Danieli 7:1-28

7  M’chaka choyamba cha ulamuliro wa Belisazara+ mfumu ya Babulo, Danieli analota maloto ndipo anaona masomphenya atagona pabedi lake.+ Pa nthawi imeneyo, analemba zimene analotazo,+ ndipo anafotokoza nkhani yonseyo.  Iye anati: “M’masomphenya ausiku, ndinaona mphepo zinayi+ zakumwamba zikuvundula nyanja yaikulu.+  Zilombo zinayi zikuluzikulu+ zinali kutuluka m’nyanjayo,+ ndipo chilichonse chinali chosiyana ndi chinzake.+  “Chilombo choyamba chinali chooneka ngati mkango+ ndipo chinali ndi mapiko a chiwombankhanga.+ Ndinapitiriza kuchiyang’ana kufikira pamene mapiko ake anathotholedwa. Ndiyeno anachitukula padziko lapansi+ ndipo anachiimiritsa ndi miyendo iwiri ngati munthu. Kenako chinapatsidwa mtima wa munthu.+  “Ndinaonanso chilombo china chachiwiri, chooneka ngati chimbalangondo.+ Chinali chotukuka mbali imodzi+ ndipo m’kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake. Chilombochi chinauzidwa kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri.’+  “Pambuyo pa zimenezi, ndinaona chilombo china chooneka ngati kambuku*+ koma chinali ndi mapiko anayi a mbalame pamsana pake. Chilombochi chinali ndi mitu inayi+ ndipo chinapatsidwa ulamuliro.  “Kenako ndinaonanso m’masomphenya ausiku chilombo chachinayi, choopsa kwambiri ndiponso chochititsa mantha komanso champhamvu kwambiri.+ Chinali ndi mano akuluakulu achitsulo ndipo chinali kudya ndi kuphwanyaphwanya chilichonse chimene chinali nacho pafupi. Zotsala chinali kuzipondaponda ndi mapazi ake. Chinali chosiyana ndi zilombo zina zonse zimene ndinaona poyamba ndipo chinali ndi nyanga 10.+  Pamene ndinali kuyang’anitsitsa nyangazo, ndinaona kuti nyanga ina yaing’ono yamera+ pakati pa nyangazo. Nyanga zitatu pa nyangazi zinazulidwa pamalo amene nyanga yaing’onoyo inamera. Nyangayi inali ndi maso ngati a munthu, ndipo inali ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula.+  “Ndiyeno ndinapitiriza kuyang’ana kufikira pamene mipando yachifumu inaikidwa+ ndipo Wamasiku Ambiri+ anakhala pa mpando wake wachifumu. Zovala zake zinali zoyera kwambiri.+ Tsitsi lake linali looneka ngati ubweya wa nkhosa woyera.+ Mpando wake wachifumu unali kuyaka moto walawilawi,+ ndipo mawilo a mpandowo anali kuyaka moto.+ 10  Mtsinje wa moto unali kuyenda kuchokera kwa iye.+ Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira nthawi zonse,+ ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake nthawi zonse.+ Bwalo la milandu+ linakhala pansi, ndipo mabuku anatsegulidwa. 11  “Pa nthawi imeneyo, ndinapitirizabe kuyang’ana chifukwa ndinali kumva mawu odzitukumula amene nyanga ija inali kulankhula.+ Ndinapitirizanso kuyang’ana kufikira pamene chilombocho chinaphedwa ndipo thupi lake linaponyedwa pamoto n’kuwonongedwa.+ 12  Koma zilombo zinazo+ anazilanda ulamuliro, ndipo anazilola kukhalapo kwa kanthawi.+ 13  “Ndiyeno m’masomphenya ausikuwo, ndinaonanso wina wooneka ngati mwana wa munthu+ akubwera m’mitambo.+ Iye analoledwa kufika kwa Wamasiku Ambiri uja,+ ndipo anamubweretsa pafupi kwambiri ndi Iye.+ 14  Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemerero,+ ndi ufumu+ kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+ 15  “Tsopano ineyo Danieli, ndinavutika kwambiri mumtima chifukwa cha zimenezi ndipo ndinachita mantha ndi masomphenya amene ndinaona.+ 16  Ndinayandikira mmodzi mwa amene anali ataimirira kuti ndimufunse tanthauzo la zonsezi.+ Choncho iye anandifotokozera kumasulira kwa nkhani zimenezi, kuti: 17  “‘Popeza zilombo zikuluzikulu zimenezi zilipo zinayi,+ pali mafumu anayi amene adzauka padziko lapansi.+ 18  Koma oyera+ a Wamkulukulu+ adzalandira ufumu ndipo adzatenga ufumuwo+ mpaka kalekale, ku nthawi zosatha.’ 19  “Ndiyeno ndinali ndi chidwi chofuna kudziwa zambiri zokhudza chilombo chachinayi chija, chimene chinali chosiyana ndi zina zonse. Chilombo chimenechi chinali choopsa kwambiri. Mano ake anali achitsulo, zikhadabo zake zinali zamkuwa, ndipo chinali kudya zinthu ndi kuziphwanyaphwanya. Zotsala chinali kuzipondaponda ndi mapazi ake.+ 20  Ndinafunanso kudziwa za nyanga 10 zimene zinali pamutu pake+ ndi nyanga ina+ imene inamera, imene inachititsa kuti nyanga zitatu zigwe.+ Nyanga imeneyi inali ndi maso ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula+ ndipo inali kuoneka yaikulu kuposa zinzake zija. 21  “Ndinapitirizabe kuyang’ana pamene nyangayo inathira nkhondo pa oyera ndipo inali kuwagonjetsa,+ 22  kufikira Wamasiku Ambiri+ anabwera ndipo anapereka chiweruzo chokomera oyera a Wamkulukulu.+ Tsopano nthawi yoti oyerawo atenge ufumuwo inakwana, ndipo anautengadi.+ 23  “Ndiyeno iye anandiuza kuti, ‘Ponena za chilombo chachinayi chimenechi, pali ufumu wachinayi umene udzakhalapo padziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu ena onse. Udzadya dziko lonse lapansi ndipo udzalipondaponda ndi kuliphwanyaphwanya.+ 24  Ponena za nyanga 10 zija, mu ufumuwo mudzatuluka mafumu 10.+ Kenako mudzatulukanso mfumu ina pambuyo pa mafumu amenewa. Mfumuyo idzakhala yosiyana ndi oyambawa+ ndipo idzagonjetsa mafumu atatu.+ 25  Idzalankhula mawu otsutsana ndi Wam’mwambamwamba+ ndipo idzazunza mosalekeza oyera a Wamkulukulu.+ Idzafuna kusintha nthawi+ ndiponso lamulo+ ndipo oyerawo adzaperekedwa m’manja mwake kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi.+ 26  Bwalo la milandulo linakhala pansi,+ ndipo pamapeto pake mfumuyo anailanda ulamuliro kuti aifafanize ndi kuiwonongeratu.+ 27  “‘Ufumu, ulamuliro, ndi ulemerero wa maufumu a padziko lonse lapansi zinaperekedwa kwa oyera a Wamkulukulu.+ Ufumu wawo+ udzakhalapo mpaka kalekale ndipo maulamuliro onse adzawatumikira ndi kuwamvera.’+ 28  “Nkhani imeneyi yathera pamenepa. Tsopano ineyo Danieli, ndinachita mantha kwambiri moti ndinakhala ngati ndakomoka. Koma nkhaniyi ndinaisunga mumtima mwanga.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “nyalugwe.”