Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zimene Mulungu Wakuchitirani?

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zimene Mulungu Wakuchitirani?

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Limeneli ndi limodzi mwa mavesi odziwika kwambiri m’Baibulo komanso limene anthu ambiri amakonda kulitchula. Anthu amanena kuti vesi ili lokha ndi limene “limafotokoza bwino mmene Mulungu amakondera anthu komanso mmene anthu angapezere chipulumutso.” Pa chifukwa chimenechi, anthu a m’mayiko ambiri amalemba vesili kapena mawu ake pagalimoto, pamalo pamene pakuchitikira zinthu zapadera komanso m’malo ena.

Anthu amene amachita zimenezi amakhulupirira kuti chikondi cha Mulungu chingawathandize kuti adzapeze chipulumutso. Kodi inuyo mumaiona bwanji nkhani imeneyi? Kodi chikondi cha Mulungu chimakukhudzani bwanji? Kodi mukuganiza kuti Mulungu anachita chiyani posonyeza kuti amakukondani inuyo?

“MULUNGU ANAKONDA DZIKO LAPANSI”

Anthu ambiri amayamikira kwambiri Mulungu chifukwa cha zinthu zonse zimene analenga, kuphatikizapo anthufe. Tinthu tamoyo tinapangidwa mogometsa zedi ndipo zimachita kuonekeratu kuti amene anapanga zimenezi ndi wanzeru kwambiri. Anthu ambiri tsiku lililonse amathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso ya moyo. Amadziwanso kuti Mulungu ndi amene amatipatsa zofunika zonse pa moyo monga mpweya, madzi, chakudya komanso nyengo zosiyanasiyana. Choncho kuti tikhale ndi moyo timadalira Mulunguyo.

Mpake kuti timathokoza Mulungu chifukwa cha zimenezi popeza iye ndi amene anatilenga komanso ndi amene amatisamalira. (Salimo 104:10-28; 145:15, 16; Machitidwe 4:24)  Tikaganizira zimenezi timaona kuti Mulungu amatikonda ndipo amafuna kuti tizisangalala ndi moyo. Pofotokoza mfundo imeneyi, mtumwi Paulo anati: “[Mulungu] amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. Pakuti chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.”—Machitidwe 17:25, 28.

Koma Mulungu anatisonyezanso chikondi m’njira ina. Anatipanga mosiyana kwambiri ndi nyama chifukwa anthufe timazindikira kufunika kolambira Mulungu ndipo timatha kuchita zimenezi. (Mateyu 5:3) Chifukwa cha zimenezi anthu omvera ali ndi chiyembekezo chodzakhala m’banja la Mulungu monga “ana” ake.—Aroma 8:19-21.

Monga mmene lemba la Yohane 3:16 likunenera, Mulungu anasonyeza kuti amatikonda potumiza Mwana wake, Yesu, padziko lapansi kuti adzatiphunzitse za Atate wake kenako n’kutifera. Koma anthu ambiri zimawavuta kumvetsa chifukwa chake zinali zofunika kuti Yesu afere anthu komanso chifukwa chake tingati imfa yakeyo ndi umboni woti Mulungu amatikonda. Tiyeni tione zimene Baibulo limanena kuti tidziwe chifukwa chake Yesu anafa komanso kufunika kwa imfa yake.

“ANAPATSA MWANA WAKE WOBADWA YEKHA”

Anthu onse amadwala, kukalamba ndiponso kufa. Koma zimenezi si zimene Mulungu ankafuna poyamba. Iye anapatsa anthu oyambirira chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Koma kuti zimenezi zitheke, iwo anafunika kumumvera. Mulungu ananena kuti akapanda kumvera lamulo lake, adzafa. (Genesis 2:17) Koma iwo sanamvere Mulungu komanso sanafune kuti aziwalamulira, ndipo izi zinabweretsa imfa kwa anthu onse. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, [Adamu] ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.”—Aroma 5:12.

