Danieli 5:1-31

5  Ndiyeno mfumu Belisazara+ anakonzera nduna zake 1,000 phwando lalikulu, ndipo iyeyo anali kumwa vinyo+ atakhala kutsogolo kwawo.  Belisazara ataledzera ndi vinyoyo+ anaitanitsa ziwiya zagolide ndi zasiliva+ zimene Nebukadinezara bambo ake anatenga m’kachisi ku Yerusalemu. Anaitanitsa zimenezi kuti mfumuyo, nduna zake, adzakazi* ake ndi akazi ake ena apambali amweremo.+  Pa nthawi imeneyo anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga m’kachisi, m’nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kenako mfumuyo, nduna zake, adzakazi ake ndi akazi ake ena apambali anayamba kumwera m’ziwiyazo.  Pakumwa vinyoyo, iwo anali kutamanda milungu yagolide, yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala.+  Pamene anali kuchita zimenezi, zala za munthu zinaonekera ndipo zinayamba kulemba pafupi ndi choikapo nyale, papulasitala wa pakhoma* la nyumba ya mfumu,+ ndipo mfumuyo inaona dzanja limene linali kulembalo.  Pa nthawi imeneyo nkhope ya mfumuyo inasintha ndipo inachita mantha.+ Miyendo yake inafooka+ ndipo mawondo ake anayamba kunjenjemera.+  Ndiyeno mfumuyo inafuula kuti aibweretsere olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi okhulupirira nyenyezi.+ Mfumuyo inauza amuna anzeru a m’Babulo amenewa kuti: “Aliyense amene angawerenge mawuwa ndi kundiuza kumasulira kwake, ndimuveka zovala zofiirira*+ ndi mkanda wagolide m’khosi, ndipo ndimuika kukhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+  Pa nthawi imeneyo amuna onse anzeru anabwera kwa mfumu koma sanathe kuwerenga mawu olembedwawo kapena kuiuza mfumu kumasulira kwake.+  Chotero Mfumu Belisazara inachita mantha kwambiri ndipo nkhope yake inasintha. Nduna zakenso zinathedwa nzeru.+ 10  Tsopano popeza mfumukazi inamva mawu a mfumu ndi a nduna zake, inalowa m’chipinda chimene anali kuchitira phwandolo. Mfumukaziyo inati: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale.+ Musachite mantha komanso nkhope yanu isasinthe. 11  Mu ufumu wanu muli munthu amene ali ndi mzimu wa milungu yoyera.+ M’masiku a bambo anu, anthu anazindikira kuti munthuyu ndi wodziwa zinthu kwambiri, wozindikira ndiponso ali ndi nzeru zofanana ndi nzeru za milungu. Chotero bambo anu, Mfumu Nebukadinezara, anamuika kukhala mkulu+ wa ansembe ochita zamatsenga, anthu okhulupirira mizimu, Akasidi ndi anthu okhulupirira nyenyezi. Ndithudi mfumu, bambo anu anamupatsa udindo umenewu. 12  Anachita zimenezi chifukwa munthuyu anali ndi luso lodabwitsa, anali wodziwa zinthu ndi wozindikira pa nkhani yomasulira maloto,+ kumasulira mikuluwiko ndi kumasula mfundo. Zinthu zonsezi zinapezeka mwa munthu ameneyu+ Danieli, amene mfumu inamupatsa dzina lakuti Belitesazara.+ Tsopano itanani Danieli kuti adzakuuzeni kumasulira kwa zolembedwazi.” 13  Choncho anabweretsa Danieli kwa mfumu, ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi iwe ndiwe Danieli, mmodzi wa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda+ ndi bambo anga mfumu?+ 14  Ndamva kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu+ ndiponso kuti ndiwe wodziwa zinthu kwambiri, wozindikira ndi wanzeru+ zodabwitsa. 15  Tsopano ineyo anandibweretsera amuna anzeru ndi anthu okhulupirira mizimu kuti awerenge zolembedwazi ndi kundiuza kumasulira kwake, koma iwo alephera kumasulira mawuwa.