Chichewa
Nkhani Zomwe Zangoikidwa Kumene Patsamba Loyamba la Webusaiti Yathu
/assets/ct/79e1b14fff/images/syn_placeholder_sqr.png

Nkhani Zomwe Zangoikidwa Kumene Patsamba Loyamba la Webusaiti Yathu

 

Akatswiri Achenjeza Kuti Kukhala Nyengo ya El Nino Yomwe ndi Yoopsa Kwambiri Komanso Yowononga

Nyengo ya El Nino yomwe ndi yoopsa kwambiri komanso yowononga ikhoza kusokoneza kwambiri nyengo padziko lonse. Kodi kusitha kwa nyengo kukukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo, nanga Baibulo limapereka chiyembekezo chotani?

Mawu A Mulungu Ndi Choonadi​—Buku Lothandiza Pophunzira Baibulo

Phunzirani mabuku a m’Baibulo lililonse palokhapalokha, ndipo phunzirani mozama pogwiritsa ntchito mfundo zothandiza zokhudza mbiri yakale, mfundo zachidule komanso mafunso.

Kuteteza Akazi—Zimene Baibulo Limanena

Mulungu amaona kuti akazi ayenera kutetezedwa. Onani chifukwa chake amaona choncho komanso zimene adzachite pothetsa nkhanza zonse zimene anthu amachitira akazi.

Kuthandiza Anthu Amene Ali ndi Vuto Losaona

Onani zimene a Mboni za Yehova akuchita pothandiza anthu amene ali ndi vuto losaona komanso amene amaona movutikira kuti amve uthenga wabwino wa m’Baibulo womwe ndi wopatsa chiyembekezo.

Kodi Patakhala Boma Labwino, Lingabweretse Mtendere Padziko Lonse?

Palibe boma la anthu limene lingakwanitse kubweretsa mtendere padziko lonse. Koma Mlengi wathu akhoza kuchita zimenezi ndipo adzachitadi.

Ndingatani Ngati Anthu Ena Amandivutitsa pa Intaneti?

Zimene muyenera kuchita komanso zimene mungachite kuti mudziteteze.

Kodi Mulungu Angayankhe Mapemphero Anga?

Kuti Mulungu ayankhe mapemphero anu zimadalira kwambiri pa zimene inuyo mumachita.

Yesu

Pezani mayankho a mafunso amene muli nawo okhudza Yesu kuchokera m’Mawu a Mulungu.

Kodi Baibulo Mungalikhulupirire?

Kuti mupeze yankho, yambani kuphunzira Baibulo kwaulere kumene kumachitika mokambirana.

 

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amadziona Kuti Ali Okhaokha?

Onani zimene zimayambitsa kuti anthu azidziona kuti ali okhaokha komanso zimene zimachititsa kuti vutoli likule.

Choonadi Chonena za Zimene Zidzachitike M’tsogolo

Werengani nkhaniyi kuti muzikhulupirira kwambiri zimene Mulungu amanena kuti zidzachitika m’tsogolo padzikoli komanso anthu amene adzakhalepo.

Kodi Yesu Ananena Chiyani Zokhudza “Zivomerezi Zamphamvu”?

’Zaka pafupifupi 2, 000 zapitazo, Yesu ananeneratu kuti kudzachitika zivomerezi zamphamvu. Nchifukwa chiyani mawu a Yesu amenewa ali ofunika kwambiri masiku ano?

Kodi Anthu Angathetse Nkhondo Komanso Zachiwawa?

Anthu akuyesetsa kuthetsa nkhondo komanso zachiwawa, koma kodi tiziyembekezera kuti angathetsedi nkhondo?

Kodi Kudziwa Zoti Mulungu Amatiganizira Kungatithandize Bwanji?

Malemba amatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro choti Mulungu adzakwaniritsa zimene watilonjeza.

Kodi Tingatani Kuti Tisamade Nkhawa Kwambiri?

Kodi ndi mavesi a m’Baibulo ati komanso zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri?