Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amaganizira Anthu Wamba

Yehova Amaganizira Anthu Wamba

 Yehova Amaganizira Anthu Wamba

KODI tifunika kukhala apamwamba kapena abwino kwambiri m’njira inayake kuti tikhale odziŵika kwa Mulungu? Abraham Lincoln, pulezidenti wa nambala 16 wa dziko la United States, akuti anati: “Ambuye amakonda anthu wamba. N’chifukwa chake amalandira anthu ambiri otere.” Anthu ambiri amadziona kuti ndi anthu wamba oti sangachite chilichonse chothandiza. Kukhala munthu wamba kungatanthauze kukhala m’mphaŵi, wonyozeka. Ndiponso, kungatanthauze kupanda udindo wina uliwonse wodziŵika bwino ndi anthu. Kodi mumakonda kucheza ndi anthu otani? Kodi mumakonda kucheza ndi anthu odzikuza, aliuma, ndi onyada? Kodi simungakonde kucheza ndi anthu ochezeka, odzichepetsa, osadzitukumula, amene amaganizira kwambiri za ena?

Popeza kuti masiku ano kusakondana ndiponso kunyozana ndi zofala m’dzikoli, ena zimawavuta kukhulupirira kuti Mulungu amawakonda iwo paokha. Munthu wina amene amaŵerenga magazini ano anati: “Ndinachokera ku banja limene silinkasonyezana chikondi. Ankandinyoza, kundinyodola, ndi kundiseka. Choncho, ndili wamng’ono ndinkadziona kuti ndinali wopanda pake. Ndili nawobe maganizo akalekale ameneŵa, omwe amandifooketsa ndikakumana ndi mavuto.” Komabe, pali zifukwa zokhulupirira kuti Mulungu amakonda anthu wamba.

Mulungu Anasonyeza Kuganizira Anthu Wamba

Mfumu Davide inalemba kuti: “Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngosasanthulika.” (Salmo 145:3) Komabe, zimenezi sizimulepheretsa Yehova kutisamalira mwachikondi ndiponso mwachifundo. (1 Petro 5:7) Mwachitsanzo, wamasalmo anati: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”​—Salmo 34:18.

Zinthu zimene anthu amatengeka nazo mitima m’dzikoli, monga kukongola, udindo wapamwamba, kapena kulemera, Mulungu sadziona ngati kanthu. Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Israyeli, chinasonyeza kuganizira ndiponso kuchitira chifundo anthu osauka, ana masiye, akazi amasiye, ndiponso alendo. Mulungu anauza Aisrayeli, amene anazunzidwa mwakhanza ku Igupto kuti: “Usasautsa mlendo kapena kum’psinja . . . Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense. Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang’ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwawo.” (Eksodo 22:21-24) Ndiponso, mneneri Yesaya anasonyeza kuti anali ndi chidaliro chakuti Mulungu amaganizira aumphaŵi. Iye anati: “Mwakhala linga la aumphawi, linga la osoŵa m’kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuŵa, pamene kuomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuomba chemba.”​—Yesaya 25:4.

Mu utumiki wake wonse, Yesu Kristu, amene ndi “chizindikiro chenicheni” cha Mulungu, anali chitsanzo kwa ophunzira ake pankhani yoganiziradi anthu wamba. (Ahebri 1:3) Ataona makamu a anthu omwe “anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa,” Yesu “anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo.”​—Mateyu 9:36.

Onaninso anthu amene Yesu anasankha kuti akhale atumwi ake. Iye anasankha anthu amene  ankatchedwa “osaphunzira ndi opulukira [“anthu wamba,” NW].” (Machitidwe 4:13) Yesu atamwalira, otsatira ake anayamba kupempha anthu amitundu yonse kudzamvetsera Mawu a Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti “wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira [“munthu wamba,” NW]” angabwere mu mpingo wachikristu ndi kukhala wokhulupirira. (1 Akorinto 14:24, 25) M’malo mosankha anthu apamwamba okhaokha malinga ndi kuona kwa anthu a dzikoli, Mulungu anasankha anthu onyozeka ambiri, anthu wamba kuti amutumikire. Mtumwi Paulo anati: “Penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iyayi; koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu; ndipo zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziliko; kuti thupi lililonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.”​—1 Akorinto 1:26-29.

Masiku ano, Mulungu amatiganiziranso kwambiri. Mulungu amafuna kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Ngati Mulungu anakonda anthu kwambiri mpaka kutumiza Mwana wake ku dziko lapansi lino kudzatifera, palibiretu chifukwa chodzionera kuti sitikondedwa kapena kuti ndife opanda pake. (Yohane 3:16) Yesu Kristu anasonyeza otsatira ake kufunika kochitira zinthu abale ake auzimu ngakhale onyozeka kwambiri ngati kuti akuchitira Yesu weniweniyo. Iye anati: “Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’onong’ono awa, munandichitira ichi Ine.” (Mateyu 25:40) Kaya dziko limationa bwanji, ngati timakonda choonadi ndife amtengo wapatali zedi kwa Mulungu.

