NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) February 2015

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzira kuyambira pa April 6 mpaka pa May 3, 2015.

Anthu a ku Japan Analandira Mphatso

Kabaibulo katsopano kakuti ‘Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyu’ kanatulitsidwa ku Japan. Kodi kanalembedwa bwanji? N’chifukwa chiyani kanalembedwa?

Khalani Odzichepetsa Ndiponso Achifundo Ngati Yesu

Lemba la 1 Petulo 2:21 limatilimbikitsa kutsatira mosamala mapazi a Yesu. Kodi anthu ochimwafe tingatani kuti tikhale odzichepetsa ndiponso achifundo ngati Yesu?

Khalani Olimba Mtima Ndiponso Ozindikira Ngati Yesu

Baibulo limatithandiza kudziwa bwino makhalidwe a Yesu. Onani zimene tingachite kuti tikhale olimba mtima ndiponso ozindikira ngati Yesu.

Kodi Tingatani Kuti Tizikondabe Kulalikira?

Tikudziwa kuti kulalikira uthenga wabwino ndi ntchito yofunika kuposa ntchito iliyonse. Kodi tingatani kuti tizikondabe kwambiri utumiki?

Zinthu Zimene Zinathandiza Kuti Anthu Aphunzire za Yehova

Kodi Akhristu oyambirira anakwanitsa bwanji kulalikira uthenga wabwino? Kodi ndi zinthu ziti zimene zinathandiza kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino kwambiri m’nthawi ya atumwi?

Yehova Akutsogolera Ntchito Yolalikira Padziko Lonse

Kodi ndi zinthu ziti zimene zathandiza kuti atumiki a Yehova azilalikira padziko lonse?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi tingachite chiyani pothandiza abale ndi alongo amene amavutika akamva fungo la perefyumu? Kodi mu utumiki mlongo ayenera kuvala chinachake kumutu pa nthawi ziti?

KALE LATHU

“Nyengo Yofunika Kwambiri”

Nsanja ya Olonda inanena kuti nthawi ya Chikumbutso inali “nyengo yofunika kwambiri” ndipo inalimbikitsa anthu kuti azipezeka pa mwambowu. Kodi kalelo anthu ankachita bwanji mwambo wa Chikumbutso?