Danieli 1:1-21

1  M’chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu+ mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu ndipo anazungulira mzindawo.+  Kenako Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda m’manja mwake.+ Anaperekanso kwa iye zina mwa ziwiya+ za m’nyumba ya Mulungu woona moti Nebukadinezara anazitengera kudziko la Sinara,+ kunyumba ya mulungu wake. Ziwiya zimenezi anakaziika m’nyumba ya mulungu wake yosungiramo chuma.+  Ndiyeno mfumu inauza Asipenazi, mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu+ kuti abweretse ena mwa ana a Isiraeli, ana a m’banja lachifumu, ndi ana a anthu olemekezeka,+  amene analibe chilema chilichonse,+ ooneka bwino, ozindikira zinthu, anzeru,+ odziwa zinthu, omvetsa zinthu mwamsanga,+ amenenso akanatha kutumikira m’nyumba ya mfumu.+ Anawabweretsa kuti awaphunzitse kulemba* ndiponso chinenero cha Akasidi.  Kuwonjezera pamenepo, mfumu inalamulanso kuti tsiku lililonse iwo aziwapatsa zakudya zabwino+ za mfumu ndi vinyo wa mfumu. Inalamulanso kuti awasamalire kwa zaka zitatu ndipo zaka zimenezi zikadzatha, akayambe kutumikira mfumu.  Pakati pa anawo panali ana ena a ku Yuda. Mayina awo anali Danieli,+ Hananiya, Misayeli ndi Azariya,+  koma mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu anapatsa anawa mayina ena.+ Danieli anamupatsa dzina lakuti Belitesazara,+ Hananiya anamupatsa dzina lakuti Sadirake, Misayeli anamupatsa dzina lakuti Mesake, ndipo Azariya anamupatsa dzina lakuti Abedinego.+  Koma Danieli anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzidetsa+ ndi zakudya zabwino za mfumu ndi vinyo wake. Choncho iye anapitirizabe kupempha mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu kuti amulole kuti asadzidetse ndi zakudyazo.+  Chotero Mulungu woona anachititsa kuti mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu asonyeze Danieli kukoma mtima kosatha ndi chifundo.+ 10  Komabe mkulu wa nduna za panyumba ya mfumuyo anauza Danieli kuti: “Ine ndikuopa mbuye wanga mfumu, amene walamula kuti mupatsidwe zakudya ndi zakumwa zake.+ Ndiye n’chifukwa chiyani mukufuna kuti aone nkhope zanu zili zachisoni poyerekeza ndi ana ena amsinkhu wanu? Komanso, bwanji mukufuna kuikitsa mutu wanga pangozi kwa mfumu?” 11  Pamenepo Danieli anakalankhula ndi munthu amene anali kuwayang’anira, amene mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu+ uja anamuika kuti aziyang’anira Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya, ndipo anati: 12  “Chonde, yesani atumiki anufe kwa masiku 10. Lolani kuti azitipatsa zakudya zamasamba+ ndi madzi oti tizimwa. 13  Pambuyo pake mudzayerekeze mmene ifeyo tikuonekera ndi mmene ana amene akudya zakudya zabwino za mfumu akuonekera, ndipo mudzachitire atumiki anufe mogwirizana ndi zimene mudzaone.” 14  Pamapeto pake, munthu amene anali kuwayang’anira uja anawamvera pa nkhani imeneyi ndipo anawayesa kwa masiku 10. 15  Masiku 10 amenewo atatha, iwo anali kuoneka bwino kwambiri ndiponso matupi awo ankaoneka athanzi kuposa ana onse amene anali kudya zakudya zabwino za mfumu.+ 16  Choncho, wowayang’anira uja anapitirizabe kuwapatsa zakudya zamasamba+ m’malo mwa zakudya zabwino za mfumu ndi vinyo wake. 17  Tsopano Mulungu anawachititsa ana anayi amenewa kudziwa ndi kuzindikira zinthu zonse zolembedwa ndiponso anawapatsa nzeru.+ Danieli anali womvetsa bwino masomphenya ndi maloto amtundu uliwonse.+ 18  Ndiyeno masiku amene mfumu inanena kuti adzabweretse ana aja pamaso pake anakwana.+ Zitatero mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu uja anabweretsa anawo pamaso pa Nebukadinezara. 19  Pamenepo mfumu inayamba kulankhula nawo ndipo pa ana onsewo, palibe aliyense amene anali ngati Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya.+ Chotero ana amenewa anapitiriza kutumikira mfumu.+ 20  Pa nkhani iliyonse imene mfumu inali kufunsira nzeru kwa iwo kuti imvetse bwino,+ inaona kuti iwo anali anzeru kuwirikiza maulendo 10 kuposa ansembe onse ochita zamatsenga+ ndi anthu onse olankhula ndi mizimu+ amene anali mu ufumu wake. 21  Chotero Danieli anapitiriza kukhala kumeneko mpaka chaka choyamba cha ulamuliro wa mfumu Koresi.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “zolemba.”