Ndi mmene Francisco, * mnyamata wopanda bambo wa ku Brazil, anamvera atakhala paubwenzi ndi Mulungu. Iye anati: “Kudziŵa Yehova ndi gulu lake kunandithandiza kuthana ndi vuto langa lodziona ngati wopanda pake ndiponso manyazi. Ndinaphunzira kuti Yehova amakonda munthu aliyense.” Kwa Francisco, Yehova anakhala Atate wake weniweni.

Amaganizira Achinyamata

Yehova amaganizira achinyamata monga gulu komanso aliyense payekha. N’zoona kuti tonsefe, achinyamata ndi achikulire omwe, sitifunika kudziona kuti ndife ofunika kwambiri kuposa mmene tilili. Komabe, tingakhale ndi maluso ndi makhalidwe amene Mulungu angadzagwiritse ntchito m’tsogolo. Yehova amadziŵa zimene tikufunika kuwongolera komanso kuphunzira kuti tigwiritse ntchito mokwanira zimene tingathe kuchita. Mwachitsanzo, onani nkhani ya pa 1 Samueli chaputala 16. Popeza mneneri Samueli anaona kuti ena amene akanatha kuloŵa ufumu wa Aisrayeli anali oyenerera kwambiri, Yehova anafotokoza chifukwa chimene anasankhira Davide, mwana wamng’ono kwambiri wa Jese, monga mfumu ya m’tsogolo ya Israyeli. Iye anati: “Usayang’ane nkhope yake, kapena  kutalika kwa msinkhu wake, popeza ine ndinam’kana iye [mkulu wake wa Davide]; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.”​—1 Samueli 16:7.

Kodi achinyamata masiku ano angakhale ndi chidaliro chakuti Yehova amawaganiziradi? Taonani za mtsikana wina wa ku Brazil dzina lake Ana. Monga achinyamata ena ambiri, katangale ndi chinyengo zimene anali kuona zikuchitika zinali kumusoŵetsa mtendere. Kenako bambo ake anayamba kupita naye ku misonkhano yachikristu pamodzi ndi ang’ono ake. Patapita nthaŵi, anayamba kusangalala ndi zimene anali kuphunzira m’Mawu a Mulungu. Iye anayamba kuŵerenga Baibulo ndi zofalitsa zachikristu ndiponso kupemphera kwa Yehova Mulungu. Pang’ono ndi pang’ono, anakhala paubwenzi wapamtima ndi Mulungu. Iye anati: “Ndinkakonda kukwera njinga kupita ku kaphiri kamene kanali pafupi ndi nyumba yathu kukaona kukongola kwa dzuŵa likamaloŵa. Ndinkapemphera kwa Yehova ndiponso kumuthokoza chifukwa cha kukoma mtima ndi kuwolowa manja kwake ndiponso ndinkamuuza momwe ndimamukondera. Kudziŵa Yehova Mulungu ndi zolinga zake kunandithandiza kukhala ndi mtendere wa m’maganizo ndiponso kudziona kuti ndine wofunika.” Kodi nanunso mumapeza nthaŵi yosinkhasinkha mmene Yehova amatisamalirira chifukwa chotikonda?

Ndi zoona kuti tingavutike kukhala ndi ubwenzi wapamtima ndi Yehova chifukwa cha kumene tinakulira. Onani chitsanzo cha Lidia. Atauza bambo ake nkhani imene inali kumudetsa nkhaŵa kwambiri, anangomunyalanyaza, amvekere: “Za zii zimenezo.” Ngakhale kuti anadziŵa kuti bambo akewo ankafuna kuti iyeyo angoiŵala vutolo, Lidia anati: “Kuphunzira Baibulo ndi kumene kunandithandiza kupeza zonse zimene ndinkafuna ndiponso zoposa pamenepo. Yehova anakhala bwenzi langa lapamtima chifukwa cha makhalidwe ake abwino. Tsopano ndili ndi Atate wachikondi, womvetsa zinthu amene ndingamuuze za kukhosi kwanga momasuka ndiponso zimene zimandidetsa nkhaŵa kwambiri. Ndingathe kulankhula ndi Munthu wofunika kwambiri m’chilengedwechi kwa maola angapo, ndi chidaliro chakuti andimvetsera.” Malemba a Baibulo monga Afilipi 4:6, 7 anamuthandiza kuona kuti Yehova amamusamalira chifukwa choti amamukonda. Lembali limati: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”

Kukuthandizani pa Zosoŵa Zanu

Yehova amasonyeza kukonda atumiki ake, aliyense payekha, komanso mpingo wake wa padziko lonse. Tingasonyeze kukonda kwathu Atate wathu wakumwamba mwa kukhala ndi nthaŵi yolankhula naye. Tisauone mopepuka ubwenzi wathu ndi iye. Davide nthaŵi zonse ankakumbukira za ubale wake ndi Yehova. Iye anati: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.”​—Salmo 25:4, 5.

