Danieli 11:1-45

11  “M’chaka choyamba cha Dariyo Mmedi,+ ine ndinakhala womulimbikitsa ndipo ndinali ngati mpanda wolimba kwambiri kwa iye.  Tsopano ndikufotokozera choonadi:+ “Mu ufumu wa Perisiya+ mudzauka mafumu atatu, ndipo mfumu yachinayi+ idzasonkhanitsa chuma chambiri kuposa ena onsewa.+ Ndipo ikadzangokhala yamphamvu chifukwa cha chuma chakecho idzaukira ufumu wa Girisi ndi mphamvu zake zonse.+  “Ndiyeno mfumu yamphamvu idzauka ndi kulamulira ndi mphamvu zazikulu,+ ndipo idzachitadi zofuna zake.+  Mfumuyo ikadzauka,+ ufumu wake udzasweka ndipo udzagawanika ndi kutengedwa ndi mphepo zinayi+ zakumwamba,+ koma sudzapita kwa mbadwa zake+ ndipo maufumuwo sadzafanana ndi ufumu wake. Zimenezi zidzachitika chifukwa ufumu wake udzazulidwa ndi kuperekedwa kwa ena.  “Mfumu ya kum’mwera, imene ndi mmodzi mwa akalonga ake, idzakhala yamphamvu. Koma iye* adzamugonjetsa ndipo adzalamuliradi ndi mphamvu zazikulu kuposa za ameneyo.*  “Ndiyeno patatha zaka zingapo iwo adzagwirizana, ndipo mwana wamkazi wa mfumu ya kum’mwera adzapita kwa mfumu ya kumpoto kuti apange mgwirizano. Koma mwana wamkaziyo sadzakhala ndi mphamvu m’dzanja lake,+ ndipo mfumuyo sidzalimba, ngakhalenso dzanja lake silidzalimba. Mwana wamkaziyo adzaperekedwa m’manja mwa anthu ena, pamodzi ndi amene anamubweretsa, amene anamubereka ndiponso amene anamuchititsa kukhala wamphamvu masiku amenewo.  Kenako, mphukira yochokera kumizu+ yake idzauka ndi kulowa m’malo mwake* ndipo idzafika kwa gulu lankhondo ndi kuukira mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri wa mfumu ya kumpoto, moti mphukirayo idzawathira nkhondo ndi kupambana.  Pamenepo, mphukirayo idzapita ku Iguputo ndi milungu yawo,+ zifaniziro zawo zopangidwa ndi chitsulo chosungunula, zinthu zawo zosiririka zasiliva ndi zagolide, pamodzi ndi anthu amene idzawagwire. Kenako idzaima patali ndi mfumu ya kumpoto kwa zaka zingapo.  “Iye* adzalowa mu ufumu wa mfumu ya kum’mwera, kenako adzabwerera kudziko lakwawo. 10  “Ana ake adzadzikonzekeretsa ndi kusonkhanitsa pamodzi gulu lankhondo lalikulu. Ndiyeno mmodzi wa iwo adzafika mwamphamvu ndi kudutsa ngati madzi osefukira m’dzikolo. Koma adzabwerera, ndipo adzachita nkhondo mpaka kumzinda wake wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. 11  “Ndiyeno mfumu ya kum’mwera idzawawidwa mtima ndipo idzapita kukamenyana ndi mfumu ya kumpoto. Mfumu ya kumpoto imeneyi idzakhala ndi khamu lalikulu, koma khamulo lidzaperekedwa m’manja mwa mfumu inayo.+ 12  Khamulo lidzatengedwa, ndipo iye* adzadzitukumula mumtima mwake+ moti adzapha anthu masauzande makumimakumi. Adzakhala wamphamvu koma sadzagwiritsa ntchito mphamvu zakezo. 13  “Pamenepo mfumu ya kumpoto idzabwerera kwawo ndi kusonkhanitsa khamu lalikulu kwambiri kuposa loyamba lija, ndipo patapita nthawi, pambuyo pa zaka zingapo, idzabwera ili ndi gulu lankhondo lalikulu+ lokhala ndi katundu wambiri.+ 14  Pa nthawi imeneyo padzakhala anthu ambiri oukira mfumu ya kum’mwera. “Ndiyeno anthu achiwawa pakati pa anthu a mtundu wako adzatengeka ndi zochitika zimenezi ndipo adzayesa kukwaniritsa masomphenya,+ koma adzapunthwa.+ 15  “Kenako mfumu ya kumpoto idzabwera ndipo idzamanga chiunda chomenyerapo nkhondo*+ ndi kulanda mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Zida zankhondo* zakum’mwera sizidzatha kulimbana nayo. Asilikali ake apamwamba kwambiri nawonso sadzatha kulimbana nayo. Iwo sadzakhala ndi mphamvu zoti apitirizebe kulimbana nayo. 16  Mfumu yobwera kudzamenyana nayo* idzachita zofuna zake, ndipo palibe adzaime pamaso pake. Mfumuyo idzaimirira m’Dziko Lokongola,+ ndipo idzapha anthu ambiri.