Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyumba Yomwe Imakumbutsa Anthu za Bomba Loopsa

Nyumba Yomwe Imakumbutsa Anthu za Bomba Loopsa

KU JAPAN mumzinda wa Hiroshima, m’mbali mwa mtsinje wa Motoyasu, muli chinyumba chomwe chinangotsala makoma okha. Chinyumbachi ndi chakalekale ndipo chinaphulitsidwa ndi bomba mu 1945. N’chifukwa chiyani sanachikonzenso ngakhale kuti tsopano patha zaka pafupifupi 70?

Nyumbayi inali yanjerwa ndipo anamaliza kuimanga mu 1915. Inali ya nsanjika zitatu komanso inkagwiritsidwa ntchito ngati malo oonetsera zamalonda. Koma pa August 6, 1945, nthawi ya 8:15 m’mawa, asilikali omwe anali m’ndege anaponya bomba loopsa kwambiri mumzinda wa Hiroshima. Bombali linaphulika m’mwamba pa mtunda wa mamita pafupifupi 550 ndipo linaphulikira pamwamba pa nyumbayi. Anthu onse amene anali m’nyumbayi anafa nthawi yomweyo. Aka kanali koyamba kuti anthu agwiritse ntchito bomba loopsa chonchi. Komabe makoma a nyumbayi sanagwe ndipo adakalipo mpaka pano.

Pofotokoza chifukwa chake nyumbayi sanaikonzenso, bungwe la UNESCO linanena kuti nyumbayi anaisiya kuti “izikumbutsa anthu za bomba loopsa limene linapha anthu ambiri.” Mu 1996, nyumbayi inaikidwa m’gulu la malo achikumbutso ofunika kwambiri padziko lonse a bungwe la UNESCO ndipo anaipatsa dzina lakuti, Hiroshima Peace Memorial.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti malo achikumbutso ngati amenewa sathandiza kuti nkhondo zithe. Nthawi zambiri nkhondo zimayamba chifukwa cha dyera komanso tsankho. Zimayambanso chifukwa cha kusiyana mayiko, mitundu kapena zipembedzo. Koma kodi nkhondo zidzatha padzikoli?

Baibulo limanena kuti zidzatha. Lemba la Salimo 46:9, limati: “[Mulungu] akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.” Mulungu adzakhazikitsa Ufumu umene udzalowe m’malo mwa maboma alipowa. Komanso Mulungu anasankha Yesu Khristu yemwe ndi “Mfumu ya mafumu” kuti akhale mfumu ya Ufumuwu.—Chivumbulutso 11:15; 19:16.

Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, anthu sadzafunikanso kukhala ndi malo owakumbutsa kuipa kwa nkhondo. Lemba la Yesaya 65:17 limati: “Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.” Zinthu zakale zimenezi ndi mavuto onse amene tikukumana nawo masiku ano.