Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamatanu—Yehova Sadzaiŵala Ntchto Yanu!

Achinyamatanu—Yehova Sadzaiŵala Ntchto Yanu!

 Achinyamatanu​—Yehova Sadzaiŵala Ntchto Yanu!

“Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”​—AHEBRI 6:10.

1. Kodi mabuku a m’Baibulo a Ahebri ndi Malaki akusonyeza bwanji kuti Yehova amayamikira utumiki wanu?

KODI munachitirapo chinthu chabwino mnzanu koma iye osakuthokozani? Zingapweteke kwambiri ngati chinthu chabwino chimene wamuchitira munthu wina, winayo wachiona mopepuka, kapenanso kuposa pamenepo, wachiiŵala kumene. Komatu zimenezo n’zosiyana kwambiri ndi mmene zimakhalira tikamatumikira Yehova ndi mtima wonse. Baibulo limati: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.” (Ahebri 6:10) Taganizirani tanthauzo la zimenezi. Yehova angaone kuti sanachite chilungamo, wachimwa, ngati ataiŵala zimene inu munachita ndiponso zimene mukupitiriza kuchita pomutumikira. Ee, iye alidi Mulungu woyamikira!​—Malaki 3:10.

2. N’chiyani chikuchititsa kutumikira Yehova kukhala kwapadera kwambiri?

 2 Muli ndi mwayi wapadera wolambira ndi kutumikira Mulungu woyamikira ameneyu. Popeza pali okhulupirira anzanu oposa sikisi miliyoni okha basi poyerekeza ndi anthu pafupifupi sikisi biliyoni padziko lonse, mwayi umene muli nawo ndi wosoŵa kwabasi. Ndiponso, kumvetsera ndi kutsatira kwanu uthenga wabwino ndi umboni wakuti Yehova amakukondani. Pajatu Yesu anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye.” (Yohane 6:44) Inde, Yehova amathandiza munthu aliyense payekha kuti apindule nayo nsembe ya Kristu.

Kuyamikira Mwayi Wanu Wapadera

3. Kodi ana a Kora anasonyeza bwanji kuyamikira mwayi wotumikira Yehova?

3 Monga mmene nkhani yapitayi yafotokozera, muli ndi mwayi wapadera wokondweretsa mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11) Zimenezi simuyenera kuziona mopepuka. Ana a Kora, mu salmo lawo lina louziridwa, anasonyeza kuyamikira kwawo mwayi wotumikira Yehova. Timaŵerenga kuti: “Tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m’nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m’mahema a choipa.”​—Salmo 84:10.

4. (a) N’chiyani chingachititse ena kuona ngati kulambira Yehova n’komanitsa zinthu? (b) Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amachita chidwi kuona ndiponso kubwezera mphoto atumiki ake?

4 Kodi ndi mmene inu mumaonera mwayi wanu wotumikira Atate wanu wakumwamba? Inde, nthaŵi zina zingaoneke ngati kutumikira Yehova kukuchepetsa ufulu wanu. N’zoona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kumafuna kudzimana ndithu. Komabe, chilichonse chimene Yehova amakupemphani kuchita n’choti mapeto ake chikupindulitseni. (Salmo 1:1-3) Ndiponso, Yehova amaona khama lanu ndipo amayamikira kukhulupirika kwanu. Ndipotu, Paulo analemba kuti Yehova “ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Yehova akufunafuna mpata woti achitire zimenezi. Mneneri wolungama mu Israyeli wakale anati: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”​—2 Mbiri 16:9.

5. (a) Kodi imodzi mwa njira zabwino kwambiri zosonyezera kuti mtima wanu uli wangwiro ndi Yehova ndi iti? (b) N’chifukwa chiyani kuwauza ena za chikhulupiriro chanu kungaoneke ngati kovuta?

5 Imodzi mwa njira zabwino kwambiri zimene mungasonyezere kuti mtima wanu uli wangwiro ndi Yehova ndiyo kuwauza ena za iye. Kodi munakhalapo ndi mpata wouza ena mwa ana a sukulu anzanu za chikhulupiriro chanu? Poyamba mungaone ngati simungakwanitse kuchita zimenezi, ndipo mungachite mantha kuti muuze ena. Mwina mungafunse kuti: ‘Nanga akandiseka? Bwanji ngati adzaganiza kuti chipembedzo changa n’chachilendo?’ Yesu anadziŵa kuti si anthu onse amene adzamvetsera uthenga wa Ufumu. (Yohane 15:20) Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti nthaŵi zonse muzingosekedwa ndi kukanidwa ayi. Mosiyana ndi zimenezo, Mboni zachinyamata zambiri zapeza ena ofuna kumvetsera ndipo zalemekezedwa kwambiri ndi  anzawo chifukwa chotsatira kwambiri zikhulupiriro zawo.

