Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Inuyo Mumatanganidwa Kwambiri?

Kodi Inuyo Mumatanganidwa Kwambiri?

Kodi mumaona kuti nthawi zonse mumakhala wotanganidwa? Ngati ndi choncho dziwani kuti si inu nokha. Magazini ina inati, “Anthu onse, kwina kuli konse amakhala otanganidwa.”​—The Economist.

PA KAFUKUFUKU wina amene anachitika m’mayiko 8 m’chaka cha 2015, anthu ambiri ogwira ntchito ananena kuti zimawavuta kupeza nthawi yokwanira yokhala pakhomo. Zimenezi zimachitika chifukwa cha kuchuluka kwa maola amene amakhala akugwira ntchito, kuwonjezeka kwa ndalama zimene amawononga komanso chifukwa chakuti ambiri amakhala ndi udindo waukulu kuntchito kapena kunyumba. Mwachitsanzo ku United States, ena anati amagwira ntchito kwa maola pafupifupi 47 mlungu uliwonse. Ndipo mmodzi pa anthu 5 alionse anati amagwira ntchito maola 60 kapena kuposa.

Pa kafukufuku winanso yemwe anachitika m’mayiko okwana 36, anthu 25 pa 100 alionse ananena kuti amatanganidwabe ngakhale pa nthawi imene sakugwira ntchito. Ana nawonso amapanikizika ngati amapatsidwa zochita zambiri.

Ngati kawirikawiri timafuna kumachita zinthu zambiri m’kanthawi kochepa, tikhoza kumakhala osasangalala mwinanso kudwala kumene. Koma kodi tingatani kuti tisamapanikizike? Kodi zimene timakhulupirira, zimene timasankha komanso zolinga zathu n’zofunika bwanji pa nkhaniyi? Choyamba tiyeni tione zinthu 4 zimene zimachititsa anthu ena kuti azitanganidwa kwambiri.

1 MTIMA WOFUNA KUSAMALIRA BWINO BANJA

Bambo wina dzina lake Gary ananena kuti: “Ndinkagwira ntchito kwa masiku onse 7 pa mlungu. Ndinkafuna kuti nthawi zonse ndizigula zinthu zabwino zoti ndikapatse ana anga. Ndinkalakalaka kuti azikhala ndi zinthu zimene ngakhale ineyo sindinakhalepo nazo.” Ngakhale kuti makolo ambiri amakhala ndi zolinga zabwino, amayenera kuona kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti. Kafukufuku wina anasonyeza kuti makolo ndiponso ana amene anazolowera kukhala ndi ndalama komanso katundu wambiri, sakhala osangalala, sakhutira ndi zimene ali nazo ndiponso sakhala ndi thanzi labwino kusiyana ndi anthu amene alibe zinthu zambiri.

Ana amene anazolowera kukhala ndi katundu wambiri sakhala osangalala

Makolo ena amapanikizika ndi ntchito komanso amapanikiza ana awo ndi zinthu zina n’cholinga choti anawo adzakhale ndi tsogolo labwino. Zimenezi zimachititsa kuti ana komanso makolowo asamasangalale.

2 MAGANIZO AKUTI ‘NDI BWINO KUKHALA NDI ZINTHU ZAMBIRI’

Otsatsa malonda amachititsa anthu kuona kuti amanidwa zinazake ngati sagula katundu amene wangotuluka kumene. Magazini ina inati: “Chifukwa cha kuchuluka kwa katundu watsopano, anthu amavutika kuti asankhe zinthu zoti awonere pa TV, zoti agule kapena zoti adye” ndipo “amaona kuti alibe nthawi yokwanira.”​—The Economist.

M’chaka cha 1930, katswiri wina wazachuma ananena kuti mtsogolomu zipangizo zamakono zidzathandiza anthu ogwira ntchito kuti azikhala ndi mpata wokwanira wopuma. Komatu zimenezi sizinali zoona. Wolemba magazini wina dzina lake Elizabeth Kolbert, anapeza kuti masiku ano “m’malo moweruka msanga, ambiri amapitiriza kugwira ntchito kuti athe kupeza zinthu zina zimene akufuna.” Komatu zinthuzi zimafuna ndalama komanso nthawi.​—New Yorker.

3 KUFUNA KUSANGALATSA ANTHU ENA

Anthu ena amagwira ntchito mwakalavulagaga n’cholinga choti asangalatse abwana awo. Enanso amaopa kuti anzawo ogwira nawo ntchito aziwanena akaweruka msanga. Mavuto azachuma amachititsanso anthu ena kuti azigwira ntchito maola ambiri kapena azingokhala okonzeka kugwira ntchito ngakhale pa nthawi imene si yantchito.

Nthawi zina makolo angamapanikizike kuti akhale ndi zinthu zimene mabanja ena ali nazo. Akalephera kuzipeza angamadziimbe mlandu n’kumaganiza kuti ana awo akumanidwa zinazake.

4 KUFUNA ENA AZIWAONA KUTI NDI OFUNIKA

Tim wa ku United States anati: “Ndinkakonda kwambiri ntchito yanga moti nthawi zonse ndinkaigwira modzipereka kwambiri. Ndinkafuna ena aziona kuti ndine wakhama komanso ndimalimbikira ntchito.”

