Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA

Kodi Mumachita Zomwe Mulungu Amafuna?

Kodi Mumachita Zomwe Mulungu Amafuna?

“Ukafuna kanthu uzingondiuza, ndizikupangira.” Kodi mungauze zimenezi munthu amene mwangokumana naye koyamba kapenanso amene simukumudziwa bwinobwino? Ayi, sizingatheke. Koma mukhoza kulankhula mawu amenewa kwa munthu amene ndi mnzanu wapamtima. Zili choncho chifukwa, mabwenzi amakonda kuchitirana zinthu zosiyanasiyana.

Baibulo limasonyeza kuti nthawi zonse Yehova amachita zinthu zomwe zingasangalatse atumiki ake. Mwachitsanzo Mfumu Davide, yemwe anali mnzake wapamtima wa Mulungu, anati: “Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa. . . . Zimachuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.” (Salimo 40:5) Kuwonjezera apa, Yehova amachitiranso zabwino ngakhale anthu omwe samudziwa n’komwe. Iye ‘amadzaza mitima yawo ndi chakudya komanso chimwemwe.’—Machitidwe 14:17.

Anthu amene timawakonda timawachitira zinthu zabwino

Popeza Yehova amasangalala kuchita zinthu zomwe zimakondweretsa anthu, nayenso amafuna kuti anthu omwe akufuna kukhala anzake, azichita zinthu zomwe zingasangalatse ‘mtima wake.’ (Miyambo 27:11) Koma kodi tingatani kuti tisangalatse Mulungu? Baibulo limatiuza kuti: “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.” (Aheberi 13:16) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kuchitira ena zabwino, monga kuwapatsa zinthu, n’kokwanira?

Ayi, chifukwa Baibulo limanenanso kuti: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” (Aheberi 11:6) Mwachitsanzo “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova,” ndipo kenako “anatchedwa ‘bwenzi la Yehova.’” (Yakobo 2:23) Yesu Khristu ananenanso kuti tiyenera ‘kukhulupirira Mulungu’ kuti atidalitse. (Yohane 14:1) Ndiye kodi mungatani kuti mukhale ndi chikhulupiriro chimene chingapangitse kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima? Nthawi zonse muyenera kuphunzira Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mudziwe “Mulungu molondola” komanso kuti “muzimukondweretsa pa chilichonse.” Mukadziwa zambiri zokhudza Yehova n’kumachita zimene mwaphunzirazo, mudzakhala ndi chikhulupiriro cholimba. Zimenezi zidzapangitsa kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima.—Akolose 1:9, 10.