Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukutsatira Machenjezo a Yehova Omveka Bwino?

Kodi Mukutsatira Machenjezo a Yehova Omveka Bwino?

Kodi Mukutsatira Machenjezo a Yehova Omveka Bwino?

“Njira ndi iyi. Yendani mmenemu anthu inu.”​—YES. 30:21.

1, 2. Kodi Satana ali ndi cholinga chotani, nanga Mawu a Mulungu amatithandiza bwanji?

CHIKWANGWANI chimene chimaloza kumalo olakwika chikhoza kukusocheretsani ndipo mukachitsatira mukhoza kukumana ndi mavuto. Tiyerekeze kuti mnzanu wina wakuchenjezani kuti pali munthu wina woipa kwambiri amene wasintha chikwangwani chinachake n’cholinga choti asocheretse anthu. Kodi simungatsatire chenjezo la mnzanuyo?

2 Satana ndi mdani wathu woipa kwambiri ndipo ali ndi cholinga chotisocheretsa. (Chiv. 12:9) Iye ndi amene anayambitsa zinthu zonse zoipa zimene tinakambirana m’nkhani yapita ija. Satana wachita zimenezi pofuna kuti tisochere n’kusiya njira ya ku moyo wosatha. (Mat. 7:13, 14) Koma chosangalatsa n’chakuti Mulungu wathu wachifundo amatichenjeza kuti tisapusitsidwe ndi Satana. Tiyeni tikambirane zinthu zina zitatu zimene Satana amasocheretsa nazo anthu ndiponso mmene Mawu a Mulungu amatithandizira kuti tisasocheretsedwe. Tikamawerenga Baibulo tingachite bwino kukhala ndi maganizo oti Yehova ali kumbuyo kwathu ndipo akutiuza kuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu anthu inu.” (Yes. 30:21) Kukambirana machenjezo omveka bwino a Yehova kutithandiza kuti tikhale ndi mtima wofuna kuwatsatira.

Musatsatire “Aphunzitsi Onyenga”

3, 4. (a) Kodi aphunzitsi onyenga amafanana bwanji ndi zitsime zouma? (b) Kodi aphunzitsi onyenga kawirikawiri amachokera kuti ndipo cholinga chawo chimakhala chiyani?

3 Tayerekezani kuti muli pa ulendo wodutsa m’chipululu chotentha kwambiri ndipo mukumva ludzu. Ndiyeno chakutsogolo mukuona chitsime ndipo mukupita pachitsimecho kuti mukamwe madzi. Kodi mungamve bwanji ngati mutafika pachitsimecho n’kupeza kuti n’chouma? Mukhoza kukhumudwa kwambiri. Aphunzitsi onyenga ali ngati zitsime zouma. Munthu aliyense amene angapite kwa anthu amenewa kuti akapeze madzi a choonadi adzakhumudwa kwambiri. Kudzera mwa mtumwi Paulo ndi Petulo, Yehova anapereka chenjezo lokhudza aphunzitsi onyenga. (Werengani Machitidwe 20:29, 30; 2 Petulo 2:1-3.) Kodi aphunzitsi onyengawa ndi ndani? Mawu ouziridwa a atumwi awiriwa amatithandiza kudziwa kumene aphunzitsi onyengawa amachokera ndiponso mmene amachitira zinthu.

4 Paulo anauza akulu a mu mpingo wa ku Efeso kuti: “Pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka.” Nayenso Petulo anauza Akhristu anzake kuti: “Padzakhala aphunzitsi onyenga pakati panu.” Ndiyeno kodi aphunzitsi onyenga amachokera kuti? Iwo angachokere mu mpingo. Anthu oterewa amakhala ampatuko. * Kodi cholinga chawo n’chiyani? Cholinga chawo si kungochoka m’gulu limene poyamba ankalikonda. Paulo ananena kuti cholinga chawo ndi ‘kupatutsa ophunzira kuti aziwatsatira.’ Apa Paulo akunena za ophunzira a Khristu. Aphunzitsi onyengawa sapita kwina kuti akapange ophunzira, m’malomwake amafuna kuba ophunzira a Khristu mu mpingo. Yesu ananena kuti aphunzitsi onyenga ali ngati “mimbulu yolusa” imene imafuna kudya nkhosa. Iwo amafuna kuwononga chikhulupiriro cha anthu mu mpingo n’cholinga choti nawonso asiye choonadi.​—Mat. 7:15; 2 Tim. 2:18.