“Yehova Adzakuthandizani”

6, 7. (a) Kodi mtsikana wina wa zaka 17 anatha bwanji kulalikira kwa ana a sukulu anzake? (b) Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhani ya Jennifer?

6 Koma kodi mungatani kuti mulimbe mtima kuuza ena za chikhulupiriro chanu? Bwanji osatsimikiza mtima kuyankha mosapita m’mbali anthu akakufunsani kuti muli chipembedzo chiti? Tamvani nkhani ya Jennifer wa zaka 17. Iye akuti: “Ndinali kudya nkhomaliro kusukulu. Atsikana amene ndinakhala nawo limodzi patebulo anayamba kukambirana za chipembedzo ndipo m’modzi mwa iwo anandifunsa chipembedzo changa.” Kodi Jennifer anachita mantha kuti ayankhe? Iye akuvomereza kuti: “Ee, ndinachita mantha chifukwa sindinadziŵe kuti ayankha bwanji ndikawauza.” Ndiyeno anatani? Iye akupitiriza kuti: “Ndinawauza atsikanawo kuti ndinali wa Mboni za Yehova. Poyamba anaoneka odabwa. Mwachionekere, iwo anali ndi maganizo akuti Mboni za Yehova ndi anthu achilendo. Zimenezi zinawachititsa kundifunsa mafunso, ndipo ndinakonza maganizo ena olakwika amene anali nawo. Ndiponso kuyambira tsiku limenelo, ena mwa atsikanawo nthaŵi zina ankandifunsa mafunso.”

7 Kodi Jennifer akudandaula kuti analakwitsa kugwiritsa ntchito mpatawo kuuza ena zimene iye amakhulupirira? Ayi. Iye akuti: “Ndinasangalala nazo kwambiri pamene nthaŵi ya nkhomaliro inatha. Atsikanawo tsopano akudziŵa bwino kuti Mboni za Yehova ndi ndani kwenikweni.” Tsopano langizo la Jennifer n’losavuta, akuti: “Ngati mukuona kuti zikukuvutani kulalikira kwa ana a sukulu anzanu kapena aphunzitsi, pempherani mwachidule. Yehova adzakuthandizani. Mudzasangalala kuti munagwiritsa ntchito bwino mpata wanu kulalikira.”​—1 Petro 3:15.

8. (a) Kodi pemphero linathandiza bwanji Nehemiya pamene anakumana ndi zochitika zosayembekezeka? (b) Kodi ndi zochitika zina ziti kusukulu pamene mungafunike kupemphera mwachidule chamumtima kwa Yehova?

8 Onani kuti Jennifer akulimbikitsa ‘kupemphera mwachidule’ kwa Yehova mpata ukapezeka wolalikira chikhulupiriro chanu. Zimenezi ndi zimenenso Nehemiya, yemwe ankagwira ntchito yopatsira Mfumu yachiperisiya, Aritasasta, zakumwa anachita pamene anakumana ndi zochitika zosayembekezeka. Nehemiya anachita kuoneka kuti wakhumudwa kwambiri chifukwa chomva kuti Ayuda anali m’mavuto aakulu ndiponso kuti malinga ndi zipata za Yerusalemu zinapasuka. Mfumuyo inaona kuti Nehemiya anaoneka kuti anali ndi nkhaŵa, motero inamufunsa chimene chinachitika. Asanayankhe, Nehemiya anapemphera kuti Mulungu amutsogolere. Ndiyeno molimba mtima anapempha kuti amulole kubwerera ku Yerusalemu ndi kukathandiza nawo kumanganso mzinda umene unagwawo. Aritasasta anamulola Nehemiya kuti apite. (Nehemiya 2:1-8) Mukuphunzirapo chiyani pamenepa? Ngati mumachita mantha mpata ukapezeka wolalikira za chikhulupiriro chanu, musanyalanyaze mwayi wanu wopemphera chamumtima. Petro analemba kuti: ‘Tayani pa [Yehova] nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.’​—1 Petro 5:7; Salmo 55:22.

