Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:

Kodi tingapindule chiyani pophunzira za banja la Safani?

Safani anali mlembi wa Mfumu Yosiya ya Yuda. Safani, yemwe anali munthu wotchuka mu ufumuwo, anathandiza mfumu pantchito yoyambitsanso kulambira koona. Ana a Safani aŵiri anakhalabe okhulupirika kwa mneneri Yeremiya. Ndipo mwana wake wina ndiponso zidzukulu zake ziŵiri zinagwiritsanso ntchito maudindo awo kuthandizira kulambira koona. Mofananamo, tiyenera kugwiritsa ntchito zinthu zathu ndi maudindo athu kuthandizira kulambira koona.​—12/15, masamba 19 mpaka 22.

Kodi Irene Hochstenbach wathana bwanji ndi vuto lake lalikulu ndi kukwanitsa kutumikira Yehova?

Iye anasiya kumva ali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Ngakhale samva, waphunzira kulankhula ndi anthu ena ndipo panopa amayenda ndi mwamuna wake (woyang’anira woyendayenda) pamene akutumikira mipingo ya ku Netherlands.​—1/1, masamba 23 mpaka 26.

Kodi ndi zida zatsopano zophunzirira ziŵiri ziti zimene zinatuluka pa Misonkhano Yachigawo yakuti “Olengeza Ufumu Achangu”?

Akristu padziko lonse lapansi anasangalala kulandira buku lakuti Lambirani Mulungu Woona Yekha, limene lakonzedwa kuti anthu atsopano aziphunzira akamaliza kuphunzira buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha; buku lina latsopano ndi lakuti Yandikirani kwa Yehova, limene likukamba kwambiri makhalidwe a Yehova ndi zochita zake. Limasonyezanso momwe tingamutsanzirire posonyeza makhalidwe ake.​—1/15, masamba 23 ndi 24.

Kodi mawu a pa Miyambo 12:5 akuti: “Maganizo a olungama ndi chiweruzo” amatanthauza chiyani?

Maganizo a anthu abwino amakhala abwino ndipo amachita zinthu mopanda tsankhu ndi molungama. Popeza kukonda Mulungu ndiponso anthu anzawo n’kumene kumalimbikitsa anthu olungama, zolinga zawo zimakhala zabwino.​—1/15, tsamba 30.

Kodi n’chiyani chingathandize munthu kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito?

Ndi bwino kuphunzira kukonda ntchito kuyambira paubwana. Baibulo limatilimbikitsa kukhala ndi maganizo abwino pa nkhani ya ntchito, kupewa ulesi. (Miyambo 20:4) Limalimbikitsanso Akristu kusatanganidwa kwambiri ndi ntchito. Tiyenera kudziŵa kuti kutumikira Mulungu ndiko kofunika kwambiri pa moyo wathu. (1 Akorinto 7:29-31) Ndiponso Akristu oona ali ndi chidaliro chakuti Mulungu sadzawasiya.​—2/1, masamba 4 mpaka 6.

Kodi ndi malo oyamba ati m’Baibulo pamene anatchula guwa la nsembe?

Ndi pa Genesis 8:20, pamene pamanena za guwa la nsembe limene Nowa anamanga atatuluka mu chingalawa, Chigumula chitapita. Komabe, n’zoonekeratu kuti Kaini ndi Abele ankagwiritsa ntchito guwa la nsembe popereka nsembe zawo. (Genesis 4: 3, 4)​—2/15, tsamba 28.

Kodi Akristu ena angatani kuti agwiritse ntchito bwino kusintha kwa zinthu?

Ena avomereza kapena akonza zosintha ntchito zimene zawathandiza kuti akhale ndi nthaŵi yochuluka yochita utumiki. Ena awonjezera nthaŵi ndiponso zochita zawo mu utumiki wa Mulungu pamene maudindo awo abanja achepa, monga pamene ana awo akula ndi kupeza mabanja.​—3/1, masamba 19 mpaka 22.

Kodi zitsanzo za Yona ndi mtumwi Petro zikutithandiza bwanji kuona ena monga momwe Yehova amawaonera?

Yona ndi Petro anali ndi maganizo olakwika odziŵika bwino ndiponso n’zodziŵika kuti analakwitsa pankhani ya mmene anachitira ndi zinthu zimene zinayesa chikhulupiriro ndi kumvera kwawo. Komabe, n’zoonekeratu kuti Yehova anaona makhalidwe abwino amene iwo anali nawo ndipo anapitiriza kuwagwiritsa ntchito mu utumiki wake. Anthu ena akatilakwira kapena kutikhumudwitsa, tingaike maganizo pa makhalidwe awo abwino amene poyamba tinali kuwasirira ndiponso pa zabwino zimene Mulungu amaona mwa iwo.​—3/15, masamba 16 mpaka 19.

N’chifukwa chiyani mabaibulo amasiyana manambala a mavesi m’buku la Masalmo?

Kalembedwe ka manambala m’Baibulo la m’chinenero cha Chihebri choyambirira kamasiyana ndi ka m’Baibulo la Septuagint ya Chigiriki limene analimasulira kuchokera ku Chihebri. Mabaibulo aposachedwapa angasiyane, malinga ndi malemba amene agwiritsa ntchito pomasulira, kaya agwiritsa ntchito malemba a Chihebri kapena a Septuagint.​—4/1, tsamba 31.