Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsopano Ndili Ndi Mtendere Wamumtima

Tsopano Ndili Ndi Mtendere Wamumtima

 Tsopano Ndili Ndi Mtendere Wamumtima

Yosimbidwa ndi Egidio Nahakbria

Poyamba ndinkadziona kuti ndine munthu wosafunika ndiponso kuti anthu sandikonda. Koma panopo ndimaona kuti ndimakondedwa kwambiri komanso ndili ndi mtendere wamumtima. Kodi chinachitika n’chiyani kuti ndiyambe kumva chonchi? Taimani ndifotokoze.

NDINABADWA m’chaka cha 1976, kudera lina la mapiri ku East Timor. Pa nthawiyi dzikoli linkalamuliridwa ndi dziko la Indonesia. M’banja mwathu tinalipo ana 10 ndipo ineyo ndinali wachi 8. Banja lathu linali losauka kwambiri moti ndinabadwira m’kanyumba ka udzu komanso kozira. Chifukwa chakuti makolo anga sankatha kusamalira ana tonsefe, anandipititsa kwa msuweni wathu kuti ndizikakhala naye ndipo m’chimwene wanga amene ndinabadwa naye mapasa anatsala ndi makolo angawo.

Mu December 1975, dziko la Indonesia linalanda dziko la East Timor. Zimenezi zinachititsa kuti mayiko awiriwa akhale pa nkhondo yomwe inatha zaka zoposa 20. Choncho, ndimati ndikakumbukira ndili mwana, chomwe chimabwera m’maganizo mwanga choyamba ndi nkhondo komanso mavuto. Ndimakumbukira kuti nthawi ina, m’mudzi mwathu munabwera asilikali n’kuyamba kuombera ndi kuba zinthu. Anthu tonse a m’mudzimo tinathawa ndipo ine ndi msuweni wanga uja tinathawira kuphiri komwe tinakapezanso anthu ena ambirimbiri a ku East Timor atabisala.

Koma kenako, asilikali aja anadziwa kumene tinkabisala ndipo anayamba kutiponyera mabomba. Ndimamva chisoni kwambiri ndikakumbukira nthawi imeneyo, kuona anthu akuzunzidwa, kuphedwa komanso zinthu zambiri zikuwonongedwa. Tinabwerera kumudzi kwathu, koma ndinkakhala mwamantha chifukwa anthu ambiri a m’mudzimo anali atasowa kapena kuphedwa ndipo ndinkaganiza kuti zimenezi zingandichitikirenso.

Ndili ndi zaka 10, msuweni wanga uja anadwala kenako anamwalira. Chifukwa cha zimenezi, ndinayamba kukhala ndi agogo anga aakazi. Amuna awo anali atamwalira ndipo chifukwa chakuti ankakumana ndi mavuto aakulu pa moyo wawo, ankangondiona ngati chimtolo cholemetsa. Agogowo anali ankhanza ndipo ankandigwiritsa ntchito ngati kapolo. Ndimakumbukira kuti tsiku lina ndinadwala kwambiri moti sindikanathanso kugwira ntchito. Koma agogowo anakwiya kwambiri ndi zimenezi moti anandimenya kwambiri n’kungondisiya ndili thapsa. Mwamwayi, msuweni wanga wina ananditenga kuti ndizikakhala naye.

Ndinayamba sukulu ndili ndi zaka 12. Pasanapite nthawi, mkazi wa msuweni wanga anayamba kudwala ndipo zimenezi zinachititsa kuti msuweni wangayo azikhala wokhumudwa nthawi zonse. Pofuna kuti ndisamulemetse, ndinathawa pa nyumba n’kumakakhala ndi gulu lina la asilikali a ku Indonesia, omwe ankakhala kunkhalango. Ndinkawachapira zovala, kuwaphikira komanso kuyeretsa malo amene ankakhalawo. Asilikaliwo ankandikonda ndipo zimenezi zinandichititsa kudziona kuti ndine munthu  wofunika. Koma patapita miyezi ingapo, abale anga anadziwa kumene ndinkakhala ndipo anakakamiza asilikaliwo kuti akanditule kumudzi kwathu.