Komabe Mulungu “amakonda chilungamo.” (Salimo 37:28) Ngakhale kuti Adamu anafunika kufa chifukwa cha kusamvera kwake, Mulungu sanalole kuti anthu onse azivutika komanso kufa mpaka kalekale chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi. Choncho, iye anatsatira mfundo yachilungamo yakuti “moyo kulipira moyo” ndipo anakonza zoti anthu omvera adzapeze moyo wosatha. (Ekisodo 21:23) Funso ndi lakuti, kodi zikanatheka bwanji kuti anthu akhalenso ndi moyo wangwiro ngati umene Adamu anali nawo asanachimwe? Yankho ndi loti: Panafunika wina woti apereke moyo wangwiro, wofanana ndi umene Adamu anataya.

Yesu anabwera padziko lapansi mosanyinyirika n’kudzapereka moyo wake kupulumutsa anthu ku uchimo ndi imfa

N’zodziwikiratu kuti palibe mbadwa ya Adamu imene ikanatha kupereka moyo wake kulipira moyo wangwiro umene Adamu anataya. Amene akanatha kuchita zimenezi anali Yesu basi. (Salimo 49:6-9) Popeza Yesu sanatengere uchimo umene anthu amabadwa nawo, anali wangwiro ngati mmene Adamu analili asanachimwe. Choncho pamene anapereka moyo wake, anawombola anthu ku ukapolo wauchimo. Apa ndiye kuti anapereka mwayi kwa ana onse a Adamu wodzakhala angwiro ngati mmene Adamu ndi Hava analili. (Aroma 3:23, 24; 6:23) Kodi ifeyo tingatani kuti  tipindule ndi chikondi chachikulu chimene Yehova ndi Yesu anasonyezachi?

“YENSE WAKUKHULUPIRIRA IYE”

Mbali ina ya lemba la Yohane 3:16 lija imati: “Yense wakukhulupirira [Yesu] asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Izi zikusonyeza kuti, tingapeze moyo wosatha pokhapokha titachita chinachake. Kuti tidzapeze “moyo wosatha,” tiyenera kukhulupirira Yesu komanso kumumvera.

Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi kumvera Yesu kumatanthauza chiyani? Kodi Yesu sananene kuti “yense wakukhulupirira Iye” adzapeza moyo wosatha?’ N’zoona kuti kukhulupirira n’kofunika. Komabe, tiyenera kukumbukira kuti Baibulo limasonyeza kuti kungokhulupirira kuti Yesu alipo sikokwanira. Buku lina lomasulira mawu limanena kuti, mawu amene Yohane anagwiritsa ntchito pavesili amatanthauza “kudalira munthu osati kungomukhulupirira chabe.” Kuti munthu akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, ayenera kuchita zambiri kuposa kungokhulupirira kuti Yesu ndi Mpulumutsi. Munthuyo ayenera kuyesetsa kumatsatira zimene Yesu anaphunzitsa. Munthu akakhala kuti sakuchita zinthu zosonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro, chikhulupiriro chakecho chimakhala chopanda ntchito. Baibulo limati: “Chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.” (Yakobo 2:26) Mwanjira ina tinganene kuti, munthu amene amakhulupirira Yesu ayenera kuchita zinthu zogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa.

Pofotokoza mfundo imeneyi, Paulo anati: “Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse . . . Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.” (2 Akorinto 5:14, 15) Ngati timayamikiradi nsembe ya Yesu, tidzakhala okonzeka kusintha moyo wathu n’kuyamba kutsatira zimene Yesu, yemwe anatifera, ankaphunzitsa. Izi zikusonyeza kuti kutsatira zimene Yesu ankaphunzitsa kuyenera kukhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu. Kuti zimenezi zitheke, tingafunike kusintha mfundo zimene timayendera, zinthu zimene timasankha pa moyo wathu komanso zinthu zina. Kodi anthu amene amatsatira zimene Yesu ankaphunzitsa adzapeza phindu lotani?

