Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zakudya Zanu N’zosamalidwa Bwino?

Kodi Zakudya Zanu N’zosamalidwa Bwino?

 Kodi Zakudya Zanu N’zosamalidwa Bwino?

“Akuluakulu a boma ku Germany atseka sukulu ina, ana ena pasukulupo atadwala chifukwa chodya zakudya zokhala ndi tizilombo toyambitsa matenda ta E. Coli.”——REUTERS NEWS SERVICE, GERMANY.

“M’madera okwanira asanu m’dziko la United States mwagwa matenda amene amayamba ndi tizilombo toyambitsa matenda ta Salmonella ndipo anthu akukhulupirira kuti tizilomboto tachulukana chifukwa cha zakudya za ng’ombe.”—USA TODAY.

“Anthu ena a m’madera okwanira 9 ku Japan adya nyama ya ng’ombe zomwe zinadya udzu wa poizoni.”—THE MAINICHI DAILY NEWS, JAPAN.

NKHANI zimene zili pamwambazi zinachitika m’milungu iwiri yokha chaka chathachi. Akatswiri ofufuza amanena kuti chaka chilichonse pafupifupi anthu 30 pa 100 alionse, a m’mayiko olemera, amadwala chifukwa chodya zakudya zosasamalidwa bwino.

Kodi inuyo mumamva bwanji mukawerenga kapena kumva nkhani ngati zimenezi? Bambo wina wa ku Hong Kong, dzina lake Hoi, ananena kuti: “Nkhani ngati zimenezi zimandimvetsa chisoni komanso zimandipsetsa mtima. Ndili ndi ana awiri ndipo ndimada nkhawa ndi zakudya zimene ana anga amadya.”

Chaka chilichonse m’mayiko osauka, anthu ambiri makamaka ana, amamwalira chifukwa chodya zakudya kapena kumwa madzi osasamalidwa bwino. Mayi wina wa ku Nigeria, dzina lake Bola, anati: “Zakudya zapamsika zimakhala ntchentche zokhazokha, zimakhala ndi fumbi komanso zimanyowa ndi mvula. Ndikamva nkhani za anthu amene adwala chifukwa chodya zakudya zosasamalidwa bwino, ndimachita mantha ndipo sindimafuna kuti zimenezi zichitikire anthu a m’banja mwanga.”

Dziwani kuti n’zotheka kuteteza anthu a m’banja mwanu kuti asadye zakudya zimene zingawadwalitse. Mwachitsanzo, bungwe lina la ku Canada loona za kasamalidwe ka zakudya linanena kuti: “Nthawi zambiri sizichedwa kudziwika ngati golosale inayake ikugulitsa zakudya zimene zingadwalitse anthu. Koma zimenezi zikhozanso kuchitika m’nyumba mwathu ngati sitinasamale bwino zakudya zathu. Mmene timasamalilira zakudya zathu zingachititse kuti tidwale kapena tisadwale nazo.”

Kodi mungatani kuti muteteze anthu a m’banja mwanu kuti asadwale ndi zakudya? Tiyeni tione njira zinayi zimene zingathandize kuti zakudya zanu zizikhala zosamalidwa bwino.

[Bokosi patsamba 3]

NDANI ANGADWALE MOSAVUTA?

Anthu otsatirawa ndi amene angadwale mosavuta chifukwa chodya zakudya zosasamalidwa bwino:

● Ana omwe sanakwanitse zaka zisanu

● Amayi oyembekezera

● Anthu opitirira zaka 70

● Anthu amene chitetezo chawo cha m’thupi ndi chochepa

Ngati inuyo kapena munthu wina amene mukukhala naye ali m’gulu lililonse la anthu amene tatchula pamwambawa, muyenera kusamala ndi zakudya zanu.

[Mawu a Chithunzi]

Zachokera ku bungwe la New South Wales Food Authority, Australia.