Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingatani Kuti Tizikondabe Kulalikira?

Kodi Tingatani Kuti Tizikondabe Kulalikira?

NTCHITO yolalikira ndi yofunika kwambiri padziko lonse. Atumiki a Yehovafe timaona kuti kugwira nawo ntchitoyi ndi mwayi waukulu kwambiri. Koma nthawi zina, apainiya ndi ofalitsa angavutike kukondabe ntchito yolalikira.

Tizikambirana ndi munthu amene tikulalikira naye

Enafe tikakhala mu utumiki timavutika kupeza anthu ofuna kumva uthenga wathu ndipo m’nyumba zina sitipeza anthu. Anthu ena amene timawapeza amakhala opanda chidwi kapena aukali. Abale ndi alongo ena amapeza anthu ambiri ofuna kuphunzira koma amada nkhawa poona kuti gawo lawo lawakulira. Ndiye pali ena amene alalikira kwa nthawi yaitali kuposa imene ankayembekezera moti panopa akugwa mphwayi.

Koma sitiyenera kudabwa ndi mavuto amene amatigwetsa mphwayi pa ntchito yolalikira. Tikutero chifukwa chakuti sizingakhale zophweka kulalikira uthenga wabwino m’dziko limene lili m’manja mwa Satana Mdyerekezi.1 Yoh. 5:19.

Kaya mukukumana ndi mavuto otani, dziwani kuti Yehova akhoza kukuthandizani. Koma kodi tingatani kuti tizikondabe kulalikira? Tiyeni tikambirane zinthu zingapo.

TIZITHANDIZA ATSOPANO

Chaka chilichonse anthu masauzande ambiri amabatizidwa. Ngati mwabatizidwa posachedwapa, mungathandizidwe ndi abale ndi alongo amene akhala akulalikira kwa nthawi yaitali. Ngati mwakhala mukulalikira kwa zaka zambiri, mungachite bwino kuthandiza anthu atsopano. Mukamachita zimenezi mudzakhala osangalala.

Yesu ankadziwa kuti ophunzira ake akufunika kuthandizidwa kuti azidzalalikira mogwira mtima. Choncho iye anawaphunzitsa mmene angachitire zimenezi. (Luka 8:1) Masiku anonso ofalitsa atsopano ayenera kuthandizidwa.

Tisamaganize kuti atsopano adzadziwa okha kuphunzitsa bwino chifukwa choti amalalikira. Zinthu zingawayendere ngati anthu ena akuwaphunzitsa mokoma mtima. Anthuwo angawaphunzitse (1) kukonzekera zimene anganene mu utumiki, (2) kukambirana ndi anthu, (3) kugawira mabuku, (4) kuchita maulendo obwereza ndiponso (5) kuyambitsa phunziro la Baibulo. Mosakayikira, zinthu zidzawayendera bwino ofalitsa atsopanowo akamatsatira njira zimene aphunzitsidwa. (Luka 6:40) Iwo angayamikire kwambiri kuyenda ndi munthu amene angawathandize, kuwayamikira kapena kuwapatsa malangizo.Mlal. 4:9, 10.

TIZIKAMBIRANA NDI AMENE TIKUYENDA NAYE

Tikakhala mu utumiki timayesetsa kulankhula ndi anthu ambiri koma nthawi zina timalimbikitsidwa kwambiri tikamalankhulana ndi amene tikuyenda naye. Kumbukirani kuti Yesu ankatumiza ophunzira ake “awiriawiri.” (Luka 10:1) Anachita zimenezi chifukwa chodziwa kuti anthuwo akamayenda limodzi akhoza kuthandizana ndiponso kulimbikitsana. Choncho tikamayenda mu utumiki ndi munthu wina tiziyesetsa kulimbikitsana.Aroma 1:12.

Kodi tingakambirane nkhani ziti? Mwina tingakambirane zinthu zolimbikitsa zimene takumana nazo. Kapena tingakambirane mfundo yochititsa chidwi imene tapeza pophunzira Baibulo patokha kapena ndi banja lathu. Apo ayi, tingauze mnzathuyo mfundo yolimbikitsa imene tinamva pa misonkhano. Nthawi zina timayenda ndi munthu amene sitikumudziwa bwino. Tikhoza kumufunsa zimene zinamuthandiza kukhala wa Mboni za Yehova. Tingamufunse zimene zinamutsimikizira kuti gulu la Yehova ndi lomweli. Kapenanso tingamufunse zimene wachita m’gulu la Yehova ndiponso zinthu zimene wakumana nazo pa moyo wake. Nafenso tingamuuze zimene takumana nazo. Kaya tipeza anthu ofuna kumva uthenga wathu kapena ayi, tikamayenda ndi anzathu mu utumiki timakhala ndi mwayi wolimbikitsana.1 Ates. 5:11.

TIZIPHUNZIRA BAIBULO MWAKHAMA

Kuphunzira Baibulo mwakhama n’kothandizanso kuti tizikonda kulalikira. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amafalitsa nkhani zosiyanasiyana m’mabuku athu. (Mat. 24:45) Choncho pali nkhani zambirimbiri zimene mungaphunzire. Mwina mungaphunzire nkhani zoyankha funso ili: Kodi ntchito yolalikira ndi yofunika bwanji? Bokosi limene lili patsamba 16 likufotokoza kufunika kwake.