‘Okonzeka Kuchita Chodzikanira’

9. Kodi Leah wa zaka 13 anatha bwanji kugawira mabuku 23 akuti Achichepere Akufunsa?

9 Taonaninso nkhani ina iyi. Leah, yemwe ali ndi zaka 13, panthaŵi yopuma masana kusukulu anali kuŵerenga buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza. * Iye akuti: “Ena anali kundiona ndipo posakhalitsa gulu la ana a sukulu linandizinga n’kumaona zimene ndinali kuŵerenga. Iwo anayamba kundifunsa kuti bukulo limanena za chiyani.” Pamene anali kuŵeruka, atsikana anayi anam’pempha Leah kuti adzawapatse mabuku a Achichepere Akufunsa. Posakhalitsa, atsikanaŵa anayamba kuuza ena za bukulo, ndipo nawonso enawo anafuna kukhala ndi mabuku awo. M’milungu ingapo yotsatira, Leah anagawira mabuku a Achichepere Akufunsa okwana 23 kwa ana a sukulu anzake ndi anzawo a ana enawo. Kodi Leah poyamba sanavutike kuyankha atamufunsa za buku limene anali kuŵerenga? Zinali zovuta! Iye akuvomereza kuti: “Poyamba, ndinachita mantha.  Koma ndinapemphera ndipo ndinadziŵa kuti Yehova anali nane.”

10, 11. Kodi mtsikana wina wamng’ono wachiisrayeli anatha bwanji kuthandiza kazembe wa khamu la nkhondo la Aaramu kuphunzira za Yehova, ndipo kodi kazembeyo anasintha bwanji?

10 Nkhani ya Leah ingakukumbutseni zochitika zofanana ndi zimenezi zimene mtsikana wamng’ono wachiisrayeli amene anatengedwa ukapolo ku Aramu anakumana nazo. Namani, kazembe wa khamu lankhondo la Aaramu, anali wakhate. Mwina mkazi wake ndi amene anayambitsa kukambirana kumene kunachititsa mtsikana wamng’onoyu kumuuza mkaziyo chikhulupiriro chake. Iye anati: “Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m’Samariya, akadamchiritsa khate lake.”​—2 Mafumu 5:1-3.

11 Chifukwa cha kulimba mtima kwa mtsikana wamng’ono ameneyu, Namani anadzadziŵa kuti “palibe Mulungu pa dziko lonse lapansi, koma kwa Israyeli ndiko.” Iye anafikanso potsimikiza mtima kuti “sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu ina, koma kwa Yehova.” (2 Mafumu 5:15, 17) Yehova mosakayika anadalitsa kulimba mtima kwa mtsikana wamng’onoyo. Iye angachite ndipo adzachita chimodzimodzi kwa achinyamata masiku ano. Zimenezi n’zimenenso zinachitikira Leah. M’kupita kwa nthaŵi, ena mwa ana a sukulu anzake anamuuza kuti buku la Achichepere  Akufunsa linali kuwathandiza pa makhalidwe awo. Leah akuti: “Ndinasangalala kwambiri chifukwa ndinadziŵa kuti ndinali kuthandiza ena kuphunzira zambiri za Yehova ndi kuwathandiza kusintha makhalidwe awo.”

12. Kodi mungalimbe mtima bwanji kuchita chodzikanira pa chikhulupiriro chanu?

12 Inunso zingakuchitikireni zimene zinachitikira Jennifer ndi Leah. Tsatirani langizo la Petro, amene analemba kuti monga Mkristu, muyenera kukhala “okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Kodi mungachite bwanji zimenezo? Tsanzirani zimene anachita Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino amene anapemphera kwa Yehova kuti awathandize kulalikira “ndi kulimba mtima konse.” (Machitidwe 4:29) Ndiyeno khalani wolimba mtima kuuza ena zimene mumakhulupirira. Mudzadabwa kuona zotsatira zake. Ndiponso, mudzakondweretsa mtima wa Yehova.

