Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Ecuador

Mu 2007, dziko la Ecuador linapempha mayiko ena kuti alithandize ndi ndalama pa mapulani ake oteteza dera la masikweya kilomita 10,000, lomwe lili m’nkhalango ya Amazon. Dzikoli linkafuna kuti anthu asamakumbe zitsime zamafuta m’derali. Koma mapulani amenewa analephereka chifukwa mayiko sanalithandize. Derali ndi limodzi mwa malo amene ali ndi zamoyo zambiri komanso za mitundu yosiyanasiyana padziko lapansi.

Japan

Nyuzipepala ina ya ku Japan inanena kuti nthawi zina zimakhala zovuta kudziwa ngati magazi a munthu ali ndi kachilombo koyambitsa Edzi. Zili choncho chifukwa munthu yemwe wangotenga kumene kachilomboka akayezedwa, magazi ake sasonyeza kuti ali nako. Munthu wotereyu amatha kupereka magazi kuchipatala chifukwa madokotala amaona ngati magazi ake ndi abwinobwino. Nyuzipepalayi inati m’chaka cha 2013, bambo wina wazaka 60 anatenga kachilombo koyambitsa Edzi ataikidwa magazi omwe anali ndi kachilomboka.

Zimbabwe

Nkhondo yapakati pa zigawenga ndi boma la Zimbabwe, yomwe inkachitika kumalire a dzikoli ndi Mozambique, inatha zaka zoposa 30 zapitazo. Komabe, mabomba okwiriridwa pansi akupitirizabe kuvulaza ndi kupha anthu komanso ziweto. Lipoti lina la bungwe la Red Cross linati: “Kuyambira mu 1980, anthu oposa 1,500 anafa ndipo enanso 2,000 anavulala kwambiri ndi mabombawa. Kuwonjezera pamenepo, ziweto zokwana 120,000 zinafa ndi mabombawa.”

Australia

Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu ambiri banja lawo likatha, amakanganirana ziweto zomwe anali nazo pakhomo pawo. Ziweto zake ndi monga agalu kapena amphaka. Ziwetozi amaziona kuti n’zofunika kwambiri ndipo zimakhala m’gulu la zinthu zimene amafunika kugawana monga malo, nyumba komanso ndalama.