NSANJA YA OLONDA Na. 1 2020 | Kufufuza Choonadi

Baibulo limatiuza mayankho olondola a mafunso ofunika kwambiri okhudza moyo.

Kufufuza Choonadi

Ngakhale kuti masiku ano n’zovuta kukhulupirira munthu komanso anthu ambiri amapotoza choonadi, pali zimene mungachite kuti mupeze mayankho olondola a mafunso ofunika kwambiri okhudza moyo.

Baibulo ndi Lodalirika Ndipo Limatiuza Choonadi

Mungakhale ndi chikhulupiriro chonse kuti zimene Baibulo limanena tingazikhulupirire chifukwa ndi zoona.

Choonadi Chonena za Mulungu Komanso Khristu

Kodi Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu ndi osiyana bwanji?

Choonadi Chonena za Ufumu wa Mulungu

Baibulo limatithandiza kudziwa Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, kumene uli, cholinga chake, olamulira ake ndiponso nzika zake.

Choonadi Chonena za Zimene Zidzachitike M’tsogolo

Werengani nkhaniyi kuti muzikhulupirira kwambiri zimene Mulungu amanena kuti zidzachitika m’tsogolo padzikoli komanso anthu amene adzakhalepo.

Mmene Kudziwa Choonadi Kungakuthandizireni

Kudziwa choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu kungakuthandizeni kwambiri.