Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndiwo Zokoma Zomwe Sitidzaziiwala

Ndiwo Zokoma Zomwe Sitidzaziiwala

Ndiwo Zokoma Zomwe Sitidzaziiwala

TSIKU lina anzathu ena anatiitana kuti tikadye chakudya kunyumba kwawo, m’tauni ina ya mumzinda wa Bangui, womwe ndi likulu la dziko la Central African Republic.

Ine ndi mkazi wanga titafika kunyumbako, Ella, yemwe ndi mwiniwake wa nyumbayo, anatiuza kuti: “Lowani. Takukonzerani chakudya.” Koma tisanalowe n’komwe nyumbamo tinamva kafungo kabwino ka anyezi, adyo ndi zinthu zina zokometsera zakudya komanso tinkamva anthu ena akuseka. Pomwe tinkadikirira chakudyacho, Ella anayamba kutiuza zambiri za chakudya chimene ankaphikacho.

Iye anayamba kufotokoza kuti: “Anthu ambiri a m’mayiko a m’chigawo chapakati ku Africa kuno amakonda kudya zinthu ngati mphalabungu, ngumbi komanso abwamnoni chifukwa chakuti ndi ndiwo zokoma komanso zopatsa thanzi. Koma lero tidya mphalabungu.”

Sitinadabwe ndi zimenezi chifukwa ngakhale kuti anthu ena sangazikonde, anthu a m’mayiko oposa 100 amaona kuti ndi chakudya chokoma kwambiri.

Ndiwo Zokoma za M’nkhalango

Anthu a ku Central African Republic amakonda kudya ndiwo zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, m’nyengo ya mvula amadya ngumbi zomwe amazitchula kuti bobo. M’madera a m’midzi, ngumbizi zikatuluka zimangozungulira pachulu pomwepo, pamene m’tawuni zimapita kumene kukuwala magetsi. Ngumbi zimakonda kutuluka madzulo ndipo nthawi zambiri ana amatenga mabasiketi n’kumazitola, kwinaku akudya zaziwisi. Ena amakonda kudya ngumbi zongoumitsa ndi dzuwa, ena amazikazinga n’kuzithira mchere ndipo ena amazithira tsabola ndi zokometsera zina. Komanso ena amaziphika n’kuzithira tomato kapena amazisakaniza ndi fulawa n’kuumba timibulutimibulu.

Nyengo yamvula ikatha, kumagwa abwamnoni omwe amawatchula kuti Kindagozo. Anthu a ku Central Africa akagwira abwamnoniwa, amawathothola miyendo ndi mapiko kenako amawakazinga kapena kuwaphika.

Ndiwo zinanso zimene anthu amakonda kudya ndi mphalabungu, zomwe ena amati malasankhuli. Kumene tinakacheza kuja anatiphikira mtundu winawake wa mphalabungu. Gulugufe akaikira mazira m’mitengo, amaswa mphalabungu ndipo zikakhwima zimasintha n’kukhala gulugufe. Anthu akagwira mphalabungu amazitsuka, kenako amaziphika n’kuzithira tomato ndi anyezi ndi zinthu zina zokometsera. Ena amaziyanika kapena kuziwamba kuti adzazidye nthawi ina ndipo akatero zimatha kukhala miyezi itatu zili bwinobwino.

Chakudya Chokoma

Ndiwo za mtundu umenewu zimakhala bwino kudya ngati zachokera m’madera amene mitengo yake siinathiridwe mankhwala ophera tizilombo komanso ngati zasungidwa ndi kukonzedwa bwino. Koma anthu amene amadwala akadya nkhanu, nkhono ndi zinthu zina zam’madzi, ayeneranso kupewa kudya zinthu ngati mphalabungu chifukwa zikhozanso kuwadwalitsa. Zinthu monga nkhanu zimakonda kudya zinthu zoola. Koma mosiyana ndi zimenezi, mphalabungu, abwamnoni ndi zinthu zina za mtunduwu zimakonda kudya masamba ndi zomera zina zomwe mwina ngati munthu atadya, thupi lake silingazigaye bwinobwino.

Ngakhale kuti mphalabungu zimaoneka zonyozeka, ndi ndiwo zopatsa thanzi kwambiri. Malinga ndi zimene nthambi ya bungwe la United Nations yoona za zakudya ndi zaulimi inanena, mphalabungu zouma ndi zopatsa thanzi kwambiri kuposa nyama ya ng’ombe. Komanso akatswiri oona za zakudya atulukira kuti ndiwozi zikhoza kuthandiza kwambiri anthu a m’mayiko osauka kuti akhale ndi thanzi labwino.

Mitundu ina ya mphalabungu imakhala yopatsa thanzi kwambiri moti munthu atadya mphalabungu zodzaza manja awiri, akhoza kupeza zinthu zimene thupi lake limafunikira patsiku monga mavitamini, kasiyamu ndi aironi. Ena amasinja mphalabungu zouma ndipo ufa wakewo amaphikira phala ana omwe alibe zakudya zokwanira m’thupi.

Kuwonjezera pa kupatsa thanzi, kudya ndiwozi kulinso ndi ubwino wina. Mwachitsanzo kumathandiza kuti zachilengedwe zisawonongeke chifukwa kuphika ndiwozi sikufuna madzi ambiri komanso sikuwonjezera mpweya woipa mlengalenga. Komanso kumathandiza kuti tizilomboti tichepe chifukwa timawononga mitengo ndi zomera zina.

Tinadya Mphalabungu

Pomwe tinkadikirira chakudyachi, tinakumbukira kuti Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli, chinkawalola kudya dzombe moti atumiki ena a Mulungu monga Yohane Mbatizi ankadya dzombe. (Levitiko 11:22; Mateyu 3:4; Maliko 1:6) Komabe anthufe nthawi zambiri timaopa kudya chakudya chimene sitinachizolowere.

Tikucheza choncho, tinangoona Ella watulukira ndi mbale imene aliyense anachita nayo chidwi kwambiri. M’nyumbamo munali ifeyo komanso anthu ena 8 a ku Central African Republic. Nkhope za anthuwa zinali zosangalala kwambiri ataona mbale ziwiri za mphalabungu. Ifeyo monga alendo tinali oyambirira kupatsidwa chakudyacho ndipo anatigawira chakudya chambiri.

Pomaliza tinganene kuti, ngati mungadzakhale ndi mwayi wodya ndiwo zosafuna ndalama zambiri, zokoma komanso zopatsa thanzi zimenezi, dzadyeni ndipo simudzaziiwala.

[Chithunzi patsamba 27]

Mphalabungu zosaphika

[Chithunzi patsamba 27]

Abwamnoni okazinga