5. Kodi aphunzitsi onyenga amachita zinthu m’njira yotani?

5 Kodi aphunzitsi onyenga amachita zinthu m’njira yotani? Amachita zinthu mochenjera kwambiri. Ampatuko amabweretsa maganizo oipa mu mpingo “mwakachetechete” ngati mmene zigawenga zimalowetsera mozemba katundu m’dziko. Anthu achinyengo akhoza kusintha zikalata zachabechabe kuti zioneke ngati zenizeni. N’chimodzimodzinso ndi anthu ampatuko. Iwo amagwiritsa ntchito “mawu achinyengo” kuti achititse mfundo zawo kuoneka ngati zoona. Iwo amaphunzitsa “zinthu zonyenga” ndiponso ‘kupotoza Malemba’ kuti agwirizane ndi mfundo zawo. (2 Pet. 2:1, 3, 13; 3:16) Apa n’zodziwikiratu kuti anthu ampatuko satifunira zabwino. Tikawatsatira tidzasochera n’kusiya njira ya ku moyo wosatha.

6. Kodi Baibulo limatipatsa malangizo omveka bwino ati okhudza aphunzitsi onyenga?

6 Kodi tingatani kuti tisasocheretsedwe ndi aphunzitsi onyenga? Baibulo limatiuza momveka bwino zoyenera kuchita ndi aphunzitsi onyengawa. (Werengani Aroma 16:17; 2 Yohane 9-11.) Mawu a Mulungu amati: “Muziwapewa.” Izi zikutanthauza kuti sitiyenera kuwayandikira ngakhale pang’ono. Tiyerekeze kuti dokotala wakuuzani kuti musayandikire munthu wina amene ali ndi matenda opatsirana omwe ndi akupha. Simungavutike kumvetsa zimene dokotalayo akunena ndipo mudzatsatira kwambiri chenjezo limeneli. Ampatuko ali ngati munthu wamatenda opatsirana. Iwo amagwiritsa ntchito ziphunzitso zawo zoipa kuti asokoneze maganizo a anthu ena n’kuwachititsa kuti aziganiza ngati iwowo. (1 Tim. 6:3, 4) Yehova monga Dokotala Wamkulu akutiuza kuti anthu amenewa tiyenera kuwapewa. Tikudziwa zimene Yehova akutanthauza, koma kodi ifeyo tatsimikiza mtima kutsatira chenjezo limeneli nthawi zonse?

7, 8. (a) Kodi tingapewe bwanji aphunzitsi onyenga? (b) N’chifukwa chiyani mumakana kwamtuwagalu aphunzitsi onyenga?

7 Kodi tingapewe bwanji aphunzitsi onyenga? Sitiwalandira m’nyumba zathu kapena kuwapatsa moni. Timakananso kuwerenga mabuku awo, kuwaonera pa TV ndiponso kuwerenga kapena kuyankha zimene alemba pa Intaneti. N’chifukwa chiyani timawakana kwamtuwagalu? Chifukwa chakuti timakonda “Mulungu wachoonadi” ndipo timadana ndi ziphunzitso zopotoka zimene zimasemphana ndi Mawu ake a choonadi. (Sal. 31:5; Yoh. 17:17) Timakondanso gulu la Yehova limene latiphunzitsa mfundo zosangalatsa za choonadi. Mwachitsanzo, taphunzira za dzina lakuti Yehova ndi tanthauzo lake, cholinga chimene Mulungu analengera dziko lapansi, zimene zimachitika munthu akamwalira ndiponso chiyembekezo chakuti akufa adzauka. Kodi mukukumbukira mmene munamvera mutangophunzira mfundo zamtengo wapatali ngati zimenezi? Musalole kuti mabodza amene aphunzitsi onyenga amanena akuchititseni kupandukira gulu la Mulungu limene lakuphunzitsani mfundo za choonadi zimenezi.​—Yoh. 6:66-69.