“ASATAYIKE, KOMA AKHALE NAWO MOYO WOSATHA”

Mbali yomaliza ya lemba la Yohane 3:16, imasonyeza zimene Mulungu adzachitire anthu amene amakhulupirira nsembe ya Yesu komanso kutsatira mfundo za m’Baibulo. Mulungu amafuna kuti anthu oterewa “asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Anthu ena adzalandira moyo wosatha umenewu kumwamba, pamene ena adzakhala padziko lapansi.

Yesu analonjeza gulu la anthu amene adzakhale ndi moyo wosatha kumwamba kuti akupita kukawakonzera malo n’cholinga choti azidzalamulira naye mu Ufumu wake. (Yohane 14:2, 3; Afilipi 3:20, 21) Amene adzapite kumwamba “adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.”—Chivumbulutso 20:6.

Ndi otsatira a Yesu ochepa chabe amene adzapeze mwayi umenewu. Ndipotu Yesu ananena kuti: “Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.” (Luka 12:32) Kodi ‘m’kagulu’ kameneka muli anthu angati? Lemba la Chivumbulutso 14:1, 4 limanena kuti: “Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa ataimirira paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo. . . . Iwowa anagulidwa kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.” Tikayerekezera anthu ambirimbiri amene akhalapo, anthu 144,000 ndi “kagulu” kochepa. Popeza anthu amenewa adzakhala mafumu, ndiye kodi adzalamulira ndani?

Yesu anatchulanso gulu lina la anthu amene adzalandire madalitso chifukwa cha Ufumu wakumwamba umenewu. Monga mmene lemba la Yohane 10:16 limanenera, Yesu ananena kuti: “Ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za khola ili, zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.” Anthu amenewa akuyembekezera kudzakhala ndi moyo padziko  lapansi ngati mmene zinalili ndi Adamu ndi Hava asanachimwe. Kodi tikudziwa bwanji kuti adzakhala padziko lapansi?

M’Baibulo muli mavesi ambiri omwe amafotokoza mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso padziko lapansi. Kuti mutsimikize zimenezi, tengani Baibulo lanu ndipo muwerenge Malemba otsatirawa: Salimo 37:9-11; 46:8, 9; 72:7, 8, 16; Yesaya 35:5, 6; 65:21-23; Mateyu 5:5; Yohane 5:28, 29 ndi Chivumbulutso 21:4. Malemba amenewa ananeneratu kuti nkhondo, njala, matenda komanso imfa, zidzatha. Ananenanso kuti anthu omvera adzamanga nyumba zawozawo, kulima minda yawo komanso kulera ana awo m’dziko lopanda mavuto. * Kodi zimenezi sizosangalatsa? N’zosakayikitsa kuti malonjezo amenewa adzakwaniritsidwa posachedwapa.

MULUNGU WAKUCHITIRANI ZINTHU ZAMBIRI

Ngati mutaganizira zimene Mulungu wachitira anthu onse komanso inuyo panokha, n’zoonekeratu kuti watichitira zinthu zambirimbiri. Watipatsa moyo, nzeru komanso zinthu zina zimene zimapangitsa kuti tizisangalala ndi moyo. Koposa zonse, anatipatsanso nsembe ya dipo la Yesu, ndipo ingatithandize kuti tidzapeze madalitso ambirimbiri ngati mmene lemba la Yohane 3:16 likunenera.

Anthu adzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso mmene simudzakhala matenda, nkhondo, njala, komanso imfa. Izi zidzapangitsa kuti tidzasangalale ndi moyo kwamuyaya. Kuti mudzalandire nawo madalitso amenewa, zikudalira zimene inuyo mumachita pa moyo wanu. Choncho funso ndi lakuti, kodi inuyo mukumuchitira chiyani Mulungu?

^ ndime 24 Kuti mudziwe zambiri za malonjezo amenewa, werengani mutu 3 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.