Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwakonzekera Kudzaonera Mpira wa Euro 2012?

Kodi Mwakonzekera Kudzaonera Mpira wa Euro 2012?

 Kodi Mwakonzekera Kudzaonera Mpira wa Euro 2012?

KODI mumakonda kumenya kapena kuonera mpira? Ngati ndi choncho muyenera kuti mukudziwa za mpira wa UEFA EURO 2012. Masewerawa adzayamba pa June 8, mumzinda wa Warsaw ku Poland ndipo masewera omalizira adzachitika pa July 1, mumzinda wa Kiev, ku Ukraine. Kodi mpikisano wa EURO 2012 ndi wotani ndipo pakuchitika zotani pokonzekera mpikisano umenewu? Nanga n’chifukwa chiyani mpikisanowu uli wapadera kwambiri?

“Kupanga Mbiri Mogwirizana”

Kuyambira m’chaka cha 1960, mpikisano wa UEFA EURO umachitika ku Europe pakatha zaka zinayi zilizonse. M’mbuyomu, mpikisanowu wakhala ukuchitikira m’mayiko osiyanasiyana ngati Austria, Belgium, England, France, Germany, Italy, Netherlands, Portugal, Spain, Sweden, Switzerland, ndi Yugoslavia.

Koma chaka chino, ndime yomaliza ya mpikisanowu idzachitikira ku Poland ndi ku Ukraine. Mizinda ya ku Poland imene kudzachitikire mpikisanowu ndi Gdańsk, Poznan, Warsaw ndi Wroclaw, ndipo ku Ukraine mpirawu udzaseweredwa m’mizinda ya Donetsk, Kharkiv, Kiev, ndi L’viv.

Bungwe la UEFA lomwe limayang’anira masewerawa linanena kuti: “Kameneka kadzakhala kachitatu kuti ndime yomaliza ya mpikisanowu ichitikire m’mayiko awiri (koyamba ndime yomaliza ya mpikisanowu inachitikira ku Belgium ndi ku Netherlands  mu 2000 kenako ku Austria ndi Switzerland mu 2008).” Koma mpikisano wa EURO 2012 ndi wapadera kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti kameneka kakhala koyamba kuti ndime yomaliza ya mpikisanowu ichitikire m’chigawo chapakati komanso m’chigawo chakumadzulo kwa Europe. N’chifukwa chake mutu wa mpikisanowu uli wakuti, “Kupanga Mbiri Mogwirizana.”

Kodi Akukonzekera Bwanji Mpikisanowu?

Pokonzekera masewero aliwonse a mpira, chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri ndi kupeza malo abwino osewerera. N’chifukwa chake akuluakulu a m’mizinda ya Poznan ndi Kharkiv, akukonzanso masitediyamu amene alipo kale kumeneko. Komanso m’mizinda ina 6 kumene kudzachitikire masewerawa mwamangidwa masitediyamu atsopano. Masitediyamu atsopanowa ndi aakulu kwambiri chifukwa iliyonse mukhoza kulowa anthu pafupifupi 358,000.

Chifukwa chakuti kudzabwera anthu ambiri, akuluakulu a m’mizindayi akonza zoti adzakhwimitse chitetezo. Mwachitsanzo, anthu ambiri ogwira ntchito zachitetezo ali pamaphunziro okonzekera mmene angadzagwirire ntchito pa nthawi imeneyi. Magazini ina inanena kuti pokonzekera zimene adzachite pa masewerawa, anthu azachitetezo “anapita m’zochitika zosiyanasiyana zokwana 140 kuti akakonzekere zimene adzachite pa masewerawa. Ku zochitika zonsezo, iwo ankaonetsetsa kuti . . . anthu asayambitse chisokonezo, anakonza m’malo oti anthu athawireko ngati patachitika ngozi komanso ankachita zinthu mogwirizana ndi azachitetezo anzawo.”—Science & Scholarship in Poland.

Koma n’chifukwa chiyani akuchita kukonzekera chonchi? Chifukwa chakuti oyang’anira za masewera akudziwa kuti anthu amakonda kuchita zauchigawenga pa nthawi ngati imeneyi. Iwo amadziwanso kuti nthawi zina anthu oonerera akhoza kuyambitsa zisokonezo kapena zachiwawa monga mmene zakhala zikuchitikira m’mbuyomu.

Musamaukonde Mopitirira Malire

N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena oonera mpira amaukonda mopitirira malire. Munthu wina wokonda mpira ananena kuti: “Sindimasangalala timu yanga ikamaluza. Ndimaikonda kwambiri moti ngati pa tsiku limene timu yanga ikusewera kutachitika ngozi inayake kapena kutayambika nkhondo, chinthu chimene ndingachidandaule kwambiri ndi kulephereka kwa mpirawo.”

Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo lili ndi malangizo abwino kwambiri ofotokoza mmene tiyenera kuonera zinthu zosangalatsa. Ponena za kukhala ndi nthawi yochita zosangalatsa, Baibulo limanena kuti pali “nthawi yoseka . . . ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.” (Mlaliki 3:1-4) Baibulo limatilimbikitsanso kuchita zinthu mosapitirira malire. (1 Timoteyo 3:2, 11) Choncho, tikamasankha zinthu zochita pamoyo wathu, tingachite bwino kutsatira malangizo anzeru a m’Baibulo akuti: “Muzisiyanitsa zinthu zofunika ndi zimene zili zosafunika,” ndiyeno “muzisankha zofunikazo.”—Afilipi 1:10, Easy-to-Read Version.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 25]

PALIBE ADZALOLEDWE KUSUTA FODYA

Pa October 20, 2011, bungwe la UEFA linalengeza kuti lakhazikitsa “lamulo loletsa kusuta, kugulitsa kapena kuitanira malonda a fodya m’malo onse amene kudzachitikire mpikisano wa UEFA EURO 2012.” N’chifukwa chiyani bungweli lakhazikitsa lamuloli? Pulezidenti wa bungweli, dzina lake Michel Platini, ananena kuti: “Tachita zimenezi poganizira thanzi la anthu amene adzafike pa masewerawa.” Winanso amene akugwirizana ndi lamuloli ndi mmodzi wa akuluakulu a bungwe la European Commission, dzina lake Androulla Vassiliou. Iye anapempha akuluakulu a m’mizinda imene kudzachitikire mpikisanowu kuti akhazikitsenso lamuloli m’malo ngati m’malesitanti ndi m’malo okwerera basi. Iye anafotokoza kuti: “Masewera a mpira komanso ena olimbitsa thupi amathandiza kuti anthu akhale athanzi, pomwe fodya amawononga thanzi, choncho fodya ndi mpira sizimayenderana.”

[Mapu patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

POLAND

WARSAW

Gdańsk

Poznan

Wroclaw

UKRAINE

KIEV

L’viv

Kharkiv

Donetsk

[Chithunzi patsamba 24]

Masewera omalizira a mpikisano wa EURO 2008, a pakati pa Germany ndi Spain, anachitikira ku Ernst Happel Stadium mumzinda wa Vienna, ku Austria

[Chithunzi patsamba 25]

Sitediyamu ya mumzinda wa Kiev, ku Ukraine

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Pages 24 and 25, both photos: Getty Images