Danieli 12:1-13

12  “Pa nthawi imeneyo Mikayeli,+ kalonga wamkulu+ amene waimirira+ kuti athandize anthu a mtundu wako, adzaimirira.+ Ndiyeno padzafika nthawi ya masautso imene sinakhalepo kuyambira pamene mtundu woyambirira wa anthu unakhalapo kufikira nthawi imeneyo.+ Pa nthawi imeneyo aliyense mwa anthu a mtundu wako amene dzina lake lidzakhala litalembedwa m’buku+ adzapulumuka.+  Anthu ambiri amene agona munthaka adzauka.+ Ena adzalandira moyo wosatha+ koma ena adzalandira chitonzo ndipo adzadedwa mpaka kalekale.+  “Anthu ozindikira adzawala ngati kuwala kwa kuthambo.+ Ndipo amene akuthandiza anthu ambiri kukhala olungama+ adzawala ngati nyenyezi mpaka kalekale, inde, kwamuyaya.  “Koma iwe Danieli, sunga mawuwa mwachinsinsi ndipo utseke ndi kumata bukuli+ kufikira nthawi yamapeto.+ Anthu ambiri adzayenda uku ndi uku ndipo adzadziwa zinthu zambiri zoona.”+  Ndiyeno ineyo Danieli nditayang’ana, ndinangoona angelo ena awiri ataimirira.+ Mngelo wina anaimirira m’mbali mwa mtsinje tsidya lino, ndipo wina anaimirira tsidya linalo.+  Kenako mmodzi mwa angelowo anafunsa munthu wovala nsalu uja,+ amene anaimirira pamwamba pa madzi a mumtsinjewo, kuti: “Kodi zidzatenga nthawi yaitali bwanji kuti zinthu zodabwitsazi zikwaniritsidwe zonse?”+  Pamenepo ndinamva mwamuna wovala nsalu uja, amene anaimirira pamwamba pa madzi a mumtsinje akuyankha. Poyankhapo, anakweza m’mwamba dzanja lake lamanja ndi lamanzere ndi kulumbira+ pa Iye amene adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ ndipo anati: “Padzapita nthawi imodzi yoikidwiratu, nthawi ziwiri zoikidwiratu, ndi hafu ya nthawi yoikidwiratu.+ Ndipo akadzangomaliza kuphwanyaphwanya+ mphamvu za anthu oyera, zinthu zonsezi zidzafika pamapeto.”  Tsopano ine ndinamva zimene ananenazo, koma sindinadziwe tanthauzo lake.+ Choncho ndinafunsa kuti: “Inu mbuyanga, kodi zinthu zimenezi zidzatha bwanji?”+  Iye anandiyankha kuti: “Pita Danieli, pakuti mawuwa asungidwa mwachinsinsi ndipo atsekedwa ndi kumatidwa kufikira nthawi yamapeto.+ 10  Anthu ambiri adzadzitsuka,+ adzadziyeretsa+ ndipo adzayengedwa.+ Anthu oipa adzachita zinthu zoipa+ ndipo palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mawu amenewa,+ koma anthu ozindikira adzawamvetsetsa.+ 11  “Kuchokera pa nthawi imene nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse+ zidzachotsedwa,+ ndiponso pamene chinthu chonyansa+ chobweretsa chiwonongeko chidzaikidwa, padzapita masiku 1,290. 12  “Wodala+ ndi munthu amene akuyembekezera mpaka kufika ku mapeto a masiku 1,335. 13  “Ndiyeno iwe pita ku mapeto+ ndipo udzapuma.+ Koma udzauka kuti ulandire gawo lako pa mapeto a masikuwo.”+

Mawu a M'munsi