+ 17  Iyo idzafika motsimikiza mtima+ kwambiri pamodzi ndi gulu lankhondo lamphamvu la ufumu wake. Adzachita nayo mgwirizano+ ndipo idzakwaniritsa zolinga zake.+ Iyo idzaloledwa kuti iwononge mwana wamkaziyo. Mwana wamkaziyo sadzapirira ndipo sadzapitiriza kukhala wokhulupirika kwa iyo.+ 18  Chotero iyo idzatembenukira kumadera a m’mbali mwa nyanja+ ndipo idzalanda madera ambiri. Pamenepo mtsogoleri wa asilikali adzathetsa kunyoza kwake, moti iye sadzanyozedwanso. Mtsogoleriyu adzachititsa kuti kunyozako kubwerere kwa iyo. 19  Iyo* idzabwerera kumizinda yakwawo yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Kumeneko idzapunthwa ndi kugwa ndipo sidzapezekanso.+ 20  “Pamalo pake padzauka wina+ amene adzachititsa wokhometsa msonkho*+ kuyendayenda mu ufumu waulemererowo, ndipo m’masiku ochepa adzathyoka, koma osati ndi dzanja la munthu kapena pa nkhondo. 21  “Ndiyeno pamalo pa ameneyo padzauka wina wonyozeka,+ ndipo sadzamupatsa ulemerero waufumu. Iye adzabwera pa nthawi imene zinthu zikuyenda bwino+ ndipo adzatenga ufumuwo mwachinyengo.+ 22  Iye adzagonjetsa magulu ankhondo+ okhala ngati madzi osefukira, ndipo magulu ankhondowo adzawonongedwa.+ Mtsogoleri+ wa pangano+ nayenso+ adzawonongedwa. 23  Chifukwa choti iwo adzagwirizana naye, iye adzachita zinthu mwachinyengo ndi kuwaukira pogwiritsa ntchito mtundu waung’ono.+ 24  Pa nthawi imene zinthu zikuyenda bwino,+ iye adzalowa m’dera labwino kwambiri la chigawo ndipo adzachita zinthu zimene ngakhale makolo ake ndi makolo a makolo ake sanachitepo. Adzamwaza pakati pa anthu zinthu zowonongedwa, zofunkhidwa, ndi katundu wosiyanasiyana. Adzakonzera ziwembu+ malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri, koma kwa kanthawi kochepa. 25  “Iye adzasonkhanitsa mphamvu zake ndi kulimbitsa mtima wake kuti aukire mfumu ya kum’mwera ali ndi gulu lankhondo lalikulu. Mfumu ya kum’mwera nayonso idzakonzekera nkhondo mwa kusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu. Koma iye* sadzalimba chifukwa adzamukonzera chiwembu. 26  Anthu amene amadya zakudya zake zokoma ndi amene adzachititsa kuti iye athyoke. “Pamenepo gulu lake lankhondo lidzagonja ngati kuti latengedwa ndi madzi osefukira, ndipo anthu ambiri adzaphedwa. 27  “Mafumu awiri amenewa adzakhala ndi mtima wofuna kuchita zoipa, ndipo azidzalankhula bodza+ patebulo limodzi.+ Koma zolinga zawo zonse sizidzatheka+ chifukwa nthawi yamapeto sinakwane.+ 28  “Choncho iye* adzabwerera kudziko lakwawo ali ndi katundu wochuluka ndipo adzakhala ndi mtima wofuna kuukira pangano lopatulika+ moti adzakwaniritsa+ zolinga zake n’kubwerera kwawo. 29  “Pa nthawi yake+ adzabwerera kwawo ndipo adzaukira dziko lakum’mwera.+ Koma sizidzakhala ngati mmene zinalili poyamba. 30  Choncho zombo za ku Kitimu+ zidzabwera ndi kumuukira ndipo adzakhala wachisoni. “Iye adzabwerera ndi kulankhula mawu amphamvu odzudzula+ pangano lopatulika+ ndipo adzachita zofuna zake. Pamenepo iye adzabwerera ndi kuganizira anthu osiya pangano lopatulika. 31  Ndiyeno padzauka magulu ankhondo* otuluka mwa iye. Maguluwo adzaipitsa malo opatulika+ amene ndi malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri, ndipo adzachotsa nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse.+ “Iwo adzaika pamalowo chinthu chonyansa+ chobweretsa chiwonongeko.+ 32  “Anthu amene akuchita zinthu zoipa motsutsana ndi pangano+ adzawatsogolera ku mpatuko+ pogwiritsa ntchito mawu achinyengo.