Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo Wokafika ku Saba

Ulendo Wokafika ku Saba

Ulendo Wokafika ku Saba

KALEKALE, kuchilumba cha Saba, chomwe chinkalamulidwa ndi dziko la Holland, kunali kuchimake kwa achifwamba amene ankalanda katundu m’sitima zapamadzi m’Nyanja ya Caribbean. Masiku ano, chilumba chaching’ono chimenechi, chomwe chili pamtunda wa makilomita 240 kum’mawa kwa Puerto Rico, chili ndi anthu pafupifupi 1,600, ndipo Mboni za Yehova ziliko 5. Komano, atumiki olimba mtima amenewa, akufunafuna chinachake chamtengo wapatali kwambiri kuposa katundu wochita kulanda. Iwo akufunafuna mwakhama anthu “ofuna moyo wosatha.”​—Machitidwe 13:48, NW.

Uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu unafika pachilumbapo kwanthawi yoyamba pa June 22, 1952. Ili ndi tsiku limene ngalawa ya Mboni za Yehova ya mamita 18, yotchedwa Sibia, inakocheza pagombe la Saba. (Mateyu 24:14) Gust Maki ndi Stanley Carter omwe anali amishonale, anadutsa kanjira kakang’ono, kotchedwa Ladder, komanso ka masitepe amiyala oposa 500. Kanjiraka kanali kulowera ku mudzi wa The Bottom, likulu la chilumba cha Saba. * Kwa zaka zambiri, kunalibenso njira ina yokafikira kumene anthu a pachilumbachi anali kukhala, kupatulapo kamsewu komweka basi.

Lipoti loyambirira la mmene ntchito yachikristu yochitira umboni ku Saba inali kuyendera linasindikizidwa mu 1966 Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Malinga ndi zimene lipotilo linanena, pachilumbachi panali Mboni imodzi yokha imene inkalalikira. Kenako, panafika banja lina la ku Canada ndipo linalalikira uthenga wabwino kumeneko kwa zaka zambiri. Posachedwapa, Russel ndi mkazi wake Kathy, a ku United States anapita ku Saba n’kukathandiza pa ntchito yolalikira kumeneko. Imvani mmene zinakhalira.

Ulendo wa ku Saba

Ine ndi mkazi wanga tinafika pachilumbachi pandege monga alendo a Ronald, amene anali Mboni yokhayo pachilumba chonsechi pafupifupi m’ma 1990 monse. Iye anatiyembekezera pabwalo la ndege monga alendo ake. Ataona bokosi laling’ono la ndiwo zamasamba zimene tinam’bweretsera monga mphatso, ananyadira kwambiri chifukwa pachilumba chimenechi anthu sagulitsa zinthu zimene amalima. Kenako tinakwera galimoto laling’ono, ndi kuyenda pang’onopang’ono kudutsa msewu wokhotakhota wa m’mbali mwa phiri. Tinali kupita pamwamba penipeni pa Phiri la Scenery limene linasiya kalekale kuphulika.

Titafika pamudzi wotchedwa Hell’s Gate tinaima chifukwa Ronald ankafuna kukaona ngati pepala loitanira anthu ku nkhani ya onse ya Lamlungu, linali lidakalipo pamalo ena omwe anthu pachilumbapo amakhomapo zimene akufuna kudziwitsa ena. Tinasangalala kumva kuti lidakali pomwepo. Kenako anakweranso m’galimoto, ndipo tinapitiriza ulendo wathu wopita ku mudzi waukulu pachilumbapo wotchedwa Windwardside. Mogwirizana ndi tanthauzo la dzina limeneli m’Chingelezi, mudzi wochititsa chidwiwu uli ku mbali ya chilumbachi kumene kumachokera mphepo, ndipo uli pamtunda wa mamita 400 kuchokera pothera madzi a nyanja zikuluzikulu. Pamene tinali kulowa mu msewu wopita kunyumba ya Ronald, tinaona chikwangwani chokongola kutsogolo kwa nyumbayo, cholembedwa kuti Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.

Pamene tinali kulandira chakudya chamasana, ndinafunsa funso lokhudzana ndi cholinga cha ulendo wathu lakuti, “Zinatheka bwanji kuti upezeke ku Saba kuno kudzalalikira za Ufumu?”