+ 16  Ndamvanso kuti iweyo umatha kumasulira zinthu+ ndi kumasula mfundo. Tsopano ngati ungathe kuwerenga mawuwa ndi kundiuza kumasulira kwake, ndikuveka zovala zofiirira ndi mkanda wagolide m’khosi, ndipo ndikuika kukhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+ 17  Pamenepo Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Sungani mphatso zanuzo ndipo mphoto zanuzo mupatse ena.+ Komabe, ndikuwerengerani zolembedwazi ndipo ndikuuzani kumasulira kwake.+ 18  Inu mfumu, Mulungu Wam’mwambamwamba+ anapatsa bambo anu+ Nebukadinezara ufumu, ukulu, ulemu ndi ulemerero.+ 19  Chifukwa chakuti Mulungu anamupatsa ukulu umenewu, anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana anali kunjenjemera ndi kuchita mantha pamaso pake.+ Iye akafuna kupha munthu aliyense anali kumupha, akafuna kuwononga munthu aliyense anali kumuwononga, akafuna kukweza munthu aliyense anali kumukweza ndipo akafuna kutsitsa munthu aliyense anali kumutsitsa.+ 20  Koma pamene mtima wake unayamba kudzitukumula ndiponso pamene anaumitsa mtima wake ndi kuchita zinthu modzikweza,+ anatsitsidwa pampando wake wachifumu ndipo ulemerero wake unachotsedwa.+ 21  Iye anathamangitsidwa pakati pa anthu ndipo mtima wake unasinthidwa n’kukhala ngati wa nyama. Anayamba kukhala limodzi ndi abulu akutchire+ ndipo anali kudya udzu ngati ng’ombe. Thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba,+ kufikira pamene anadziwa kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti akafuna kuika munthu aliyense kuti akhale wolamulira, amamuika.+ 22  “Koma inuyo a Belisazara,+ amene ndinu mwana wake, simunadzichepetse mumtima mwanu+ ngakhale kuti munali kudziwa zonsezi.+ 23  Mwadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba+ ndipo anthu akubweretserani ziwiya za m’nyumba yake.+ Inuyo, nduna zanu, adzakazi anu ndi akazi anu ena apambali mwamwera vinyo m’ziwiya zimenezi. Mwatamanda milungu wamba yasiliva, yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala+ imene siona, kumva kapena kudziwa kalikonse.+ Koma Mulungu amene amasunga mpweya wanu+ ndi njira zanu zonse m’dzanja lake,+ simunamulemekeze.+ 24  Chotero Mulungu watumiza dzanja ndipo wachititsa kuti mawu amenewa alembedwe.+ 25  Mawu amene alembedwa ndi awa: MENE, MENE, TEKELI, ndi PARASINI. 26  “Kumasulira kwa mawuwa ndi uku: MENE, Mulungu wawerenga masiku a ufumu wanu ndipo waumaliza.+ 27  “TEKELI, mwayezedwa pasikelo ndipo mwapezeka kuti mukuperewera.+ 28  “PERESI,* ufumu wanu wagawanika ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+ 29  Pamenepo Belisazara analamula kuti Danieli amuveke zovala zofiirira ndi mkanda wagolide m’khosi mwake, ndipo analengeza kuti Danieli akhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo.+ 30  Usiku womwewo, Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa,+ 31  ndipo Dariyo+ Mmedi anapatsidwa ufumuwo ali ndi zaka pafupifupi 62.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”
Onani mawu a m’munsi pa Da 2:2.
Anthu olemera, olemekezeka ndi mafumu ndi amene ankavala zovala zamtundu umenewu.
Mawu achiaramu akuti “PERESI” ndi otchulira chinthu chimodzi. Zikakhala zinthu zambiri mawu ake ndi “PARASINI” amene ali muvesi 25.