Danieli 6:1-28

6  Ndiyeno Dariyo anaona kuti ndi bwino kuti aike masatarapi* 120 oyang’anira zigawo zonse za ufumu wake.+  Anaikanso nduna zapamwamba zitatu zoyang’anira masatarapiwo, ndipo Danieli anali mmodzi wa ndunazo.+ Anaika nduna zimenezi kuti nthawi zonse masatarapiwo+ aziziuza chilichonse chimene chikuchitika, ndi cholinga chakuti zinthu za mfumu zisawonongeke.+  M’kupita kwa nthawi, Danieli anaonetsa kuti anali wodziwa kugwira ntchito bwino+ kuposa nduna zonse zapamwamba ndi masatarapi onse, chifukwa anali ndi luso lodabwitsa+ ndipo mfumu inali kuganiza zomukweza kuti akhale pamwamba pa wina aliyense mu ufumuwo.  Poona zimenezi, nduna zapamwamba ndi masatarapi aja nthawi zonse anali kufunafuna chomunamizira Danieli pa kayendetsedwe kake ka zinthu mu ufumuwo.+ Koma iwo sanapeze chifukwa chilichonse chomunamizira kapena chinthu chilichonse chachinyengo chimene anachita, pakuti iye anali wokhulupirika. Iwo anapeza kuti Danieli sanali kunyalanyaza kanthu kapena kuchita zachinyengo zilizonse.+  Chotero amuna amphamvuwa anati: “Danieliyu sitingamupezere chifukwa chilichonse. Ngati tikufuna kumupezera chifukwa, chikhale chokhudzana ndi lamulo la Mulungu wake.”+  Choncho nduna zapamwamba zimenezi ndi masatarapi aja anapita kwa mfumu ali chigulu.+ Iwo anauza mfumuyo kuti: “Inu mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo mpaka kalekale.+  Nduna zonse zapamwamba za mu ufumu uno, akuluakulu a boma, masatarapi, alangizi a mfumu, ndi abwanamkubwa agwirizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo+ loletsa munthu aliyense kupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense kwa masiku 30, kupatulapo kwa inu nokha mfumu. Aliyense amene samvera lamulo limeneli aponyedwe m’dzenje la mikango.+  Tsopano inu mfumu khazikitsani lamulo ndipo musaine+ kuti lamulolo lisasinthe, mogwirizana ndi malamulo a Amedi ndi Aperisiya,+ amene sasintha.”+  Mogwirizana ndi zimenezi, Mfumu Dariyo inasainira lamulolo.+ 10  Koma Danieli atangodziwa kuti lamulo limeneli lasainidwa, analowa m’nyumba mwake, ndipo mawindo a nyumba yake oyang’ana ku Yerusalemu+ anali otsegula. M’nyumbamo, iye anali kugwada ndi kupemphera+ kwa Mulungu wake ndi kumutamanda+ katatu pa tsiku,+ monga mmene anali kuchitira nthawi zonse lamuloli lisanasainidwe.+ 11  Nthawi yomweyo, amuna amphamvu amenewa analowa m’nyumbamo ali chigulu ndipo anapeza Danieli akuchonderera ndi kupempha Mulungu wake kuti amukomere mtima.+ 12  Kenako anapita kwa mfumu ndi kuifunsa za lamulo limene inakhazikitsa lija, kuti: “Kodi inu mfumu, si paja mwakhazikitsa lamulo lonena kuti kwa masiku 30 munthu aliyense wopezeka akupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense, kupatulapo kwa inu nokha, aponyedwe m’dzenje la mikango?”+ Mfumuyo inayankha kuti: “Nkhani imeneyi ndi yodziwika bwino, mogwirizana ndi malamulo a Amedi ndi Aperisiya, amene sasintha.”+ 13  Nthawi yomweyo iwo anauza mfumuyo kuti: “Danieli,+ mmodzi wa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda,+ sanakumvereni mfumu komanso sanamvere lamulo limene munasainira ndipo akupemphera katatu pa tsiku.”