Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zozizwitsa Zimene Inuyo Mwaona!

Zozizwitsa Zimene Inuyo Mwaona!

 Zozizwitsa Zimene Inuyo Mwaona!

LIWU lakuti “chozizwitsa” lilinso ndi tanthauzo lina lomwe ndi “chochitika chosayembekezeka, kapena chinthu chovuta kumvetsa kuti anatha bwanji kuchipanga.” Tonsefe taonapo zozizwitsa zoterezi, zomwe sizinachitike ndi dzanja la Mulungu.

Popeza kuti anthu adziwa zochuluka zokhudza malamulo a chilengedwe, akutha kuchita zinthu zimene kale zinkaoneka ngati n’zosatheka. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti anthu ambiri zaka 100 zapitazo, ankaganiza kuti n’zosatheka kuchita zinthu zimene zafala masiku anozi chifukwa cha makompyuta, wailesi zakanema, luso lomatha kupita  mumlengalenga ndi zinthu zina zimene zikuchitika masiku ano.

Asayansi ena akuvomereza kuti sanganenenso motsimikiza kuti chozizwitsa chinachake n’chosatheka, chifukwa azindikira kuti akudziwa zinthu zochepa chabe zokhudza kudabwitsa kwa sayansi ya m’chilengedwe cha Mulungu. Motero nthawi zambiri asayansiwo akapanda kumvetsetsa chozizwitsa chinachake amangoti n’chokayikitsa basi. Amanena choncho kuti m’tsogolo adzaone pothawira zinthu zina zimene zikuoneka kuti n’zosatheka panopa zikadzatheka.

Ngati titatenga tanthauzo la m’nkhani yoyamba ija la mawu akuti “chozizwitsa,” lotanthauza zinthu zimene tingati “zimachitika ndi mphamvu zauzimu,” tinganenenso kuti aliyense wa ife waonapo zozizwitsa. Mwachitsanzo, timaona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, zonsezi zinakhalako chifukwa cha “mphamvu zauzimu,” za Mlengi weniweniyo. Komanso, ndani angafotokoze mwatsatanetsatane mmene thupi la munthu limagwirira ntchito? mmene ubongo umagwirira ntchito? kapena mmene mluza wa munthu umayambira? Buku lakuti The Body Machine limati: “Thupi la munthu, limene nthawi zonse limadalira ubongo ndiponso mitsempha ina yotumizira mauthenga, ndi chipangizo chocholowana kwambiri, ndi injini yoyenda yodziimira payokha, kompyuta yokhoza kudzikonza yokha, chilengedwe chodabwitsa ndi chovuta kuchimvetsa m’njira zambiri.” Mulungu amene analenga “thupi la munthu” anachitadi chozizwitsa, chimene chikupitirizabe kutithetsa nzeru. Palinso zozizwitsa zamtundu wina zimene inuyo mwaziona, ngakhale kuti simunazilingalirepo motero.

Kodi Buku Lingakhale Chozizwitsa?

Palibe buku lina limene lafalitsidwa kwambiri kuposa Baibulo. Kodi inuyo Baibulo mumaliona ngati chozizwitsa? Kodi tinganene kuti Baibulo linakhalapo chifukwa cha “mphamvu zauzimu”? N’zoona kuti Baibulo linalembedwa ndi anthu, koma iwo ananena kuti sanalembe maganizo awoawo koma a Mulungu. (2 Samueli 23:1, 2; 2 Petro 1:20, 21) Taganizani. Anthuwa analipo 40, ndipo onse anakhala ndi moyo m’nthawi zosiyanasiyana m’kati mwa zaka 1,600. Ankachita zinthu zosiyanasiyana m’moyo wawo, ena anali abusa, asilikali, asodzi, ogwira ntchito m’boma, madokotala, ansembe, ndi mafumu. Komabe analemba uthenga wogwirizana wa chiyembekezo umene uli woona ndi wolondola.

