Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo la Berleburg

Baibulo la Berleburg

 Baibulo la Berleburg

M’ZAKA za m’ma 1600 ndi 1700, m’Tchalitchi cha Lutheran cha ku Germany, munayambika gulu linalake lachipembedzo lolimbikitsa kudzipereka kwambiri kwa Mulungu. Ena otsatira gulu limeneli anali kunyozedwa ngakhalenso kuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Akatswiri ambiri amaphunziro awo a m’gulu limeneli anathawira ku Berleburg, pafupifupi makilomita 150 kumpoto kwa mzinda wa Frankfurt am Main. Amene anawaloleza kukhala kumeneko, ndi munthu wina wolemekezeka m’deralo, dzina lake Count Casimir von Wittgenstein Berleburg, amene ankalemekeza kwambiri chipembedzo. Popeza kuti ku Berleburg kunali alaliki ndiponso anthu amaphunziro apamwamba amenewa, Baibulo latsopano linasindikizidwa kumeneko, limene masiku ano limadziwika ndi dzina lakuti Baibulo la Berleburg. Kodi zinatheka bwanji kuti amasulire Baibulo limeneli?

Mmodzi wa anthu amene anathawira kumeneko anali Johann Haug, amene anaumirizika kuchoka kwawo ku Strasbourg chifukwa chakuti anthu amaphunziro azaumulungu kwawoko sankagwirizana naye. Huag anali wophunzira kwambiri komanso anali katswiri pankhani ya zinenero. Iye anauza akatswiri anzake amaphunziro awo ku Berleburg kuti chimene akulakalaka kwambiri m’moyo wake ndicho “kumasulira Baibulo losapotoza kanthu m’pang’ono pomwe kuti akonze zimene Luther analakwitsa m’Baibulo lake, kumasulira liwu lililonse mogwirizana ndendende ndi tanthauzo lake m’Mawu a Mulungu komanso mogwirizana ndi cholinga cha liwulo.” (Die Geschichte der Berlenburger Bibel [Mbiri ya Baibulo la Berleburg]) Cholinga chake chinali kumasulira Baibulo lokhala ndi mawu ofotokozera ndiponso ndemanga, komanso loti anthu wamba azitha kulimvetsa mosavuta. Haug anapempha akatswiri ena amaphunziro m’mayiko ena ku Ulayako kuti athandizane naye, ndipo anagwira ntchito imeneyi zaka 20. Baibulo la Berleburg anayamba kulisindikiza m’chaka cha 1726. Chifukwa chakuti lili ndi mawu ambiri ofotokozera, Baibuloli lili ndi mavoliyumu asanu ndi atatu.

Ndipotu Baibulo limeneli la Berleburg lili ndi mfundo zina zochititsa chidwi. Mwachitsanzo, m’Baibuloli lemba la Eksodo 6:2, 3 limati: “Mulungu analankhulanso ndi Mose nati kwa iye: Ine ndine AMBUYE! Ndipo ndinaonekera kwa Abrahamu/​kwa Isake ndi kwa Yakobo/​monga Mulungu Wamphamvuyonse: koma sindinadziwike kwa iwo ndi dzina langa lakuti YEHOVA.” Mawu ake ofotokozera amati: “Dzina lakuti YEHOVA . . . , ndi dzina lopatulika/​kapena kuti/​dzina limene Mulungu watiululira.” Dzina lenileni la Mulungu lakuti, Yehova, likupezekanso m’ndemanga pa Eksodo 3:15 ndi pa Eksodo 34:6.

Chotero Baibulo la Berleburg ndi lokhalo mwa mabaibulo ambirimbiri ku Germany limene limatchula dzina la Yehova m’malemba enieniwo, m’mawu am’munsi, kapena m’ndemanga. Limodzi mwa mabaibulo amakono kwambiri amene akupereka ulemu woyenerera ku dzina lenileni la Mulungu ndi Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.