Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dzuwa ndi Mapulaneti Olizungulira Zinakhalako Bwanji?

Kodi Dzuwa ndi Mapulaneti Olizungulira Zinakhalako Bwanji?

 Kodi Dzuwa ndi Mapulaneti Olizungulira Zinakhalako Bwanji?

PALI zinthu zambiri zomwe zimapangitsa kuti malo omwe kuli dzuwa lathu ndi mapulaneti olizungulira akhale apadera kwambiri m’chilengedwe chonse. Malo amenewa ali pakati pa zigawo ziwiri za mlalang’amba wa Milky Way, komwe kulibe nyenyezi zambiri. Pafupifupi nyenyezi zonse zomwe timatha kuona usiku zili kutali kwambiri moti ngakhale akaziyang’ana ndi zipangizo zamphamvu zoonera zinthu zakutali, nyenyezizo zimangoonekabe ngati timadontho towala. Kodi dzuwa lathu ndi mapulaneti olizungulira ziyenera kukhala pa malo amenewa?

Dzuwa lathu ndi mapulaneti olizungulira zikanakhala pakati penipeni pa mlalang’amba wa Milky Way, tikanavutika kwambiri chifukwa chokhala pafupi ndi nyenyezi zambiri zoyandikana. Mwachitsanzo, zimenezi zikanachititsa kuti dziko lapansi lisinthe mmene limayendera pozungulira dzuwa, ndipo moyo wa anthu ukanasokonezeka kwambiri. Koma, dzuwa ndi mapulaneti olizungulira sizikumana ndi vuto limeneli chifukwa zili pa malo abwino kwambiri m’mlalang’amba wathu. Sizikumananso ndi mavuto ena, monga kutenthedwa kwambiri podutsa mitambo yopangidwa ndi mpweya komanso kukumana ndi nyenyezi zimene zikuphulika kapena cheza chakupha.

Dzuwa ndi nyenyezi yabwino kwambiri kwa ife. Limayaka nthawi zonse, n’lokhalitsa, si lalikulu kwambiri ndiponso silitentha mopambanitsa. Nyenyezi zambiri m’mlalang’amba wathu n’zazing’ono poyerekezera ndi dzuwa lathu ndipo siziwala kapena kutentha mokwanira kuti papulaneti ngati dziko lapansi pakhale moyo. Ndiponso, nyenyezi zambiri zimakokana ndi nyenyezi zina, ndipo zimayenda mozungulirana. Koma mosiyana ndi zimenezi, dzuwa lathu silikokana ndi nyenyezi zina. Tikanakhala ndi nyenyezi ziwiri kapena zingapo zangati dzuwa, mosakayikira zikanasokoneza dziko lapansi ndi mapulaneti ena ozungulira dzuwa chifukwa cha mphamvu yokoka ya nyenyezizo.

Chinthu china chimene chimachititsa kuti dzuwa lathu ndi mapulaneti olizungulira zikhale zapadera, n’choti mapulaneti aakulu ali kutali ndi dzuwalo. Ndipo mapulanetiwa akamazungulira dzuwa mphamvu yawo yokoka sisokoneza mapulaneti ena apafupi ndi dzuwa, okhala ndi nthaka ngati dziko lapansi. * M’malo mwake, mapulaneti akutaliwa amatchinga mapulaneti ena kuti zinthu zoopsa zisawagunde. Akatswiri awiri a sayansi, Peter D. Ward ndi Donald Brownlee m’buku lawo lakuti Rare Earth​—Why Complex Life Is Uncommon in the Universe, anati: “Miyala ya mumlengalenga ndi nyenyezi zoyenda sizigunda dziko lathu kawirikawiri chifukwa cha mapulaneti aakulu ampweya akutali monga Jupiter.” Papezekanso nyenyezi zina zangati dzuwa zomwe zili ndi mapulaneti aakulu ozizungulira. Koma ambiri a mapulaneti amenewa akamazungulira dzuwa lawo akhoza kuwononga mapulaneti ena aang’ono ofanana ndi dziko lapansi.

