Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Ndi Mphamvu Yosaoneka?

Kodi Mulungu Ndi Mphamvu Yosaoneka?

Yankho la m’Baibulo

 Mulungu amasonyeza mphamvu zake zopanda malire m’chilengedwe chonse. Ponena za nyenyezi mabiliyoni osawerengeka zimene analenga, Baibulo limati: “Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo? Ndi [Mulungu] amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezizo malinga ndi chiwerengero chake, ndipo amaziitana potchula iliyonse dzina lake. Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa, ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu, palibe imene imasowa.”—Yesaya 40:25, 26.

 Koma Mulungu alinso ndi makhalidwe ena kuwonjezera pa mphamvu. Baibulo limasonyeza kuti iye amatha kukonda kapena kudana ndi zinthu zinazake. (Salimo 11:5; Yohane 3:16) Baibulo limasonyezanso kuti Mulungu amakhudzidwa ndi zimene anthu amachita.—Salimo 78:40, 41.