Mavidiyo ndi Zochita Zapadera

13. Kodi ndi mipata yotani imene achinyamata ena atengerapo mwayi kulalikira? (Onani mabokosi pa masamba 20 ndi 21.)

13 Achinyamata ambiri auza ana a sukulu anzawo kapena aphunzitsi za chikhulupiriro chawo pogwiritsa ntchito mavidiyo. Nthaŵi zina zochita zina za sukulu zaperekanso mpata wotamanda Yehova. Mwachitsanzo, anyamata ena aŵiri a zaka 15, omwe ndi Mboni za Yehova, anapatsidwa ntchito imene inali mbali ya phunziro lawo la histole ya dziko lonse kuti alembe lipoti lofotokoza chimodzi mwa zipembedzo za padziko lonse. Anyamata aŵiriŵa anagwirizana n’kulembera limodzi lipoti lofotokoza za Mboni za Yehova, pogwiritsa ntchito buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom monga gwero lawo. * Iwo anafunikanso kulifotokoza pakamwa kwa mphindi zisanu. Atatero, aphunzitsi ndi ana a sukulu anali ndi mafunso ambiri moti anyamatawo anakhala kutsogolo kwa kalasilo kwa mphindi zinanso 20. Milungu ingapo yotsatira  zimenezi zitachitika, ana a sukulu anzawowo anapitiriza kufunsa mafunso okhudza Mboni za Yehova!

14, 15. (a) N’chifukwa chiyani kuopa munthu ndi msampha? (b) N’chifukwa chiyani muyenera kulimba mtima kuuza ena zikhulupiriro zanu?

14 Monga mmene nkhani za anthu ena zimene takambiranazi zikusonyezera, mungapindule kwambiri ngati muuza ena chikhulupiriro chanu monga wa Mboni za Yehova. Musalole kuti kuopa munthu kukutayitseni mwayi ndi chimwemwe chimene chimakhalapo chifukwa chothandiza ena kudziŵa Yehova. Baibulo limati: “Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.”​—Miyambo 29:25.

15 Kumbukirani kuti monga Mkristu wachinyamata, muli ndi chinthu china chimene anzanu akuchifuna kwambiri, chomwe ndi moyo wabwino kwambiri pakalipano ndi lonjezo la moyo wosatha m’tsogolo. (1 Timoteo 4:8) N’zochititsa chidwi kuti ku United States, kumene mwina mungaganize kuti anthu ambiri ndi osalabadira kapena ndi okondetsa za m’dziko, kafukufuku wina anasonyeza kuti achinyamata osachepera theka amaona kuti chipembedzo n’chofunika kwambiri. Ndiponso, wachinyamata m’modzi mwa atatu alionse anati chipembedzo ndicho “chinthu chofunika kwambiri chimene chimatsogolera” moyo wake. Mwachionekere, zimenezi zilinso choncho m’madera ena ambiri padziko lonse. Ndiyetu n’zotheka kuti anzanu kusukulu adzasangalala kumva zimene mungawauze za m’Baibulo.

Monga Wachinyamata, Yandikirani kwa Yehova

16. N’chiyaninso chikufunika kuti musangalatse Yehova kuwonjezera pa kuuza ena za iye?

16 Komabe, kusangalatsa mtima wa Yehova kumafuna zambiri osati kungouza kokha ena za iye. Khalidwe lanu liyeneranso kugwirizana ndi miyezo yake. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Mudzaona kuti zimenezi n’zoonadi ngati muyandikira kwa Yehova. Kodi mungachite bwanji zimenezo?

17. Kodi mungayandikire bwanji kwa Yehova?

17 Patulani nthaŵi yoŵerenga Baibulo ndi mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Mukaphunzira kwambiri za Yehova, sizidzakuvutani kumumvera ndiponso kuuza ena za iye. Yesu anati: “Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake . . . pakuti mkamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.” (Luka 6:45) Motero, dzadzani mtima wanu ndi zinthu zabwino. Bwanji osadziikira zolinga pa mbali imeneyi? Mwina mungawongolere kukonzekera kwanu misonkhano ya mpingo mlungu ukubwerawu. Cholinga chanu chachiŵiri chingakhale kuyankha nawo pa misonkhanoyo mwa kupereka ndemanga zachidule koma zogwira mtima. Komanso n’kofunika kwambiri kuti muzichita zimene mumaphunzira.​—Afilipi 4:9.