Ntchito ya Mwezi

Kuyambira kalekale, anthu akhala akuchita chidwi ndi mwezi wathu. Wachititsa anthu kulemba ndakatulo ndi nyimbo. Mwachitsanzo, wolemba ndakatulo wina wachiheberi wakale anafotokoza kuti mwezi “udzakhazikika . . . ku  nthawi yonse . . . ngati mboni yokhulupirika kuthambo.”​—Salmo 89:37.

Njira imodzi yofunika imene mwezi umakhudzira moyo padziko lapansi ndi mmene mphamvu yake yokoka imachititsira mafunde a m’nyanja kukwera kapena kutsika. Akatswiri amati kukwera ndi kutsika kwa mafunde n’kofunika kwambiri kuti madzi a m’nyanja aziyenda. Ndipo kuyenda kwa madzi a m’nyanja kumeneku kumachititsa nyengo zosiyanasiyana.

Ndiponso mphamvu yokoka ya mwezi imathandiza kuti dziko lapansi likhale mopendekeka ndipo lisamasunthesunthe likamazungulira dzuwa. Magazini ya sayansi yotchedwa Nature, imanena kuti popanda mwezi, kupendekeka kwa dziko lapansi kukanasintha kwambiri m’kupita kwa nthawi. Tangoganizani zomwe zingachitike dziko lapansi likanakhala kuti silinapendekeke. Sitikanakhala ndi nyengo zosiyanasiyana zosangalatsa ndipo si bwenzi kukugwa mvula yokwanira. Komanso, kupendekeka kwa dziko lapansi kumathandiza kuti kusamatenthe kapena kuzizira kwambiri moti anthu sangathe kukhalapo. Katswiri wa zakuthambo, Jacques Laskar, anati: “Nyengo za padziko lapansi n’zodalirika chifukwa cha Mwezi.” Mwezi wathu umathandiza choncho chifukwa ndi waukulu kuposa miyezi ya mapulaneti aakulu.

Ntchito inanso ya mwezi inafotokozedwa ndi wolemba buku la m’Baibulo la Genesis amene anati mwezi umaunikira usiku.​—Genesis 1:16.

Kodi Zinangokhalako Zokha Kapena Zinachita Kupangidwa?

Kodi munthu angafotokoze bwanji zinthu zosiyanasiyana zimene zimapangitsa kuti padziko lapansi pakhale moyo komanso kuti moyowo ukhale wosangalatsa? Pangakhale zifukwa ziwiri zokha. Chifukwa choyamba chingakhale choti zonsezi zinangokhalako zokha. Ndipo chachiwiri chingakhale choti zinapangidwa ndi cholinga chapadera.

Zaka masauzande ambiri zapitazo, Malemba Opatulika ananena kuti chilengedwe chonse chinapangidwa ndi Mlengi, yemwe ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Ngati zimenezi n’zoona, ndiye kuti dzuwa lathu ndi mapulaneti olizungulira sizinangokhalako zokha ayi, koma zinachita kulengedwa. Ndipo Mlengi anatilembera zimene anachita kuti padziko lapansi pakhale moyo. Mwina zingakudabwitseni kudziwa kuti ngakhale kuti zimenezi zinalembedwa m’buku la Baibulo la Genesis pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, zikugwirizana ndi zimene asayansi amakhulupirira. Tiyeni tione zimene buku la Genesis limanena.

Nkhani ya mu Genesis Yonena za Kulengedwa kwa Zinthu

“Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Mawu oyambirira a m’Baibulo amenewa amanena za kulengedwa kwa dzuwa lathu ndi mapulaneti olizungulira, kuphatikizapo dziko lathu lapansi, ndiponso nyenyezi zonse za m’milalang’amba  mabiliyoni ambiri yomwe ili m’chilengedwe. Baibulo limanena kuti panthawi inayake dziko lapansi “linali lopanda kanthu.” Kunalibe makontinenti kapena mtunda. Koma mawu otsatira amatchula zimene asayansi amati ndi chinthu chofunika kwambiri kuti papulaneti pakhale moyo. Chinthucho ndi madzi ambiri. “Mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi.”​—Genesis 1:2.