Ndinayamba Kumenyera Ufulu wa Dziko Lathu

Nditamaliza sukulu ya sekondale, ndinayamba kuphunzira pa yunivesite ina mumzinda wa Dili, womwe ndi likulu la dziko la East Timor. Ku yunivesiteko ndinakumana ndi achinyamata ambiri amene anakula mofanana ndi mmene ndinakulira. Tinagwirizana kuti tizichita za ndale pofuna kumenyera ufulu wa dziko lathu komanso kuti zinthu zisinthe. Gulu lathu linkachita zionetsero zomwe nthawi zambiri zinkakhala zachiwawa. Chifukwa cha zimenezi, anzanga ambiri anavulazidwa ndipo ena anaphedwa.

Pamene dziko la East Timor limalandira ufulu wodzilamulira mu 2002, n’kuti zinthu zambiri zitawonongedwa, anthu masauzande ambiri ataphedwa ndipo enanso ambiri atathawira m’madera ena. Nkhondoyi itatha ndinkayembekezera kuti zinthu zisintha koma zimenezi sizinachitike chifukwa ulova komanso mavuto a zandale anali akupitirirabe.

Zinthu Zinasintha pa Moyo Wanga

Nthawi imeneyo ndinkakhala ndi achibale anga ena, ndipo mmodzi wa iwo anali Andre, yemwe ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ineyo ndinali Mkatolika wodzipereka choncho sindinkasangalala kuona mbale wanga akuphunzira za chipembedzo china. Komabe, ndinkafunitsitsa kudziwa zimene Baibulo limanena ndipo nthawi zina ndinkawerenga Baibulo la Andre. Zimene ndinkawerengazo zinachititsa kuti ndikhale ndi chidwi kwambiri ndi Baibulo.

M’chaka cha 2004, Andre anandipatsa kapepala kondiitanira kumwambo wokumbukira imfa ya Yesu ndipo ndinalola. Chifukwa chakuti sindinawone bwino nthawi yomwe inali pakapepalako, ndinafika mofulumira kwambiri, kutatsala maola awiri kuti mwambowu uyambe. Kenako anthu anayamba kufika ndipo ankandipatsa moni wapadzanja mwansangala kwambiri, moti ndinkamva kuti ndalandilidwa. Ndinachita chidwi kwambiri ndi zimenezi. Pamene nkhani ya pa mwambowo inkakambidwa, ndinkalemba mavesi onse amene wokamba nkhaniyo anawatchula. Nditabwerera kunyumba, ndinawerenganso mavesiwo m’Baibulo langa lachikatolika ndipo ndinapeza kuti zimene wokamba nkhani uja ankanena zinali zoona.

Mlungu wotsatira, ndinapita ku mwambo wa Misa ku tchalitchi kwathu. Chifukwa choti enafe tinafika mochedwa, wansembe anakwiya kwambiri moti anatola ndondo n’kuyamba kutithamangitsa kuti tituluke m’tchalitchimo. Wansembeyo anachititsa mwambo wonsewo ife tili panja, ndipo pomalizira anauza anthu amene anali m’tchalitchimo kuti: “Mtendere wa Ambuye ukhale nanu.” Koma mayi wina wolimba mtima anafunsa wansembeyo kuti: “Tikhala bwanji ndi mtendere pomwe inuyo mwathamangitsa anthu ena m’tchalitchi muno?” Wansembeyo anangonamizira ngati kuti sanamve zimene mayiyo ananena. Kuyambira pompo sindinapitenso kutchalitchiko.

Kenako ndinayamba kuphunzira Baibulo komanso kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova limodzi ndi Andre. Achibale athu anakhumudwa kwambiri ndi zimenezi moti anayamba kuchita zinthu zoti tisiye kuphunzira Baibulo. Agogo aakazi a Andre anatiopseza kuti: “Mukapitiriza kuphunzira za chipembedzo chimenechi, ndikuphani ndithu.” Komabe zimene agogowa ananena sizinatifooketse ndipo tinapitirizabe kuphunzira Baibulo.

Khalidwe Langa Linasintha

Kuphunzira Baibulo kunandithandiza kudziwa kuti ndinafunika kusintha khalidwe langa. Mwachitsanzo, ndinali munthu wovuta komanso sindinkakhulupirira aliyense. Komabe, a Mboni ankandikonda kuchokera pansi pa mtima. Nthawi ina ndinadwala ndipo azibale anga sanabwere kudzandiona. Koma a Mboni ankabwera kudzandiona komanso kundithandiza zina ndi zina. Iwo sankandikonda ndi “mawu okha kapena ndi pakamwa pokha,” koma ankandisonyeza ‘chikondi chenicheni m’zochita zawo.’—1 Yohane 3:18.

