Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi ana angaphunzire bwanji kukonda Mulungu?

Mungagwiritse ntchito zinthu zomwe Mulungu analenga pothandiza ana anu kudziwa komanso kukonda Mulungu

Ana anu angaphunzire kukonda Mulungu pokhapokha ngati ali ndi umboni woti iye alipo ndiponso amawakonda. Komanso ayenera kudziwa mfundo zosiyanasiyana zokhudza Mulungu. (1 Yohane 4:8) Mwachitsanzo, ayenera kudziwa mayankho a mafunso otsatirawa: Kodi Mulungu analengeranji anthu? N’chifukwa chiyani amalola kuti anthufe tizivutika? Kodi Mulungu adzawachitira chiyani anthu m’tsogolomu?—Werengani Afilipi 1:9.

Pofuna kuthandiza ana anu kuti azikonda Mulungu, muyenera kusonyeza kuti inunso mumakonda Mulungu. Ana anu akaona kuti mumakonda Mulungu, nawonso angayambe kumukonda.—Werengani Deuteronomo 6:5-7; Miyambo 22:6.

Kodi mungatani kuti muziphunzitsa ana anu mogwira mtima?

Mawu a Mulungu ndi amphamvu. (Aheberi 4:12) Choncho thandizani ana anu kudziwa mfundo zosavuta kumvetsa za m’Baibulo. Pophunzitsa, Yesu ankagwiritsa ntchito mafunso, ankamvetsera anthu akamalankhula komanso ankafotokoza Malemba. Izi zinachititsa kuti aziphunzitsa mogwira mtima. Inunso mukamachita zimenezi pophunzitsa ana anu, mungathe kuwafika pa mtima.—Werengani Luka 24:15-19, 27, 32.

Komanso, m’Baibulo muli nkhani zosonyeza mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi anthu. Nkhani zimenezi zingathandize ana anu kuti amudziwe bwino Mulungu komanso kuti azimukonda. Mabuku ofotokoza nkhani zoterezi akupezeka pa webusaiti ya www.jw.org/ny.—Werengani 2 Timoteyo 3:16.