Pitani ku nkhani yake

Kodi Kusuta Ndi Tchimo?

Kodi Kusuta Ndi Tchimo?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo silinena chilichonse pa nkhani ya kusuta * kapena kunenapo chilichonse pa njira zina zogwiritsira ntchito fodya. Komabe, lili ndi mfundo zosonyeza kuti Mulungu amadana ndi zinthu zomwe zimawononga moyo komanso kuipitsa thupi la munthu. Choncho ndi zodziwikiratu kuti kusuta ndi tchimo.

  • Kulemekeza moyo. Baibulo limati, “Mulungu . . . amapatsa anthu onse moyo, [ndi] mpweya.” (Machitidwe 17:24, 25) Popeza kuti moyo ndi mphatso imene Mulungu anatipatsa, sitiyenera kuchita chilichonse chomwe chingawononge moyo wathu. Kusuta ndi chimodzi mwa zinthu zomwe zimachititsa kuti anthu azifa ndi matenda omwe akanatha kuwapewa.

  • Kukonda anzathu. Baibulo limati, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyu 22:39) Kusuta fodya anthu ena ali pomwepo, n’kupanda chikondi. Ndipotu anthu amene nthawi zambiri amapuma mpweya wa fodya chifukwa chokhala pafupi ndi munthu yemwe akusuta, amakhala pangozi yoti akhoza kudwala matenda ofanana ndi omwe anthu osutawo amavutika nawo.

  • Kufunitsitsa kukhala oyera. Baibulo limati, “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu.” (Aroma 12:1) Limanenanso kuti, “Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Munthu amene amasuta amaipitsa thupi lake ndipo sakhala woyera. Tikutero chifukwa choti mu fodya mumakhala poizoni yemwe amawononga thupi la munthu.

Kodi Baibulo limanenapo chilichonse pa nkhani yosuta chamba kapena kugwiritsa ntchito mankhwala aliwonse osokoneza bongo?

M’Baibulo mulibe mawu akuti chamba kapena dzina lililonse la mankhwala osokoneza bongo. Komabe muli mfundo zomveka bwino zosonyeza kuti kugwiritsa ntchito mankhwala a mtundu umenewu ndi kolakwika. Kuwonjezera pa mfundo zomwe tazitchula kale, taonaninso mfundo zotsatirazi:

  • Kukhala oganiza bwino. Baibulo limati, “Uzikonda Yehova Mulungu wako . . . ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37, 38) Limanenanso kuti, “Khalanibe oganiza bwino.” (1 Petulo 1:13) Munthu amalephera kuganiza bwinobwino akamagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndipo anthu ambiri omwe amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, sangathe kuchita chilichonse popanda mankhwalawo. Anthuwa amangokhalira kuganiza zosuta komanso mmene angapezere mankhwala ena m’malo moganizira zinthu zofunika kwambiri.​—Afilipi 4:8.

  • Kumvera malamulo a boma. Baibulo limati, ‘Muzimvera maboma ndiponso olamulira.’ (Tito 3:1) M’mayiko ena, boma limaika malamulo okhwima pa nkhani zokhudza kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Mulungu amasangalala tikamamvera akuluakulu a bomawa.​—Aroma 13:1.

^ ndime 1 Mawu akuti kusuta akutanthauza kupuma mwadala utsi wa fodya kaya kudzera m’ndudu kapena m’mapaipi. Ndipo mfundo za m’Baibulo zimagwiranso ntchito kwa anthu amene amachita kutafuna fodya, kununkhiza kapena kwa amene amagwiritsa ntchito mankhwala aliwonse osokoneza bongo..