Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo Wauzimu Kodi Ukulowera Kuti?

Moyo Wauzimu Kodi Ukulowera Kuti?

Moyo Wauzimu Kodi Ukulowera Kuti?

“Anthu 30 anapezeka pamsonkhano wamadzulo wa [Akatolika] wolangiza anthu amene akufuna kukwatirana. Mwa anthu 30 amene anapezekapowo ndi atatu okha omwe anati ali ndi chikhulupiriro.” Inatero nyuzipepala ya Chikatolika ya ku France yakuti La Croix.

KUPEMBEDZA kukuloŵa pansi. Magazini ya Newsweek ya July 12, 1999, yofalitsidwa m’mayiko ambiri inafunsa pa tsamba lake loyamba kuti: “Kodi Mulungu Wafa?” Magaziniyi inanena kuti kumadzulo kwa Ulaya, zikuoneka kuti zilidi choncho. Pofotokoza zomwe zinachitika pamsonkhano wa bungwe la Tchalitchi cha Katolika womwe unachitikira ku Roma mu October chaka cha 1999, nyuzipepala yachifalansa ya Le Monde inati: “N’zovuta kwambiri kuposa kale kuti Tchalitchi chiuze uthenga wake anthu omwe sakulabadira uthengawo . . . Ku Italy, Chikatolika sichilinso chogwirizana. . . . Ku Germany, mkangano wokhudza malo kumene amalangizira anthu ofuna kuchotsa mimba wachititsa kuti kusiyana maganizo kwa papa ndi anthu omwe safunanso kuuzidwa chochita kuwonjezereke. Anthu ena anena kuti maganizo a anthu a ku [Netherlands] pankhani ya makhalidwe abwino ndiponso kumaliza munthu amene akudwala mwakayakaya kuti asavutike kwambiri, akhalapo chifukwa chakuti dzikolo mwadzidzidzi linaleka Chikristu.”

Ndi mmene zinthu zilili kwina kulikonse. Mu 1999 Bishopu wamkulu wa ku Canterbury, George Carey anachenjeza kuti Tchalitchi cha ku England “changotsala mbadwo umodzi kuti chithe.” Mu nkhani ya mutu wakuti: “Kutha kwa Chikristu ku Ulaya,” nyuzipepala yachifalansa ya Le Figaro inati: “Zinthu zikuchitika mofanana kulikonse. . . . Anthu akukayikira kwambiri moyo wauzimu ndi ziphunzitso.”

Anthu Opita ku Tchalitchi Achepa

Ku Ulaya, chiŵerengero cha anthu opita ku tchalitchi chatsika kwambiri. Akatolika achifalansa ochepera 10 mwa 100 alionse ndi amene amapezeka pa Misa Lamlungu lililonse pamene ku Paris, Akatolika atatu kapena anayi mwa Akatolika 100 alionse ndi amene amapita ku tchalitchi nthaŵi zonse. Ku United Kingdom, Germany ndi mayiko a ku Scandinavia, ziŵerengero za opita ku tchalitchi ndi zofanana ndi zimenezi kapena mwina n’zotsika kuposa pamenepa.

Chimene chikudetsa nkhaŵa kwambiri akuluakulu achipembedzo ndi kusoŵa kwa anthu omwe angakhale ansembe. Pa zaka zosaposa 100, chiŵerengero cha ansembe ku France chatsika kwambiri. Masiku ano anthu 10,000 omwe ankayang’aniridwa ndi ansembe 14 akuyang’aniridwa ndi wansembe mmodzi. Mu Ulaya yense, ansembe ambiri ndi achikulire ndipo kuchepa kwa chiŵerengero cha ansembe kwakhudza ngakhale mayiko monga Ireland ndi Belgium. Panthaŵi imodzimodzi, chiŵerengero cha ana olembedwa m’makalasi a katekisima chikuchepa kwambiri ndipo zikukayikitsa kwambiri ngati Tchalitchi cha Katolika chingathe kukonzanso zinthu kuti zikhale bwino.