Ngakhale kuti ndinali munthu wovuta komanso ndinkaoneka woopsa, a Mboni za Yehova ankandichitira zinthu mwachifundo komanso ‘ankandikonda monga mbale.’ (1 Petulo 3:8) Aka kanali koyamba pa moyo wanga kumva kuti ndikukondedwa. Khalidwe langa linayamba kusintha moti ndinayamba kukonda Mulungu komanso anthu anzanga. Kenako m’mwezi wa December 2004, ndinadzipereka kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa. Pasanapite nthawi, Andre nayenso anabatizidwa.

Ndinapeza Madalitso

Nditangobatizidwa, ndinkafunitsitsa kuthandiza ena kuti nawonso adziwe chikondi chenicheni komanso chilungamo. Choncho ndinayamba utumiki wa nthawi zonse, womwe Mboni za Yehova zimautchula kuti upainiya. Kuuza anthu uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo kunali kosangalatsa kwambiri kuposa kuchita ziwonetsera kapena zachiwawa. Ndinasangala kuti tsopano ndinkagwira ntchito yothandiza anthu.

Mu 2006, kusagwirizana pa nkhani za ndale kunayambikanso ku East Timor. Magulu osiyanasiyana anayamba kumenyana chifukwa chokhumudwa kuti zimene ankayembekezera sizikuchitika. Asilikali  anazungulira mzinda wa Dili ndipo anthu ambiri a m’chigawo cha kum’mawa kwa dziko la East Timor anathawira m’madera ena. Ine pamodzi ndi a Mboni ena tinathawira m’tawuni ya Baucau, yomwe ili pamtunda wa makilomita pafupifupi 120, kuchokera ku Dili. Moyo kumeneko unali wovuta komabe tinadalitsidwa chifukwa tinapanga mpingo watsopano, womwe unali mpingo woyamba kupangidwa kunja kwa mzinda wa Dili.

Patatha zaka zitatu, mu 2009, anandiitana kuti ndikachite nawo sukulu ya atumiki a nthawi zonse yomwe inachitikira mumzinda wa Jakarta, ku Indonesia. A Mboni za Yehova a ku Jakarta ankandikonda kwambiri komanso ankandiitanira m’nyumba zawo. Chikondi chawo chochokera pansi pamtima chinandikhudza kwambiri. Zimene ankandichitirazi zinandithandiza kuona kuti ndili ‘m’gulu la abale’ a padziko lonse, omwe amakondana kwambiri ngati banja limodzi.—1 Petulo 2:17.

Tsopano Ndili Ndi Mtendere

Nditamaliza sukuluyi, ndinabwerera ku Baucau, komwe ndikukhalabe mpaka pano. Ndimasangalala kuthandiza anthu mwauzimu ngati mmene enanso anandithandizira. Mwachitsanzo, ineyo ndi abale ena timaphunzitsa Baibulo anthu pafupifupi 20 m’mudzi wina wakutali, womwe uli kunja kwa mzinda wa Baucau. Ena mwa anthuwa ndi achikulire ndipo satha kuwerenga ndi kulemba. Anthu onsewa amapezeka pa misonkhano mlungu uliwonse moti atatu anabatizidwa.

Zaka zingapo zapitazo, ndinakumana ndi mtsikana wina dzina lake Felizarda. Iye anali wochezeka komanso ankachita zinthu mwachifundo kwambiri. Felizarda anaphunzira Baibulo ndipo anapita patsogolo mofulumira n’kubatizidwa. Kenako tinakwatirana mu 2011. Ndine wosangalalanso kuti mbale wanga Andre akutumikira ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko la East Timor. Achibale anga ambiri, kuphatikizapo agogo ake a Andre, amene ankati adzatipha aja, amalemekeza kwambiri chikhulupiriro changa.

Poyamba, ndinali munthu wosasangalala. Ndinkaona kuti anthu sandikonda komanso sindinkakonda anthu. Koma panopa ndimathokoza Yehova chifukwa anthu amandikonda, ndimakonda anthu komanso ndili ndi mtendere wamumtima.

[Chithunzi patsamba 19]

Pa nthawi imene Egidio ankamenyera ufulu wa dziko lake

[Chithunzi patsamba 21]

Egidio, mkazi wake Felizarda limodzi ndi anthu ena a mu mpingo wa Baucau, ku East Timor