8 Kaya aphunzitsi onyenga anene zotani, ife sitingawatsatire. Titati tiwatsatire tikhoza kukhumudwa kwambiri chifukwa ali ngati zitsime zouma. M’malomwake, tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. Gulu limeneli silinatikhumudwitsepo ndipo kwa nthawi yaitali lakhala likutipatsa madzi oyera a choonadi ochokera m’Mawu a Mulungu.​—Yes. 55:1-3; Mat. 24:45-47.

Musatsatire “Nkhani Zonama”

9, 10. M’kalata yopita kwa Timoteyo, kodi Paulo anapereka chenjezo lotani lokhudza “nkhani zonama,” ndipo mwina Paulo ankanena za chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi.)

9 Nthawi zina zimakhala zosavuta kudziwa kuti chikwangwani chasinthidwa ndipo chikuloza kumalo olakwika. Koma nthawi zina zimakhala zovuta. N’chimodzimodzi ndi mabodza a Satana. Ena ndi osavuta kuwazindikira pamene ena ndi ovuta. Mtumwi Paulo anatichenjeza kuti Satana amagwiritsa ntchito “nkhani zonama.” (Werengani 1 Timoteyo 1:3, 4.) Koma kodi nkhani zonama ndi ziti ndipo tingazipewe bwanji? Tiyenera kupeza mayankho a mafunso amenewa kuti tisasochere n’kusiya njira ya ku moyo wosatha.

10 Chenjezo la Paulo lokhudza nkhani zonama lili m’kalata yoyamba imene analembera Timoteyo. Pa nthawiyo, Timoteyo anali mkulu wachikhristu ndipo anali ndi udindo woteteza mpingo ku zinthu zodetsa komanso wothandiza Akhristu anzake kukhala okhulupirika. (1 Tim. 1:18, 19) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “nkhani zonama” amatanthauza “nkhani zopeka” kapena “nthano.” Buku lina limanena kuti mawu oti “nkhani zonama” amatanthauza “nkhani (yachipembedzo) imene imanena za zinthu zimene sizinachitike.” (The International Standard Bible Encyclopaedia) Mwina Paulo ankanena za mabodza achipembedzo ochokera m’nthano zakalekale zimene anthu ankakonda kukamba ndiponso kumvetsera. * Paulo ananena kuti nkhani zimenezi si zabwino chifukwa “zimangoyambitsa mafunso.” Iye ankatanthauza kuti anthu amene amamvetsera nkhanizi amayamba kudzifunsa mafunso pa nkhani zabodza n’kumataya nthawi yawo pofufuza mayankho. Satana amagwiritsa ntchito nkhani zonama zimenezi ndiponso mabodza achipembedzo n’cholinga choti anthu asiye kuganizira zinthu zofunika kwambiri. N’chifukwa chake Paulo anapereka malangizo omveka bwino akuti: Musamvere nkhani zonama.

11. Kodi Satana akugwiritsa ntchito bwanji chipembedzo chonyenga kusocheretsa anthu ndipo tiyenera kutsatira chenjezo liti kuti tisasocheretsedwe?

11 Ngati sitisamala, kodi nkhani zina zabodza zimene zingatisocheretse ndi ziti? Mawu akuti “nkhani zonama” angatanthauze mabodza alionse achipembedzo kapena nthano zimene zingatichititse ‘kusiya kumvetsera choonadi.’ (2 Tim. 4:3, 4) Satana ndi wochenjera ndipo amagwiritsa ntchito chipembedzo chonyenga kuti asocheretse anthu. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti iye amadzisandutsa “mngelo wa kuwala.” (2 Akor. 11:14) Mwachitsanzo, matchalitchi amene amati ndi achikhristu amaphunzitsa mabodza. Iwo amati Mulungu ndi Utatu, anthu oipa amazunzidwa kumoto komanso amati mzimu wa munthu sufa. Matchalitchi amenewa amalimbikitsanso zikondwerero za Khirisimasi ndi Isitala. Anthu ambiri amaganiza kuti zikondwerero zimenezi zimasangalatsa Mulungu. Koma zinthu zimene anthu amachita pa zikondwererozi n’zochokera m’kulambira konyenga. Kuti tipewe kusocheretsedwa ndi nkhani zonama tiyenera kutsatira chenjezo lakuti tilekane nawo ndiponso ‘tisakhudze chinthu chodetsedwa.’​—2 Akor. 6:14-17.