Mfundo za m’bokosili zingakuthandizeni kuti muzikondabe kulalikira. Koma mungachite bwino kufufuza mfundo zina zokulimbikitsani kukonda ntchito yolalikira. Ndiyeno muyenera kuganizira kwambiri mfundozo komanso malemba ake. Izi zingakuthandizeni kuti muzikonda kwambiri utumiki.

TIZITSATIRA MALANGIZO AMENE TAPATSIDWA

Gulu la Yehova limapereka malangizo otithandiza kugwira bwino ntchito yolalikira. Kuwonjezera pa kulalikira kunyumba ndi nyumba, tikhoza kulalikiranso pogwiritsa ntchito mafoni ndi makalata. Tingapitenso m’malo opezeka anthu ambiri, m’misewu, m’maofesi ndiponso m’mashopu. Tingalalikirenso mwamwayi kwina kulikonse. Kapenanso tingakonze zokalalikira kumadera kumene kulibe a Mboni ambiri.

Kodi inuyo munayesapo kuchita zimenezi? Anzanu ambiri atsatira malangizowa ndipo akusangalala kwambiri. Tiyeni tione zitsanzo zitatu.

Chitsanzo choyamba ndi cha mlongo April amene anatsatira malangizo a mu Utumiki wathu wa Ufumu okhudza kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Chifukwa chotsatira malangizowa, iye anayambitsa maphunziro ndi anthu atatu amene ankagwira nawo ntchito. Iye anasangalala kwambiri anthu onsewa atavomera n’kuyambanso kupezeka pa misonkhano.

Chitsanzo china ndi cha woyang’anira dera wa ku United States. Iye anatsatira malangizo oti tiziona nkhani za m’magazini n’kuganizira anthu amene angazikonde. Ataona nkhani yonena za matayala mu Galamukani!, anapita kwa mabwana a m’masitolo ogulitsa matayala n’kukawapatsa. Iye ndi mkazi wake anakaperekanso Galamukani! yonena za madokotala m’maofesi a madokotala oposa 100. M’baleyu anati: “Zimene tinachitazi zinathandiza anthu kudziwa bwino za ntchito yathu komanso mabuku athu. Zathandizanso kuti tichite maulendo obwereza ambiri.”

Chitsanzo chachitatu ndi cha mlongo Judy amene anatsatira malangizo okhudza ulaliki wa pa foni. Mlongoyu analembera kalata kulikulu lathu yoyamikira malangizowa. Iye anafotokoza kuti mayi ake ali ndi zaka 86 ndipo amadwaladwala. Koma mayiwo amalalikira pa foni ndipo akusangalala kwambiri chifukwa njira imeneyi yawathandiza kuti aziphunzira ndi mayi wina wazaka 92.

Malangizo amene timapatsidwa ndi othandiza kwambiri, choncho ndi bwino kuwatsatira. Akhoza kutithandiza kuti tizikondabe kulalikira ndiponso tizisangalala.

TIZIKHALA NDI ZOLINGA ZIMENE TINGAKWANITSE

Ena amaganiza kuti akuchita bwino mu utumiki ngati amagawira mabuku ambiri, kuchititsa maphunziro ambiri kapena ngati athandiza anthu ambiri kuti ayambe kutumikira Yehova. Koma zimenezi si zoona. Nowa anangothandiza anthu am’banja lake okha kuti atumikire Yehova. Koma sitinganene kuti sanagwire bwino ntchito yolalikira. Chofunika kwambiri ndi kukhala wokhulupirika kwa Yehova.1 Akor. 4:2.

Abale ndi alongo ambiri amaona kuti kukhala ndi zolinga zimene angakwanitse kumawathandiza kuti azikondabe kulalikira. Kodi tingakhale ndi zolinga zotani? Onani zina m’bokosi limene lili pambalipa.

Yesetsani kuchita zimene mungathe kuti muzisangalala ndiponso kuchita bwino mu utumiki ndipo dziwani kuti Yehova adzakudalitsani. Mukakwaniritsa zolinga zanu mudzasangalala kwambiri podziwa kuti mukuchita zonse zimene mungathe kuti mulalikire uthenga wabwino.

N’zoona kuti kulalikira uthenga wabwino kungakhale kovuta. Koma pali zinthu zimene zingakuthandizeni kuti muzilalikira mwakhama. Takambirana kuti tizilimbikitsana ndi munthu amene tayenda naye, tiziphunzira Baibulo mwakhama, tizitsatira malangizo amene kapolo wokhulupirika amatipatsa ndiponso tizikhala ndi zolinga zimene tingakwaniritse. Koma chofunika kwambiri ndi kukumbukira kuti Mulungu watipatsa mwayi wamtengo wapatali wokhala Mboni zake ndiponso wolalikira uthenga wabwino. (Yes. 43:10) Tikamayesetsa kukondabe utumiki tidzakhala osangalala kwambiri.