Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Davide, amene anali munthu wapamtima wa Mulungu, ankachitira nkhanza anthu omwe anawagwira kunkhondo, monga mmene ena amaganizira akawerenga 2 Samueli 12:31 ndi 1 Mbiri 20:3?

Ayi. Davide anangolamula Aamoni ogwidwa kunkhondowo kugwira ntchito ya thangata. Anthu amamva molakwa zomwe Davide anachita chifukwa cha mmene mabaibulo ena anamasulirira mavesi amenewa.

Pofotokoza zimene Davide anachitira Aamoni, mabaibulo amenewa amaonetsa kuti Davide anawachitira nkhanza zoopsa. Mwachitsanzo, pa 2 Samueli 12:31, Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu limati: “Natulutsa anthu a m’mudzimo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi nkhwangwa zachitsulo; nawapsitiriza ndi chitsulo, nawapititsa m’ng’anjo yanjerwa; natero ndi midzi yonse ya ana a Amoni.” Lemba la 1 Mbiri 20:3 limanenanso chimodzimodzi.

Koma malinga ndi zomwe ananena Samuel Rolles Driver, katswiri wa maphunziro a Baibulo, “zonse zimene ife tikudziwa zokhudza umunthu ndi mtima wa Davide, sizisonyeza” kuti anali wa nkhanza. Ndipo ndemanga ina m’Baibulo la The Anchor Bible inati: “Pamenepa Davide anali kugawira ntchito magulu a anthu ogwidwa kunkhondo kuti chuma chiziyenda bwino m’madera ogonjetsedwawo. Zikuoneka kuti izi n’zimene mfumu iliyonse yopambana pa nkhondo inkachita.” Mogwirizana ndi maganizo amenewa, Adam Clarke ananena kuti: “Chotero tanthauzo la lembali ndi lakuti, Davide anatenga anthuwo kukhala akapolo, ndi kuwapatsa ntchito yocheka matabwa, kupanga zolimira zachitsulo, kapena kukumba miyala yamtengo wapatali, . . . kusema zipangizo zamitengo, ndi kuumba njerwa. Malembawa satanthauza kuti anthuwo anali kuwang’amba pakati, kuwacheka ndi mpeni wamanomano, kuwadula nthulinthuli, kapena kuwatematema. Ndipo Davide sakanachita zoterezi kwa Aamoni.”

Mogwirizana ndi kamvedwe kolondola kameneka, mabaibulo ambiri amakono amafotokoza nkhaniyi momveka bwino moti Davide sayenera kuimbidwa mlandu wochitira anthu nkhanza. * Taonani mmene Baibulo la New English Translation (la m’chaka cha 2003) linamasulirira malembawa. Linati: “Iye anatulutsa anthu a mumzindawo n’kuyamba kuwagwiritsa ntchito yamphamvu ndi macheka, zokumbira zachitsulo, ndi nkhwangwa zachitsulo, ndipo anawagwiritsa ntchito pa uvuni ya njerwa. Umu ndi mmene ankachitira ndi mizinda yonse ya Aamoni.” (2 Samueli 12:31) “Iye anatenga anthu okhala mumzindawo nawagwiritsa ntchito ndi macheka, zokumbira zachitsulo, ndi nkhwangwa. Davide anachita zimenezi m’mizinda yonse ya Aamoni.” (1 Mbiri 20:3) Baibulo la New World Translation nalo linamasulira malemba amenewa mogwirizana ndi mmene akatswiri amaphunziro a Baibulo amawamvera masiku ano. Baibuloli linati: “Anthu amene anali mmenemo, iye anawatulutsa kuti akawagwiritse ntchito ndi macheka amiyala ndi zipangizo zakuthwa zachitsulo ndi nkhwangwa zachitsulo, ndipo anawagwiritsa ntchito youmba njerwa.” (2 Samueli 12:31) “Iye anatulutsa anthu amene anali mmenemo, ndipo anawagwiritsa ntchito ndi macheka amiyala, ndi zipangizo zakuthwa zachitsulo, ndi nkhwangwa; ndipo umu ndi mmene Davide anachitira ndi mizinda yonse ya ana a Amoni.”​—1 Mbiri 20:3.

Davide sanaume mtima n’kuwachitira nkhanza Aamoni ogonjetsedwawo ndiponso kuwapulula. Iye sanatengere miyambo yankhanza ndi yopanda chifundo yomwe anthu m’masiku amenewo ankachita pa nkhondo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mwa kungosintha chilembo chimodzi chokha, malemba achihebri angamveke ngati akunena kuti “anawalowetsa m’macheka” kapena kuti “anawadula zidutswazidutswa (ndi macheka).” Komanso mawu akuti “uvuni ya njerwa” angatanthauzenso “chikombole cha njerwa.” Chikombole chotere chinali chaching’ono kwambiri mwakuti munthu sangakwanemo.