12, 13. (a) Tchulani mabodza amene Satana amalimbikitsa ndiponso mfundo zoona pa bodza lililonse. (b) Kodi tingapewe bwanji kusocheretsedwa ndi nkhani zabodza zimene Satana amalimbikitsa?

12 Satana akulimbikitsanso mabodza ena amene akhoza kutisocheretsa ngati sitisamala. Tiyeni tikambirane mabodza atatu amtunduwu. Bodza loyamba ndi lakuti: Mungachite zilizonse zimene mukufuna. Mungasankhe nokha zimene ndi zabwino kapena zoipa. Mfundo imeneyi imatchulidwatchulidwa pa TV, m’mafilimu, m’magazini, m’manyuzipepala ndiponso pa Intaneti. Popeza timamva zimenezi nthawi ndi nthawi m’posavuta kuti tipusitsidwe n’kumayendera maganizo oipa a m’dzikoli. Koma zoona zake n’zakuti ifeyo timafunikira kuti Mulungu azititsogolera. (Yer. 10:23) Bodza lachiwiri ndi lakuti: Mulungu sadzasintha chilichonse padzikoli. Maganizo amenewa amachititsa anthu kuti asamaganizire za m’tsogolo ndiponso kuti asamakondweretse Mulungu. Ife tikatengera maganizo amenewa tingayambe kukhala “ozilala kapena osabala zipatso” mu utumiki wathu. (2 Pet. 1:8.) Koma zoona zake n’zakuti tsiku la Yehova likubwera mofulumira ndipo tiyenera kuliyembekezera. (Mat. 24:44) Bodza lachitatu ndi lakuti: Mulungu alibe nafe ntchito. Kukhulupirira bodza la Satana limeneli kungatichititse kutaya mtima n’kumadziona ngati anthu achabechabe amene Mulungu sangatikonde. Koma zoona zake n’zakuti Yehova amatikonda ndipo amafunira zabwino mtumiki wake aliyense payekha.​—Mat. 10:29-31.

13 Tiyenera kusamala kwambiri chifukwa chakuti maganizo amene afala m’dziko la Satanali angaoneke ngati abwino ndiponso olondola. Tisaiwale kuti Satana ndi katswiri pa nkhani yopusitsa anthu. Ngati tikufuna kuti tisapusitsidwe ndi “nkhani zabodza zopekedwa mochenjera,” tiyenera kutsatira malangizo ndiponso mfundo za m’Mawu a Mulungu.​—2 Pet. 1:16.

‘Musatsatire Satana’

14. Kodi Paulo anapereka chenjezo lotani kwa akazi ena amasiye, nanga n’chifukwa chiyani tonsefe tiyenera kutsatira chenjezoli?

14 Tayerekezani kuti mwapeza chikwangwani chonena kuti “Mukafuna Kutsatira Satana, Dzerani Uku.” Kodi mungatsatire chikwangwani choterocho? Mtumwi Paulo anatchula njira zingapo zimene zingachititse kuti Akhristu odzipereka kwa Mulungu ‘apatutsidwe n’kumatsatira Satana.’ (Werengani 1 Timoteyo 5:11-15.) M’kalatayi Paulo ankanena za akazi ena omwe anali “akazi amasiye achitsikana” koma mfundo zake zimagwiranso ntchito kwa tonsefe. M’nthawi ya Paulo akazi achikhristu amenewa sankadziwa kuti akutsatira Satana koma zochita zawo zinkasonyeza kuti ankamutsatiradi. Kodi tingapewe bwanji kutsatira Satana mosazindikira? Tiyeni tikambirane chenjezo la Paulo pa nkhani ya miseche.