Mofanana ndi Tim, ena amaganizira kwambiri za mmene moyo wawo ulili komanso mmene anthu ena aziwaonera. A Elizabeth Kolbert omwe tawatchula poyamba aja ananenanso kuti: “Anthu ambiri amadziwika kuti ndi otanganidwa, ndipotu ukamatanganidwa kwambiri m’pamenenso umaoneka kuti ndiwe wofunika.”

MUZIYESA KUDZIIKIRA MALIRE

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizigwira ntchito mwakhama. (Miyambo 13:4) Koma limanenanso kuti tisamachite zinthu mopitirira malire. Lemba la Mlaliki 4:6 limati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”

Kuchita zinthu mosapitirira malire kungatithandizenso kukhala ndi moyo wathanzi. Koma kodi n’zotheka kudziikira malire kuti tisamatanganidwe kwambiri? Inde, taganizirani njira 4 zotsatirazi:

1 MUZIKHALA NDI ZOLINGA

N’zoona kuti aliyense amafuna kukhala ndi ndalama. Koma kodi munthu ayenera kukhala ndi ndalama zingati kuti akhutire kuti ali ndi ndalama zokwanira? Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti munthu zikumuyendera? Kodi ndi kukhala ndi ndalama zambiri komanso katundu wambiri? Komanso dziwani kuti kungokhala ndi nthawi yambiri yopuma kapena yochita zosangalatsa sikungathandizenso munthu kukhala wosangalala.

Tim, tamutchula poyamba uja anati: “Ine ndi mkazi wanga tinaganizira mofatsa za moyo wathu ndipo tinasintha zinthu zina. Tinalemba ndandanda ya zimene tikufuna kumachita. Tinakambirananso zotsatirapo za zosankha zimene tinapanga m’mbuyomu komanso zimene tingachite kuti tikwaniritse zolinga zathu.”

2 MUSAMATENGEKE NDI A MALONDA

Baibulo limatilangiza kuti tizipewa “chilakolako cha maso.” (1 Yohane 2:15-17) Koma otsatsa malonda akhoza kutichititsa kukhala ndi chilakolako chimenechi. Zimenezi zingachititse kuti munthu azigwira ntchito kwa maola ambiri n’cholinga choti azipeza ndalama zambiri zochitira zosangalatsa. N’zoona kuti sitingapeweretu kugula chilichonse chomwe a malonda akutsatsa, koma timafunika kukhala ndi malire. Tingachite zimenezi poganizira zinthu zimene tikufunikiradi.

Muyeneranso kusamala ndi zinthu zimene anzanu ocheza nawo amachita. Ngati nthawi zonse amangokhalira kukamba za ndalama kapena amaona kuti munthu angakhale wosangalala chifukwa cha katundu amene ali naye, mungachite bwino kupeza anzanu amene amaika zinthu zofunika pamalo oyamba. Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.”​—Miyambo 13:20.

3 MUZIDZIIKIRA MALIRE A NTHAWI YOGWIRA NTCHITO

Muzifotokozera abwana anu za zinthu zina zimene mumafuna kuti muzichita. Musamadziimbe mlandu kuti ntchito siiyenda bwino ngati inuyo kulibe. Buku lina linati: “Anthu amene amadziikira malire pa kagwiridwe kawo kantchito komanso amene amapeza nthawi yocheza ndi mabanja awo kapena kupita kutchuthi, amayendera mfundo yofanana yakuti ntchito singaime ngakhale utakhala kuti iweyo palibe.”​—Work to Live.

A Gary omwe tawatchula poyamba aja, anali ndi ndalama zambiri moti anaganiza zochepetsa nthawi imene ankagwira ntchito. Iwo anati: “Ndinakambirana ndi banja langa kuti tisinthe zinthu zina pa moyo wathu ndipo tinayambadi kusintha pang’onopang’ono. Ndinapemphanso abwana anga kuti ndizigwira ntchito masiku ochepa pa mlungu, ndipo anavomera.”

4 MUZIPEZA NTHAWI YOKWANIRA YOCHEZA NDI BANJA LANU

Amuna ndi akazi okwatirana amafunika azipeza nthawi yochezera limodzi. Nawonso ana amafuna kuti makolo azikhala ndi nthawi yocheza nawo. Choncho, musamachite zinthu n’cholinga choti mufanane ndi mabanja amene amakhala otanganidwa nthawi zonse. A Gary ananenanso kuti: “Muzipeza nthawi yopuma ndipo musamachite zinthu zomwe ndi zosafunika kwenikweni.”

Mukakhala limodzi ndi banja lanu, musamalole kuti TV, mafoni kapena zipangizo zilizonse zamakono zikusokonezeni. Muziyesetsa kudyera limodzi, mwina kamodzi patsiku, ndipo muzigwiritsa ntchito nthawi imeneyi kucheza ndi banja lanu. Makolo akamatsatira malangizo amenewa, ana awo amasangalala ndiponso amakhala a nzeru kusukulu.

Muzigwiritsa ntchito nthawi yakudya kucheza ndi banja lanu

Pomaliza, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimafuna kuti moyo wanga ukhale wotani? Nanga ndimafunira banja langa zotani?’ Ngati mumafuna kuti muzisangalala komanso mukhale ndi moyo wabwino, muziika zinthu zofunika pamalo oyamba ndipo muzigwiritsa ntchito nzeru zopezeka m’Baibulo.