Ronald anati: “Ntchito yomanga nthambi ya Mboni za Yehova ku Puerto Rico itatha mu 1993, ine ndi mkazi wanga tinkafuna kutumikirabe m’mayiko akunja. Nthawi inayake m’mbuyomu, tinafikapo ku Saba kuno limodzi ndi banja lina limene linali kuchita upainiya, ndipo tinamva kuti kuli anthu 1,400 koma kulibe Mboni. Choncho tinakambirana ndi Komiti ya Nthambi ya Puerto Rico za maganizo athu osamukira kuno.

“Zonse zinayenda bwino kwambiri, ndipo pamapeto pake anatilola kusamuka. Koma patatha zaka ziwiri, mkazi wanga anadwala modetsa nkhawa ndipo tinabwerera ku California. Kenaka anamwalira ndipo ineyo ndinabwerera ku Saba. Inetu ndikayamba chinthu, sindifuna kuchisiira panjira, osachimaliza.”

Kulalikira Nyumba ndi Nyumba ku Saba

Malo ochezera m’nyumba ya Ronald yomwe yakhala zaka 100, amagwiritsidwanso ntchito ngati Nyumba ya Ufumu. * Pamene tinali kudya chakudya cha m’mawa ndi kukonzekera kupita kolalikira, kunagwa mvula kwa kanthawi kochepa ndipo inanyowetsa malo ophikira amene anali pabwalo. Titamaliza kudya, mitambo ili apo ndi apo, tinanyamuka kupita kukalalikira khomo ndi khomo m’mudzi wa The Bottom. Pakhomo lililonse, Ronald akamalonjerana ndi mwini nyumba aliyense ankamutchula dzina lake. Makambirano athu anagona pa nkhani zimene zinali zitangochitika kumene m’deralo. Anthu ambiri amam’dziwa bwino Ronald ndi utumiki wakewo, ndipo ambiri amalandira mosavuta mabuku ofotokoza Baibulo.

Ngati anthu a m’mudzimo sukuwadziwa bwino, n’zovuta kukumbukira anthu amene ali ndi chidwi ndi uthenga wa Ufumu. N’chifukwa chiyani zili choncho? Ronald anati: Chifukwa chakuti “kumeneko kuli lamulo lakuti nyumba zonse azizipaka utoto wa mtundu umodzi.” Ndipo n’zoonadi, chifukwa nditaunguzaunguza ndinaona kuti nyumba zonse mu Saba n’zoyera ndipo madenga ake ndi ofiira.

Tikamaliza kukambirana Baibulo ndi mwini nyumba, timam’pempha kuti Lamlungu adzamvetsere nkhani ya Baibulo ku Nyumba ya Ufumu. Ronald akakhala kuti ali pachilumbapo amakamba nkhani ya onse mlungu uliwonse. Panopa pachilumba cha Saba pali maphunziro a Baibulo okwana 17. Mu 2004, anthu 20 anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Ndipo ngakhale kuti nambala imeneyi ikuoneka yaing’ono, ikuimira munthu mmodzi pa anthu 100 alionse omwe ali pachilumbachi.

Ndithudi, Mboni za Yehova zayesetsa kufikira anthu ambiri zedi ndi uthenga wa Mulungu wa chipulumutso. Kaya ndi pachilumba chaching’ono ngati cha Saba kapena m’dziko lalikulu, Mboni za Yehova mokhulupirika zikugwira ntchito ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse.’​—Mateyu 28:19.

Ulendo wathu wosangalatsawu unathera pamenepa. Pamene timakwera ndege, tinakweza mikono polawirana. Ulendo wathu wokacheza ku Saba ndiponso wokafika ku mudzi wa The Bottom sitidzauiwala!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Zikuoneka kuti achifwamba amene ankalanda katundu m’sitima zapamadzi anautcha mudziwu kuti The Bottom (kapena kuti pamunsi) chifukwa chakuti ankaganiza kuti unali pamunsi pa chidzenje chotuluka chiphalaphala cha pansi padziko.

^ ndime 12 Pa September 28, 2003, antchito ongodzipereka ochokera ku Florida, U.S.A., anapita ku Saba kukakonza nyumba ina yapafupi, imene tsopano akuigwiritsa ntchito ngati Nyumba ya Ufumu.

[Mapu patsamba 10]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

PUERTO RICO

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Background: www.sabatourism.com