+ 14  Mfumuyo itangomva mawu amenewa, inakhumudwa kwambiri+ ndipo inayamba kuganiza za mmene ingapulumutsire Danieli.+ Inakhala ikufunafuna njira yomupulumutsira mpaka dzuwa linalowa. 15  Pamapeto pake, amuna amphamvu amenewa anapita kwa mfumu ali chigulu ndipo anaiuza kuti: “Inu mfumu, mukudziwa kuti malamulo a Amedi ndi Aperisiya amanena kuti lamulo lililonse+ lokhazikitsidwa ndi mfumu siliyenera kusinthidwa.”+ 16  Zitatero mfumuyo inalamula kuti abweretse Danieli. Atabwera naye anamuponya m’dzenje la mikango.+ Koma mfumu inauza Danieli kuti: “Mulungu wako amene umamutumikira mosalekeza akupulumutsa.”+ 17  Ndiyeno anabweretsa mwala ndi kutseka pakhomo la dzenjelo. Kenako mfumu inadinda mwalawo ndi mphete yake yodindira ndipo nduna zakenso zinaudinda ndi mphete yawo yodindira, kuti chilichonse chokhudza Danieli chisasinthidwe.+ 18  Kenako mfumu inapita kunyumba yake yachifumu. Usiku umenewo mfumuyo inasala kudya+ ndipo sanaiimbire nyimbo ndi zipangizo zoimbira, komanso sinathe kugona tulo.+ 19  Ndiyeno kutangoyamba kuwala m’bandakucha, mfumuyo inadzuka ndipo inapita mofulumira kudzenje la mikango lija. 20  Itayandikira dzenjelo, inafuulira Danieli ndi mawu achisoni kuti: “Danieli mtumiki wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako amene umamutumikira mosalekeza+ wakupulumutsa kwa mikango?”+ 21  Nthawi yomweyo Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. 22  Mulungu wanga+ watumiza mngelo wake+ kudzatseka pakamwa pa mikango.+ Chotero mikangoyo sinandivulaze, chifukwa iye sanandipeze ndi mlandu uliwonse+ ndiponso sindinakulakwireni chilichonse inu mfumu.”+ 23  Pamenepo mfumuyo inasangalala kwambiri+ ndipo inalamula kuti Danieli amutulutse m’dzenjemo. Danieli anatulutsidwadi m’dzenjelo ndipo sanavulale paliponse chifukwa anakhulupirira Mulungu wake.+ 24  Zitatero, mfumu inalamula kuti abweretse amuna amphamvu amene ananenera Danieli zoipa aja,+ ndipo anawabweretsadi. Kenako anawaponya m’dzenje la mikango+ pamodzi ndi ana awo ndi akazi awo.+ Iwo asanafike n’komwe pansi pa dzenjelo, mikango inawakhadzulakhadzula ndi kuphwanya mafupa awo onse.+ 25  Ndiyeno mfumu Dariyo inalemba makalata opita kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana ndi anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana okhala padziko lonse lapansi,+ kuti: “Mukhale ndi mtendere wochuluka.+ 26  Ine ndikulamula+ kuti m’zigawo zonse za ufumu wanga, anthu azinjenjemera ndi kuchita mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli.+ Pakuti iye ndi Mulungu wamoyo, amene adzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo ufumu wake+ sudzawonongeka+ komanso ulamuliro wake udzakhalapo kwamuyaya.+ 27  Iye amapulumutsa ndi kulanditsa anthu ake,+ ndipo amachita zizindikiro komanso zinthu zodabwitsa kumwamba+ ndi padziko lapansi,+ moti wapulumutsa Danieli kwa mikango.” 28  Choncho zinthu zinamuyendera bwino Danieli mu ufumu wa Dariyo+ ndiponso mu ufumu wa Koresi Mperisiya.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.