18. Ngakhale ena atakutsutsani, kodi mungakhale ndi chidaliro chotani?

18 Madalitso amene timapeza chifukwa chotumikira Yehova ndi okhalitsa, inde, osatha. N’zoona kuti nthaŵi zina ena adzakutsutsani kapena kukunyozani chifukwa chokhala wa Mboni za Yehova. Koma ganizirani za Mose. Baibulo limanena kuti “anapenyerera chobwezera cha mphotho.” (Ahebri 11:24-26) Inunso mungadalire kuti Yehova adzakupatsani mphoto chifukwa cha khama lanu pofuna kuphunzira za iye ndi kuuza ena za iye. Inde, iye ‘sadzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.’​—Ahebri 6:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 13 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani mungakhulupirire kuti Yehova amayamikira utumiki wanu?

• Kodi ndi njira zolalikira kusukulu ziti zimene ena aona kuti n’zothandiza kwambiri?

• Kodi mungalimbe mtima bwanji kulalikira kwa ana a sukulu anzanu?

• Kodi mungayandikire bwanji kwa Yehova?

[Mafunso]

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 20]

Ndi Ana Aang’ono Omwe Akutamanda Yehova!

Ndi ana osakwanitsa zaka 13 omwe, alalikira kusukulu. Tamvani nkhani izi:

Ana a m’kalasi limene Amber wa zaka khumi anali, la giredi faifi, anali kuŵerenga buku lofotokoza za kumenya Ayuda kumene a Nazi anachita panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse. Amber anaganiza zobweretsa vidiyo yakuti Purple Triangles n’kuwapatsa aphunzitsi ake. Aphunzitsiwo anadabwa kudziŵa kuti Mboni za Yehova zinalinso kuzunzidwa ndi olamulira a Nazi. Iwo anaonetsa vidiyoyo kwa ana onse m’kalasiyo.

Alexa, wa zaka eyiti, analembera kalata ana a m’kalasi yake, kuwafotokozera chifukwa chake sanali kuchita nawo chikondwerero cha Khirisimasi. Aphunzitsi ake anachita chidwi kwambiri moti anauza Alexa kuti awaŵerengere kalatayo anzake m’kalasiyo ndiponso kukaiŵerenga m’makalasi ena aŵiri. Chakumapeto kwa kalatayo iye ananena kuti: “Ndaphunzitsidwa kulemekeza anthu ena amene zikhulupiriro zawo n’zosiyana ndi zanga, ndipo ndikukuthokozani chifukwa cholemekeza zimene ndasankha zosakondwerera Khirisimasi.”

Eric atangoyamba kumene kalasi ya giredi yoyamba, anatenga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kusukulu ndipo anapempha chilolezo kuti awaonetse anzake m’kalasiyo. Aphunzitsi ake anati: “Ndili ndi maganizo ena. Bwanji uwaŵerengere anzakoŵa nkhani imodzi?” Eric anatero, ndipo pomaliza anapempha kuti onse amene anafuna kuti akhale ndi buku lawolawo aimike manja. Anthu 18 anaimika manja kuphatikizapo aphunzitsiwo. Eric tsopano amaona kuti ali ndi gawo lake lapadera lolalikira.

Whitney yemwe ndi wa zaka zisanu ndi zinayi amayamikira bulosha lakuti Mboni za Yehova ndi Maphunziro. * Iye anati: “Mayi amapatsa aphunzitsi anga bulosha limeneli chaka chilichonse, koma chaka chino ndawapatsa ndekha. Mothandizidwa ndi buloshali, aphunzitsi anga anandisankha kukhala ‘mwana wabwino kwambiri mlungu umenewo.’”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 56 Vidiyo, buku ndi bulosha zimene tatchulazi n’zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 21]

Zochitika Zimene Ena Azigwiritsira Ntchito Kuuza Anthu Ena Chikhulupiriro Chawo

Ena atauzidwa kuti apeze nkhani imene adzachita lipoti kusukulu yawo kapena kupatsidwa zochita zina za kusukulu, asankha nkhani imene inawathandiza kulalikira.

Achinyamata ambiri apatsa aphunzitsi awo vidiyo kapena buku kapena magazini imene ikugwirizana ndi nkhani imene akukambirana m’kalasiyo.

Achinyamata ena poŵerenga Baibulo kapena buku lothandiza kuphunzira Baibulo panthaŵi yopuma, ana a sukulu anzawo awafikira ndi kuwafunsa mafunso.

[Chithunzi patsamba 18]

Anthu amene azoloŵera utumiki angathandize kuphunzitsa achinyamata kutumikira Yehova