NSANJA YA OLONDA December 2014 | Mulungu Akhoza Kukhala Mnzanu Wapamtima

Kodi mumaona kuti Mulungu ali kutali kwambiri moti n’zosatheka kukhala naye pa ubwenzi? Kodi mumaona kuti n’zotheka Mulungu kukhala mnzanu wapamtima?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi N’zotheka Mulungu Kukhala Mnzanu Wapamtima?

Pali anthu enanso ambiri amene amaona kuti Mulungu ndi mnzawo wapamtima.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mumadziwa Ndiponso Kutchula Dzina la Mulungu?

Kudzera m’Baibulo tingati Mulungu wakuuzani dzina lake kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.”

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mumalankhulana ndi Mulungu?

Timalankhula ndi Mulungu popemphera kwa iye, nanga iye amatilankhula bwanji?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mumachita Zomwe Mulungu Amafuna?

Mulungu amafuna kuti tizimumvera. Koma kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu kumafuna zambiri.

NKHANI YAPACHIKUTO

Palibe Chinthu Chabwino Kwambiri Kuposa Kukhala pa Ubwenzi Ndi Mulungu

Zinthu zitatu zomwe zingakuthandizeni kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima.

Kodi Mumzinda wa Timgad Munkachitika Zotani?

Aroma anakonza pulani kuti azitha kukhala mwamtendere ndi anthu a kumpoto kwa Africa.

ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Tiyenera Kudziwa pa Nkhani ya Khirisimasi?

Mungadabwe mutadziwa mmene zinthu zomwe zimachitika pa Khirisimasi zinayambira.

“Kuzindikira Kumachititsa Munthu Kubweza Mkwiyo”

Nkhani ya Davide, mfumu ya ku Isiraeli, ingakuthandizeni kuti muziugwira mtima munthu akakukhumudwitsani.

Kodi Ndibwerekedi Ndalama?

Mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita.

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi mungatani kuti muziphunzitsa ana anu mogwira mtima mfundo za m’Baibulo?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Mulungu Ndi Mphamvu Yosaoneka?

Baibulo limanena kuti Mulungu analenga zinthu zonse. Koma kodi iye amatiwerengera?