Mfundo yopanga ubwenzi wapamtima ndi Mulungu ingakhale yachilendo kwa inu. Kaya mukhale ndi mavuto amtundu wanji, nthaŵi zonse mungakhale ndi chidaliro chakuti Wam’mwambamwamba adzakuthandizani, mogwirizana ndi chifuniro chake. (1 Yohane 5: 14, 15) Choncho, phunzirani kupemphera molunjika, moganizira mmene zinthu zilili kwa inu ndiponso zosoŵa zanu.

Pemphero limene Mfumu Solomo inapemphera potsegulira kachisi limagogomezera kufunika kodziŵa zosoŵa zathu. Limati: “Mukakhala njala m’dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala chinsikwi, kapena chinoni, dzombe, kapena kapuche; akawamangira misasa adani awo, m’dziko la midzi yawo; mukakhala mliri uli wonse, kapena nthenda ili yonse; pemphero ndi pembedzero lili lonse likachitika ndi munthu ali yense, kapena ndi anthu anu onse Aisrayeli, akadziŵa yense chinthenda chake, ndi chisoni chake . . . pamenepo mumvere m’Mwamba . . . nimukhululukire, ndi kubwezera ali yense monga mwa njira zake zonse.” (2 Mbiri 6:28-30) Inde, mumadziŵa nokha ‘chinthenda chanu, ndi chisoni chanu.’ Choncho, n’kofunika kwambiri kudziŵa zimene mukusoŵa ndiponso mukufuna kwenikweni. Mukatero, ‘[Yehova] adzakupatsani zokhumba mtima wanu.’​—Salmo 37:4.

Limbitsani Ubwenzi Wanu ndi Yehova

Yehova amasangalala kukhala paubwenzi wapamtima ndi anthu wamba. Mawu ake amatitsimikizira kuti: “Ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.” (2 Akorinto 6:18) Zoona, Yehova ndi Mwana wake amafuna kuti zinthu zitiyendere bwino ndiponso tidzapeze moyo wosatha. Ndi zolimbikitsa kwambiri kudziŵa kuti Yehova adzatithandiza posamalira maudindo a m’banja, akuntchito, ndi a mumpingo wachikristu.

Komabe, tonse timavutika. Matenda, mavuto a m’banja, a zachuma, kapena chinthu china chake chingativutitse maganizo. Sitingadziŵe mochitira pamene tikumana ndi chiyeso. Mavuto amene akuchulukirachulukirawa, mwachindunji kapena kudzera m’zinthu zina, amayambitsa ndi woneneza woipa, Satana Mdyerekezi, amene akumenya nkhondo yauzimu ndi anthu a Mulungu. Komabe, pali wina amene amatimvetsa ndi kutithandiza kuti tikhalebe paubwenzi wabwino ndi Yehova. Ameneyu si winanso ayi, koma Yesu Kristu pa udindo wake wapamwamba kumwamba. Timaŵerenga kuti: “Sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusoŵa.”​—Ahebri 4:15, 16.

N’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti sitifunika kukhala otchuka kapena olemera kuti Mulungu atiyanje. Ngakhale pamavuto aakulu, khalani ngati wamasalmo amene anapemphera kuti: “Ine ndine wozunzika ndi waumphaŵi; koma Ambuye andikumbukira ine: Inu ndinu mthandizi wanga, ndi mpulumutsi wanga.” (Salmo 31:9-14; 40:17) Khalani ndi chidaliro chakuti Yehova amakonda anthu odzichepetsa, anthu wamba. Ndithudi, ‘tingataye pa Iye nkhaŵa zathu zonse pakuti Iye asamalira ife.’​—1 Petro 5:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Tasintha maina ena.

[Zithunzi patsamba 29]

Otsatira a Yesu ambiri anali osaphunzira ndiponso anthu wamba

[Chithunzi patsamba 30]

Akristu amayesetsa kukhala ndi chikhulupiriro cholimba

[Zithunzi patsamba 31]

Sikuti tifunika kukhala otchuka kuti Mulungu atiyanje