GALAMUKANI! November 2014 | Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala?

M’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni kukhala wosangalala. Onani zitsanzo 4 zosonyeza kuti malangizo a m’Baibulo ndi othandiza.

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake ndi monga: mapulani oteteza nkhalango analephereka ku Ecuador, kachilombo koyambitsa matenda a Edzi kakumavuta kukazindikira komanso kukanganirana nyama zapakhomo ku Australia.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala?

Kodi malangizo a m’Baibulo angatithandizedi kukhala osangalala? Nkhaniyi ili ndi mfundo 4 zimene zingathandize munthu kukhala wosangalala.

Ngalande za Madzi za ku Roma Ankazimanga Mwaukadaulo

N’chifukwa chiyani anthu a ku Roma wakale ankamanga ngalande? N’chifukwa chiyani chikusonyeza kuti ngalandezi ngalandezi zinkamangidwa mwaukadaulo?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Zimene Mungachite Ngati Mwana Wanu Amanama

Kodi mungatani ngati mwana wanu wanama? Nkhaniyi ikufotokoza malangizo a m’Baibulo amene angakuthandizeni kuphunzitsa mwana wanu kufunika kunena zoona.

MBIRI YA MOYO WANGA

Yehova Anandithandiza pa Nthawi Yomwe Ndinkafunikiradi Kuthandizidwa

Ali ndi zaka 20, Miklós Aleksza analumala atachita ngozi. Kodi Baibulo linamuthandiza bwanji kukhala ndi chiyembekezo?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Ukhondo Komanso Makhalidwe Abwino

Werengani malangizo othandiza a m’Baibulo omwe athandiza anthu ambiri kukhala oyera komanso athanzi.

Nyumba Yomwe Imakumbutsa Anthu za Bomba Loopsa

N’chifukwa chiyani chinyumba chomwe chinawonongeka mu 1945, mumzinda wa Hiroshima ku Japan, sanachikonzebe mpaka pano? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe za chinyumba chimenechi komanso zimene Baibulo limalonjeza pa nkhani ya nkhondo.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?

Dziwani zimene mungachite ngati nthawi zonse mumangokhala wokhumudwa.

N’chifukwa Chiyani Ndikufunika Kumathandiza Ena?

Kuchitira ena zabwino kumakuthandizani m’njira ziwiri. Kodi njira zimenezi ndi zotani?

Khadi la M’Baibulo Lonena za Miriamu

Kodi MIriamu ankagwiritsira ntchito chiyani poimba nyimbo? Koperani khadi la m’Baibuloli kuti mudziwe zambiri zokhudza Miriamu.