Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu a ku Japan Analandira Mphatso

Anthu a ku Japan Analandira Mphatso

MSONKHANO wapadera unachitika mumzinda wa Nagoya ku Japan pa April 28, 2013. Tikaphatikiza anthu amene analipo ndi amene ankamvetsera m’malo ena, anali 210,000. Pa msonkhanowu, anthu anasangalala kwambiri pamene M’bale Anthony Morris, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira, anatulutsa Kabaibulo katsopano m’Chijapanizi kakuti Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyu. Anthu onse amene anamvetsera anawomba m’manja kwa nthawi yaitali.

Uthenga wa Mateyuwu unatengedwa m’Baibulo la Dziko Latsopano lachijapanizi. Kabaibuloka ndi kapadera ndipo kali ndi masamba 128. M’bale Morris anafotokoza kuti kanalembedwa “m’njira yoyenerera anthu a ku Japan.” Kodi kanalembedwa bwanji? N’chifukwa chiyani kanalembedwa? Ndipo kodi anthu akusangalala nako?

KODI KANALEMBEDWA BWANJI?

Anthu anadabwa ndi mmene analembera Kabaibuloka. Zilembo zachijapanizi zingalembedwe m’mizere yopita pansi kapena yopita m’mbali. Magazini ndi mabuku ambiri amalembedwa m’mizere yopita m’mbali. N’chimodzimodzi ndi mabuku athu aposachedwapa. Koma Kabaibuloka kalembedwa m’mizere yopita pansi mofanana ndi mabuku ena ndiponso nyuzipepala zambiri. Anthu ambiri a ku Japan amaona kuti mabuku olembedwa m’njirayi ndi osavuta kuwerenga. Komanso mawu opezeka pamwamba pa tsamba lililonse analembedwa pakati pa mavesi ngati timitu. Anachita zimenezi n’cholinga choti anthu aziona mosavuta mfundo zikuluzikulu.

Abale ndi alongo a ku Japan atangolandira Kabaibuloka anayamba kukawerenga nthawi yomweyo. Mlongo wina wazaka za m’ma 80 anati: “Ndawerenga buku la Mateyu mobwerezabwereza. Koma kuwerenga Kabaibulo kolembedwa m’mizere yotsika pansi komanso kokhala ndi timituto kunandithandiza kumvetsa kwambiri ulaliki wa paphiri.” Mlongo wina wachitsikana analemba kuti: “Nditayamba kuwerenga kabuku ka Mateyu kameneka sindinakasiye mpaka nditakamaliza. Ineyo ndazolowera mabuku a mizere yopita m’mbali koma anthu ambiri ku Japan amakonda a mizere yopita pansi.”

N’KOYENERADI ANTHU A KU JAPAN

N’chifukwa chiyani tinganene kuti Kabaibuloka n’koyeneradi anthu a ku Japan? Anthu ambiri a ku Japan sadziwa zambiri zokhudza Baibulo koma amafuna kuliwerenga. Kabukuka kathandiza kuti anthu amene sanaonepo Baibulo akhale ndi mwayi woona mbali yake n’kuiwerenga.

N’chifukwa chiyani anasankha buku la Mateyu polemba kabukuka? Anthu ambiri a ku Japan akaganiza za Baibulo amaganizanso za Yesu Khristu. Choncho anasankha buku la Mateyu chifukwa muli mndandanda wa makolo onse a Yesu, nkhani ya kubadwa kwake, ulaliki wake wa paphiri ndiponso ulosi wake wochititsa chidwi wokhudza masiku otsiriza. Izi ndi nkhani zimene anthu a ku Japan angachite nazo chidwi.

 Abale ndi alongo anayamba kugwira mwakhama ntchito yopereka Kabaibuloka kunyumba ndi nyumba komanso pa maulendo obwereza. Mlongo wina analemba kuti: “Panopa ndikhoza kugawira Mawu a Mulungu kwa anthu ambiri moti ndinapereka kabuku ka Mateyu kwa munthu wina pa tsiku lomwelo la msonkhano wapaderawu.”

KODI ANTHU AKUSANGALALA NAKO?

Kodi ofalitsa amanena chiyani pofuna kugawira kabuku ka Mateyu? Anthu ambiri ku Japan amadziwa mawu monga akuti ‘chipata chopapatiza,’ “kuponyera nkhumba ngale” komanso akuti “musamade nkhawa za tsiku lotsatira.” (Mat. 6:34; 7:6, 13) Iwo amadabwa kumva kuti Yesu Khristu ndi amene ananena mawuwa. Akaona mawuwa m’buku la Mateyu, ambiri amati: “Kuyambira kale ndakhala ndikufuna kuwerenga Baibulo.”

Ofalitsa akabwereranso kwa anthuwo, ambiri amanena kuti anawerenga mbali zina kapena Kabaibulo konse atangokalandira. Bambo wina wazaka za m’ma 60 anauza wofalitsa wina kuti: “Ndinawerenga kabukuka mobwerezabwereza ndipo kandilimbikitsa. Ndiphunzitseni zambiri zokhudza Baibulo.”

Anthu akugwiritsanso ntchito Kabaibuloka polalikira m’malo opezeka anthu ambiri. Mlongo wina anapereka adiresi yake ya imelo kwa mtsikana wina amene anakalandira. Patangopita ola limodzi, mtsikanayo analembera mlongoyu imelo n’kumuuza kuti anali atawerenga mbali ina ya Kabaibuloka ndipo ankafuna kudziwa zambiri. Patapita mlungu umodzi, anayamba kuphunzira Baibulo ndipo pasanapite nthawi anayamba kupita ku misonkhano.

Timabaibulo takuti Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyu toposa 1,600,000 tatumizidwa kumipingo ya ku Japan. Ndiyeno mwezi uliwonse a Mboni akugawira masauzande ambiri a Timabaibuloti. Mawu oyamba amafotokoza cholinga cha ofalitsa ake ponena kuti: “Tikufunitsitsa kuti kabukuka kakuthandizeni kukhala ndi mtima wofuna kuphunzira Baibulo.”