Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Mmene Mumaganizira?

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Mmene Mumaganizira?

Anthu amafunika kuphunzira zokhudza sukulu, ntchito kapena zinthu zina ndipo zipangizo zamakono zimathandiza. M’mbuyomu zinali zovuta kwambiri kuti munthu apeze zinthu zokhudza sukulu, ntchito kapena zinthu zina ali kunyumba.

Komabe anthu amene amakonda kugwiritsa ntchito kwambiri zipangizo zamakono amapeza kuti . . .

  • zimawavuta kuika maganizo awo pa zimene akuwerenga.

  • zimawavuta kuika maganizo awo pa chinthu chimodzi.

  • sachedwa kuboweka akakhala paokha.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

KUWERENGA

Anthu ena amene amakonda kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono, nthawi zina sakhala oleza mtima moti n’kuwerenga nkhani yonse bwinobwino koma amangowerenga pomwe pawasangalatsa.

Kuwerenga patalipatali ndi kwabwino makamaka ukamafuna yankho mwamsanga. Komabe, kuwerenga kumeneku sikwabwino ngati ukufuna kumvetsa nkhani yonse.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mumakwanitsa kuwerenga nkhani yaitali? Nanga kuchita zimenezi kungakuthandizeni bwanji kuphunzira zinthu zina?​—MIYAMBO 18:15.

KUIKA MAGANIZO PA CHINTHU CHIMODZI

Anthu ambiri amaganiza kuti zipangizo zamakono zimawapatsa mwayi woti akhoza kumachita zinthu ziwiri pa nthawi imodzi. Mwachitsanzo, akhoza kumalembera anthu ena mameseji uku akuwerenga. Komatu amasokonezeka moti sakwanitsa kuchita ngakhale chimodzi mwa zinthuzo.

Kuika maganizo pa chinthu chimodzi kumafuna kudziletsa, ndipo ndi kothandiza kuti munthu aphunzire. Mtsikana wina dzina lake Grace ananena kuti: “Sulakwitsa zinthu zambiri komanso sukhala ndi nkhawa kwambiri. Ndaphunzira kuti ndi bwino kuchita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi m’malo mochita zinthu zambiri.”

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi kuchita zinthu zina kwinaku mukuwerenga, kumakusokonezani kapenanso kumakuchititsani kuti musakumbukire zomwe mwawerenga?​—MIYAMBO 17:24.

MUKAKHALA KWA NOKHA

Anthu ena samva bwino akakhala okha ndipo amagwiritsa ntchito zipangizo zamakono kuti azimva ngati ali ndi winawake. Mayi wina dzina lake Olivia anati: “Pakamatha 15 minitsi ndisanagwiritse ntchito foni, tabuleti kapenanso kuonera TV, sindimamva bwino.”

Komabe, munthu ukakhala wekha umakhala ndi mwayi woganizira mozama zinthu zimene waphunzira ndipo zimenezi sizikukhudza achinyamata okha, koma ngakhalenso anthu akuluakulu.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mumagwiritsa ntchito moyenera nthawi yomwe muli nokha?—1 TIMOTEYO 4:15.

ZIMENE MUNGACHITE

GANIZIRANI MMENE MUMAGWIRITSIRA NTCHITO ZIPANGIZO ZAMAKONO

Kodi zipangizo zamakono zingakuthandizeni bwanji kuphunzira zinthu? Kodi zipangizo zamakono zingakulepheretseni bwanji kuphunzira komanso kuika maganizo anu pa zimene mukuphunzirazo?

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Usunge nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.”​—MIYAMBO 3:21.