Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi imfa ya Yesu imatipindulitsa bwanji?

Mulungu analenga anthu n’cholinga choti akhale ndi moyo kwamuyaya padziko lapansi. Sanafune kuti anthu azivutika ndi matenda komanso imfa. Komabe, munthu woyambirira, Adamu, sanamvere Mulungu. Zimenezi zinapangitsa kuti asakhalenso ndi moyo kwamuyaya. Popeza anthufe tinachokera kwa Adamu, nafenso timafa. (Aroma 5:8, 12; 6:23) Choncho, Yehova Mulungu anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti adzafe ndi kuwombola anthu kuti adzakhalenso ndi moyo wosatha umene Adamu anataya.—Werengani Yohane 3:16.

Yesu anafa n’cholinga choti anthu adzapeze moyo wosatha. Taganizirani mmene anthu adzasangalalire padzikoli imfa ikadzatha

Imfa ya Yesu inapangitsa kuti Mulungu azitikhululukira machimo komanso kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Baibulo limafotokoza mmene moyo udzakhalire wosangalatsa, ukalamba, matenda ndiponso imfa zikadzatha.—Werengani Yesaya 25:8; 33:24; Chivumbulutso 21:4, 5.

Kodi tizikumbukira bwanji imfa ya Yesu?

Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu analamula ophunzira ake kuti azikumbukira imfa yake pochita mwambo wachidule. Kukumbukira imfa ya Yesu pochita mwambo umenewu, kumatithandiza kuganizira kwambiri mmene Yehova ndi Yesu amatikondera anthufe.—Werengani Luka 22:19, 20; 1 Yohane 4:9, 10.

Chaka chino, mwambo wokumbukira imfa ya Yesu, udzachitika Lolemba pa April 14, dzuwa litalowa. Tikukuitanani kuti mudzapezeke pa mwambo umene a Mboni za Yehova adzachite kudera lanulo.—Werengani Aroma 1:11, 12.