Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1. Muzisamala Pogula Zakudya

1. Muzisamala Pogula Zakudya

 1. Muzisamala Pogula Zakudya

NGATI simulima nokha zakudya, ndiye kuti mumakagula kumsika kapena kusitolo. Ndiyeno mukamagula zakudya, kodi mungatani kuti muzisankha zakudya zosamalidwa bwino?

Muzidziwiratu nthawi yoyenera kugula zakudya.

Bungwe loona za kasamalidwe ka zakudya la ku Australia linanena kuti: “Mukamagula zakudya, muziyamba ndi kugula zakudya zomwe sizingawonongeke mwamsanga ndipo muzimalizira ndi zimene zimafunika kuziika m’firiji.” Komanso ngati mwagula zakudya zophikaphika, muzipita nazo kunyumba mwamsanga.—Food Safety Information Council.

Muzigula zakudya zimene sizinakhalitse pamsika.

Ngati n’zotheka muzionetsetsa kuti mwagula zakudya zimene angobwera nazo kumene. * Mayi wina wa ku Nigeria yemwe ali ndi ana awiri, dzina lake Ruth, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimapita kumsika m’mawa kwambiri, chifukwa nthawi imeneyi zakudya zimakhala zitangobwera kumene.” Mayi winanso wa ku Mexico, dzina lake Elizabeth, amene amakagula zakudya zake kumsika, ananena kuti: “Ndimakonda kukagula zipatso komanso masamba kumsika waung’ono, chifukwa zimakhala zitangofika kumene. Komanso ndikamagula nyama, ndimaonetsetsa kuti ikhale imene yaphedwa tsiku lomwelo. Nyama ina ikatsala ndimaisunga m’firiji.”

Muzionetsetsa mukamagula zakudya.

Mukamagula zakudya muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zakudyazi zikuoneka bwanji? Kodi nyamayi ikumveka fungo linalake?’ Ngati chakudya chimene mukufuna kugula chili m’pepala, liyang’anitsitseni bwino pepalalo. Ngati litakhala long’ambika, tizilombo toyambitsa matenda tikhoza kulowa mosavuta.

Bambo wina wa ku Hong Kong, dzina lake Chung Fai, amakonda kugula zakudya zake kusitolo ndipo ananena kuti: “Mukamagula zakudya muzionanso ngati deti limene zakudyazo zidzawonongeke silinadutse.” N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezi? Akatswiri amanena kuti zakudya zimene zawonongeka zikhoza kudwalitsa munthu ngakhale kuti zingaoneke, kununkhira komanso kukoma ngati zabwinobwino.

Muzilongedza mosamala.

Ngati pokagula zinthu mumagwiritsa ntchito majumbo, muziwachapa ndi sopo m’madzi otentha. Muziika nyama ndi nsomba m’majumbo osiyana ndipo onetsetsani kuti zisagundane ndi zakudya zina.

Enrico ndi mkazi wake Loredana amakhala ku Italy, ndipo amagula zakudya zawo kumsika. Iwo ananena kuti: “Timagula zakudya zathu kumsika chifukwa tikakagula kusitolo, timayenda ulendo wautali ndipo zakudyazo zimawonongeka.” Ngati mukufuna kugula nyama yomwe ili m’firiji ndipo mukuona kuti mutenga nthawi yaitali musanafike kunyumba, mwina kupitirira mphindi 30, muzionetsetsa kuti nyamayo isasungunuke.

Mu nkhani yotsatira tiphunzira mmene tingasungire zakudya zathu mosamala tikafika kunyumba.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani nkhani yakuti, “1—Muzidya Zakudya Zoyenera,” m’magazini ya Galamukani! ya March 2011.

[Bokosi patsamba 4]

PHUNZITSANI ANA ANU: “Ndinawaphunzitsa ana anga kuti asanagule zakudya kusitolo, aziyamba aona ngati deti limene zakudyazo zidzawonongeke lisanadutse.”—Anatero Ruth wa ku Nigeria