15. Kodi cholinga cha Satana n’chiyani, nanga Paulo anafotokoza bwanji njira zimene Satana amagwiritsa ntchito?

15 Satana amafuna kuti tisamalankhule za chikhulupiriro chathu ndiponso kuti tisiye kulalikira uthenga wabwino. (Chiv. 12:17) Kuti akwanitse zimenezi, iye amayesetsa kutichititsa kutaya nthawi yathu ndi zinthu zosathandiza kapena zimene zingatichititse kudana. Paulo anatchula zinthu zina zimene Satana amagwiritsa ntchito pofuna kuti tichite zofuna zake. Ananena kuti akazi amasiyewo anali ndi “chizolowezi chomangokhala osachita kanthu, n’kumangoyendayenda.” Masiku ano, zipangizo zamakono zili ponseponse ndiye n’zosavuta kuti tiziwononga nthawi yathu ndiponso ya anthu ena potumizirana mauthenga osathandiza kwenikweni ngakhalenso abodza. Paulo ananenanso kuti akazi amasiyewo anali “amiseche.” Zimakhala zosavuta kuti munthu wamiseche ayambe kunena mabodza oipitsa anthu ena ndipo izi zimayambitsa mikangano. (Miy. 26:20) Munthu aliyense amene amanena mabodza oipitsa anthu ena amakhala akutsanzira Satana Mdyerekezi kaya mozindikira kapena mosazindikira. * Kenako Paulo ananena kuti akazi amasiyewo ankakonda ‘kulowerera nkhani za eni.’ Palibe munthu amene ali ndi udindo womauza ena zochita pa nkhani zimene aliyense angasankhe yekha. Zinthu zonsezi n’zosathandiza ndipo zingatisokoneze kuti tisiye kugwira ntchito yolalikira Ufumu imene Mulungu watipatsa. Tikasiya kugwira nawo ntchito imene Yehova watipatsa, timakhala tikutsatira Satana. Munthu aliyense ayenera kusankha kukhala mbali ya Yehova kapena ya Satana ndipo n’zosatheka kukhala wopanda mbali.​—Mat. 12:30.

16. Kodi tiyenera kutsatira malangizo ati ngati sitikufuna ‘kupatuka n’kuyamba kutsatira Satana’?

16 Kumvera malangizo a m’Baibulo kungatithandize kuti ‘tisapatuke n’kuyamba kutsatira Satana.’ Paulo anaperekanso malangizo ena amene angatithandize. Iye ananena kuti tiyenera ‘kukhala ndi zochita zambiri mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Kukhala ndi zochita zambiri m’ntchito ya Yehova kungatithandize kuti tipewe zinthu zosafunika zimene zingatiwonongere nthawi ndiponso kutibweretsera mavuto. (Mat. 6:33) Paulo ananenanso kuti mawu athu azikhala “olimbikitsa.” (Aef. 4:29) Tiyenera kupeweratu kulankhula kapena kumvetsera miseche. (Onani bokosi lakuti “Kuulutsa Nthenga.”) Tizikhulupirira Akhristu anzathu ndiponso kuwalemekeza. Tikatero, tizilankhula mawu olimbikitsa osati oyambitsa mikangano. Paulo ananenanso kuti tiyenera kupewa ‘kulowerera mu nkhani za eni.’ (1 Ates. 4:11) Ndi bwino kusonyeza kuti timaganizira ena komabe m’pofunika kuwalemekeza popewa kulowerera m’nkhani zawo zimene sizikutikhudza kapena zimene sakufuna kuuza ena. Tiyeneranso kupewa kuuza ena zochita pa nkhani zimene aliyense ayenera kusankha yekha.​—Agal. 6:5.

17. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amatipatsa machenjezo amene takambiranawa? (b) Kodi inuyo mwatsimikiza kuchita chiyani pa nkhani yoyenda pa njira imene Yehova akutilozera?