Chifukwa chophunzira Baibulo mwakuya, Mboni za Yehova zimavomereza kuti Baibulo silili ‘mawu a anthu, komatu monga momwe lilili ndithu, mawu a Mulungu,’ monga momwe mtumwi Paulo analembera. (1 Atesalonika 2:13) Kwa zaka zambiri mabuku awo afotokoza mmene malemba a m’Baibulo omwe anthu amati amatsutsana amagwirizanirana ndi uthenga wonse wa m’Baibulo. Kugwirizana kwa malemba kumeneku pakokha ndi umboni wakuti amene analemba ndi Mulungu. *

Pa mabuku onse ndi Baibulo lokha limene anthu ayesetsa mwakhama kuti aliwononge. Koma, si ili lilipoli! Ndipotu likupezeka lonse lathunthu kapena zigawo zake m’zinenero zoposa 2,000. Kutetezeka kwa buku lenilenilo komanso kutetezeka kwa malemba akewo kuti akhalebe oona ndi umboni wakuti Mulungu anaikapo dzanja lake. Ndithudi, Baibulo ndi chozizwitsa!

Chozizwitsa ‘Chamoyo Ndiponso Champhamvu’

Zozizwitsa zakale monga machiritso ndi kuukitsa akufa, sizichitika masiku ano. Koma tili n’chifukwa chotsimikizira kuti m’dziko latsopano la Mulungu limene likudzalo, zozizwitsa zoterozo zidzachitikanso, ndipo panthawiyo zidzachitika padziko lonse  lapansi. Zidzathetseratu mavuto onse ndipo zidzakwaniritsa zinthu zomwe panopo sitingathe kumvetsa.

Baibulo limenenso lili chozizwitsa, masiku ano lingachite zinthu zomwe tingatinso n’zozizwitsa mwa kulimbikitsa anthu kusintha umunthu wawo kuti ukhale wabwinoko. (Onani chitsanzo m’bokosi lakuti “Mphamvu ya Mawu a Mulungu,” patsamba 8.) Lemba la Ahebri 4:12 limati: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” Inde, Baibulo lathandiza kwambiri kusintha miyoyo ya anthu oposa 6 miliyoni a padziko lonse lapansi, ladzaza miyoyo yawo ndi cholinga ndi kuwapatsa chiyembekezo cha m’tsogolo chamtengo wapatali.

Bwanji inuyo osalola kuti Baibulo lichite zozizwitsa m’moyo wanu?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Ngati mukufuna kudziwa bwino za malemba amene ena amati amatsutsana, ndiponso kuti muone kugwirizana kwawo, mungapeze zitsanzo zambiri za malemba oterewa m’mutu 7 wa buku lakuti Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 7]

KODI ANALI ATAFA KALE KAPENA AYI?

Malinga ndi zimene lemba la Yohane 19:33, 34, limanena, Yesu anali atafa kale pamene “mmodzi wa asilikali anam’gwaza ndi nthungo m’nthiti yake, ndipo panatuluka pomwepo mwazi ndi madzi.” Koma m’mabaibulo ena, lemba la Mateyu 27:49, 50 limasonyeza kuti pamene izi zinkachitika, n’kuti Yesu ali moyo. N’chifukwa chiyani pali kusiyana kumeneku?

Chilamulo cha Mose chinaletsa kuti munthu amene walamulidwa kuti aphedwe asamam’siye atam’pachika pamtengo usiku wonse. (Deuteronomo 21:22, 23) Chotero m’masiku a Yesu, munthu wotere amene am’pachika pamtengo akafika madzulo adakali moyo, kawirikawiri ankathyola miyendo yake kuti afe mwamsanga. Akam’thyola miyendo munthuyo sankathanso kudziwongola kuti azipuma bwinobwino. Mfundo yakuti asilikali anathyola miyendo ya zigawenga ziwiri zimene anazipachika limodzi ndi Yesu, koma osathyola miyendo ya Yesuyo, ikungosonyeza kuti asilikaliwo ankaganiza kuti wafa kale. N’kutheka kuti asilikaliwo anam’gwaza ndi nthungo m’nthiti mwake kuti pasakhale kukayikira kulikonse komanso kuti asatsitsimuke kuopera kuti ena angadzafalitse bodza lakuti wachita kuuka kwa akufa.

