeka yosambitsa mapazi awo afumbi. Yesu ndiye anachita zimenezi. Kenako anati: “Ndakupatsani chitsanzo.”​—Yohane 13:2-15.

20 Amuna amene amasonyeza mtima wodzichepetsa ngati wa Yesu mosakayikira akazi awo angamachite zinthu mogwirizana nawo. Koma m’pofunika kuleza mtima. Patapita nthawi usiku womwewo, atumwiwo anakangananso zoti ndani wa iwo anali wamkulu. (Luka 22:24) Kuti munthu asinthe maganizo ndi khalidwe lake, kawirikawiri pamafunika nthawi ndiponso zimachitika pang’onopang’ono. Koma zimakhala zosangalatsa kwambiri akasintha monga mmene atumwi anachitira!

21. Pokumana ndi mavuto masiku ano, kodi amuna akulimbikitsidwa kuchita chiyani?

21 Masiku ano, ukwati ukukumana ndi mavuto aakulu kuposa kale lonse. Anthu ambiri salemekezanso malumbiro awo a ukwati. Choncho amunanu, ganizirani za chiyambi cha ukwati. Kumbukirani kuti Mulungu wathu wachikondi, Yehova ndiye anayambitsa ukwati. Iye anapereka Mwana wake, Yesu, osati kuti akhale chabe Wopereka dipo, kapena Mpulumutsi wathu, koma kuti akhalenso chitsanzo kwa amuna.​—Mateyo 20:28; Yohane 3:29; 1 Petulo 2:21.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani m’pofunika kuzindikira mmene ukwati unayambira?

• Kodi amuna akulimbikitsidwa kusonyeza motani chikondi kwa akazi awo?

• Kodi ndi zitsanzo ziti za mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ophunzira ake zimene zikusonyeza mmene mwamuna angakhalire mutu ngati Khristu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 14]

N’chifukwa chiyani amuna ayenera kuganizira mozama zitsanzo zosonyeza momwe Yesu ankachitira zinthu ndi akazi?

[Chithunzi patsamba 15]

Ophunzira ake atatopa, Yesu anawaganizira

[Chithunzi patsamba 16]

Amuna ayenera kulangiza akazi awo ndi mawu okoma mtima ndi abwino