+ Koma anthu amene amadziwa Mulungu wawo+ adzapambana+ ndi kukwaniritsa zolinga zawo. 33  Anthu ozindikira+ pakati pa anthuwo adzathandiza anthu ambiri kumvetsa zinthu.+ Iwo adzapunthwa kwa kanthawi ndi lupanga ndi malawi a moto. Adzapunthwanso mwa kutengedwa ukapolo ndi kuwonongedwa kwa zinthu zawo.+ 34  Koma akadzapunthwa adzathandizidwa ndi thandizo lochepa,+ ndipo ambiri adzadziphatika kwa iwo mwachinyengo.+ 35  Ena mwa anthu ozindikirawo adzapunthwa.+ Zidzatero kuti ntchito yoyenga ichitike* ndiponso kuti anthu ozindikira atsukidwe ndi kuyeretsedwa+ kufikira nthawi ya mapeto,+ pakuti nthawi yake idzafika.+ 36  “Mfumuyo idzachita zofuna zake ndipo idzadzikweza ndi kudzikuza kuposa mulungu aliyense.+ Iyo idzalankhula zinthu zodabwitsa zotsutsana ndi Mulungu wa milungu.+ Idzapambana kufikira chidzudzulo champhamvu chitaperekedwa chonse,+ chifukwa chinthu chimene chakonzedwa chiyenera kuchitika. 37  Iyo sidzaganizira Mulungu wa makolo ake. Sidzaganiziranso zofuna za akazi kapena za mulungu wina aliyense koma idzadzikweza pamwamba pa aliyense.+ 38  Ndipo idzapereka ulemu kwa mulungu wa m’malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Idzapereka ulemu kwa mulungu amene makolo ake sanamudziwe ndipo idzapatsa mulunguyo golide, siliva, miyala yamtengo wapatali ndi zinthu zosiririka. 39  Mfumuyo idzakwaniritsa zolinga zake polimbana ndi malo otetezeka kwambiri okhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo idzachita zimenezi pamodzi ndi mulungu wachilendo. Aliyense woivomereza idzamupatsa ulemerero waukulu ndipo idzachititsa anthu oterowo kulamulira pakati pa anthu ambiri. Iyo idzagawa malo ndi kuwagulitsa. 40  “Ndiyeno m’nthawi ya mapeto mfumu ya kum’mwera+ idzayamba kukankhana nayo ndipo mfumu ya kumpoto idzabwera mwamphamvu kudzamenyana nayo. Idzabwera ndi magaleta, asilikali okwera pamahatchi* ndi zombo zambiri. Mfumuyo idzalowa m’mayiko ndi kudutsamo ngati madzi osefukira. 41  Iyo idzalowanso+ m’Dziko Lokongola+ ndipo idzachititsa mayiko ambiri kupunthwa,+ koma Edomu, Mowabu+ ndi mbali yaikulu ya ana a Amoni adzapulumuka m’manja mwake. 42  Iyo idzapitirizabe kutambasulira dzanja lake pa mayiko ndipo dziko la Iguputo+ silidzapulumuka. 43  Idzalamulira chuma chobisika cha golide ndi siliva. Ndipo idzalamuliranso zinthu zonse zosiririka za dziko la Iguputo. Anthu a ku Libiya ndi a ku Itiyopiya adzakhala akumutsatira. 44  “Koma kotulukira dzuwa+ ndi kumpoto kudzachokera mauthenga amene adzaisokoneza.+ Pamenepo iyo idzapita ndi ukali waukulu kuti ikafafanize ndi kuwononga ambiri.+ 45  Ndipo idzamanga mahema okhala ngati nyumba yachifumu pakati pa nyanja yaikulu ndi phiri lopatulika la Dziko Lokongola.+ Ndiyeno iyo idzafika kumapeto a moyo wake+ ndipo sipadzapezeka woithandiza.+

Mawu a M'munsi

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kum’mwera.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kum’mwera.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kum’mwera.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “magulu ankhondo.”
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kum’mwera.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Mawu amene tawamasulira kuti “wokhometsa msonkho” akhozanso kutanthauza munthu amene amalemba anthu ntchito yausilikali.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Mawu ake enieni, “zida zankhondo.”
Mawu ake enieni, “kuti ntchito yoyenga ichitike chifukwa cha iwo.”
Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”