Pulaneti iyenera kutalikirana bwino ndi dzuwa lake kuti madzi asaundane kapena kusanduka nthunzi. Katswiri wa mapulaneti, Andrew Ingersoll, anafotokoza kuti: “Ku Mars kumazizira kwambiri, ku Venus kumatentha kwambiri, koma padziko lapansi m’pabwino.” Komanso, kuti zomera zikule bwino pamafunika kuwala kokwanira bwino. Ndipo Baibulo limafotokoza kuti chakumayambiriro kwa nyengo zakulenga, Mulungu anachititsa kuwala kwa dzuwa kudutsa mitambo yakuda ya nthunzi ya madzi imene inali kuphimba nyanja ngati ‘nsalu yokulungira’ mwana.​—Yobu 38:4, 9; Genesis 1:3-5.

M’mavesi otsatira a Genesis, timawerenga kuti Mlengi anapanga “thambo.” (Genesis 1:6-8) Thambo limeneli lili ndi mpweya wosiyanasiyana womwe wazungulira dziko lapansi.

Kenaka Baibulo limafotokoza kuti Mulungu anasintha dziko lopanda kanthu kuti pakhale mtunda. (Genesis 1:9, 10) Zikuoneka kuti anapangitsa nthaka ya dziko lapansi kutumphuka n’kusuntha. Zimenezi mwina zinapangitsa kuti zigwembe zozama zipangike ndipo mtunda utuluke m’nyanja.​—Salmo 104:6-8

Panthawi inayake m’mbuyomo, Mulungu analenga ndere zing’onozing’ono kwambiri m’nyanja. Ndere zokhala ndi selo limodzi zimenezi zimatha kubereka popanda zinzake. Pogwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa, zinayamba kusandutsa mpweya woipa kukhala chakudya chawo n’kumatulutsa mpweya wabwino m’mlengalenga. Zimenezi zinayamba kuchitika kwambiri panyengo yachitatu yakulenga pamene zomera, zomwe zinadzakuta dziko lonse, zinalengedwa. Motero mpweya wabwino unachuluka, choncho anthu ndi zinyama zikanatha kumapuma n’kukhala ndi moyo.​—Genesis 1:11, 12.

Mlengi analenga tizilombo tosaoneka ndi maso tambirimbiri ta m’nthaka kuti ikhale yachonde. (Yeremiya 51:15) Tizilomboti timawoletsa zinthu n’kuzisandutsa chakudya cha zomera. Tizilombo tina tapadera ta m’nthaka timasintha mpweya winawake n’kuusandutsa chakudya chofunikira kwambiri cha zomera. N’zodabwitsa kuti m’dothi lachonde lodzadza dzanja mungakhale tizilombo tokwana 6 biliyoni.

Lemba la Genesis 1:14-19 limafotokoza kuti dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi zinalengedwa pa nyengo yachinayi yakulenga. Poyamba zimenezi zingaoneke ngati zikutsutsana ndi zimene malemba amene tatchula kale akunena. Komabe kumbukirani kuti Mose amene analemba Genesis, analemba nkhani yake malinga ndi mmene angaonere munthu wa padziko lapansi amene akuona zinthuzi zikulengedwa. Zikuoneka kuti dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi zinayamba kuoneka pa dziko lapansi panthawi imeneyo.

Nkhani ya m’Genesis imanena kuti zinyama zokhala m’madzi zinalengedwa pa nyengo yachisanu yakulenga ndipo zinyama za pamtunda ndi anthu zinalengedwa pa nyengo yachisanu ndi chimodzi yakulenga.​—Genesis 1:20-31.