M’mabaibulo ena, lemba la Mateyu 27:49, 50 limafotokoza zochitikazo m’njira yosiyana. Limati: “Munthu wina anatenga mkondo ndi kum’baya m’nthitimu, ndipo panatuluka magazi ndi madzi. Pamenepo Yesu anafuulanso mokweza mawu, napereka mzimu wake.” Koma mawu amene tawapendeketsawo, sapezeka m’mipukutu yonse yakale ya Baibulo. Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti patapita nthawi, mawu amenewa anawawonjezera palembali kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Yohane koma anawaika pa malo olakwika. Choncho mabaibulo ambiri amaika mawu amenewa m’mabulaketi kapena kuti mkutiramawu, apo ayi amaika mawu am’munsi ofotokozera, kapena amangochotsa chiganizo chonsecho.

Malemba achigiriki a Westcott ndi Hort, omwe anagwiritsidwa ntchito kwambiri pa Baibulo la New World Translation, anaika mawuwa m’mabulaketi awiri ngati awa [[ ]]. Ndiyeno ananena kuti “n’kutheka kuti alembi ndi amene anawonjezera” chiganizo chimenechi.

Chotero mfundo yosatsutsika ndi yakuti lemba la Yohane 19:33, 34 limanena zoona komanso, Yesu anali atafa kale pamene msilikali wachiroma anam’lasa ndi nthungo.

 [Bokosi/​Chithunzi patsamba 8]

MPHAMVU YA MAWU A MULUNGU

Detlef ali wachinyamata, ukwati wa makolo ake unatha, ndipo iye anayamba kumwa mankhwala osokoneza bongo, mowa, ndiponso kumvetsera nyimbo za chamba chinachake chaphokoso kwambiri. * Analowa m’kagulu ka achinyamata achifwamba, ndipo posakhalitsa apolisi anayamba kum’funafuna chifukwa cha khalidwe lake lachiwawa.

Mu 1992, achinyamata 60 a m’kagulu kachifwambako anayambitsa chipolowe polimbana ndi kagulu kenanso ka achinyamata ovuta okwana 35 pamalo ena ogulitsira mowa ndi chakudya kumpoto cha kummawa m’dziko la Germany. Thomas, mmodzi wa achinyamata ovutawo, anamenyedwa koopsa ndipo anamwalira chifukwa chakuti anavulazidwa kwambiri. Pambuyo pa mlandu umene unafalitsidwa kwambiri ndi atolankhani, atsogoleri ambiri a maguluwa limodzi ndi Detlef, analamulidwa kukakhala m’ndende.

Posakhalitsa Detlef atatuluka m’ndendemo, Mboni za Yehova zinam’patsa kapepala. Kapepala kameneko kanali ndi mutu wakuti “Nchifukwa Ninji Moyo Uli Ndi Mavuto Ochuluka Motere?” Nthawi yomweyo Detlef anazindikira kuti kapepalako kakunena zoona, ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Izi zinasinthiratu moyo wake. Kuchokera m’chaka cha 1996 mpaka pano, iye ndi Mboni ya Yehova yakhama.

Siegfried, amene anali m’kagulu ka achinyamata ovuta aja, anali bwenzi lapamtima la Thomas, mnyamata amene anaphedwa uja. Patapita nthawi nayenso anakhala Mboni ndipo tsopano ndi mkulu mu mpingo. Siegfried atapita kukakamba nkhani ya Baibulo ku mpingo wa Detlef (kumenenso mayi ake a Thomas amasonkhana nthawi zina), Detlef anamutenga kukadya naye chakudya cha masana. Likanakhala kale, zaka pafupifupi khumi zapitazo, sakanatha kuugwira mtima chifukwa cha chidani chawo. Koma lero, n’zosachita kufunsa kuti amakondana monga abale.

Detlef ndi Siegfried akulakalaka kudzalandira Thomas akadzauka kwa akufa m’dziko lapansi la paradaiso. Detlef anati: “Ndikamaganiza zimenezi ndimagwetsa misozi. Ndimamva chisoni kwambiri chifukwa cha zomwe ndinachita.” Pamene akuthandiza ena masiku ano kum’dziwa Yehova ndi kukondwera ndi chiyembekezo cha m’Baibulo, Detlef ndi Siegfried akufunitsitsa kudzathandizanso Thomas panthawiyo.

Kunena zoona Mawu a Mulungu n’ngamphamvu kwambiri!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 25 Tasintha mayina.

[Chithunzi patsamba 6]

Thupi la munthu analipanga modabwitsa

[Mawu a Chithunzi]

Anatomy Improved and Illustrated, London, 1723, Bernardino Genga