17 Tikusangalala kwambiri kuti Yehova watiuza zinthu zimene sitiyenera kutsatira. Tiyenera kukumbukira kuti Yehova watipatsa machenjezo amene ali m’nkhani ino ndiponso amene ali m’nkhani yapita ija chifukwa choti amatikonda kwambiri. Iye safuna kuti tipusitsidwe ndi Satana n’kugwera m’mavuto. Njira imene Yehova akutiuza kuti tidutse ndi yopanikiza koma ndi yokhayo imene imapita ku moyo wosatha. (Mat. 7:14) Tiyeni tiziyesetsa nthawi zonse kutsatira malangizo a Yehova akuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu.”​—Yes. 30:21.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mawu akuti “mpatuko” amatanthauza kupanduka n’kusiya kulambira koona.

^ ndime 10 Chitsanzo cha nkhani zonama zimene zinalipo m’nthawi ya Paulo ndi buku la Tobit (kapena kuti Tobias) limene anthu ena amaganiza kuti ndi mbali ya Baibulo. Bukuli linalembedwa zaka za m’ma 200 B.C.E. ndipo lili ndi nkhani zambiri zabodza ndiponso zamatsenga. Nkhani zake zimakhala zoti sizingachitike koma m’bukuli anazilemba ngati kuti ndi zoona.​—Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 122.

^ ndime 15 Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “mdyerekezi” amatanthauza “munthu amene amanena mabodza oipitsa mbiri ya munthu wina.” Mdyerekezi ndi dzina linanso la Satana chifukwa chakuti ndi amene anayamba kunena mabodza oipitsa munthu wina.​—Yoh. 8:44; Chiv. 12:9, 10.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi machenjezo amene ali m’malemba otsatirawa mungawagwiritse ntchito bwanji pa moyo wanu?

2 Petulo 2:1-3

1 Timoteyo 1:3, 4

1 Timoteyo 5:11-15

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 19]

Kuulutsa Nthenga

Pali nthano ina ya Ayuda imene imasonyeza kuopsa kwa miseche.

Munthu wina ankafalitsa nkhani zabodza zonena za munthu wanzeru kwambiri wa m’mudzi mwawo. Tsiku lina munthu wabodzayo anafuna kuti munthu wanzeruyo amukhululukire. Ndiyeno anafunsa munthuyo kuti: “Ndichite chiyani kuti mudziwe zoti ndikumva chisoni kwambiri ndi mabodza okhudza inuyo amene ndakhala ndikufalitsa?” Munthu wanzeruyo anayankha kuti: “Pali chinthu chimodzi chimene uyenera kuchita. Utenge pilo wanthenga n’kumung’amba ndipo ukatero uulutse nthenga zonse zimene zili mkatimo.” Ngakhale kuti munthuyo sanamvetse cholinga chake, anakachitadi zimenezi. Kenako anabwerera kwa munthu wanzeru uja n’kumufunsa kuti:

“Kodi tsopano mwandikhululukira?”

Munthu wanzeruyo anayankha kuti: “Ayi. Upite kukatolera kaye nthenga zonse zimene waulutsa zija.”

Munthuyo anayankha kuti: “Zimenezo sizingatheke. Mphepo yabalalitsa nthenga zija moti sindingazipeze zonse.”

Ndiyeno munthu wanzeruyo anati: “Mofanana ndi nthenga zimene zapita kutali ndipo sungazipezenso, mabodza ako afalikira kwa anthu ambirimbiri ndipo n’zosatheka kuti anthuwo aiwale.”

Kodi mwaona phunziro limene lili m’nthanoyi? Munthu sangafafanize zimene wanena ndipo sangasinthe zotsatira zoipa za mabodza amene wanena. Choncho tisanayambe kufalitsa miseche, ndi bwino kukumbukira kuti mawu athu ali ngati nthenga zomwe zingaulutsidwe ndi mphepo.

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi anthu ena amaitanira bwanji ampatuko m’nyumba zawo?