 Dziko Lapansi Linapangidwa Kuti Tizisangalala Nalo

Kodi simukuona kuti moyo padziko lapansi, wopangidwa mmene nkhani ya m’Genesis imafotokozera, unapangidwa kuti tizisangalala nawo? Kodi munayamba mwadzukapo tsiku lina dzuwa likuwala, n’kupuma mpweya wabwino, n’kusangalala kuti muli moyo? Kapena mwina munayenda m’munda wa maluwa n’kusangalala ndi maluwa okongola onunkhira bwino. Kapenanso mwina munayenda m’munda wa mitengo n’kuthyola zipatso zake zokoma kwambiri. Zosangalatsa zonsezi sizikanatheka popanda izi: (1) madzi ambiri, (2) kutentha ndi kuwala kokwanira kwa dzuwa, (3) mpweya wosiyanasiyana wofunikira, ndi (4) nthaka yachonde.

Zinthu zonsezi, zomwe ku Mars, Venus, ndi mapulaneti ena ozungulira dzuwa lathu kulibe, sizinangokhalako mwangozi. Zinapangidwa bwino kwambiri kuti moyo padziko lapansi ukhale wosangalatsa. Nkhani yotsatira isonyeza kuti Baibulo limanena kuti Mlengi analenga dziko lathu lokongolali kuti likhale kosatha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Dziko lapansi, Mercury, Venus ndi Mars ndiwo mapulaneti anayi oyandikana kwambiri ndi dzuwa lathu. Mapulaneti amenewa ali ndi nthaka ndi miyala. Koma mapulaneti aakulu okhala kutali ndi dzuwa lathu otchedwa Jupiter, Saturn, Uranus, ndi Neptune, n’ngopangidwa makamaka ndi mpweya.

[Bokosi patsamba 6]

“Ine ndine katswiri wa zamiyala. Tiyerekezere kuti ndapemphedwa kuti ndifotokoze mwachidule zimene anthu amakono amaganiza za chiyambi cha dziko lapansi ndi mmene moyo unayambira, kwa anthu wamba oweta ziweto, ngati mafuko amene anawalembera Buku la Genesis. Sindingapeze njira yabwino kwambiri yofotokozera zimenezi kuposa kugwiritsira ntchito mawu ofanana ndi amene ali m’chaputala choyamba cha Genesis.”​—Anatero katswiri wa zamiyala, Wallace Pratt.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 7]

NDI MALO ABWINO KWAMBIRI OPHUNZIRIRA ZAKUTHAMBO

Dzuwa likanakhala pa malo ena mu mlalang’amba wathu, si bwenzi nyenyezi tikuziona bwinobwino. Buku la The Privileged Planet, limati: “Dzuwa lathu ndi mapulaneti olizungulira zili . . . kutali ndi malo afumbi ndiponso owala kwambiri, ndipo zimenezi zimathandiza kuti tiziona bwino kwambiri nyenyezi zapafupi komanso malo akutali m’chilengedwe.”

Komanso kukula kwa mwezi ndi kutalikirana kwake ndi dziko lapansi, n’zoyenerera bwino kuti mwezi uzitha kuphimba dzuwa panthawi ya kadamsana. Kadamsana, wochititsa chidwi kwambiri amene sachitika kawirikawiri, amapatsa akatswiri a zakuthambo mpata wophunzira zambiri za dzuwa. Maphunziro amenewa awathandiza kuzindikira zinthu zambiri zokhudza momwe nyenyezi zimawalira.

[Chithunzi patsamba 5]

Mwezi ndi waukulu bwino kuti dziko lapansi likhale mopendekeka ndiponso lisamasunthesunthe

[Zithunzi patsamba 7]

N’chiyani chimapangitsa kuti padziko lapansi pakhale moyo? Madzi ambiri, kuwala ndi kutentha kokwanira, mpweya wosiyanasiyana, ndi nthaka yachonde

[Mawu a Chithunzi]

Globe: Based on NASA Photo; wheat: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.