Anthu sakukhulupiriranso chipembedzo. Anthu 6 mwa anthu 100 alionse ku France ndi amene amakhulupirira kuti “choonadi chingapezeke m’chipembedzo chimodzi chokha,” pamene mu 1981 analipo anthu 15 mwa anthu 100 alionse ndipo mu 1952 anali anthu 50 mwa anthu 100 alionse. Kuchita mphwayi ndi chipembedzo kukufalikira. Chiŵerengero cha anthu amene amati alibe chipembedzo chawonjezeka kuchoka pa anthu 26 mwa anthu 100 alionse mu 1980 kufika pa anthu 42 mwa anthu 100 alionse mu 2000.​—Les valeurs des Français​—Évolutions de 1980 à 2000 (Makhalidwe Achifalansa​—Kusintha Kwake Kuyambira 1980 mpaka 2000).

Kusintha Kwakukulu kwa Makhalidwe Abwino

Kusintha kwa zinthu kukuonekeranso pankhani ya makhalidwe abwino. Monga mmene tanenera poyamba, anthu ambiri amene amapita ku tchalitchi amakana kutsatira malamulo a makhalidwe abwino a tchalitchi chawo. Iwo amatsutsa mfundo yoti atsogoleri achipembedzo ndi amene ayenera kuwapangira malamulo okhudza khalidwe. Anthu amodzimodzi amene amagwirizana ndi maganizo a papa pankhani ya ufulu wa anthu amakana kutsatira zimene papa wanena ngati zikukhudza moyo wawo paokha. Mwachitsanzo, anthu ambiri amakana zimene papa amanena pankhani ya kulera, ngakhalenso Akatolika okwatirana ambiri.

Maganizo otero amakhudza anthu opembedza ndi osapembedza omwe, kaya akhale olemera kapena osauka. Makhalidwe omwe Malemba Opatulika amatsutsiratu, amawavomereza. Zaka 20 zapitazo, anthu 45 mwa 100 alionse a ku France sanali kuvomereza kugonana kwa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. Masiku ano, anthu 80 mwa 100 alionse amavomereza. Ngakhale kuti anthu ambiri amavomereza kukhulupirika muukwati, anthu 36 okha mwa anthu 100 alionse ndi amene amati kusakhulupirika n’kosaloleka.​—Aroma 1:26, 27; 1 Akorinto 6:9, 10; Ahebri 13:4.

Kuphatikiza Zikhulupiriro za Zipembedzo

Ku mayiko a Azungu, chipembedzo chongodzipangira chimene munthu amadzisankhira yekha zimene akufuna kukhulupirira chikukulirakulira. Ziphunzitso zina amazivomereza pamene zina amazikana. Anthu ena amadzitcha Akristu ngakhale kuti amakhulupirira kuti munthu amabadwanso akamwalira ndipo ena amatsatira ziphunzitso za zipembedzo zingapo panthaŵi imodzi. (Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4, 20; Mateyu 7:21; Aefeso 4:5, 6) Buku lakuti Les valeurs des Français (Makhalidwe Achifalansa) linasonyeza mosapita m’mbali kuti okhulupirira ambiri masiku ano akusiyiratu njira zimene tchalitchi chinakhazikitsa.

Komabe maganizo ameneŵa ofuna kukhala ndi chipembedzo chongodzisankhira ali ndi zovuta zake. Jean Delumeau wolemba mbiri ya zipembedzo ndiponso membala wa Institut de France, amakhulupirira kuti munthu sangapange chipembedzo chake osadalira zomwe zilipo kale. “Chikhulupiriro sichingakhalitse ngati si chozikidwa pa chipembedzo chinachake.” Moyo wauzimu wabwino ndiponso mfundo zachipembedzo zabwino ziyenera kugwirizana ndi chipembedzo. Kodi kugwirizana kotereku kungapezeke kuti pakati pa anthu amene amasinthasintha?

Baibulo lonse limatiuza kuti ndi Mulungu amene amakhazikitsa malamulo a khalidwe labwino ngakhale kuti amapatsa anthu ufulu wakuwatsatira kapena ayi. Anthu ambirimbiri padziko lapansi azindikira kuti buku lomwe anthu akhala akulilemekeza kwanthaŵi yaitali limeneli ndi lothandiza kwambiri masiku ano ndiponso kuti ‘ndilo nyali ya ku mapazi awo, ndi kuunika kwa panjira pawo.’ (Salmo 119:105) Kodi n’chiyani chawapangitsa kuti azindikire zimenezi? Nkhani yotsatira idzafotokoza zimenezi.